Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Linamuthandiza Kugonjetsa Mayesero

Baibulo Linamuthandiza Kugonjetsa Mayesero

Baibulo Linamuthandiza Kugonjetsa Mayesero

Masiku ano, pali mayesero ambiri padzikoli. Kutsatira mfundo za m’Baibulo sikophweka. Mwachitsanzo, zingakhale zovuta kutsatira langizo la m’Baibulo lakuti: “Thaŵani dama.”​—1 Akorinto 6:18.

Wa Mboni za Yehova wina, amene timutche kuti Sebastian, ankagwira ntchito pa kampani ya ku Scandinavia ku Poland. Anafunika kulimba kwambiri kuti akhalebe wokhulupirika.

Sebastian anadziŵika kuti anali wa Mboni za Yehova. Mabwana ake, anam’patsa maudindo osiyanasiyana chifukwa cha kugwira kwake ntchito molimbika komanso khalidwe lake labwino. Komano kunapezeka kuti maudindowo anafunika kuti azichita nawo misonkhano ya zamalonda kumene kunkakhala zosangulutsa zosayenera.

Posakhalitsa, Sebastian anayamba kukayikira. “Abwana angaŵa akudziŵa kuti ndine wa Mboni za Yehova. N’chifukwa chake anandipatsa maudindoŵa ndiponso amandidalira kwambiri. Ngati ndingakane kuchita nawo misonkhanoyi andichotsa ntchito, yomwe ndinavutika kuti ndiipeze. Bwanji ngati nditamangoonerera nawo?”

Ndiyeno Sebastian anadziŵa kuti panali zinthu zambiri zimene amamuyembekezera kuti achite. Anayenera kusamalira makasitomala akunja mwa kuwapezera mahule oti aziwachezetsa usiku. Kodi akanachita bwanji?

Sebastian anaganiza zokumbutsa abwana ake mmene iye amaonera nkhani za chiwerewere malinga ndi mfundo za m’Baibulo. Pasanapite nthaŵi zinaoneka kuti ntchitoyi sinamuyenere Sebastian ndipo m’kupita kwa nthaŵi anafunika kuisiya. Anapeza ntchito ina ya malipiro ocheperapo koma imene inalibe mayesero oterowo. Tsopano ali ndi chikumbumtima chabwino.

Kodi mungachite bwanji ngati munthu wina akuumirizani kuchita nawo kapena kuvomereza zachiwerewere? Kodi mudzakhala okonzeka kusinthiratu zinthu? Zimenezo n’zimene Yosefe wakale anachita, malinga ndi mmene lemba la Genesis 39:7-12 limafotokozera.