Achinyamata, Kodi Mukukonzekera Tsogolo?
Achinyamata, Kodi Mukukonzekera Tsogolo?
“Ndidziŵa malingiriro amene ndilingiririra inu, . . . malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu [“tsogolo,” NW] ndi chiyembekezero.”—YEREMIYA 29:11.
1, 2. Kodi zaka zaunyamata zingaonedwe m’njira zosiyana ziti?
ACHIKULIRE ambiri amaona nthaŵi ya unyamata kukhala nthaŵi yabwino kwambiri pa moyo. Amakumbukira mphamvu ndi changu zimene anali nazo pamene anali achinyamata. Amakumbukira bwino nthaŵi imene analibe maudindo ambiri, nthaŵi yomwe anali kusangalala kwambiri ndipo ankati akaganiza za m’tsogolo ankaona kuti ali ndi mwayi wochita zinthu zambiri pa moyo wawo.
2 Inu amene muli achinyamata mwachionekere muli ndi maganizo osiyana ndi ameneŵa. Mungakhale mukuvutika kulamulira kusintha kwa maganizo ndi thupi kwa paunyamata. Mwina kusukulu anzanu amakuumirizani kuchita zimene iwo akufuna. Mungafunike kulimba mtima poyesetsa kukana kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, mowa, ndiponso chiwerewere. Ambiri mwa inu mukukumananso ndi nkhani ya kusaloŵerera m’nkhani za ndale kapena nkhani zina zokhudza chikhulupiriro chanu. Inde, nthaŵi ya unyamata ingakhale yovuta kwambiri. Komabe, nthaŵi ya unyamata ilidi nthaŵi yokhala ndi mwayi wochita zambiri. Funso n’lakuti, Kodi mwayi umenewo muugwiritsa ntchito bwanji?
Sangalalani ndi Unyamata Wanu
3. Kodi Solomo analangiza chiyani achinyamata ndipo anawachenjeza motani?
3 Anthu achikulire angakuuzeni kuti unyamata suchedwa kutha, ndipo akulondola ponena choncho. Unyamata wanu udzakhala utatha m’zaka zochepa chabe. Motero, sangalalani ndi unyamata pamene muli pausinkhu umenewu. Zimenezi n’zimene Mfumu Solomo inalangiza. Inalemba kuti: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona.” Komabe, Solomo anachenjeza achinyamata kuti: “Chotsani zopweteka m’mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ubwana ndi unyamata ngwa chabe.”—Mlaliki 11:9, 10.
4, 5. N’chifukwa chiyani ndi chinthu chanzeru kuti achinyamata akonzekere tsogolo? Perekani chitsanzo.
4 Kodi mukumvetsa zimene Solomo anatanthauza? Mwachitsanzo, taganizirani wachinyamata amene walandira mphatso yaikulu, mwina chuma chimene makolo ake amusiyira. Kodi adzachita nacho chiyani? Akhoza kuchimwaza chumacho podzisangalatsa yekha, monga mmene anachitira mwana woloŵerera wa m’fanizo la Yesu. (Luka 15:11-23) Koma kodi n’chiyani chidzachitike chumacho chikadzatha? Mwachidziŵikire adzadandaula kuti sanagwiritse bwino ntchito chumacho. Komano, tiyerekeze kuti wagwiritsa ntchito chumacho kukonza tsogolo lake, mwina kuika ku banki kapena kuchita bizinesi. M’kupita kwa nthaŵi, akamapeza phindu pa chuma chakecho, mukuganiza kuti adzadandaula kuti sanagwiritse ntchito chuma chake chonse posangalala pa unyamata wake? Ayi.
5 Ganizirani zaka zimene muli paunyamata kukhala mphatso yochokera kwa Mulungu, ndipo ndi chonchodi. Kodi mugwiritsa ntchito bwanji zaka zimenezi? Mukhoza kuwononga mphamvu ndi changu chonsecho pochita zofuna zanu, kumangosangalala popanda kuganizira za tsogolo lanu. Koma ngati mungachite zimenezo, ndiye kuti kwa inu “ubwana ndi unyamata” udzakhaladi ‘wachabe.’ Ndiyetu ndi bwino kwambiri kuti mugwiritse ntchito unyamata wanu pokonzekera tsogolo.
6. (a) Kodi ndi malangizo ati a Solomo amene angatsogolere achinyamata? (b) Kodi Yehova angakonde kuchitira chiyani achinyamata, ndipo wachinyamata angapindule bwanji ndi zimenezi?
