Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulalikira Mwamwayi M’gawo Lolankhula Chingelezi ku Mexico

Kulalikira Mwamwayi M’gawo Lolankhula Chingelezi ku Mexico

Kulalikira Mwamwayi M’gawo Lolankhula Chingelezi ku Mexico

POTENGERAPO mwayi pa nthaŵi imene anali kuyembekezera anzake apaulendo ku Atene, mtumwi Paulo analalikira mwamwayi. Baibulo limati: “Anatsutsana [“anakambirana,” NW] . . . m’bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nawo.” (Machitidwe 17:17) Yesu ali paulendo wake wopita ku Galileya kuchokera ku Yudeya, analalikira mwamwayi kwa mkazi wachisamariya pachitsime. (Yohane 4:3-26) Kodi mumagwiritsa ntchito mpata uliwonse umene mwapeza kulankhula za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu?

Gawo la anthu olankhula Chingelezi ku Mexico ndi labwino kwambiri kuchitamo ulaliki wamwamwayi. Alendo odzaona malo amapita ku malo osangalalira, pamakhala ophunzira atsopano m’mayunivesite nthaŵi zonse, ndiponso anthu ochokera ku mayiko ena amene apuma pantchito ku Mexico amapita ku malo osungira zinthu zachilengedwe ndi ku malesitiranti. Mboni za Yehova zambiri zimene zimalankhula Chingelezi zapeza luso loyambitsa makambirano ndi anthu oterowo. Ndipo zimakhala tcheru kufufuza mpata woti zilankhule ndi munthu aliyense amene akuoneka kuti ndi wachilendo kapena amene amalankhula Chingelezi. Tiyeni tione mmene zimachitira zimenezo.

Nthaŵi zambiri Mboni zochokera ku mayiko akunja zimene zikutumikira m’gawo la anthu olankhula Chingelezi zimangodzidziŵikitsa zokha kwa anthu amene akuonekeratu kuti ndi ochokera ku mayiko ena ndi kuwafunsa kumene akuchokera. Zimenezi zimachititsa anthuwo kufunsa kuti Mboniyo ikuchita chiyani ku Mexico ndipo zimenezi zimapereka mpata woti awauze zikhulupiriro zachikristu. Mwachitsanzo, Gloria, amene akutumikira kudera limene kukufunika olalikira ambiri m’gawo la anthu olankhula Chingelezi ku Oaxaca, amaona kuti n’zosavuta kuyambitsa kukambirana mwa njira imeneyi. Pobwerera kunyumba kuchokera ku tauni imene anakalalikira mwamwayi, Gloria anaimitsidwa ndi mwamuna ndi mkazi wake, ochokera ku England. Mkaziyo anadabwa, amvekere: “Sindinayembekezere kuona mzimayi wachikuda akuyenda m’misewu ya kuno ku Oaxaca!” M’malo moipidwa ndi zimenezo, Gloria anaseka, ndipo anayamba kucheza nawo n’kumakambirana chifukwa chake iye anali ku Mexico. Mkaziyo anapempha Gloria kuti adzapite kunyumba kwawo akamwe khofi. Atapangana tsiku loti adzakumane, Gloria anam’patsa mkaziyo magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, koma mkaziyo anakana n’kunena kuti iye sakhulupirira Mulungu. Gloria anayankha kuti amakonda kulankhula ndi anthu amene sakhulupirira Mulungu ndipo akufuna kumva kuti maganizo ake ndi otani pa nkhani yakuti “Kodi Timafunikira Malo Olambiriramo?” Mkaziyo anavomera, n’kunena kuti: “Ngati ungakwanitse kunditsimikizira kuti ndikhulupirire kuti Mulungu aliko, ndiye kuti zikhala zodabwitsa kwabasi.” Anakambirana bwino kwambiri nkhani zingapo akumwa khofi. Kenako banjalo linabwerera ku England, koma anapitiriza kukambirana kudzera pa mauthenga a pa kompyuta.

Gloria anakambirananso ndi Saron, wophunzira amene anachokera ku Washington, D.C., amene anali ku Oaxaca kudzagwira ntchito yodzipereka ndi azimayi a komweko pofuna kumaliza maphunziro ake kuti apeze digiri yapamwamba. Atayamikira Saron chifukwa cha ntchito yabwino imeneyo, Gloria anafotokoza chifukwa chake anali ku Mexico. Zimenezi zinachititsa kuti akambirane za Baibulo ndi zimene Mulungu adzachite osati kwa osauka okha koma kwa aliyense. Saron anafotokoza kuti zinali zodabwitsa kuti sanalankhulepo ndi Mboni ku United States, koma n’kupezeka kuti mmodzi mwa anthu oyambirira kukumana nawo ku Mexico anali wa Mboni za Yehova. Saron anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndipo anayamba kupezeka pa misonkhano yachikristu nthaŵi yomweyo.

