Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:
• Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anali ndi abale ndi alongo?
Baibulo limatiuza zimenezi pa Mateyu 13:55, 56 ndi Marko 6:3. Mawu a Chigiriki (akuti adelphos) amene ali pa malemba ameneŵa amawagwiritsa ntchito kusonyeza “ubale weniweni kapena walamulo [ndipo] amangotanthauza ubale wochokera kwa makolo onse aŵiri kapena kwa kholo limodzi basi.” (The Catholic Biblical Quarterly, January 1992)—12/15, tsamba 3.
• Kodi nkhondo yasintha motani, ndipo nthaŵi zambiri n’chiyani chakhala chikuyambitsa nkhondozi?
M’zaka zaposachedwapa nkhondo zimene zavutitsa anthu makamaka ndi nkhondo zapachiŵeniŵeni, nkhondo zapakati pamagulu otsutsana a nzika za m’dziko limodzi. Zifukwa zimene zimayambitsa nkhondozi ndi kudana chifukwa chosiyana mafuko, kusiyana zipembedzo, kusoŵa chilungamo, ndi chipwirikiti cha ndale. Chifukwa chinanso ndi kufuna kukhala wolamulira ndiponso kufuna kukhala ndi ndalama.—1/1, masamba 3-4.
• Kodi timadziŵa bwanji kuti Yesu sanafune kuti Akristu aziloweza pamtima mawu a m’pemphero lachitsanzo n’kumalitchula mobwerezabwereza?
Yesu anapereka chitsanzo cha pemphero chimenechi pa Ulaliki wake wa Paphiri. Patatha pafupifupi chaka chimodzi ndi theka, anabwereza mfundo zazikulu za malangizo amene anapereka m’mbuyomo okhudza pemphero. (Mateyu 6:9-13; Luka 11:1-4) Chochititsa chidwi n’chakuti sanabwereze mawu ake ndendende mmene anawanenera poyamba, zimene zikusonyeza kuti pemphero limene anawapatsalo silinali loti aliloweze pamtima n’kumalitchula mobwerezabwereza.—2/1, tsamba 8.
• Chigumula chitatha, kodi njiwa inakatenga kuti tsamba la azitona limene inabweretsa m’chingalaŵa?
Sitikudziŵa kuti madzi a chigumula anali ndi mchere wochuluka bwanji ndiponso anali otentha kapena ozizira bwanji. Koma mitengo ya azitona imadziŵika kuti imaphukira ngakhale itadulidwa. Motero, mwina mitengo ina inapulumuka madzi a chigumula ndi kuyambanso kuphukira.—2/15, tsamba 31.
• Dera la Biafra litatsekedwa panthaŵi ya nkhondo yapachiŵeniŵeni ku Nigeria, kodi Mboni za Yehova m’derali zinkalandira bwanji chakudya chauzimu?
Mwamuna wina wogwira ntchito m’boma anapatsidwa ofesi ku Ulaya ndipo winanso anapatsidwa ofesi pa bwalo la ndege ku Biafra. Aŵiri onseŵa anali Mboni. Iwo anadzipereka kuchita ntchito yoopsa yoloŵetsa chakudya chauzimu ku Biafra, zimene zinathandiza abale ambiri kumeneko mpaka pamene nkhondoyo inatha mu 1970.—3/1, tsamba 27.
• Kodi pangano la mtendere la ku Westphalia linachita zotani, ndipo zipembedzo zinakhudzidwa bwanji?
Kusintha zinthu kwakukulu m’chipembedzo cha Roma Katolika kunagaŵa Ufumu Wopatulika wa Roma m’zipembedzo zitatu, chipembedzo cha Katolika, cha Lutheran, ndi cha Calvinist. Mabungwe a Mgwirizano wa Apulotesitanti, ndi Mgwirizano wa Akatolika anapangidwa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1600. Ndiyeno panabuka mkangano wa zipembedzo ku Bohemia ndipo unakula n’kukhala nkhondo ya mayiko osiyanasiyana yolimbirana ulamuliro. Olamulira achikatolika ndi achipulotesitanti analimbana kuti akhale amphamvu pa zandale ndiponso pa zamalonda. Kenaka anakambirana za mtendere ku chigawo cha dziko la Germany cha Westphalia. Atakambirana kwa zaka pafupifupi zisanu, anasainirana Pangano la ku Westphalia mu 1648, n’kuthetsa nkhondo imene inatenga zaka 30. Panganoli linayambitsanso Ulaya watsopano monga kontinenti yokhala ndi mayiko odzilamulira okha.—3/15, masamba 20-23.
• Kodi chizindikiro, kapena kuti dzina, cha “chilombo,” chomwe ndi nambala ya 666, chimatanthauza chiyani?
Chizindikirochi, kapena kuti chilembo, achitchula pa Chivumbulutso 13:16-18. Chilombocho chimaimira maulamuliro a anthu, ndipo zoti chilombocho chili ndi ‘chiŵerengero cha munthu’ zikusonyeza kuti maboma amasonyeza kupanda ungwiro kwa anthu. Kuphatikiza namambala ya 6 ndi 60 kuphatikizaponso 600 kukusonyeza kuti chilombochi n’chopereŵera kwambiri pamaso pa Mulungu. Amene amakhala ndi chizindikiro chimenechi amapereka ulemu wolambira ku maboma andale, kapena amadalira mabomawo kuti adzawapulumutsa.—4/1, masamba 4-7.