Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maso Anga Anatseguka Ngakhale Kuti Ndinali Wakhungu!

Maso Anga Anatseguka Ngakhale Kuti Ndinali Wakhungu!

Mbiri ya Moyo Wanga

Maso Anga Anatseguka Ngakhale Kuti Ndinali Wakhungu!

YOSIMBIDWA NDI EGON HAUSER

Patapita miyezi iŵiri ndili wakhungu, maso anga anatseguka n’kuona choonadi cha m’Baibulo chimene ndinachinyalanyaza m’moyo wanga wonse.

NDIKAMAKUMBUKIRA zochitika m’zaka zoposa 70 zapitazi, mbali zambiri za moyo wanga ndimakhutira nazo. Koma zikanakhala zotheka kusintha chinthu china, ndikanasankha kudziŵa za Yehova Mulungu kuyambira ndili wamng’ono.

Ndinabadwa m’chaka cha 1927 ku Uruguay, dziko laling’ono limene lili pakati pa dziko la Argentina ndi la Brazil ndipo lili ndi malo okongola a makilomita angapo m’mbali mwa gombe la nyanja ya Atlantic. Ambiri mwa anthu a m’dzikoli ndi mbadwa za Ataliyana ndi Aspanya amene analoŵa m’dzikoli kuchokera ku mayiko a kwawo. Komabe, makolo anga anali ochokera ku Hungary, ndipo pamene ndinali wamng’ono kwambiri, tinkakhala m’dera la anthu osati opeza bwino kwenikweni, koma ogwirizana kwambiri. Sitinkafunikira kuika maloko pa zitseko zathu kapena kuika zitsulo m’mawindo zotetezera akuba. Sitinkasankhana mitundu. Tonse, ochokera mayiko ena komanso a m’dziko lomwelo, kaya akuda, kapena azungu, tinali mabwenzi.

Makolo anga anali Akatolika, ndipo ndinadzakhala mnyamata wothandizira misa ndili ndi zaka khumi. Nditakula, ndinkagwira ntchito ku parishi yakwathuko ndipo ndinali m’gulu la alangizi a bishopu wa chigawocho. Popeza ndinasankha ntchito ya udokotala, ndinapemphedwa kukakhala nawo pa msonkhano umene unachitikira ku Venezuela umene unakonzedwa ndi mpingo wa Katolika. Monga madokotala amene tinaphunzira kwambiri za matenda a akazi, gulu lathu linapatsidwa ntchito yofufuza za mankhwala akumwa olerera amene anangoyamba kumene kugulitsidwa panthaŵiyo.

Chidwi Chimene Ndinali Nacho Poyamba Ndikuphunzira Udokotala

Ndikuphunzirabe udokotala n’kuona mmene thupi la munthu lilili, ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene thupi linapangidwira ndipo zinasonyeza kuti panagona nzeru polipanga. Mwachitsanzo, ndinachita chidwi kuti thupi limatha kudzichiza lokha ndiponso limatha kupola likakhala ndi bala, monga ngati mmene chiwindi kapena nthiti zina zimakulira ndi kubwerera mwakale zikadulidwa pang’ono.

Komanso, ndinaona anthu ambiri amene anachita ngozi zoopsa, ndipo ndinkamva chisoni pamene anali kumwalira chifukwa chakuti anaikidwa magazi. Ndikukumbukirabe mpaka pano mmene zinalili zovuta kulankhula ndi achibale a odwala amene anamwalira chifukwa cha mavuto amene anakhalapo chifukwa choikidwa magazi. Nthaŵi zambiri, achibalewo sankauzidwa kuti okondedwa awowo anamwalira chifukwa choikidwa magazi. M’malo mwake ankauzidwa zifukwa zina. Ngakhale kuti papita zaka zambiri, ndikukumbukirabe kuti ndinali kukayikakayika ngati kuika munthu magazi kunali koyenera, ndipo kenako ndinaona kuti kuchita zimenezi kunali kolakwika. Zikanakhala bwino ndikanadziŵa lamulo la Yehova pankhani ya kupatulika kwa magazi. Ndikanadziŵa, sindikanakayikakayika ngati zimene ndinaona zikuchitikazo zinali zoyenera kapena ayi.​—Machitidwe 15:19, 20.

