Anthu a Mulungu Ayenera Kukonda Khalidwe la Kukoma Mtima
Anthu a Mulungu Ayenera Kukonda Khalidwe la Kukoma Mtima
“Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo [“kukoma mtima,” NW] ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—MIKA 6:8.
1, 2. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti Yehova amafuna kuti anthu ake azisonyeza kukoma mtima? (b) Kodi ndi mafunso ati okhudza kukoma mtima amene tifunika kuwapenda?
YEHOVA ndi Mulungu wachifundo kapena kuti wokoma mtima. (Aroma 2:4; 11:22) Anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava ayenera kuti anayamikira kwambiri zimenezo. M’munda wa Edene, anthuŵa anali kuona zinthu zolengedwa zimene zinapereka umboni wakuti Mulungu amakomera mtima anthu, amene akanasangalala nazo zinthuzo. Ndipo Mulungu akupitiriza kukomera mtima anthu onse, ngakhale osayamika ndi oipa.
2 Popeza anthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, iwo angathe kusonyeza makhalidwe a Mulunguyo. (Genesis 1:26) N’zosadabwitsa kuti Yehova amafuna kuti tizisonyeza kukoma mtima. Monga mmene Mika 6:8 amanenera, anthu a Mulungu ayenera “kukonda kukoma mtima.” Koma kodi kukoma mtima n’kutani? Kodi khalidweli limagwirizana bwanji ndi makhalidwe ena a Mulungu? Popeza anthu angathe kusonyeza kukoma mtima, n’chifukwa chiyani anthu m’dzikoli ndi ankhanza ndiponso osaganizirana? N’chifukwa chiyani ife monga Akristu tiyenera kuyesetsa kusonyeza kukoma mtima pochita zinthu ndi anthu ena?
Kodi Kukoma Mtima N’kutani?
3. Kodi kukoma mtima mungakufotokoze bwanji?
3 Kukoma mtima kumasonyezedwa mwa kufunira zabwino anthu ena. Kumasonyezedwa mwa kuchita zinthu zothandiza ena ndiponso mwa mawu oganizira ena. Kukhala wokoma mtima kumatanthauza kuchita zabwino, osachita zinthu zimene zingapweteke ena. Munthu wokoma mtima ndi wochezeka, wofatsa, wachifundo, ndiponso wachisomo. Amakhala wowoloŵa manja ndiponso amaganizira anthu ena. Mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti: “Valani . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima.” (Akolose 3:12) Motero, kukoma mtima ndi mbali ya chovala chophiphiritsira cha Mkristu woona aliyense.
4. Kodi Yehova ali patsogolo motani pankhani yosonyeza kukoma mtima kwa anthu?
4 Yehova Mulungu ndi amene ali patsogolo pankhani yosonyeza kukoma mtima. Monga mmene Paulo anafotokozera, nthaŵi imene “kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka” ndi pamene “anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera.” (Tito 3:4, 5) Mulungu ‘amatsuka’ kapena kuti kuyeretsa Akristu odzozedwa m’mwazi wa Yesu, zimene zikutanthauza kuti amagwiritsa ntchito mtengo wa nsembe ya dipo ya Kristu m’malo mwawo. Amawapanganso kukhala atsopano kudzera mwa mzimu woyera n’kukhala ‘olengedwa atsopano’ monga ana a Mulungu obadwa ndi mzimu. (2 Akorinto 5:17) Ndiponso, kukoma mtima kwa Mulungu ndi chikondi chake amazisonyezanso kwa a “khamu lalikulu,” amene “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.”—Chivumbulutso 7:9, 14; 1 Yohane 2:1, 2.
5. N’chifukwa chiyani anthu amene amatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu ayenera kusonyeza kukoma mtima?
5 Kukoma mtima ndi mbalinso ya chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito. Paulo anati: “Chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.” (Agalatiya 5:22, 23) Motero, anthu amene amatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu ayenera kusonyeza kukoma mtima kwa ena, kodi si choncho?