Mlaliki 12:1) Chimenechi ndiye chinsinsi chakuti zinthu zikuyendereni bwino—mverani Yehova ndipo chitani chifuniro chake. Yehova anauza Aisrayeli akale zimene anafuna kuwachitira. Anati: “Ndidziŵa malingiriro amene ndilingiririra inu, . . . malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu [“tsogolo,”] ndi chiyembekezero.” (Yeremiya 29:11) Yehova angakondenso kukupatsani “tsogolo ndi chiyembekezero.” Ngati mumukumbukira m’zochita zanu, maganizo anu, ndi zosankha zanu, tsogolo loterolo ndi chiyembekezo chimenecho mudzazipeza.—Chivumbulutso 7:16, 17; 21:3, 4.
6 Solomo anafotokoza mfundo imene ingakuthandizeni kugwiritsa ntchito mwanzeru unyamata wanu. Iye anati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” (“Yandikirani kwa Mulungu”
7, 8. Kodi wachinyamata angayandikire bwanji kwa Mulungu?
7 Yakobo anatilimbikitsa kukumbukira Yehova pamene anatiuza kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Yehova ndiye Mlengi, Wolamulira wakumwamba wachilengedwe chonse, yemwe ndi woyenerera kumulambira ndi kumutamanda. (Chivumbulutso 4:11) Komabe, ngati tiyandikira kwa iye, naye adzayandikira kwa ife. Kodi kuganizira anthu mwachikondi koteroko sikukusangalatsa mtima wanu?—Mateyu 22:37.
8 Timayandikira kwa Yehova m’njira zingapo. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anati: “Chitani khama m’kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko.” (Akolose 4:2) M’mawu ena, khalani ndi chizoloŵezi chopemphera. Musangodalira kunena kuti amen bambo anu kapena Mkristu mnzanu mumpingo akakuimirani m’pemphero. Kodi munamuuzapo Yehova zakumtima kwanu, ndi kumuuza zimene mukuganiza, zimene mukuopa, mavuto amene mukukumana nawo? Kodi munamuuzapo zinthu zimene mungachite manyazi kuuza munthu wina aliyense? Kupemphera moona mtima ndiponso mochokera pansi pa mtima kumabweretsa mtendere. (Afilipi 4:6, 7) Kupemphera koteroko kumatithandiza kuyandikira kwa Yehova ndi kuona kuti naye akutiyandikira.
9. Kodi wachinyamata angamvere bwanji Yehova?
9 Njira ina yoyandikirira kwa Yehova tikuiona m’mawu ouziridwa akuti: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako.” (Miyambo 19:20) Inde, ngati mumvera Yehova ndiye kuti mukukonzekera tsogolo lanu. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumamvera Yehova? Mosakayika, mumapezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse ndi kumvetsera nkhani pamisonkhanoyo. Ndiponso, ‘mumalemekeza atate wanu ndi amanu’ mwa kuchita nawo phunziro la Baibulo la banja. (Aefeso 6:1, 2; Ahebri 10:24, 25) Mukuchita bwino kwambiri. Komabe, kuwonjezera pamenepo, kodi ‘mumachita machawi,’ kapena kuti kuombola nthaŵi, kukonzekera misonkhano, kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ndiponso kufufuza? Kodi mumayesetsa kugwiritsa ntchito zimene mumaŵerenga, kuti muyende monga munthu ‘wanzeru’? (Aefeso 5:15-17; Salmo 1:1-3) Ngati mumachita zimenezi, mukuyandikira kwa Yehova.
10, 11. Kodi ndi phindu lalikulu lotani limene achinyamata amalandira akamvera Yehova?
10 M’mawu otsegulira buku la Miyambo, wolemba wouziridwayo anafotokoza cholinga cha buku la m’Baibulo limeneli. Iye anati cholinga chake n’chakuti munthu ‘adziŵe nzeru ndi mwambo; kuzindikira mawu ozindikiritsa; kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika; kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziŵa ndi kulingalira.’ (Miyambo 1:1-4) Motero, mukamaŵerenga ndi kugwiritsa ntchito mawu a m’buku la Miyambo, pamodzinso ndi Baibulo lonse, mudzakulitsa chilungamo ndipo Yehova adzasangalala kuti mumuyandikire. (Salmo 15:1-5) Mukamakulitsa chiweruzo, kuchenjera kapena kuti nzeru, kudziŵa zinthu, ndi kulingalira, mudzasankha zochita mwanzeru.