Kukhutira Pothandiza Anthu

Patapita nthaŵi, ndinakhala dokotala wa opaleshoni ndiponso ndinali mkulu wa pachipatala cha Santa Lucía. Ndinkagwiranso ntchito zina ku bungwe la National Institute of Biological Science. Zimenezi zinandikhutiritsa kwambiri. Ndinawathandiza anthu pa matenda awo, kuthetsa kuvutika kwawo, ndipo nthaŵi zambiri kupulumutsa miyoyo, ndiponso kubadwitsa ana mwa kuthandiza azimayi panthaŵi yobereka. Chifukwa cha zimene ndinaona m’mbuyo pankhani ya kuika magazi, ndinapeŵa kuika anthu magazi ndipo ndinachita maopaleshoni ambirimbiri popanda kuika magazi. Ndinkaona kuti kutayika kwa magazi kukufanana ndi kutayika kwa madzi mumgolo wobooka. Njira yothetsera kutayika kwa madziko ndi kukonza pamene pabookapo, osati kuthira madzi ena mumgolomo.

Kuthandiza Odwala Omwe Anali Mboni

Ndinayamba kudziŵana ndi a Mboni za Yehova cha m’ma 1960 pamene anayamba kubwera kuchipatala chathu kuti adzachitidwe opaleshoni yopanda magazi. Sindidzaiŵala nkhani ya wodwala wina, yemwe anali mpainiya (mtumiki wa nthaŵi zonse) dzina lake Mercedes Gonzalez. Anali ndi magazi ochepa kwambiri moti madokotala a pachipatala cha pa yunivesite anaona kuti sangaike dala moyo wake pachiswe pomuchita opaleshoni, chifukwa anali otsimikiza kuti sangakhale ndi moyo ngati atachita zimenezo. Ngakhale kuti anali kutaya magazi, tinamuchita opaleshoni pa chipatala chathu. Opaleshoniyo inayenda bwino, ndipo anapitiriza kuchita upainiya kwa zaka zoposa 30 mpaka pamene anamwalira posachedwapa ali ndi zaka 86.

Nthaŵi zonse ndinkachita chidwi ndi chikondi ndiponso kuganizirana kumene Mboni zinkasonyeza zikamasamalira abale awo achikristu amene anali m’chipatala. Ndikamayendera odwala m’chipatala, ndinkakonda kumvetsera akamalankhula za zikhulupiriro zawo, ndipo ndinkalandira mabuku amene ankandipatsa. Sindinaganize kuti pasanapite nthaŵi yaitali sindidzangokhala dokotala wawo chabe koma ndidzakhalanso mbale wawo wauzimu.

Ndinayamba kukumana kwambiri ndi Mboni pamene ndinakwatira Beatriz, mwana wa munthu wina amene anali kudwala. Ambiri mwa anthu a m’banja lake anali atayamba kale kusonkhana ndi Mboni, ndipo titakwatirana, nayenso anakhala Mboni yachangu. Koma ine ndinali wotanganidwa kwambiri ndi ntchito yanga ndipo ndinali wotchuka ndithu pankhani ya zamankhwala. Moyo unkaoneka kuti ukukoma. Sindinadziŵe kuti zinthu zisintha pasanapite nthaŵi yaitali.

