Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Wolimba Mtima Ngati Yeremiya

Khalani Wolimba Mtima Ngati Yeremiya

Khalani Wolimba Mtima Ngati Yeremiya

“Yembekeza Yehova: limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.”​—SALMO 27:14.

1. Kodi Mboni za Yehova zikupeza madalitso aakulu ati?

MBONI ZA YEHOVA zikukhala m’paradaiso wauzimu. (Yesaya 11:6-9) M’dziko limene ladzala ndi mavutoli, Akristu ameneŵa ali m’malo auzimu apadera ndipo ali pamtendere ndi Yehova Mulungu ndiponso pamtendere wina ndi mnzake. (Salmo 29:11; Yesaya 54:13) Ndipo paradaiso wawo wauzimu akukulirakulira. Onse amene ‘akuchita chifuniro cha Mulungu kuchokera mumtima’ amathandizira kukulitsa paradaiso ameneyu. (Aefeso 6:6) Motani? Mwa kutsatira mfundo za m’Baibulo ndiponso mwa kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, motero amawapempha kupeza nawo madalitso aakulu a paradaiso ameneyu.​—Mateyu 28:19, 20; Yohane 15:8.

2, 3. Kodi ndi zinthu ziti zimene Akristu oona afunika kupirira?

2 Komabe, kukhala kwathu m’paradaiso wauzimu sikutanthauza kuti sitikumana ndi mavuto. Tikadali opanda ungwiro ndipo timavutika ndi matenda, ukalamba, ndipo pamapeto pake timafa. Ndiponso, tikuona kukwaniritsidwa kwa maulosi onena za “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1) Nkhondo, upandu, njala, ndi mavuto ena aakulu akuvutitsa anthu onse, ndipo nazonso Mboni za Yehova zimavutika nawo.​—Marko 13:3-10; Luka 21:10, 11.

3 Kuwonjezeranso pamenepo, tikudziŵa bwino kuti ngakhale kuti ndife otetezeka m’paradaiso wauzimu, anthu amene sali m’paradaisoyu akupitirizabe kutitsutsa. Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. Kumbukirani mawu amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso.” (Yohane 15:18-21) Zimenezi zikuchitikanso masiku ano. Anthu ambiri sakumvetsabe kalambiridwe kathu kapena sakaona ngati n’kofunika. Ena amatitsutsa, kutinyoza, kapena ngakhale kutida kumene, monga momwe Yesu anachenjezera. (Mateyu 10:22) Nthaŵi zambiri amatiipitsira mbiri mwa kufalitsa nkhani zabodza ndiponso zoipa kudzera m’manyuzipepala, mawailesi, ndi pa TV. (Salmo 109:1-3) Inde, tonsefe timakumana ndi mavuto ndipo ena mwa ife tingayambe kutaya mtima. Kodi tingapirire bwanji?

4. Kodi thandizo loti tipirire timalipeza kuti?

4 Yehova adzatithandiza. Wamasalmo analemba mouziridwa kuti: “Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova am’landitsa mwa onseŵa.” (Salmo 34:19; 1 Akorinto 10:13) Ambiri mwa ife tingachitire umboni kuti tikamakhulupirira Yehova ndi mtima wonse, iye amatilimbikitsa kuti tipirire mavuto ena alionse. Kumukonda kwathu ndiponso chimwemwe chimene tikuchiyembekezera zimatithandiza kulimbana ndi zinthu zolefula ndiponso mantha. (Ahebri 12:2) Motero, ngakhale kuti timavutika, timapitirizabe kukhala olimba.

Mawu a Mulungu Analimbikitsa Yeremiya

5, 6. (a) Kodi tili ndi zitsanzo zotani za olambira oona amene anapirira? (b) Kodi Yeremiya anachita zotani ataitanidwa kuti akhale mneneri?

