Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kusaloŵerera M’ndale Kumalepheretsa Kusonyeza Chikondi Chachikristu?

Kodi Kusaloŵerera M’ndale Kumalepheretsa Kusonyeza Chikondi Chachikristu?

Kodi Kusaloŵerera M’ndale Kumalepheretsa Kusonyeza Chikondi Chachikristu?

KUKHALA Mkristu kumafuna zambiri kuwonjezera pa kuŵerenga Baibulo, kupemphera, ndi kuimba nyimbo zachipembedzo patsiku Lamlungu. Kumafunanso kuchitira zinthu Mulungu ndiponso anthu. Baibulo limati: “Tisakonde ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’choonadi.” (1 Yohane 3:18) Yesu ankawadera nkhaŵa anthu ena, ndipo Akristu afunika kum’tsanzira. Mtumwi Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti nthaŵi zonse azikhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Koma kodi ntchito ya Ambuye ndi yotani? Kodi ikuphatikizapo kuyesa kusintha mfundo za boma pofuna kuthandiza anthu osauka ndiponso oponderezedwa? Kodi zimenezo ndi zomwe Yesu anachita?

Ngakhale kuti anthu anakakamiza Yesu kuti aloŵerere kapena kukhalira mbali nkhani za ndale, iye sanalole zimenezo. Anakana zoti Satana am’patse ulamuliro pa maufumu onse a dziko lapansi, anakana kuloŵetsedwa mu mkangano wokhudza kukhoma msonkho, ndipo anathaŵa pamene gulu lina lotchuka linafuna kum’longa ufumu. (Mateyu 4:8-10; 22:17-21; Yohane 6:15) Koma kusaloŵerera kwake m’ndale sikunamulepheretse kuthandiza anthu ena.

Yesu anaikira mtima kwambiri pa zinthu zomwe zikanathandiza anthu ena kwa nthaŵi yaitali. Ngakhale kuti zomwe iye anachita podyetsa anthu zikwi zisanu komanso kuchiritsa odwala zinapatsa anthu ochepa mpumulo wakanthaŵi, zomwe anaphunzitsa zinapangitsa kuti anthu onse athe kupeza madalitso osatha. Yesu sankadziŵika ngati wokonza zopereka chithandizo, koma ankadziŵika monga “Mphunzitsi” basi. (Mateyu 26:18; Marko 5:35; Yohane 11:28) Iye anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.”​—Yohane 18:37.

Kulalikira Zinthu Zabwino Kwambiri Kusiyana ndi Ndale

Choonadi chomwe Yesu anaphunzitsa sichinali mfundo zokhudza ndale. M’malo mwake choonadicho chinkafotokoza za Ufumu womwe Mfumu yake ndi Yesu mwiniyo. (Luka 4:43) Ufumu umenewu ndi boma lakumwamba, ndipo udzaloŵa m’malo mwa maboma onse a anthu ndi kuwabweretsera anthu mtendere wamuyaya. (Yesaya 9:6, 7; 11:9; Danieli 2:44) Motero, ndi Ufumu wokhawu womwe ukupatsa anthu chiyembekezo chenicheni. Kodi sichingakhale chikondi chachikulu kulengeza za chiyembekezo chodalirika chimenechi m’malo molimbikitsa anthu kudalira anthu anzawo kuti awakonzera tsogolo labwino? Baibulo limati: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti am’thandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake.” (Salmo 146:3-5) Motero m’malo motuma ophunzira ake kuti akalalikire njira yabwino yoyendetsera maboma, Yesu anawaphunzitsa kulalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’​—Mateyu 10:6, 7; 24:14.

Motero imeneyi ndiyo “ntchito ya Ambuye” imene alaliki achikristu anauzidwa kuti agwire. Popeza kuti nzika za Ufumu wa Mulungu zifunika kukondana, Ufumu umenewu udzathetsa umphaŵi mwa kugaŵa bwino zinthu zothandiza pa moyo wa munthu. (Salmo 72:8, 12, 13) Uwu ndiye uthenga wabwino ndipo ukuyenereradi kulalikidwa.

Masiku ano, Mboni za Yehova zikugwira “ntchito ya Ambuye” imeneyi mwadongosolo m’mayiko 235. Mogwirizana ndi lamulo la Yesu, zimalemekeza maboma onse. (Mateyu 22:21) Koma zimalemekezanso ndi kutsatira mawu aŵa omwe Yesuyo anauza omutsatira ake, akuti: “Simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi.”​—Yohane 15:19.

