Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusamalira Okalamba ndi Udindo wa Akristu

Kusamalira Okalamba ndi Udindo wa Akristu

Kusamalira Okalamba ndi Udindo wa Akristu

“Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu.”​—YESAYA 46:4.

1, 2. Kodi chisamaliro cha Atate athu akumwamba n’chosiyana motani ndi chisamaliro chimene makolo amapereka?

MAKOLO odzipereka amasamalira ndi kuteteza ana awo kuyambira ali makanda mpaka pamene akukula kufika paunyamata. Ngakhale pamene achinyamatawo akula n’kukhala ndi mabanja awoawo, atate ndi amayi awo amapitiriza kuwasamalira mwachikondi ndiponso kuwathandiza.

2 Ngakhale kuti pali malire a zimene anthu angachitire ana awo, Atate athu akumwamba nthaŵi zonse amasamalira mwachikondi atumiki ake okhulupirika ndi kuwateteza. Polankhula kwa anthu ake akale omwe anawasankha, Yehova anati: “Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu.” (Yesaya 46:4) Ameneŵa ndi mawu olimbikitsa kwambiri kwa Akristu okalamba. Yehova sasiya anthu amene akhalabe okhulupirika kwa iye. M’malo mwake, amalonjeza kuti adzawachirikiza, kuwathandiza, ndiponso kuwatsogolera m’moyo wawo wonse, ngakhale paukalamba wawo.​—Salmo 48:14.

3. Kodi m’nkhaniyi tikambirana chiyani?

3 Kodi tingatengere motani zimene Yehova amachita posamalira mwachikondi anthu okalamba? (Aefeso 5:1, 2) Tiyeni tione zimene ana a anthu okalamba, oyang’anira mumpingo, ndiponso Mkristu aliyense payekha angachite posamalira zosoŵa za okalamba amene ali pakati pa abale athu a padziko lonse.

Udindo Wathu Anafe

4. Kodi ana achikristu ali ndi udindo wotani kwa makolo awo?

4 “Lemekeza atate wako ndi amako.” (Aefeso 6:2; Eksodo 20:12) Pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva koma atanthauzo kwambiri ameneŵa ochokera m’Malemba Achihebri, mtumwi Paulo anakumbutsa ana udindo umene ali nawo kwa makolo awo. Koma kodi mawu ameneŵa akugwira ntchito motani pankhani yosamalira okalamba? Chitsanzo cholimbikitsa kwambiri cha zomwe zinachitika Chikristu chisanayambe chitithandiza kuyankha funso limeneli.

5. (a) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yosefe sanaiwale udindo umene anali nawo kwa makolo ake? (b) Kodi kulemekeza makolo athu kumatanthauzanji, ndipo pankhaniyi Yosefe anatipatsa chitsanzo chabwino chotani?

5 Yosefe anakhala zaka zoposa 20 asanaonane ndi bambo ake okalamba, kholo lakale Yakobo. Komabe, n’zoonekeratu kuti Yosefe anali kumukondabe Yakobo monga atate ake. Ndipotu, Yosefe atadziulula kwa abale ake, anafunsa kuti: “Kodi akali ndi moyo atate wanga?” (Genesis 43:7, 27; 45:3) Nthaŵi imeneyo n’kuti ku Kanani kuli njala. Motero Yosefe anatumiza uthenga kwa atate ake, wakuti: “Tsikirani kwa ine, musachedwe. Ndipo mudzakhala m’dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, . . . ndipo ndidzachereza inu komweko.” (Genesis 45:9-11; 47:12) Inde, kulemekeza makolo okalamba kumaphatikizapo kuwateteza ndi kuwapatsa chithandizo panthaŵi yomwe sangathe kudzithandiza okha. (1 Samueli 22:1-4; Yohane 19:25-27) Yosefe analandira udindo umenewu mosanyinyirika.

6. Kodi Yosefe anasonyeza motani chikondi chake kwa atate ake, ndipo tingatsanzire motani chitsanzo chake?

6 Mothandizidwa ndi Yehova, Yosefe anakhala mmodzi mwa anthu olemera ndi amphamvu kwambiri ku Igupto. (Genesis 41:40) Koma sanadzione kuti anali wofunika kwambiri kapena wotanganidwa kwambiri moti n’kulephera kulemekeza atate ake omwe anali ndi zaka 130. Atamva kuti Yakobo (kapena kuti Israyeli) wayandikira, “Yosefe anamanga galeta lake nakwera kumka kukakomana naye Israyeli atate ake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m’kulira pakhosi pake.” (Genesis 46:28, 29) Kuwachingamira kumeneku sikuti kunali kusonyeza ulemu mwamwambo chabe. Yosefe ankawakonda kwambiri atate ake okalamba ndipo sanachite manyazi kusonyeza chikondi chakecho. Ngati tili ndi makolo okalamba, kodi nafenso timawasonyeza chikondi mosachita manyazi?