5 M’mbiri yonse ya anthu, atumiki okhulupirika a Yehova apeza chimwemwe ngakhale kuti akumana ndi mavuto. Ena anakhalako m’nthaŵi ya chiweruzo pamene Yehova anasonyeza mkwiyo wake kwa anthu osakhulupirika. Ena mwa olambira okhulupirika oterowo anali Yeremiya ndi anthu ena ochepa a m’nthaŵi yake, ndiponso Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Zitsanzo zofunika kwambiri zimenezo, azitchula m’Baibulo kuti zitilimbikitse, ndipo tingaphunzirepo zambiri mwa kuphunzira nkhani zawo. (Aroma 15:4) Mwachitsanzo, taganizirani za Yeremiya.

6 Yeremiya ali mnyamata, anaitanidwa kuti akhale mneneri ku Yuda. Imeneyi sinali ntchito yophweka. Anthu ambiri anali kulambira milungu yonyenga. Ngakhale kuti Yosiya, amene anali mfumu pamene Yeremiya anayamba utumiki wake, anali wokhulupirika, mafumu onse amene anatsatira pambuyo pake anali osakhulupirika. Ndiponso, ambiri mwa anthu amene anali ndi udindo wolangiza anthu, monga aneneri ndi ansembe, sankatsatira choonadi. (Yeremiya 1:1, 2; 6:13; 23:11) Motero, kodi Yeremiya anamva bwanji pamene Yehova anamuitana kuti akhale mneneri? Anaopa kwambiri. (Yeremiya 1:8, 17) Yeremiya anafotokoza mmene anachitira poyambirira kuti: “Ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.”​—Yeremiya 1:6.

7. Kodi anthu a m’gawo la Yeremiya anali otani, ndipo iye anatani?

7 Anthu ambiri amene anali m’gawo la Yeremiya anali osalabadira, ndipo nthaŵi zambiri anali kumutsutsa kwambiri. Nthaŵi ina Pasuri, wansembe, anam’panda ndi kumuika m’matangadza. Yeremiya anafotokoza mmene anamvera nthaŵi imeneyo. Anati: “Nditi, Sindidzam’tchula Iye [Yehova], sindidzanenanso m’dzina lake.” Mwina inunso nthaŵi zina mumamva chimodzimodzi, kufuna kuti mungosiya. Onani zimene zinamuchititsa Yeremiya kulimbikirabe. Iye anati: “M’mtima mwanga muli [mawu a Mulungu, kapena kuti uthenga] ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.” (Yeremiya 20:9) Kodi mawu a Mulungu amakukhudzaninso motero?

Anzake a Yeremiya

8, 9. (a) Kodi mneneri Uriya anasonyeza kufooka kotani, ndipo zotsatira zake zinali zotani? (b) N’chifukwa chiyani Baruki analefulidwa, ndipo anathandizidwa motani?

8 Yeremiya sanali yekha pantchito yolosera. Anali ndi anzake ndipo zimenezo ziyenera kuti zinamulimbikitsa. Komabe, nthaŵi zina anzakewo sanachite zinthu mwanzeru. Mwachitsanzo, mneneri mnzake dzina lake Uriya anali kalikiliki kuchenjeza anthu kuti Yerusalemu ndi Yuda adzawonongedwa “monga mwa mawu onse a Yeremiya.” Komabe, pamene Mfumu Yehoyakimu inalamula kuti Uriya aphedwe, mneneriyu anachita mantha n’kuthaŵira ku Igupto. Zimenezo sizinamuthandize kuti apulumuke. Anthu a mfumu anamulondola, anamugwira, ndipo anamubweretsa ku Yerusalemu, kumene anaphedwa. Zimenezi ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Yeremiya.​—Yeremiya 26:20-23.

