Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Angelo Kuti Atithandize?

Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Angelo Kuti Atithandize?

Kodi Tiyenera Kupemphera kwa Angelo Kuti Atithandize?

KODI m’poyenera kupemphera kwa angelo kuti atithandize panthaŵi ya mavuto? Anthu ambiri amaganiza choncho. Moti buku lakuti New Catholic Encyclopedia limati: “Munthu amapemphera kwa . . . angelo . . . koma ndi cholinga choti iwo atiimire kwa Mulungu basi.” Kodi tiyenera kupempha angelo kuti atiimire kwa Mulungu?

M’Mawu a Mulungu muli mayina a angelo aŵiri okha okhulupirika a Mulungu, omwe ndi Mikaeli ndi Gabrieli. (Danieli 8:16; 12:1; Luka 1:26; Yuda 9) Popeza kuti mayinaŵa amatchulidwa m’Baibulo, ndiye kuti mngelo aliyense ndi munthu wauzimu payekha wokhala ndi dzina, osati mphamvu chabe. Komabe, angelo ena anakana kuulula mayina awo. Mwachitsanzo, Yakobo atam’funsa dzina mngelo amene anamuyendera, iye anakana kumuuza dzinalo. (Genesis 32:29; Oweruza 13:17, 18) M’Baibulo mulibe mndandanda wa mayina a angelo, pofuna kuti anthu asamakhale ndi chidwi kwambiri ndi angelowo.

Zina mwa ntchito za angelo ndi kupereka kwa anthu mauthenga a Mulungu. Ndipo mawu a Chihebri ndi Chigiriki choyambirira omwe anatembenuzidwa kuti “mngelo” kwenikweni amatanthauza “mthenga.” Koma sikuti angelo amakhala amkhalapakati ofikitsa mapemphero a anthu kumpando wa Wam’mwambamwamba. Mulungu anakonza zakuti mapemphero aziperekedwa kwa iye m’dzina la Mwana wake, Yesu Kristu, yemwe anati: ‘Chilichonse mukapempha Atate m’dzina langa akakupatsani inu.’​—Yohane 15:16; 1 Timoteo 2:5.

Yehova Mulungu satanganidwa kwambiri moti n’kulephera kutimvetsera ngati tam’fikira moyenerera. Baibulo limatitsimikizira izi: “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m’choonadi.”​—Salmo 145:18.