Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chifukwa chiyani pa 1 Akorinto 10:8 amanena kuti Aisrayeli amene anaphedwa tsiku limodzi chifukwa chochita dama anali 23,000 pamene pa Numeri 25:9 amati anali 24,000?

Pali zifukwa zingapo zimene zingachititse kuti pakhale kusiyana kwa manambala amene awatchula m’mavesi aŵiriŵa. Chifukwa chosavuta chingakhale chakuti chiŵerengero chenicheni chinali pakati pa 23,000 ndi 24,000, zimene ngati munthu atalemba m’masauzande mokha angalembe 23,000 kapena 24,000.

Taonani chifukwa chinanso chimene chingakhale kuti n’chimene chinachititsa zimenezo. Mtumwi Paulo ananena zimene zinachitikira Aisrayeli ku Sitimu monga chitsanzo chowachenjeza Akristu a ku mzinda wakale wa Korinto, umene unali wotchuka ndi chiwerewere. Iye analemba kuti: “Tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.” Paulo anatchula nambalayo kuti inali 23,000 pofuna kungopatulapo anthu amene Yehova anawapha chifukwa choti anachita dama.​—1 Akorinto 10:8.

Koma mu Numeri chaputala 25, amatiuza kuti “Israyeli anaphatikana ndi Baala Peori, Mulungu anapsa mtima pa Israyeli.” Ndiyeno Yehova analamula Mose kuti aphe “akulu onse a anthu.” Naye Mose anauza oweruza kuti achite zimene Yehova anamulamulazo. Kenako, pamene Pinehasi anachitapo kanthu mwamsanga kupha Mwiisrayeli amene anabweretsa mkazi wachimidyani mumsasa, “mliri unaletseka.” Nkhaniyo ikumaliza ndi mawu akuti: “Akufa nawo mliri ndiwo zikwi makumi aŵiri ndi zinayi.”​—Numeri 25:1-9.

Nambala imene aitchula m’buku la Numeri mwachionekere inaphatikizapo “akulu onse a anthu” amene anaphedwa ndi oweruza ndiponso anthu amene anaphedwa mwachindunji ndi Yehova. Zingatheke kuti akulu a anthuwo amene anaphedwa ndi oweruza analipo okwana wani sauzande, zimene zinachititsa kuti nambalayo ikwane 24,000. Kaya akulu ameneŵa, kapena kuti atsogoleri, anachita nawo dama, mapwando, kapena kugwirizana ndi anthu amene anachita zimenezo, koma anali ndi mlandu ‘wophatikana ndi Baala Peori.’

Pankhani ya liwu lakuti “kuphatikana,” buku lina lofotokozera Baibulo linanena kuti liwuli lingatanthauze kuti “kudzigwirizanitsa ndi munthu wina.” Aisrayeli anali anthu odzipatulira kwa Yehova, koma pamene “anaphatikana ndi Baala Peori,” anachita zinthu zosemphana ndi kudzipatulira kwawo kwa Mulungu. Patapita zaka pafupifupi 700, Yehova ananena za Aisrayeli kudzera mwa mneneri Hoseya kuti: “Anadza kwa Baala Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.” (Hoseya 9:10) Anthu onse amene anachita zimenezo anayenerera kulangidwa ndi Mulungu. Motero, Mose anakumbutsa ana a Israyeli kuti: “Maso anu anapenya chochita Yehova chifukwa cha Baala Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala Peori, Yehova Mulungu wanu anawawononga pakati panu.”​—Deuteronomo 4:3.