Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Mulungu Akufuna Zikadzachitika Padziko Lapansi

Zimene Mulungu Akufuna Zikadzachitika Padziko Lapansi

Zimene Mulungu Akufuna Zikadzachitika Padziko Lapansi

PAMENE Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti, “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano,” anali kulankhula monga munthu amene anakhalapo kumwamba ndi Atatewo. (Mateyu 6:10; Yohane 1:18; 3:13; 8:42) Yesu asanakhale munthu, anakhalako pa nthaŵi imene zonse zimene zinkachitika kumwamba ndi padziko lapansi zinali zogwirizana ndi zofuna za Mulungu. Imeneyo inali nthaŵi yosangalala chifukwa chokwaniritsa zomwe zinali kufunika komanso kukhutira ndi zomwe zachitikazo.​—Miyambo 8:27-31.

Zinthu zoyamba zimene Mulungu analenga zinali zolengedwa zauzimu, “angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mawu ake.” Angelowo anali “atumiki ake akuchita chom’kondweretsa Iye,” ndipo akadali otero mpaka pano. (Salmo 103:20, 21) Kodi mngelo aliyense anali ndi chom’kondweretsa kapena kuti zofuna zakezake? Inde, ndipo pamene anali kulenga dziko lapansi, ‘ana a Mulungu [ameneŵa] anafuula ndi chimwemwe.’ (Yobu 38:7) Chimwemwe chawocho chinasonyeza kuti aliyense wa iwo anali kusangalala ndi zimene Mulungu anafuna ndipo zofuna zawo zinali zogwirizana ndi zofuna za Mulungu.

Mulungu atalenga dziko lapansi, analikonza kuti anthu akhalemo ndipo kenako analenga mwamuna ndi mkazi oyamba. (Genesis, chaputala 1) Kodi zimenezinso zinali zoyenera kuzisangalalira? Nkhani youziridwayo imati: “Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu,” inde, zinalibe chilema, zinali zangwiro.​—Genesis 1:31.

Kodi chifuniro cha Mulungu kwa makolo athu oyambirirawo ndi ana awo chinali chotani? Malinga ndi Genesis 1:28, chifuniro chakecho chinalinso chabwino kwambiri. Lembalo limati: “Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” Kuti akwaniritse ntchito yabwino kwambiri imeneyo, makolo athu oyambirirawo anafunika kukhalabe ndi moyo, mpaka muyaya, ndipo ana awonso anayenera kuchita chimodzimodzi. Palibe chimene chinasonyeza kuti adzakumana ndi mavuto, kusoŵa chilungamo, chisoni, kapena imfa.

Imeneyi inali nthaŵi imene zofuna za Mulungu zinali kuchitika kumwamba ndi padziko lapansi. Amene anali kuchita zofuna za Mulungu anali kusangalala kwambiri chifukwa chochita zimenezo. Nanga kodi chinalakwika n’chiyani?

Mosayembekezeka, wina anatsutsa zofuna za Mulungu. Sinali nkhani yoti sikanayankhidwa. Komabe, inayambitsa chisoni ndi mavuto kwa nthaŵi yaitali zimene zinasokoneza kwambiri zofuna za Mulungu kwa anthu. Tonsefe timavutika chifukwa cha zimenezi. Kodi anatsutsa bwanji?

Zofuna za Mulungu Panthaŵi ya Kupanduka

Mmodzi mwa “ana a Mulungu” auzimu anaona kuti n’zotheka kusokoneza zofuna za Mulungu kwa anthu, ndipo cholinga chake chinali choti zimukomere iyeyo. Pamene cholengedwa chauzimu chimenechi chinali kuganizira kwambiri zimenezo, zinaonekera kwambiri kuti zinali zotheka ndipo anaziona kuti zinali zabwino kwambiri. (Yakobo 1:14, 15) Ayenera kuti anaganiza kuti ngati akanatha kuchititsa anthu oyambawo kumumvera m’malo momvera Mulungu, ndiye kuti Mulungu sakanachitira mwina koma kulolera kuti pakhale ulamuliro wina wotsutsana ndi Iye. Ayeneranso kuti anaganiza kuti Mulungu sakanawapha, chifukwa ngati akanatero zikanatanthauza kuti walephera kukwaniritsa cholinga Chake. M’malo mwake, Yehova Mulungu akanafunika kusintha cholinga chake, kuvomereza ulamuliro wa mwana wauzimu ameneyu yemwe anthu tsopano adzamumvera. Moyenerera, patapita nthaŵi mwana woukira ameneyu anatchedwa Satana, kutanthauza kuti “Wotsutsa.”​—Yobu 1:6.