Anthu ambiri ochokera ku mayiko ena akukhala m’malo osangalatsa a m’mbali mwa nyanja ku Mexico, pofuna kukhala m’malo onga paradaiso. Laurel amagwiritsa ntchito zimenezi kuyambitsa makambirano ku Acapulco. Amawafunsa anthuwo ngati mzinda wa Acapulco ukufanana ndi paradaiso kusiyana ndi kumene achokera, ndiponso chimene amakondera mzindawo. Ndiyeno amafotokoza kuti posachedwapa dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso weniweni. Kukambirana ndi anthu mwa njira imeneyi kunachititsa kuti ayambe kuphunzira Baibulo ndi mkazi wina wa ku Canada amene anakumana naye pa ofesi ya vetenale. Kodi kukambirana ndi anthu mwa njira imeneyi kungathandize kumene mukukhalako?

‘M’misewu ndi M’mabwalo’

Nthaŵi zambiri Mboni zimayambitsa kukambirana ndi anthu m’misewu ndi m’mabwalo mwa kufunsa anthuwo kuti: “Kodi mumalankhula Chingelezi?” Anthu ambiri a ku Mexico amalankhula Chingelezi chifukwa cha ntchito imene amagwira kapena chifukwa chakuti anakhalapo ku United States.

Banja lina la Mboni linalankhula ndi mayi wina wachikulire amene anali pa njinga ya olumala imene amaikankha ndi nesi. Anamufunsa mayiyo ngati amalankhula Chingelezi. Anayankha kuti amalankhula chifukwa chakuti anakhalapo ku United States kwa zaka zambiri. Analandira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, zimene anali asanaŵerengepo, ndipo anawauza dzina lake, kuti ndi Consuelo, n’kuwapatsa adiresi yake. Atapita kukamuchezera pogwiritsa ntchito adiresi ija patapita masiku anayi, anapeza kuti anali kukhala ku nyumba yosamalira anthu okalamba ya avirigo achikatolika. Poyamba, zinali zovuta kulankhula ndi Consuelo chifukwa avirigowo anali kukayikira ndipo ananena kuti Consuelo sangawalandire. Banjalo linalimbikira kupempha kuti avirigowo amuuze Consuelo kuti iwo afika ndipo akufuna kum’patsa moni. Consuelo anaitana banjalo kuti liloŵe. Kuyambira nthaŵi imeneyo, mzimayi wa zaka 86 ameneyu wakhala akuphunzira Baibulo nthaŵi zonse, ngakhale kuti avirigowo amanena zofuna kumukhumudwitsa kuti asamaphunzire. Wakhalanso akupezeka pa misonkhano ina yachikristu.

Lemba la Miyambo 1:20 limati: “Nzeru ifuula panja [“m’misewu,” NW]; imveketsa mawu ake pabwalo.” Tamvani mmene zimenezo zinachitikira m’bwalo la San Miguel de Allende. Tsiku lina m’maŵa, Ralph analankhula ndi mwamuna wina wachikulire ndithu amene anakhala pa benchi. Mwamunayo anadabwa kwambiri kupatsidwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndipo anamuuza Ralph za moyo wake.

Anati iye ndi msilikali wopuma pantchito amene anamenya nawo nkhondo ya ku Vietnam. Chifukwa cha kusokonezeka maganizo poona anthu ambiri akumwalira, anadwala matenda okhudza maganizo panthaŵi imene anali msilikaliyo. Anamuchotsa komenya nkhondoko n’kumupititsa ku kampu ya asilikali. Kumeneko anamupatsa ntchito yosambitsa mitembo ya asilikali pokonzekera kuti itumizidwe ku United States. Panthaŵiyi, patapita zaka 30 kuchokera pamene zimenezi zinachitika, anali kuvutikabe ndi maloto oopsa ndi kuchita mantha kwambiri. M’maŵa umenewo, atakhala pabwalopo, anali kupemphera chamumtima kuti athandizidwe.