Ndinakumana ndi Mavuto

Chimodzi mwa zinthu zoipa kwambiri zimene zingamuchitikire dokotala wa opaleshoni ndicho kusiya kuona. Ndi zimene zinandichitikira ine. M’kati mwa maso anga onse aŵiri munawonongeka mwadzidzidzi, ndipo ndinakhala wakhungu. Sindinadziŵe ngati ndidzayambanso kuona. Atandichita opaleshoni, ndinagona pabedi maso anga onse atamangidwa bandeji ndipo ndinavutika maganizo kwambiri. Ndinadziona ngati wopanda ntchito ndiponso wopanda chiyembekezo moti ndinaganiza zodzipha. Popeza ndinali pa nsanjika yachitatu pa nyumba yosanjikiza, ndinadzuka pa bedi ndipo ndinayambasira khoma, kufuna kuti ndifike pawindo. Ndinafuna kuti ndikafika pawindopo ndidumphe kuti ndife. Koma m’malo mofika pawindo, ndinapezeka kuti ndili m’njira ya m’kati mwa chipatalacho, ndipo nesi ananditenga n’kundibwezera pa bedi langa.

Sindinayeserenso kuchita zimenezi. Komabe chifukwa choti sindinali kuona, ndinapitirizabe kuvutika maganizo ndipo ndinali wokwiya. Panthaŵi imene sindimaonayi, ndinalonjeza Mulungu kuti ngati ndingadzathenso kuona, ndidzaŵerenga Baibulo lonse. Patapita nthaŵi, ndinayamba kuona pang’ono ndipo ndinkatha kuŵerenga. Koma sindikanapitiriza kugwira ntchito monga dokotala wa opaleshoni. Komabe, ku Uruguay kuli mwambi wakuti “No hay mal que por bien no venga,” “Palibe chinthu choipa kwambiri moti sichingatulutse chinthu chabwino.” Panangotsala nthaŵi yochepa kuti nditsimikizire kuti mwambiwu ndi woona.

Kuyamba Molakwika

Ndinafuna kugula Baibulo la The Jerusalem Bible la zilembo zazikulu, koma ndinamva kuti Mboni za Yehova zinali ndi Baibulo lotsika mtengo kwambiri, ndipo Mboni ina yachinyamata inadzipereka kuti idzabweretsa kunyumba kwanga. Tsiku lotsatira m’maŵa, iye anafika n’kuima pakhomo la kumaso kwa nyumba yanga atatenga Baibulolo. Mkazi wanga anatsegula chitseko ndipo analankhula naye. Ndinalankhula mwamwano ndiponso mokalipa ndili m’nyumbamo kuti ngati mkazi wangayo wapereka ndalama zogulira Baibulolo, panalibe chifukwa choti mnyamatayo akhalebe pa nyumba panga ndipo ayenera kupita, ndipo anaterodi mwamsanga. Sindinadziŵe kuti munthu ameneyu posakhalitsa adzathandiza kwambiri moyo wanga.

Tsiku lina ndinalonjeza mkazi wanga chinthu chimene ndinalephera kukwaniritsa. Motero, pofuna kukonza zinthu ndi kum’sangalatsa, ndinanena kuti ndidzapita naye limodzi ku Chikumbutso cha imfa ya Yesu chimene chimachitika chaka ndi chaka. Tsikulo litafika, ndinakumbukira lonjezo langa ndipo ndinapita limodzi ndi mkazi wanga ku Chikumbutsoko. Ndinachita chidwi kwambiri ndi ubwenzi umene ndinaona ndiponso mmene anandilandirira mwachikondi. Wokamba nkhani atayamba nkhani yake, ndinadabwa kuona kuti ndi mnyamata yemwe uja amene ndinamuuza mwamwano kuti achoke panyumba panga. Nkhani yakeyo inandikhudza kwambiri, ndipo ndinadzimvera chisoni kuti sindinamuchitire zinthu mokoma mtima. Kodi ndikanatani tsopano kuti ndikonze zinthu?

Ndinapempha mkazi wanga kuti am’pemphe kuti adzadye nafe chakudya chamadzulo, koma mkazi wangayo anati: “Mukuona bwanji, sizingakhale bwino kuti mum’pemphe inuyo? Ingokhalani pomwepa atipeza.” Ananena zoona. Mnyamatayo anabwera kudzatipatsa moni ndipo anavomera mosangalala kuti adzabwera kunyumba kwathu.

