Kulalikira Anthu Kuntchito Kwawo
Olengeza Ufumu Akusimba
Kulalikira Anthu Kuntchito Kwawo
KODI n’chiyani chinali chofanana pakati pa mtumwi Mateyu, mtumwi Petro, mtumwi Andreya, mtumwi Yakobo, ndi mtumwi Yohane? Onseŵa anaitanidwa ndi Yesu ali pantchito zawo. Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane anali kalikiliki pantchito yawo yosodza pamene Yesu anawaitana, kuti: “Tiyeni pambuyo panga.” Mateyu anali mu ofesi yokhometsera msonkho pamene anaitanidwa kuti akhale wophunzira wa Yesu.—Mateyu 4:18-21; 9:9.
Kulalikira anthu kuntchito kwawo kungakhale ndi zotsatirapo zabwino. Pozindikira zimenezi, Mboni za Yehova ku Japan posachedwapa zinaikira mtima kwambiri pa ulaliki wamtunduwu. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Patangotha miyezi yoŵerengeka yokha, Mbonizo zinapanga maulendo obwereza ambirimbiri, ndipo zinayambitsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 250. Taonani zochitika zotsatirazi.
Mtumiki wina wa nthaŵi zonse ku Tokyo anakumana ndi bwana wa lesitiranti ina amene anali atalankhulapo ndi Mboni pafupifupi zaka 30 m’mbuyomo, akali mwana wa sukulu. Ngakhale kuti bwanayo sankamvetsa zambiri mwa zinthu zimene ankauzidwa nthaŵi yomwe anali pasukuluyo, koma anakhala ndi chidwi ndi Baibulo. Tsopano popeza chidwicho chinayambiranso, iye anavomera mofulumira phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Kuwonjezera apo, iye anayamba kuŵerenga Baibulo payekha madzulo aliwonse asanakagone.
Mpainiya wina wapadera anapita ku ofesi ina. Ngakhale kuti bwana wa paofesipo sanali mu ofesi mwake, mtsikana amene anayankha telefoni ya mu ofesi mwa bwanayo anafunsa kuti, “Kodi mungakonde kulankhula ndi ine?” Atalankhulana pang’ono patelefonipo, mtsikanayo anabwera pamalo olandirira alendo n’kunena kuti ali ndi chidwi choŵerenga Baibulo. Mpainiya wapaderayo anakonza zopitanso ku ofesiyo ndi Baibulo ndipo anayamba naye phunziro la Baibulo, lomwe ankachitira pamitengo ina pafupi ndi ofesiyo nthaŵi ya ntchito isanakwane.
Pa ofesi ina, bambo wina anaona mzake wogwira naye ntchito akulandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! koma anawataya mwamsanga Mboniyo itangochoka. Bamboyo atapita kunyumba, anafotokozera mkazi wake yemwe ndi wa Mboni za nkhaniyi ndipo anati akanakhala iye akanamvetserako pang’ono. Mwana wake wamkazi, yemwe ankamva zonena za bamboyo, anakafotokoza nkhaniyi kwa Mboni ina imene inkalalikira m’dera lomwe bamboyo amagwira ntchito. Mboniyo inakafika mofulumira ku ofesi ya mwamunayo ndi kuyamba naye phunziro la Baibulo. Pasanapite nthaŵi, bamboyo anayamba kufika pamisonkhano ya Lamlungu nthaŵi zonse.
Kulalikira anthu kuntchito kwawo kwakhala kopindulitsanso m’njira zina zambiri. Ofalitsa ambiri ku Japan tsopano apeza luso lochitira maulendo obwereza ku masitolo, mafakitale, ndi ku maofesi. Kuwonjezera apo, polalikira mwa njira imeneyi, apeza anthu ambiri omwe anasiya kulalikira ndipo ayambanso kuphunzira nawo. Zotsatirapo zake zakhala zabwino kwambiri. Mpingo wina wa m’katikati mwa Tokyo posachedwapa unapereka lipoti la maphunziro a Baibulo a panyumba 108. Maphunziroŵa anali oposa kuwirikiza kaŵiri maphunziro omwe mpingowu unaperekera lipoti chaka chimodzi m’mbuyo mwake.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.