9 Mnzake wina wa Yeremiya anali mlembi wake, Baruki. Baruki anamuthandiza bwino kwambiri Yeremiya, koma nthaŵi ina nayenso anasiya kuona zinthu mwauzimu. Iye anayamba kudandaula, kuti: “Kalanga ine tsopano! pakuti Yehova wawonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.” Baruki atalefulidwa, anayamba kusiya kuona zinthu zauzimu kukhala zofunika kwambiri. Komabe, Yehova mokoma mtima anam’langiza mwanzeru Baruki, ndipo anasintha. Ndiyeno anamutsimikizira kuti adzapulumuka Yerusalemu akamadzawonongedwa. (Yeremiya 45:1-5) Yeremiya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri pamene Baruki anayambanso kuona bwino zinthu mwauzimu.

Yehova Anathandiza Mneneri Wake

10. Kodi Yehova analonjeza Yeremiya kuti amuthandiza bwanji?

10 Chofunika kwambiri n’chakuti Yehova sanasiye Yeremiya. Anali kumvetsa mmene mneneri wakeyo anali kumvera ndipo anamulimbikitsa ndi kumuthandiza monga momwe anafunikira. Mwachitsanzo, kuchiyambi kwa utumiki wa Yeremiya, iye atafotokoza kuti ankadziona ngati ndi wosayenerera, Yehova anamuuza kuti: “Usaope nkhope zawo; chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.” Ndiyeno, atamuuza mneneri wakeyo za ntchito yake, Yehova anati: “Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.” (Yeremiya 1:8, 19) N’zolimbikitsatu kwambiri zimenezo! Ndipo Yehova anaterodi.

11. Tikudziŵa bwanji kuti Yehova anakwaniritsa lonjezo lake loti adzathandiza Yeremiya?

11 Motero, ataikidwa m’matangadza ndiponso atanyozedwa pagulu, Yeremiya ananena mtima uli m’malo kuti: “Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzapunthwa, sadzandilaka; adzakhala ndi manyazi ambiri.” (Yeremiya 20:11) M’zaka zotsatira pamene anthu anayesera kuti aphe Yeremiya, Yehova anakhala nayebe. Ndiponso, mofanana ndi Baruki, Yeremiya anapulumuka pamene Yerusalemu anawonongedwa ndipo anakhala mfulu, pamene anthu amene ankamuzunzawo ndiponso amene ananyalanyaza machenjezo ake ena anafa ndipo ena anatengedwa ukapolo kupita ku Babulo.

12. Ngakhale kuti pangakhale zinthu zotilefula, kodi tiyenera kukumbukira chiyani?

12 Mofanana ndi Yeremiya, Mboni za Yehova zambiri masiku ano zimakumana ndi mavuto. Monga tafotokozera poyamba paja, ena mwa mavuto ameneŵa amayambika ndi kupanda ungwiro kwathu, ena amayambika ndi chisokonezo chimene chili m’dzikoli, ndipo mavuto enanso amayambika ndi anthu amene amatsutsa ntchito yathu. Mavuto oterowo angatilefule. Mofanana ndi Yeremiya tingafike pokayikira zopitirizabe utumiki wathu. Inde, tingayembekezere kulefulidwa nthaŵi ndi nthaŵi. Zolefula zimayesa kukula kwa chikondi chathu kwa Yehova. Motero tiyeni tiyesetse kuti kulefulidwa kusatichititse kusiya kutumikira Yehova monga mmene anachitira Uriya. M’malo mwake, tiyeni titsanzire Yeremiya ndi kukhulupirira kuti Yehova adzatithandiza.

Mmene Tingalimbanirane ndi Zolefula

13. Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha Yeremiya ndi Davide?