Zimene tinakambirana madzulo amene iye anabwera kudzacheza kwathuko zinakhala chiyambi cha zinthu zambiri zimene zinasintha pa moyo wanga. Anandisonyeza buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, * ndipo ndinam’sonyeza mabuku ameneŵa okwana sikisi. Mboni zosiyanasiyana zimene zinali kudwala zinandipatsa mabuku ameneŵa kuchipatala, koma ndinali ndisanawaŵerenge. Tikudya chakudyacho komanso titamaliza, ndinafunsa mafunso ambiri mpaka usiku kwambiri, ndipo anayankha mafunso onse pogwiritsa ntchito Baibulo. Tinakambirana mpaka kufika maola oyambirira a mmaŵa wa tsiku lotsatira. Asanachoke, mnyamatayo anadzipereka kuti aziphunzira nane Baibulo, pogwiritsa ntchito buku lakuti Coonadi. Tinamaliza kuphunzira buku limenelo m’miyezi itatu ndipo tinapitiriza kuphunzira m’buku lakuti “Babylon the Great Has Fallen!” God’s Kingdom Rules! * Titamaliza buku limeneli, ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova Mulungu ndipo ndinabatizidwa.

Kuyambanso Kudziona Kuti Ndine Wofunika

Chifukwa cha khungu lenileni, ‘maso a mtima wanga’ anatseguka n’kuona choonadi cha Baibulo chimene ndinachinyalanyaza mpaka kudzafika panthaŵiyi. (Aefeso 1:18) Kudziŵa Yehova ndi cholinga chake chachikondi kunasintha moyo wanga wonse. Ndayambanso kudziona kuti ndine wofunika ndipo ndikusangalala. Ndimathandiza anthu pa mavuto okhudza thupi lawo ndiponso kuwathandiza mwauzimu. Ndimawasonyezanso mmene angachitire kuti moyo wawo utalikirepo kwa zaka zingapo m’dongosolo la zinthu lino ndiponso kuti adzakhale ndi moyo kosatha m’dziko latsopano.

Ndimayenderabe limodzi ndi kupita patsogolo kwa zamankhwala, ndipo ndachita kafukufuku wokhudza mavuto amene amakhalapo chifukwa choika munthu magazi, njira zina zothandizira odwala popanda kuwaika magazi, ufulu wa odwala, ndi malamulo a zamankhwala okhudza khalidwe labwino. Ndakhala ndi mwayi wouza anthu odziŵa zamankhwala m’dziko lathu nkhani zimenezi pamene ndakhala ndikuitanidwa kukakamba nkhani zimenezi pa misonkhano ya zamankhwala. Mu 1994, ndinakachita nawo msonkhano woyamba wokhudza chithandizo cha mankhwala chosagwiritsa ntchito magazi ku Rio de Janeiro, ku Brazil, ndipo ndinakamba nkhani yokhudza mmene madokotala angachitire wodwala akamataya magazi. Mbali ina ya nkhaniyo inaphatikizidwa mu nkhani imene ndinalemba yakuti, “Una propuesta: Estrategias para el Tratamiento de las Hemorragias” (“Mfundo Zothandiza Popereka Chithandizo Choletsa Kutayika kwa Magazi”), imene inafalitsidwa m’magazini ya zamankhwala ya Hemoterapia.

Kukhala Wokhulupirika Panthaŵi Yoyesedwa

Poyambirira, ndinali kukayikira zoika munthu magazi makamaka chifukwa cha maphunziro anga a sayansi. Koma pamene nanenso ndinadwala n’kugonekedwa m’chipatala, ndinaona kuti sizinali zophweka kukana kuikidwa magazi ndi kukhala wokhulupirika pamene madokotala anali kundiumiriza. Nditadwala kwambiri mtima, ndinafotokoza maganizo anga kwa dokotala wa opaleshoni kwa nthaŵi yoposa maola aŵiri. Dokotalayo anali mwana wa anzanga okondeka ndipo ananena kuti sangalolere kuti ndimwalire pamene iye akuona kuti ndikhoza kuchira ngati atandiika magazi. Ndinapemphera kwa Yehova chamumtima, kum’pempha kuti amuthandize dokotalayu kumvetsa ndi kutsatira maganizo anga ngakhale kuti sanali kugwirizana nawo. Mapeto ake, dokotalayo analonjeza kuti adzatsatira zofuna zanga.