Mwamunayu analandira magazini ndiponso anavomera zoti apite nawo ku Nyumba ya Ufumu. Atachita nawo misonkhano, ananena kuti maola aŵiri amene anakhala ku Nyumba ya Ufumuyo, anapeza mtendere kwa nthaŵi yoyamba m’zaka 30. Mwamunayu anakhala ku San Miguel de Allende kwa milungu ingapo chabe, koma anaphunzira Baibulo kangapo ndipo anali kupezeka pamisonkhano yonse mpaka pamene anabwerera kwawo. Panakonzedwa zoti akapitirize kuphunzirako.

Kulalikira Mwamwayi Kuntchito ndi Kusukulu

Kodi mumadzidziŵikitsa kuti ndinu wa Mboni za Yehova kuntchito kwanu? Adrián, amene amachititsa lendi nyumba kwa anthu amene ali patchuti ku Cape San Lucas, amachita zimenezo. Chifukwa cha zimenezi, wantchito mnzake, Judy, anati: “Zaka zitatu chabe zapitazo, munthu wina akanandiuza kuti ndidzakhala wa Mboni za Yehova, ndikananena kuti, ‘Sindingachite.’ Koma ndinaganiza kuti ndikufunika kuŵerenga Baibulo. Ndinalingalira kuti, ‘Kodi zingandivute kuchita zimenezi, munthu woti ndimakonda kuŵerenga?’ Ndisanaŵerenge masamba oposa asanu ndi limodzi, ndinazindikira kuti ndikufunika thandizo. Munthu amene ndinamuganizira kuti angandithandize anali wantchito mnzanga dzina lake Adrián. Ndinkakonda kulankhula naye chifukwa ndi yekhayo amene anali wamakhalidwe abwino kuntchitoko.” Mwamsanga, Adrián anakonza zobwera ndi Katie, mlongo amene anali kuyembekezera kumukwatira, ndipo anayankha mafunso onse a Judy. Katie anayamba kuphunzira naye Baibulo, ndipo pasanapite nthaŵi yaitali anabatizidwa n’kukhala Mboni.

Bwanji nanga zolalikira mwamwayi kusukulu? Mboni zina ziŵiri zinali kuphunzira Chispanya pa yunivesite ina koma zinajomba tsiku lina kuti zikachite nawo msonkhano waukulu wachikristu. Atabwerako n’kudzaloŵa m’kalasi, anafunsidwa kuti afotokoze m’Chispanya zimene anakachita. Anagwiritsa ntchito mwayi umenewo kulalikira m’mene akanathera m’Chispanya. Mphunzitsi wawo, Silvia, anachita chidwi kwambiri ndi ulosi wa Baibulo. Anavomera kuphunzira Baibulo m’Chingelezi ndipo tsopano ndi wofalitsa uthenga wabwino. Anthu ena angapo a m’banja mwake akuphunziranso. Silvia anati: “Ndinapeza zimene ndinkafuna moyo wanga wonse.” Inde, kulalikira mwamwayi kungabale zipatso zabwino kwambiri.

Kugwiritsa Ntchito Mipata Ina

Kukhala wochereza kungathandizenso kuti munthu alalikire. Jim ndi Gail, amene akutumikira ku San Carlos, ku Sonora, anaona kuti zimenezi zimathandizadi. Mzimayi wina amene anali kuyenda ndi agalu ake sikisi koloko mmaŵa, anaima ndi kusirira bwalo la nyumba yawo. Jim ndi Gail anamuitana mzimayiyo kuti aloŵe amwe nawo khofi. Kwa nthaŵi yoyamba m’zaka 60, anamva za Yehova ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Anayamba kuphunzira naye Baibulo.

Adrienne amachitanso chimodzimodzi, kuwakomera mtima anthu osawadziŵa. Akudya mu lesitiranti ina ku Cancún, mnyamata wina anafika n’kumufunsa ngati anali wochokera ku Canada. Atayankha kuti inde, mnyamatayo anafotokoza kuti iye ndi mayi ake anali kuyesa kuthandiza mchemwali wake kukonza lipoti la kusukulu lokhudza anthu a ku Canada. Mayi ake a mnyamatayo, omwe amalankhula Chingelezi, anafika. Atayankha moleza mtima mafunso awo okhudza anthu a ku Canada, Adrienne anati: “Koma pali chifukwa chofunika kwambiri chimene ndinabwerera kuno kuchokera ku Canada. Ndinabwera kudzathandiza anthu kuphunzira Baibulo. Kodi mungakonde kuphunzira?” Mayiyo anavomera kuti angakonde. Anali atachoka m’chipembedzo chake zaka khumi zapitazo ndipo ankayesera kuphunzira Baibulo payekha. Anam’patsa Adrienne adiresi yake ndi nambala yake ya telefoni, ndipo anayamba kuphunzira naye Baibulo moti phunzirolo linali kuyenda bwino.