13 Yeremiya ankalankhula ndi Yehova Mulungu nthaŵi zonse, kumuuza mmene ankamvera mumtima mwake ndiponso kumupempha kuti amulimbikitse. Chimenecho ndi chitsanzo chabwino choti titsanzire. Davide wakale, amene anadalira Gwero lomweli la chilimbikitso, analemba kuti: “Mverani mawu anga, Yehova, zindikirani kulingirira kwanga. Tamvetsani mawu a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga: pakuti kwa Inu ndimapemphera.” (Salmo 5:1, 2) Nkhani youziridwa yosimba za moyo wa Davide imasonyeza kuti Yehova anayankha mobwerezabwereza mapemphero a Davide oti amuthandize. (Salmo 18:1, 2; 21:1-5) Mofananamo, tikakumana ndi chiyeso chachikulu kapena mavuto amene tili nawo akamaoneka ngati osatheka kuwagonjetsa, zimatonthoza tikapemphera kwa Yehova ndi kumuuza zimene zili mumtima mwathu. (Afilipi 4:6, 7; 1 Atesalonika 5:16-18) Yehova sakana kutimvetsera. M’malo mwake amatitsimikizira kuti ‘amatisamalira.’ (1 Petro 5:6, 7) Komabe, sikungakhale kwanzeru kupemphera kwa Yehova ndiyeno osamvetsera zimene iye amanena, kodi sichoncho?

14. Kodi mawu a Yehova anamukhudza bwanji Yeremiya?

14 Kodi Yehova amalankhula nafe motani? Taganiziraninso za Yeremiya. Popeza Yeremiya anali mneneri, Yehova ankalankhula naye mwachindunji. Yeremiya anafotokoza mmene mawu a Mulungu anakhudzira mtima wake. Anati: “Mawu anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mawu anu anakhala kwa ine chikondwerero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.” (Yeremiya 15:16) Inde, Yeremiya anakondwera kuti anatchedwa ndi dzina la Mulungu, ndipo mawu Ake anali amtengo wapatali kwa mneneriyu. Motero, mofanana ndi mtumwi Paulo, Yeremiya anafunitsitsa kulengeza uthenga umene anapatsidwa.​—Aroma 1:15, 16.

15. Kodi tingaike bwanji mawu a Yehova mumtima mwathu, ndipo sitingakhale chete ngati tiganizira zinthu ziti?

15 Yehova salankhula mwachindunji ndi munthu aliyense masiku ano. Komabe, tili ndi mawu a Mulungu m’Baibulo. Motero, ngati tiphunzira Baibulo mwakhama ndi kusinkhasinkha mwakuya zimene tikuphunzira, mawu a Mulungu adzakhala “chikondwerero ndi chisangalalo” cha mtima wathunso. Ndipo tingasangalale kuti timatenga dzina la Yehova tikamakauza anthu ena mawu amenewo. Tiyeni tisaiwale kuti palibe anthu enanso padziko lapansi masiku ano amene amalengeza dzina la Yehova. Ndi Mboni zake zokha zimene zimalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene wakhazikitsidwa ndiponso zimaphunzitsa anthu ofatsa kuti akhale ophunzira a Yesu Kristu. (Mateyu 28:19, 20) Ndifetu odala kwambiri! Poona ntchito imene Yehova watipatsa mwachikondi, kodi tingakhalirenji chete?

Tisamale ndi Ocheza Nawo

16, 17. Kodi Yeremiya anaona bwanji anthu ocheza nawo, ndipo tingamutsanzire bwanji?

16 Yeremiya anafotokoza chinthu china chimene chinamuthandiza kukhala wolimba mtima. Anati: “Sindinakhala m’msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.” (Yeremiya 15:17) Yeremiya anaona kuti ndi bwino kukhala yekha kusiyana ndi kusokonezedwa ndi anthu ocheza nawo oipa. Masiku anonso timaiona nkhaniyi mofanana ndi mmene Yeremiya ankaionera. Sitiiŵala chenjezo la mtumwi Paulo lakuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma,” ngakhale makhalidwe okoma amene takhala nawo kwa zaka zambiri.​—1 Akorinto 15:33.