11 Kodi n’kulakwa kuyembekezera kuti wachinyamata achite zinthu mwanzeru moteremu? Ayi, chifukwa achinyamata achikristu ambiri 1 Timoteo 4:12) Makolo awo amasangalala nawo kwambiri, ndipo Yehova amati achinyamata oterowo amakondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Ngakhale kuti ndi achinyamata, angakhulupirire kuti mawu ouziridwa otsatiraŵa akugwira ntchito kwa iwo: “Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.”—Salmo 37:37.
akuchita zimenezo. Chifukwa chochita zimenezo, anthu ena amawalemekeza ndipo ‘sapeputsa ubwana wawo.’ (Pangani Zosankha Zabwino
12. Kodi chimodzi mwa zosankha zofunika kwambiri zimene achinyamata amapanga ndi chiti, ndipo n’chifukwa chiyani chosankha chimenecho chimakhala ndi zotsatirapo zokhalitsa?
12 Unyamata ndi nthaŵi yopanga zosankha, ndipo zina mwa zosankhazo zimakhala ndi zotsatirapo zokhalitsa. Zosankha zina zimene mukupanga pakalipano zidzakhudza moyo wanu kwa zaka zambiri. Kusankha zinthu mwanzeru kudzakuthandizani kuti mukhale ndi moyo wachimwemwe ndiponso kuti zinthu zikuyendereni bwino. Kusankha zochita mopanda nzeru kungawononge moyo wanu wonse. Taonani mmene zimenezi zimakhaliradi choncho pa zosankha ziŵiri zimene mumafunika kupanga. Choyamba: Kodi mumasankha kucheza ndi anthu otani? N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? Mwambi wouziridwa umati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) M’mawu ena, m’kupita kwa nthaŵi timadzakhala ngati anthu amene timacheza nawowo, kaya kukhala anzeru kapena opusa. Kodi mungakonde kukhala munthu wotani?
13, 14. (a) Kupatula pa kukhala pamodzi ndi anthu ena, kodi kucheza ndi anthu kumaphatikizapo chiyani? (b) Kodi ndi kulakwitsa kotani kumene achinyamata ayenera kupeŵa?
13 Mukamanena za kucheza ndi anthu, mosakayika mumaganizira zokhala pamodzi ndi anthu ena. N’zoona zimenezo, koma si zokhazo. Mukamaonera pulogalamu ya pa TV, kumvetsera nyimbo, kuŵerenga buku, kukaonera filimu, kugwiritsa ntchito Intaneti, mumakhala mukucheza ndi anthu. Ngati kucheza koteroko kumakuchititsani kuonera chiwawa ndi zachiwerewere kapena kulimbikitsa kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, uchidakwa, kapena china chilichonse chotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo, mukucheza ndi “wauchitsiru,” amene amachita zinthu ngati kuti Yehova kulibeko.—Salmo 14:1.
14 Mwina mukuganiza kuti popeza mumapezeka pa misonkhano yachikristu ndipo ndinu 1 Akorinto 15:33) N’zomvetsa chisoni kuti achinyamata ambiri achikristu amene ankaoneka kuti adzachita bwino kwambiri mwauzimu, makhalidwe awo aipitsidwa pocheza ndi anthu olakwika. Motero, onetsetsani kuti mukupeŵa kucheza ndi anthu otero. Ngati muchita zimenezo, mudzatsatira langizo la Paulo lakuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”—Aroma 12:2.
wachangu kumpingo, ndiye kuti ndinu wolimba kwambiri moti simungakhudzidwe ndi filimu yachiwawa kapena nyimbo yomwe kaimbidwe kake n’kabwino koma mawu ake ndi oipa. Mwina mukuganiza kuti sipangakhale zotsatira zoipa ngati mutangoona mwapatalipatali zinthu zolaula pa Intaneti. Mtumwi Paulo akukuuzani kuti mukuganiza molakwika kwambiri. Iye akuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (15. Kodi chosankha chachiŵiri chimene achinyamata amafunika kupanga n’chiti, ndipo nthaŵi zina amaumirizika kuchita chiyani pankhani imeneyi?