Pofuna kuchita zimene anali kulakalaka, Satana anapita kwa mkazi. Anamulimbikitsa kunyalanyaza zofuna za Mulungu ndi kuti akhale wodziimira payekha, ponena kuti: “Kufa simudzafai . . . mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:1-5) Mkaziyo anaona kuti zimenezi zidzam’patsa ufulu, ndipo anakhulupirira kuti kuchita zimenezo kudzamuthandiza kukhala ndi moyo wabwinopo. Kenako, anakopa mwamuna wake n’kuchita chimodzimodzi.​—Genesis 3:6.

Zimenezi si zimene Mulungu anafuna kwa anthu aŵiriwo. Zinali zofuna zawo. Ndipo zotsatira zake zinali zopweteka kwambiri. Mulungu anali atawauziratu kuti akadzachita zimenezo adzafa. (Genesis 3:3) Sanawalenge moti angathe kuchita bwinobwino zinthu popanda kudalira Mulungu. (Yeremiya 10:23) Kuwonjezera pamenepo, anali kudzakhala opanda ungwiro, ndiponso kudzapatsira ana awo kupanda ungwiro ndi imfa. (Aroma 5:12) Satana sakanatha kusintha zimenezi kuti zibwerere mwakale.

Kodi zimenezi zinasinthiratu kosatha zolinga za Mulungu, kapena kuti zofuna zake, kwa anthu ndi dziko lapansi? Ayi. (Yesaya 55:9-11) Koma zinadzutsa mafunso amene anafunika kuyankhidwa akuti: Kodi anthu ‘angafanane ndi Mulungu, n’kumadziŵa chabwino ndi choipa,’ monga momwe Satana ananenera? M’mawu ena, ngati titapatsidwa nthaŵi yokwanira, kodi tingadziŵe patokha chabwino ndi choipa, zimene zingatipindulitse ndi zimene zingativulaze, m’mbali zonse za moyo? Kodi Mulungu akuyenereradi kumumvera ndi mtima wonse, chifukwa chakuti ulamuliro wake ndi wabwino kuposa wina uliwonse? Kodi n’koyenera kumvera ndi mtima wonse zofuna zake? Kodi inu mungayankhe bwanji mafunso ameneŵa?

Panali njira imodzi yokha yoyankhira mafunso ameneŵa pamaso pa zolengedwa zonse zanzeru: Kuwalola amene anafuna kudziimira paokhawo kuyesera zimenezo kuti aone ngati zingawayendere bwino. Kungowapha anthuwo sikukanayankha mafunso amene anabukaŵa. Kulola kuti anthu adziimire paokha kwa nthaŵi yokwanira kukanayankha mafunsoŵa chifukwa zotsatira zake zikanaonekeratu. Mulungu anasonyeza kuti adzathetsa nkhaniyo mwa njira imeneyi pamene anauza mkaziyo kuti adzakhala ndi ana. Motero, anthu anali kudzayamba kuchulukana. Ife tili ndi moyo lero chifukwa chakuti Mulungu anasamalira motero nkhaniyo.​—Genesis 3:16, 20.

Komabe, zimenezi sizinatanthauze kuti Mulungu adzalola anthu ndi mwana wauzimu wopandukayo kuchita chilichonse monga mmene angafunire. Mulungu sanasiye kulamulira chilengedwe chonse, ndiponso sanasinthe cholinga chake. (Salmo 83:18) Anasonyeza zimenezi mwa kulosera kuti woyambitsa kupandukayo adzaphwanyidwa komanso zoipa zonse zimene zakhalapo chifukwa cha zimenezi zidzathetsedwa. (Genesis 3:15) Motero, kuyambira pachiyambi pomwe, anthu anali ndi chiyembekezo choti adzapeza mpumulo.

Koma panthaŵiyi, makolo athu pamodzinso ndi ana awo am’tsogolo anali atadzisiyanitsa ku ulamuliro wa Mulungu. Ngati Mulungu atati azilepheretsa zinthu zonse zomvetsa chisoni zimene zingachitike chifukwa cha zimene anthuwo anachita, angafunike kuumiriza anthu kuchita zofuna zake pankhani iliyonse. Kuchita zimenezo kungafanane ndi kusawalola kuti ayesere kudziimira paokha.

Komabe, munthu aliyense payekha akanatha kusankha ulamuliro wa Mulungu. Akanaphunzira zofuna za Mulungu kwa anthu m’nthaŵi imeneyi ndi kutsatira zimenezo monga momwe akanathera. (Salmo 143:10) Koma adzakumanabe ndi mavuto mpaka pamene nkhani ya kudziimira paokha kwa anthu idzathetsedwe.

Zotsatirapo za zosankha za munthu zinaonekeratu kuchiyambi komweko. Mwana woyamba kubadwa m’banja la anthu, Kaini, anapha mbale wake Abele chifukwa chakuti “ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.” (1 Yohane 3:12) Zimenezi sizinali zofuna za Mulungu, chifukwa Mulungu anachenjeza Kaini ndipo kenako anamulanga. (Genesis 4:3-12) Kaini anasankha kudziimira payekha monga momwe Satana anafunira kuti anthu azichita, motero “anali wochokera mwa woipayo.” Anthu enanso anachita chimodzimodzi.