Kukoma Mtima Kwenikweni Si Kufooka
6. Kodi ndi pa zochitika zotani pamene kukoma mtima kumakhala kufooka, ndipo chifukwa chiyani?
6 Anthu ena amaona ngati kukoma mtima n’kufooka. Amaganiza kuti munthu ayenera kukhala wouma mtima, ngakhale kuchita mwano kumene nthaŵi zina, kuti anthu ena azidziŵa kuti ndi wamphamvu. Komabe, zoona zake n’zakuti munthu amafunika kukhala wamphamvu kuti asonyeze kukoma mtima kwenikweni ndi kupeŵa kusonyeza kukoma mtima kolakwika. Popeza kukoma mtima kwenikweni ndi mbali ya chipatso cha mzimu wa Mulungu, silingakhale khalidwe lofooka, lololera zinthu zolakwika. Koma kukoma mtima kolakwika n’kufooka, kumene kumachititsa munthu kulekelera zinthu zolakwika.
7. (a) Kodi Eli anasonyeza bwanji kulekerera? (b) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kusamala kuti asasonyeze kukoma mtima kolakwika?
7 Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya mkulu wansembe wa ku Israyeli, Eli. Iye analekerera osalanga ana ake, Hofeni ndi Pinehasi, amene anali kugwira ntchito ya unsembe pa chihema. Chifukwa chosakhutira ndi gawo la nsembe limene anapatsidwa malinga ndi Chilamulo cha Mulungu, iwo anali kuuza anyamata kuti munthu wopereka nsembe aziwapatsa nyama yaiwisi asanapsereze mafuta pa guwa la nsembe. Ana a Eli analinso kugona ndi akazi amene anali kutumikira pakhomo la chihema. Komabe, Eli m’malo mochotsa Hofeni ndi Pinehasi pantchito ya unsembe, anangowadzudzula pang’ono. (1 Samueli 2:12-29) N’zosadabwitsa kuti “masiku aja mawu a Yehova anamveka kamodzikamodzi.” (1 Samueli 3:1) Akulu achikristu ayenera kusamala kuti asasonyeze kukoma mtima kolakwika kwa anthu olakwa omwe angaike pangozi moyo wauzimu wa mpingo. Kukoma mtima kwenikweni sikunyalanyaza mawu ndi zochita zoipa zimene zimaswa mfundo za Mulungu.
8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kukoma mtima kwenikweni?
8 Yesu Kristu, Chitsanzo chathu, sanasonyeze n’kamodzi komwe kukoma mtima kolakwika. Iye anali chitsanzo chabwino cha kukoma mtima kwenikweni. Mwachitsanzo, ‘anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha anthu, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, okunga nkhosa zopanda mbusa.’ Anthu oona mtima anali omasuka kulankhula ndi Yesu, ngakhale kudza ndi tiana tawo kwa iye. Taganizirani kukoma mtima ndi chifundo chimene anasonyeza pamene “anatiyangata, natidalitsa.” (Mateyu 9:36; Marko 10:13-16) Ngakhale kuti Yesu anali wokoma mtima, anali wolimba pa zinthu zimene zinali zoyenera pamaso pa Atate wake wakumwamba. Yesu sanalekerere zoipa; anali ndi mphamvu zimene Mulungu anam’patsa zodzudzula atsogoleri achipembedzo onyenga. Malinga ndi mmene Mateyu 23:13-26 amafotokozera, anabwereza nthaŵi zingapo kunena kuti: “Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga!”