15 Chosankha chachiŵiri ndi chimene mumapanga nthaŵi ikafika yoti musankhe zimene mukufuna kuchita mukamaliza sukulu. Ngati mukukhala m’dziko limene ntchito n’zosoŵa, mungaumirizike kupeza ntchito iliyonse yabwino imene ingapezeke. Ngati mukukhala m’dziko lolemera, pangakhale ntchito zosiyanasiyana zimene mungasankhe, ndipo zina mwa izo zingakhale zokopa kwambiri. Pokufunirani zabwino kuchokera pansi pa mtima, aphunzitsi anu kapena makolo anu angakulimbikitseni kuphunzira ntchito imene ikuoneka kuti simudzakhala ndi mavuto azachuma, ngakhalenso kulemera kumene. Komabe, kuphunzira ntchito imeneyo, kungachepetse kwambiri nthaŵi imene mungathere potumikira Yehova.
16, 17. Fotokozani mmene malemba osiyanasiyana angathandizire wachinyamata kusamala pankhani ya mmene amaonera ntchito.
16 Kumbukirani kuona mfundo za m’Baibulo musanasankhe zochita. Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito kuti tikhale ndi moyo, zimene zikusonyeza kuti tili ndi udindo wodzipezera zosoŵa pa moyo wathu. (2 Atesalonika 3:10-12) Komabe, pali zinthu zina zofunika. Tikukulimbikitsani kuŵerenga malemba otsatiraŵa ndi kuganizira mmene angathandizire wachinyamata kusamala pankhani yosankha ntchito: Miyambo 30:8, 9; Mlaliki 7:11, 12; Mateyu 6:33; 1 Akorinto 7:31; 1 Timoteo 6:9, 10. Pamene mwaŵerenga mavesi ameneŵa, kodi mukuona mmene Yehova amaonera nkhani imeneyi?
17 Ntchito siyenera kukhala yofunika kwambiri moti n’kuphimba kutumikira kwathu Yehova. Ngati mungapeze ntchito yabwinopo pogwiritsa ntchito maphunziro a ku sekondale, zili bwino. Ngati mungafunike maphunziro ena owonjezera mutamaliza maphunziro a ku sekondale, imeneyo ndi nkhani yoti mukambirane ndi makolo anu. Komabe, musasiye kuganizira “zinthu zofunika kwambiri,” zinthu zauzimu. (Afilipi 1:9, 10, NW) Musalakwitse monga mmene anachitira Baruki, mlembi wa Yeremiya. Anaona kuti mwayi wotumikira umene anali nawo sunali wofunika kwambiri ndipo ‘anadzifunira yekha zinthu zazikulu.’ (Yeremiya 45:5) Iye anaiŵala kwa kanthaŵi, kuti palibe ‘chinthu chachikulu’ m’dzikoli chimene chikanamuyandikizitsa kwa Yehova kapena kumuthandiza kupulumuka pamene Yerusalemu anali kudzawonongedwa. Masiku anonso n’chimodzimodzi.
Onani Zinthu Zauzimu Kukhala Zofunika
18, 19. (a) Kodi ambiri mwa anthu amene ali m’dera lanu akuvutika ndi chiyani, ndipo muyenera kuwamvera chiyani? (b) N’chifukwa chiyani ambiri samva njala yauzimu?
18 Kodi munaonapo m’manyuzipepala, ndi pa TV zithunzi za ana a m’mayiko amene akuvutika ndi njala? Ngati munaonapo, mosakayika munawamvera chisoni kwambiri. Kodi mumawamveranso chisoni mofananamo anthu amene ali m’dera limene mukukhala? N’chifukwa chiyani muyenera kuwamvera chisoni? Chifukwa chakuti ambiri mwa iwo alinso ndi njala yaikulu. Akuvutika ndi njala imene Amosi analosera, kuti: “Akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena Amosi 8:11.
ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.”—19 N’zoona kuti ambiri mwa anthu amene akuvutika ndi njala yauzimu imeneyi ‘sazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.’ (Mateyu 5:3) Ambiri samva kuti ali ndi njala yauzimu. Ena angafike ngakhale poona kuti akudya bwino. Koma ngati akuona choncho, akutero chifukwa chakuti akudya “nzeru ya dziko lapansi” yopanda phindu imene ikuphatikizapo kukondetsa chuma, malingaliro a sayansi, maganizo a anthu pankhani ya makhalidwe, ndi zina zotero. Ena amaganiza kuti “nzeru” zamakono zimachititsa ziphunzitso za Baibulo kukhala zachikale, zopanda ntchito. Komabe, “dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziŵa Mulungu.” Nzeru ya dziko lapansi singakuthandizeni kuyandikira kwa Mulungu. Nzeru ya dziko lapansi ndi “yopusa kwa Mulungu.”—1 Akorinto 1:20, 21; 3:19.