Patapita zaka 1,500 kuyambira pamene anthu analengedwa, “dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa.” (Genesis 6:11) Anafunika kuchitapo kanthu mwamsanga kuti ateteze dziko kuti lisawonongeke. Mulungu anachita zimenezo mwa kubweretsa chigumula padziko lonse ndi kuteteza banja limodzi lokha lolungama limene linali likadali moyo, Nowa, mkazi wake, ana ake, ndi akazi awo. (Genesis 7:1) Tonsefe ndife ana awo.

M’mbiri yonse ya anthu kuyambira nthaŵi imeneyo, Mulungu wakhala akupereka malangizo kwa anthu amene amafuna ndi mtima wonse kudziŵa chifuniro chake. Anauzira anthu okhulupirika kulemba mawu ake oti athandize anthu alionse amene anafuna kuti iye awatsogolere. Mawu ameneŵa alembedwa m’Baibulo. (2 Timoteo 3:16) Mwachikondi, iye analola anthu okhulupirika kukhala naye paubale, ngakhale kukhala mabwenzi ake. (Yesaya 41:8) Ndiponso anawapatsa mphamvu zimene anafunika kuti apirire mavuto amene anthu akumana nawo m’zaka zambirimbiri zimene akhala akudziimira paokha. (Salmo 46:1; Afilipi 4:13) Tiyenera kuyamikira zonsezi.

‘Kufuna Kwanu Kuchitidwe’ Mokwanira

Zimene Mulungu wachita kudzafika pano, si zonse zimene iye amafuna kwa anthu. Mtumwi wachikristu Petro analemba kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Mawu ophiphiritsira ameneŵa akunena za ulamuliro watsopano kwa anthu ndiponso anthu atsopano amene adzakhala mu ulamuliro umenewo.

Pogwiritsa ntchito mawu omveka bwino, mneneri Danieli analemba kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Ulosi umenewu ukulosera kutha kwa dongosolo la zinthu lomwe silikuyenda bwinoli ndipo lidzaloŵedwa m’malo ndi Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma lake. Umenewutu ndi uthenga wabwino! Mikangano ndi kudzikonda kumene kwachititsa kuti dzikoli lidzaze ndi chiwawa chimene nachonso chingaipitse dziko lapansi, tsiku lina zidzakhala zinthu zakale.

Kodi zimenezi zidzachitika liti? Ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Zija zidzaoneka liti? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu n’chiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Mbali ina ya yankho la Yesu inali yakuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”​—Mateyu 24:3, 14.

Anthu ambiri akudziŵa kuti tsopano ntchito yolalikira imeneyi ikuchitika padziko lonse lapansi. Inunso muyenera kuti mwaona zimenezi zikuchitika m’dera limene mukukhala. Pulofesa Charles S. Braden, m’buku lake lakuti These Also Believe, analemba kuti: “Mboni za Yehova zafika kulikonse padziko lapansi ndi ntchito yawo yolalikira. . . . Palibe chipembedzo n’chimodzi chomwe padziko lapansi chimene chasonyeza changu ndiponso kulimbikira poyesetsa kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu kuposa Mboni za Yehova.” Mboni zikulengeza uthenga wabwino umenewu m’mayiko oposa 230, m’zinenero pafupifupi 400. Ntchito imene ananeneratu kuti idzachitikayi, sinachitikepo padziko lonse lapansi monga momwe zilili pakalipano. Ntchito imeneyi ndi umboni umodzi mwa maumboni ambiri osonyeza kuti nthaŵi yayandikira yoti Ufumuwo ulowe m’malo mwa maboma a anthu.

Ufumu umene Yesu ananena kuti udzalalikidwa ndi Ufumu womwewo umene anatiphunzitsa kuti tiziupempherera m’pemphero lake lachitsanzo, kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Inde, Ufumu umenewo ndiwo chida chimene Mulungu adzagwiritse ntchito kukwaniritsa zolinga zake, kapena kuti, zofuna zake kwa anthu ndi dziko lapansi.

Kodi zimenezo zikutanthauza chiyani? Lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 likuyankha kuti: “Ndinamva mawu akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Zikadzatero, zimene Mulungu akufuna zidzachitikadi mokwanira padziko lapansi ndi kumwamba komwe. * Kodi simungafune kudzakhala mu Ufumu umenewo?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 26 Ngati mukufuna kudziŵa zambiri za Ufumu wa Mulungu, funsani Mboni za Yehova m’dera lanulo kapena lemberani ku adiresi imodzi mwa maadiresi amene ali pa tsamba 2 la magazini ino.

[Chithunzi patsamba 5]

Kudziimira paokha kwa anthu mosatsatira zofuna za Mulungu kunayambitsa mavuto