Kugwirizana kwa Kukoma Mtima ndi Makhalidwe Ena a Mulungu
9. Kodi kukoma mtima kumagwirizana bwanji ndi kuleza mtima ndi ubwino?
9 Kukoma mtima kumagwirizana ndi makhalidwe ena a mzimu wa Mulungu monga kuleza mtima ndi ubwino. Ndipotu, munthu amene amakulitsa kukoma mtima amasonyeza khalidwe limeneli mwa kukhala woleza mtima. Amaleza mtima ngakhale kwa anthu omwe si okoma mtima. Kukoma mtima kumagwirizana ndi ubwino m’njira yakuti nthaŵi zambiri munthu amasonyeza
kukoma mtima mwa kuchita zinthu zabwino zoti zipindulitse anthu ena. Nthaŵi zina, mawu achigiriki amene anawagwiritsa ntchito m’Baibulo omwe awamasulira kuti “kukoma mtima” angamasuliridwenso kuti “ubwino.” Pamene Akristu oyambirira anali kusonyeza khalidwe limeneli, anthu achikunja anadabwa nazo kwambiri moti anatcha otsatira a Yesuwo kuti ndi ‘anthu a khalidwe la kukoma mtima,’ malinga ndi zimene Tertullian analemba.10. Kodi kukoma mtima ndi chikondi n’zogwirizana bwanji?
10 Pali kugwirizana pakati pa kukoma mtima ndi chikondi. Yesu ananena za ophunzira ake kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Ndipo ponena za chikondi chimenechi, Paulo anati: “Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima.” (1 Akorinto 13:4) Kukoma mtima kumagwirizananso ndi chikondi m’liwu lakuti “kukoma mtima kwachikondi,” limene lagwiritsidwa ntchito nthaŵi zambiri m’Malemba. Uku ndi kukoma mtima kumene kumakhalapo chifukwa cha chikondi chokhulupirika. Liwu lachihebri limene analimasulira kuti “kukoma mtima kwachikondi” limaphatikizapo zambiri osati kungomukonda chabe munthu. Ndi kukoma mtima kumene kumadziphatika mwachikondi ku chinthu chinachake mpaka cholinga chake chokhudza chinthucho chitakwaniritsidwa. Kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova, kapena kuti chikondi chake chokhulupirika, amakusonyeza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amasonyeza zimenezi mwa kupulumutsa ndi kuteteza anthu.—Salmo 6:4; 40:11; 143:12. *
11. Kodi kukoma mtima kwachikondi kwa Mulungu kumatichititsa kukhala ndi chikhulupiriro chotani?
11 Kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova kumachititsa anthu kumuyandikira. (Yeremiya 31:3) Atumiki okhulupirika a Mulungu akafuna kuti awapulumutse kapena kuwathandiza, amadziŵa kuti kukoma mtima kwake kwachikondi kulidi chikondi chokhulupirika. Sikudzawagwiritsa fuwa lamoto. Motero, angapemphere ndi chikhulupiriro, monga mmene anachitira wamasalmo amene ananena kuti: “Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.” (Salmo 13:5) Popeza chikondi cha Mulungu n’chokhulupirika, atumiki ake angam’khulupirire ndi mtima wonse. Amakhala ndi chikhulupiriro chakuti “Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholandira chake.”—Salmo 94:14.
N’chifukwa Chiyani Anthu M’dzikoli Ndi Ankhanza?
12. Kodi ndi liti pamene ulamuliro wopondereza unayambika ndipo unayambika bwanji?
12 Yankho la funso limeneli lagona pa zimene zinachitika m’munda wa Edene. Kuchiyambiyambi kwa mbiri ya anthu, wolengedwa wauzimu amene anakhala wodzikonda ndiponso wodzikuza anayamba kuchita zinthu zoti akhale wolamulira wa dziko lonse. Chifukwa cha zimene anachita, anakhaladi “mkulu wa dziko ili lapansi,” ndipo anakhala mkulu kapena kuti wolamulira wopondereza kwambiri. (Yohane 12:31) Anadzatchedwa Satana Mdyerekezi, wotsutsa wamkulu wa Mulungu ndiponso wotsutsa anthu. (Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9) Zinthu zodzikonda zimene ankaganiza zofuna kukhazikitsa ulamuliro wotsutsana ndi ulamuliro wokoma mtima wa Yehova zinaonekera pasanapite nthaŵi yaitali Hava atalengedwa. Motero, ulamuliro woipa unayambika Adamu atasankha kudziimira payekha osadalira ulamuliro wa Mulungu, kukaniratu kukoma mtima Kwake. (Genesis 3:1-6) M’malo modzilamuliradi okha, Adamu ndi Hava anayamba kulamulidwa ndi Mdyerekezi wodzikonda komanso wodzikuza, n’kukhala anthu ake.