20. N’chifukwa chiyani n’kupanda nzeru kufuna kutsanzira anthu amene salambira Yehova?
20 Mukamaona zithunzi za ana anjalawo, kodi mumafuna mutafanana nawo? Mwachionekere ayi. Komatu, achinyamata ena m’mabanja achikristu asonyeza kuti akufuna kukhala ngati anthu amene akuvutika ndi njala yauzimu amene akukhala nawo pafupi. Mwachionekere, achinyamata oterowo amaganiza kuti achinyamata m’dzikoli ndi omasuka, akusangalala ndi moyo. Amaiŵala kuti achinyamata oterowo ndi otalikirana ndi Yehova. (Aefeso 4:17, 18) Amaiŵalanso zotsatirapo zopweteka za njala yauzimu. Zina mwa zimenezi ndi mimba zapathengo za achinyamata osakwanitsa zaka 20 ndiponso kuvutika maganizo ndi mavuto amene munthu amakhala nawo pa thupi lake chifukwa cha chiwerewere, kusuta, kuledzera, ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Kukhala ndi njala yauzimu kumachititsa munthu kukhala ndi mtima wopanduka, kusoŵa chiyembekezo, ndiponso kusadziŵa mmene angachitire ndi moyo wake.
21. Kodi tingadziteteze bwanji kuti tisatengere maganizo olakwika a anthu amene salambira Yehova?
21 Motero, mukakhala kusukulu pamodzi ndi ana asukulu anzanu amene salambira Yehova, musatengeke ndi maganizo awo. (2 Akorinto 4:18) Ena anganyoze zinthu zauzimu. Ndiponso, manyuzipepala, mawailesi ndi ma TV anganene mabodza osonyeza kuti palibe cholakwika kuchita chiwerewere, kuledzera, kapena kutukwana. Kanani zimenezo. Nthaŵi zonse chezani ndi anthu amene ali ndi “chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma.” Nthaŵi zonse khalani “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.” (1 Timoteo 1:19; 1 Akorinto 15:58) Khalani otanganidwa pa Nyumba ya Ufumu ndi muutumiki wakumunda. Pa zaka zimene muli pa sukulu, chitani nawo upainiya wothandiza nthaŵi ndi nthaŵi. Limbitsani moyo wanu wauzimu mwa kuchita zimenezi, ndipo simudzatengeka n’kusiya zinthu zauzimu.—2 Timoteo 4:5.
22, 23. (a) N’chifukwa chiyani Mkristu wachinyamata nthaŵi zambiri angapange zosankha zimene ena sangazimvetse? (b) Kodi achinyamata akulimbikitsidwa kuchita chiyani?
22 Kuona zinthu mwauzimu mwachionekere kudzakuchititsani kupanga zosankha zimene anthu ena sangazimvetse. Mwachitsanzo, mnyamata wina wachikristu anali ndi luso loimba ndiponso ankakhoza bwino kwambiri phunziro lililonse kusukulu. Atamaliza maphunziro, anayamba kugwira ntchito imene bambo ake ankagwira, yotsuka mawindo, n’cholinga choti athe kugwira ntchito imene anasankha yokhala mlaliki wa nthaŵi zonse, kapena kuti mpainiya. Aphunzitsi ake sanamvetse chifukwa chake anasankha kuchita zimenezi, koma ngati inu mwayandikira kwa Yehova, tikukhulupirira kuti mukumvetsa chifukwa chake.
23 Pamene mukuganizira mmene mungagwiritsire ntchito unyamata wanu wamtengo wapatali, ‘dzikundikireni nokha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti mukagwire moyo weniweniwo.’ (1 Timoteo 6:19) Onetsetsani kuti ‘mukukumbukira Mlengi wanu’ pa unyamata wanu, ndiponso kwa moyo wanu wonse. Imeneyi ndiyo njira yokhayo imene mungakonzekerere tsogolo labwino, tsogolo limene silidzatha.
Kodi Mukuganiza Bwanji Tsopano?
• Kodi ndi malangizo ouziridwa ati amene amathandiza achinyamata pokonzekera tsogolo?
• Kodi ndi njira zina ziti zimene wachinyamata ‘angayandikirire kwa Mulungu’?
• Kodi ndi zosankha zina ziti zimene wachinyamata angapange zimene zingakhudze tsogolo lake?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 15]
Kodi mudzalola kuti kuchita zofuna zanu kukuthereni mphamvu ndi changu chanu chonse cha paunyamata?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Achinyamata achikristu anzeru amaona zinthu zauzimu kukhala zofunika