‘Ponyani Zakudya Zanu Pamadzi’

Nthaŵi zambiri, kulankhula za choonadi cha m’Baibulo nthaŵi iliyonse kumachititsa kuti munthu alankhule ndi anthu amene amangokhala ndi mpata wochepa kapena sapeza n’komwe mpata womva uthenga wa Ufumu. Mu lesitiranti ina imene mumabwera anthu ambiri m’tauni ya Zihuatanejo yomwenso ndi doko, Mboni ina inauza alendo aŵiri okwatirana kuti agwiritse ntchito tebulo lake chifukwa lesitirantiyo inali yodzaza. Banjali linakhala likuyenda panyanja kupita kumalo osiyanasiyana kwa zaka zisanu ndi ziŵiri. Linasonyeza kuti silisangalala ndi Mboni za Yehova. Atasiyana ku lesitirantiko, Mboniyo inakacheza ndi banjalo m’bwato lawo ndipo inaliitana kuti lidzafike kunyumba kwake. Analandira magazini oposa 20 ndi mabuku 5 ndipo analonjeza kuti akafunafuna Mboni pa doko lotsatira limene akafike.

Jeff ndi Deb anaona banja lina limene linali ndi mwana wakhanda wamkazi wokongola pamalo odyerapo m’dera lina la masitolo ku Cancún. Atalankhula za mwanayo, makolo akewo anawapempha kuti adzadye nawo zakudya zina zotchedwa pizza. Anapeza kuti banjali linachokera ku India. Anali asanamvepo za Mboni za Yehova, ndipo anali asanaonepo mabuku athu. Anachoka pa masitolopo atatenga mabuku a Mboni.

Zochitika zinanso zofanana ndi zimenezi zinachitika ku chilumba chimene chili pafupi ndi gombe la Yucatán. Atchaina aŵiri amene anangokwatirana kumene anam’pempha Jeff kuti awatole zithunzi, ndipo iye anachita zimenezo mwansangala. Polankhula nawo anapeza kuti ngakhale kuti anakhalapo ku United States kwa zaka 12 zapitazo, anali asanaonepo kapena kumva za Mboni za Yehova. Anayamba kukambirana mosangalala. Jeff anawalimbikitsa kuti akafufuze Mboni akabwerera kwawo.

Mwina pangakhale zochitika zapadera m’dera lanu zimene zingapereke mpata wolalikira mwamwayi. Pulezidenti wa ku United States atapita kukacheza ndi Pulezidenti wa ku Mexico pa famu yake kufupi ndi ku Guanajuato, atolankhani ochokera madera osiyanasiyana padziko lonse anaulutsa zimenezi. Banja lina la Mboni linaganiza zotengerapo mwayi mpata umenewu kulalikira m’Chingelezi. Anthu anamvetsera kwambiri. Mwachitsanzo, mtolankhani wina anaulutsapo za nkhondo zingapo monga nkhondo za ku Kosovo ndi ku Kuwait. Mtolankhani mnzake anafera m’manja mwake ataomberedwa ndi munthu wina woombera mwakabisira. Atamva za kuuka kwa akufa, mtolankhaniyo anathokoza Mulungu akutulutsa misozi chifukwa chomudziŵitsa kuti moyo uli ndi cholinga. Iye anati ngakhale kuti sadzakumana nalonso banja la Mbonilo, uthenga wabwino wa m’Baibulo umenewu ukhalabe mumtima mwake.

Monga mmene taoneramu, nthaŵi zambiri sitingadziŵe zotsatira za maulaliki otereŵa. Komabe, Mfumu yanzeru Solomo inati: “Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.” Iyo inanenanso kuti: “Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziŵiri zidzakhala bwino.” (Mlaliki 11:1, 6) Inde, ‘ponyani zakudya zanu’ mwachangu pa madzi ambiri ndipo ‘fesani mbewu zanu’ mowoloŵa manja, monga mmene anachitira Paulo ndi Yesu ndiponso monga mmene zikuchitira Mboni zamakono zimenezi ku gawo lolankhula Chingelezi ku Mexico.