13-15. (a) Kodi zina mwa zotsatira za kukana ulamuliro wolungama wa Yehova zinali zotani? (b) N’chifukwa chiyani anthu m’dzikoli saganizirana?
13 Taonani zina mwa zotsatira zake. Adamu ndi Hava anawathamangitsa m’chigawo cha dziko lapansi chimene chinali paradaiso. Anachoka m’munda wabwino kwambiri umene unali ndi zomera ndi zipatso zothandiza kwambiri pa thanzi la munthu n’kumakhala movutika kwambiri kunja kwa munda wa Edene. Mulungu anauza Adamu kuti: “Chifukwa kuti wamvera mawu a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m’kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: minga ndi mitula idzakubalira iwe.” Kutembereredwa kwa nthaka kunatanthauza kuti tsopano Genesis 3:17-19; 5:29.
kudzakhala kovuta kwambiri kulima nthakayo. Mbadwa za Adamu zinamvetsa zotsatira za kutembereredwa kwa nthaka, imene inabala minga ndi mitula, moti bambo ake a Nowa, Lameke, anatchulapo za ‘zovuta za manja awo, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova.’—14 Adamu ndi Hava anasiyanso moyo wabwino n’kumakhala moyo wovutika. Mulungu anauza Hava kuti: “Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” Kenako, Kaini, mwana woyamba kubadwa wa Adamu ndi Hava, anachita nkhanza yaikulu kwambiri pakupha mbale wake Abele.—Genesis 3:16; 4:8.
15 Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mofanana ndi wolamulira wa dzikoli, anthu m’dzikoli masiku ano amasonyeza makhalidwe oipa monga kudzikonda ndi kudzikuza. N’zosadabwitsa kuti ladzala ndi kusaganizirana ndiponso nkhanza. Koma silidzakhala lotere mpaka kalekale. Yehova adzaonetsetsa kuti kukoma mtima ndi chifundo zidzakhale paliponse mu Ufumu wake m’malo mwa kusaganizirana ndi nkhanza.
Anthu Adzakhala Okoma Mtima Kwambiri mu Ufumu wa Mulungu
16. N’chifukwa chiyani ulamuliro wa Mulungu kudzera mwa Kristu Yesu ndi wokoma mtima, ndipo zimenezi ziyenera kutipangitsa kuchita chiyani?
16 Yehova pamodzi ndi Mfumu ya Ufumu Wake, Kristu Yesu, amafuna kuti anthu awo azidziŵika ndi kukoma mtima. (Mika 6:8) Yesu Kristu anatisonyeza mmene ulamuliro umene Atate ake anam’patsa udzakhalire wokoma mtima. (Ahebri 1:3) Tingaone zimenezi m’mawu a Yesu amene anavumbula atsogoleri achipembedzo onyenga amene analemetsa anthu ndi katundu wolemera. Iye anati: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Olamulira ambiri a dzikoli, kaya akhale achipembedzo kapena ayi, amalemetsa anthu ndi katundu wotopetsa wa malamulo ambirimbiri ndiponso ntchito zimene sawayamikira akazichita. Komatu, zimene Yesu amafuna kwa anthu amene amamutsatira zimagwirizana ndi zofuna zawo ndiponso zimene angathe. Goli lake ndi lofeŵadi, lopatsa mpumulo. Kodi zimenezi sizitilimbikitsa kukhala ngati iye posonyeza kukoma mtima kwa ena?—Yohane 13:15.
17, 18. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti amene adzalamulira ndi Kristu kumwamba ndiponso anthu omuimira padziko lapansi adzasonyeza kukoma mtima?
