Chinsinsi cha Moyo Wautali Ndiponso Wachimwemwe
Chinsinsi cha Moyo Wautali Ndiponso Wachimwemwe
ANTHU ena amati munthu aliyense amafuna kukula, koma palibe amene amafuna kukalamba. Ambiri akamayandikira zaka zopuma pantchito, amayembekezera kuti adzakhala ndi nthaŵi yambiri yochitira zofuna zawo ndiponso adzakhala ndi udindo wochepa. Koma amada nkhaŵa kuti mwina adzakhala opanda chochita chilichonse komanso opanda phindu. Amadanso nkhaŵa kuti mwina azidzangokhala okhaokha, opanda chimwemwe, ndi opanda moyo wamphamvu.
Choncho, kodi chinsinsi cha moyo wachimwemwe n’chiyani? Achinyamata komanso okalamba amapeza chimwemwe pokhala ndi mabwenzi abwino ndiponso banja lokondana. Koma sikuti munthu wokalamba amapeza chimwemwe kokha chifukwa cha zinthu zomwe ena akum’chitira pa moyo wake. Chofunika kwambiri ndi zimene wokalambayo amachitira anthu ena.
Kafukufuku wina amene anachitika nthaŵi yaitali pa mabanja 423 a anthu okalamba, anasonyeza kuti “kuthandiza ena pamoyo wawo kungatalikitse moyo wa munthu wothandizayo.” Stephanie Brown, amene anachita kafukufukuyu, anati: “Zimene tapezazi zikusonyeza kuti sitipindula kwambiri ndi zimene timapeza pogwirizana ndi anzathu; koma timapindula ndi zimene ifeyo timawapatsa.” Kupatsa kumeneku kungaphatikizepo kuthandiza ena ntchito zapakhomo, kulera ana, kuwapitira kwina ndi kwina, kuwathandiza kayendedwe, kapena kumvetsera munthu wina amene akufuna kutilankhula.
Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu Kristu anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kukhala ndi ndalama zambiri ku banki kapena kumwa makhwala oletsa kukalamba kayanso kudya zakudya zinazake, sikuthandiza kuti munthu akhale ndi moyo wautali ndiponso wachimwemwe. Koma, chofunika ndicho kukhala wotakataka ndi kugwiritsa ntchito nthaŵi ndi mphamvu zathu kuthandiza ena.
Komabe, kupatsa sikungathetse kukalamba, kudwala ndi kufa. Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzathetse zinthu zimenezi. Ufumuwo ukamadzalamulira, sipadzakhalanso matenda ngakhalenso “imfa.” (Chivumbulutso 21:3, 4; Yesaya 33:24) Ndipotu, anthu omvera adzakhala ndi moyo wosatha mwachimwemwe m’paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43) Mboni za Yehova zimasangalala kufotokozera ena chinsinsi cha m’Baibulo chimenechi chokhalira ndi moyo wautali ndiponso wachimwemwe.