17 Kucheza ndi anthu olakwika kungachititse kuti mzimu wa dziko uwononge maganizo athu. (1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2; Yakobo 4:4) Motero tiyeni tiphunzitse zizindikiritso zathu kapena kuti maganizo athu kuti tizizindikira anthu ocheza nawo amene angatisokoneze ndipo tiwapeŵeretu. (Ahebri 5:14) Ngati Paulo akanakhala kuti ali moyo masiku ano, mukuganiza kuti akanati chiyani kwa Mkristu amene amaonerera mafilimu oonetsa anthu akugonana kapena akuchita chiwawa kapenanso maseŵera achiwawa? Kodi akanamulangiza chiyani mbale amene amapanga ubwenzi pa Intaneti ndi anthu omwe sakuwadziŵa m’pang’onong’ono pomwe? Kodi akanamuganizira chiyani Mkristu amene amathera maola ambirimbiri kuseŵera maseŵera a pa vidiyo kapena kuonerera TV koma yemwe alibe chizoloŵezi chabwino chophunzira payekha?​—2 Akorinto 6:14b; Aefeso 5:3-5, 15, 16.

Khalanibe M’paradaiso Wauzimu

18. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe olimba mwauzimu?

18 Timaona kuti paradaiso wathu wauzimu ndi wamtengo wapatali. Palibe chimene chingafanane ndi paradaiso ameneyu m’dziko lapansi masiku ano. Ngakhale anthu osakhulupirira amayamikira chikondi, kuganizirana, ndi kukoma mtima kumene Akristu amasonyezana. (Aefeso 4:31, 32) Komabe, masiku ano kuposa ndi kale lonse, tifunika kulimbana ndi kulefulidwa. Kucheza ndi anthu abwino, kupemphera, ndi chizoloŵezi chabwino chophunzira zingatithandize kukhalabe olimba mwauzimu. Zidzatilimbikitsanso kudalira Yehova ndi mtima wonse polimbana ndi mavuto alionse.​—2 Akorinto 4:7, 8.

19, 20. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira? (b) Kodi nkhani yotsatirayi yalembedwera ndani, ndipo ingapindulitsenso ndani?

19 Tisalole kuti anthu amene amadana ndi uthenga wathu wa m’Baibulo atiopseze ndi kufooketsa chikhulupiriro chathu. Mofanana ndi adani amene anazunza Yeremiya, amene akulimbana nafe akulimbana ndi Mulungu. Sadzapambana. Yehova, yemwe ndi wamphamvu kuposa adani athu, amatiuza kuti: “Yembekeza Yehova: limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.” (Salmo 27:14) Tiyeni titsimikize mtima kusabwerera m’mbuyo pochita chabwino, tikukhulupirira Yehova ndi mtima wonse. Tiyeni tikhale ndi chikhulupiriro chonse kuti, mofanana ndi Yeremiya ndi Baruki, tidzatuta ngati sitifooka.​—Agalatiya 6:9.

20 Kulimbana ndi zolefula ndi nkhondo imene Akristu ambiri akumenya mosalekeza. Komabe, achinyamata amakumana ndi mavuto apadera. Koma alinso ndi mwayi wochita zambiri. Nkhani yotsatirayi yalembedwera achinyamata amene ali pakati pathu. Ingapindulitsenso makolo ndi achikulire onse odzipatulira mumpingo amene mwa mawu awo, mwa chitsanzo chawo, ndiponso mwa kulimbikitsa mwachindunji, angathandize achinyamata mumpingo.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tingayembekezere kukumana ndi zolefula, ndipo tiyenera kudalira ndani kuti atithandize?

• Kodi Yeremiya anagonjetsa bwanji kulefulidwa ngakhale kuti anali ndi ntchito yovuta kwambiri?

• N’chiyani chingachititse mtima wathu ‘kukondwera ndi kusangalala’ ngakhale tili m’mavuto?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 9]

Yeremiya anaganiza kuti anali wamng’ono kwambiri ndiponso sanali kudziŵa zambiri moti n’kukhala mneneri

[Chithunzi patsamba 10]

Ngakhale pamene anali kuzunzidwa, Yeremiya anadziŵa kuti Yehova anali naye “ngati wamphamvu ndi woopsa”