17 Mawu osangalatsa amene Yesu analankhula kwa atumwi ake amasonyeza mmene ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu ukusiyanirana kwambiri ndi ulamuliro wa anthu. Baibulo limati: “Kunakhala kutsutsana mwa iwo [ophunzira], ndani wa iwo ayesedwe wamkulu. Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino. Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng’ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira. Pakuti Luka 22:24-27.
wamkulu ndani, iye wakuseyama pachakudya kapena wakutumikirapo? si ndiye wakuseyama pachakudya kodi? koma Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira.”—18 Anthu omwe ali ndi ulamuliro amafuna kuonetsa ukulu wawo mwa ‘kuchita ufumu’ pa anthu ndiponso mwa kufuna kukhala ndi mayina aulemu apamwamba, ngati kuti mayina aulemuwo amawachititsa kukhala apamwamba kwambiri kuposa anthu amene akuwalamulirawo. Koma Yesu anati ukulu weniweni umakhalapo ngati munthu atumikira ena, kuyesetsa kuchita zimenezo mwakhama ndiponso mosalekeza. Onse amene adzalamulira ndi Kristu kumwamba kapena kutumikira monga omuimira ake padziko lapansi ayenera kuyesetsa kutsatira chitsanzo chake cha kudzichepetsa ndi kukoma mtima.
19, 20. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kukula kwa kukoma mtima kwa Yehova? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yehova posonyeza kukoma mtima?
19 Tiyeni tione malangizo ena abwino amene Yesu anapereka. Posonyeza kukula kwa kukoma mtima kwa Yehova, Yesu anati: ‘Ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? pakuti ochimwa omwe akonda iwo akukondana nawo. Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? pakuti anthu ochimwa omwe amachita chomwecho. Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzawo, kuti alandirenso momwemo. Koma takondanani nawo adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa. Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo.’—Luka 6:32-36.
20 Kukoma mtima kumene Mulungu amasonyeza n’kopanda dyera. Safuna kuti alandirepo kanthu akasonyeza kukoma mtimako. Yehova mokoma mtima “amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:43-45; Machitidwe 14:16, 17) Potsanzira Atate wathu wakumwamba, sitingopeŵa kuchitira zoipa anthu osayamika koma timawachitiranso zabwino, ngakhale anthu amene atichitira zinthu ngati ndife adani awo. Mwa kukomera mtima anthu ena, timasonyeza Yehova ndi Yesu kuti timafuna kudzakhala mu Ufumu wa Mulungu, pamene kukoma mtima ndiponso makhalidwe ena a Mulungu zidzakhala pakati pa anthu onse.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonyeza Kukoma Mtima?
21, 22. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza kukoma mtima?
21 Kwa Mkristu weniweni, kusonyeza kukoma mtima n’kofunika kwambiri. Ndi umboni wakuti mzimu wa Mulungu ukugwira ntchito mwa ife. Ndiponso, tikamasonyeza kukoma mtima kwenikweni, timatsanzira Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu. Kukoma mtima ndikonso khalidwe limene likufunika kwa anthu amene adzakhala mu Ufumu wa Mulungu. Motero, tifunika kukonda khalidwe la kukoma mtima ndiponso kuphunzira kulisonyeza.
22 Kodi ndi njira zina zothandiza ziti zimene tingasonyezere kukoma mtima pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku? Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 M’mavesi a m’Baibulo amene tawatchula ndi kuwagwira mawu m’ndime ino ndi m’ndime yotsatira, liwu la m’chinenero choyambirira limene alimasulira kuti “chifundo” ndi “kukoma mtima.” M’Baibulo la New World Translation analimasulira moyenera kuti “kukoma mtima kwachikondi.”
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kukoma mtima n’kutani?
• N’chifukwa chiyani anthu m’dzikoli ndi ankhanza ndiponso osaganizirana?
• Kodi timadziŵa bwanji kuti kukoma mtima kudzakhala paliponse mu ulamuliro wa Mulungu?
• N’chifukwa chiyani kusonyeza kukoma mtima n’kofunika kwambiri kwa anthu amene akufuna kudzakhala mu Ufumu wa Mulungu?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 13]
Akulu achikristu amayesetsa kukhala okoma mtima pochitira zinthu nkhosa
[Chithunzi patsamba 15]
Kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova sikudzagwiritsa fuwa lamoto atumiki ake panthaŵi zovuta
[Zithunzi patsamba 16]
Yehova amawalitsa dzuŵa ndi kuvumbitsa mvula mokoma mtima kwa anthu onse