Ena amene kale ankalimbikitsa za ndale asintha ataphunzira bwino Baibulo. Mkulu wina wandale ku Italy amene anali membala wa bungwe la Catholic Action, lomwe limayendetsedwa ndi tchalitchi, anati: “Ndinayamba ndale poganiza kuti munthu afunika kuthandiza nawo kwambiri pantchito zandale ndiponso zachitukuko.” Atatula pansi udindo woyang’anira mzinda wina m’dzikolo n’cholinga choti azilalikira za Ufumu wa Mulungu monga mmodzi wa Mboni za Yehova, iye anafotokoza chifukwa chake ntchito za andale omwe ndi oona mtima sizipindula. Anati: “Dzikoli lili mmene lililimu, osati chifukwa chakuti anthu amakhalidwe abwino sanayesepo kusintha zinthu, koma, makamaka chifukwa chakuti kuipa kwa anthu ambiri kwapondereza zinthu zabwino zomwe anthu ochepa oona mtimawo amachita.”

Kusaloŵerera m’ndale n’cholinga cholalikira chiyembekezo chokha chodalirika cha anthu sikuti kumalepheretsa Akristu oona kuthandiza bwino anthu ena. Anthu amene iwo amawathandiza kuti akhale nzika za Ufumu wa Mulungu amaphunzira kusiya makhalidwe oipa, amaphunzira kulemekeza boma, kutukula miyoyo ya mabanja awo, ndiponso kukhala ndi malingaliro abwino pankhani ya chuma. Ndipo chofunika kuposa zonsezi n’chakuti Mboni za Yehova zimathandiza anthu kukhala paubwenzi wolimba ndi Mulungu.

Anthu amene amalalikira za Ufumu wa Mulungu amapindulitsa anthu a m’dera lomwe iwo akukhala. Koma kuposa pamenepo, iwo amathandiza anthu kudalira boma lomwe ndi lenileni ndipo lidzabweretsa mtendere wamuyaya kwa anthu onse okonda Mulungu. Chifukwa chakuti Akristu ameneŵa saloŵerera m’ndale, iwo ngomasuka kupereka thandizo lamuyaya ndiponso labwino kwambiri lomwe lilipo masiku ano.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

Kusiya Ndale N’kuyamba Kulalikira za Ufumu wa Mulungu

Átila ali mnyamata anaphunzira zakuti mpingo uyenera kubweretsa ufulu kwa anthu. Iye anaphunzira izi kuchokera kwa ansembe ake a pa parishi ya ku Belém, m’dziko la Brazil. Ankasangalala kwambiri akamamva kuti m’kupita kwa nthaŵi anthu adzamasuka ndipo sazidzaponderezedwanso ndipo anakaloŵa gulu lina lotsutsa boma, komwe anaphunzira zokonza zionetsero zosonyeza kusakondwa ndiponso zolimbikitsa anthu kutsutsa malamulo a boma.

Koma Átila ankasangalalanso kuphunzitsa ana a anthu a m’gululo, pogwiritsa ntchito buku lomwe anapatsidwa lakuti Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo. * Bukuli linkaphunzitsa za kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kumvera boma. Izi zinapangitsa Átila kudabwa kuti n’chifukwa chiyani anthu omwe amalimbikitsa mfundo yakuti mpingo uyenera kubweretsa ufulu kwa anthu satsatira makhalidwe abwino a Yesu ndiponso kuti n’chifukwa chiyani ena saganiziranso anthu oponderezedwa iwo akapeza udindo. Iye anachoka m’gulu lotsutsa bomalo. Kenako Mboni za Yehova zinam’peza kunyumba kwake ndi kumuuza za Ufumu wa Mulungu. Pasanapite nthaŵi yaitali, iye anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anali kuphunzira za njira yeniyeni yothetsera kuponderezedwa kwa anthu.

Akuphunzira Baibulo choncho, Átila anakachita nawo msonkhano wokhudza chipembedzo ndi ndale womwe unakonzedwa ndi Akatolika. Alangizi pa msonkhanowo anafotokoza kuti, “Chipembedzo ndi ndale ndi njira zosiyana zoonera chinthu chimodzi.” Anapitanso ku msonkhano wina pa Nyumba ya Ufumu. Panali kusiyana kwakukulu! Mwachitsanzo, panalibe kusuta fodya, kumwa mowa, kapena nthabwala zotukwana. Anaganiza zoti azigwira nawo ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova, ndipo posapita nthaŵi anabatizidwa. Tsopano akutha kuona chifukwa chake mfundo yakuti mpingo uyenera kubweretsa ufulu kwa anthu si njira yeniyeni yothetsera mavuto a anthu osauka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Zithunzi patsamba 6]

Kusaloŵerera m’ndale komwe atumiki achikristu amachita sikuwalepheretsa kuthandiza anthu ena