Ulendo wina, panafunika kuti andichotse chotupa pa kachiwalo kena kotchedwa prostate. Magazi ambiri anatayika. Ndinayeneranso kufotokoza chifukwa chake sanayenera kundiika magazi, ndipo ngakhale kuti ndinataya magawo aŵiri mwa magawo atatu a magazi anga onse, madokotala anatsatira zimene ndinafuna.

Kusintha Maganizo

Popeza ndine wa m’bungwe loona za malamulo a zamankhwala la International Association of Bioethics, ndasangalala kuona madokotala ndi akuluakulu a zamalamulo akusintha maganizo pankhani ya ufulu wa odwala. Maganizo oti wodwala ayenera kutsatira zimene dokotala wanena akusintha ndipo tsopano akulemekeza zimene wodwala wasankha atadziŵa zonse. Tsopano akulola odwala kusankha chithandizo chimene akufuna. Mboni za Yehova tsopano sizikuonedwanso ngati anthu oumirira zinthu mosayenera omwe sakuyenerera kulandira chithandizo kuchipatala. M’malo mwake amaonedwa kukhala odwala odziŵa zinthu omwe ufulu wawo uyenera kulemekezedwa. Pa misonkhano ya zamankhwala ndiponso pa mapulogalamu a pa TV, mapulofesa odziŵika bwino anenapo mawu akuti: “Chifukwa cha khama la Mboni za Yehova, tikutha kumvetsa tsopano . . . ” “Taphunzira kwa Mboni . . . ” ndiponso kuti “[Mboni] zatiphunzitsa kuwongolera.”

Pali mawu akuti moyo ndi wofunika kwambiri kuposa china chilichonse chifukwa ufulu ndi ulemu zikanakhala zopanda phindu pakadapanda moyo. Anthu ambiri tsopano akuvomereza mfundo yaikulu yokhudzana ndi malamulo, kuzindikira kuti munthu aliyense ali ndi ufulu wake ndipo ndi iye yekha amene angasankhe kuti ndi zinthu ziti zimene ziyenera kukhala pa malo oyamba pa zochitika zina zilizonse. Mwa njira imeneyi, kulemekezana, ufulu wosankha, ndiponso zikhulupiriro za chipembedzo zimaikidwa patsogolo. Wodwala ali ndi ufulu wosankha zinthu zokhudza thanzi lake. Dipatimenti Yopereka Chidziŵitso cha Zachipatala imene Mboni za Yehova zinakhazikitsa yathandiza madokotala ambiri kuti azimvetsa bwino nkhani zimenezi.

Zimene a m’banja langa akuchita popitiriza kundithandiza, zandichititsa kuti ndithe kutumikira Yehova ndiponso kukhala mkulu mumpingo wachikristu. Monga momwe ndafotokozera poyamba, ndimadandaula kwambiri kuti sindinaphunzire za Yehova ndikadali wamng’ono. Komabe, ndikuthokoza kwambiri kuti anatsegula maso anga n’kukhala ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chodzakhala mu Ufumu wa Mulungu, mmene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—Yesaya 33:24. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 24 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 24 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 34 Mbale Egon Hauser anamwalira nkhani ino ikukonzedwa. Anamwalira ali wokhulupirika, ndipo tikukondwera naye limodzi kuti chiyembekezo chake n’chotsimikizika.

[Chithunzi patsamba 24]

Ndikugwira ntchito ku chipatala ku Santa Lucía ndili ndi zaka za m’ma 30

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili ndi mkazi wanga Beatriz, mu 1995