7. N’chifukwa chiyani Yakobo anafuna kukaikidwa m’manda a ku Kanani?

7 Yakobo anakhalabe wodzipereka kwambiri kwa Yehova mpaka pamene anamwalira. (Ahebri 11:21) Chifukwa chokhulupirira malonjezo a Mulungu, Yakobo anapempha kuti akaikidwe m’manda a ku Kanani. Yosefe analemekeza atate ake mwa kumvera pempho lawo, ngakhale kuti kutero kunafuna zambiri komanso inali ntchito yaikulu.​—Genesis 47:29-31; 50:7-14.

8. (a) Kodi chinthu chachikulu chimene chimatilimbikitsa kusamalira makolo okalamba n’chiyani? (b) Kodi mtumiki wina wa nthaŵi zonse anachita chiyani pofuna kusamalira makolo ake okalamba? (Onani bokosi patsamba 17.)

8 Kodi n’chiyani chinachititsa Yosefe kusamalira atate ake? Ngakhale kuti anachita zimenezi chifukwa cha chikondi komanso pofuna kusonyeza kuyamikira munthu amene anam’patsa moyo ndi kumulera, sitikukayikira kuti Yosefe ankafunitsitsanso kusangalatsa Yehova. Nafenso tiyenera kutero. Paulo analemba kuti: “Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi n’cholandirika pamaso pa Mulungu.” (1 Timoteo 5:4) Inde, kukonda Yehova ndiponso kumuopa momupatsa ulemu kudzatilimbikitsa kusamalira makolo okalamba, mosaganizira kuti kuchita zimenezo kungabweretse mavuto otani. *

Mmene Akulu Amasonyezera Kuti Amadera Nkhaŵa

9. Kodi Yehova waika ndani kuti aŵete nkhosa, kuphatikizapo Akristu okalamba?

9 Chakumapeto kwa moyo wake wautali, Yakobo anati Yehova ndi “Mulungu amene anandidyetsa ine nthaŵi zonse za moyo wanga kufikira lero.” (Genesis 48:15) Masiku ano Yehova akudyetsa kapena kuti kuŵeta atumiki ake apadziko lapansi kudzera mwa oyang’anira achikristu, kapena kuti akulu, omwe akuyang’aniridwa ndi Mwana wake, Yesu Kristu, yemwe ndi “Mbusa wamkulu.” (1 Petro 5:2-4) Kodi oyang’anira angatsanzire motani Yehova pamene akusamalira nkhosa zokalamba?

10. Kodi n’chiyani chachitika pofuna kupereka chithandizo kwa Akristu okalamba? (Onani bokosi patsamba 19.)

10 Mpingo wachikristu utangokhazikitsidwa, atumwi anasankha “amuna asanu ndi aŵiri . . . odzala ndi mzimu ndi nzeru” kuti ayang’anire ntchito yogaŵa chakudya “tsiku ndi tsiku” kwa akazi achikristu amasiye. (Machitidwe 6:1-6) Patapita nthaŵi, Paulo analangiza Timoteo, amene anali woyang’anira, kuti akazi amasiye okalamba amene anali achitsanzo chabwino awaike pamndandanda wa anthu ofunika kulandira chithandizo. (1 Timoteo 5:3, 9, 10) Mofanana ndi zimenezi, oyang’anira m’mipingo masiku ano amakhala ofunitsitsa kukonza zothandiza Akristu okalamba ngati pangafunike kutero. Koma pamafunika zambiri pankhani yothandiza okalamba okhulupirika.

11. Kodi Yesu ananenanji za mkazi wamasiye waumphaŵi amene anapereka ndalama yochepa kwambiri?

11 Chakumapeto kwa utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu anakhala pansi pakachisi “napenya . . . khamu la anthu ali kuponya ndalama mosungiramo.” Kenako anachita chidwi kwambiri ndi munthu wina. Nkhaniyo imati: “Anadza mkazi wamasiye waumphaŵi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiŵiri tating’ono tofa kakobiri kamodzi.” Yesu anaitana ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphaŵi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo: pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zawo; koma iye anaponya mwa kusoŵa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.” (Marko 12:41-44) Tikaganizira za kuchuluka kwa ndalama, mkazi wamasiyeyo anapereka ndalama yochepa kwambiri, koma Yesu anadziŵa kuti Atate ake akumwamba amaona kuti kudzipereka ndi mtima wonse koteroko ndi kwamtengo wapatali. Mosaganizira kuti mkazi wamasiye waumphaŵiyo anali ndi zaka zingati, Yesu anayamikira zomwe anachita.

12. Kodi akulu angasonyeze motani kuti amayamikira zimene Akristu okalamba amachita?

12 Mofanana ndi Yesu, oyang’anira achikristu sapeputsa zimene okalamba amachita popititsa patsogolo kulambira koona. Akulu ayenera kuyamikira okalamba chifukwa choloŵa mu utumiki, kutenga nawo mbali pamisonkhano, kulimbikitsa mpingo, ndiponso chifukwa cha kupirira kwawo. Mawu ochoka pansi pamtima oyamikira okalamba angawathandize ‘kukhala ndi chodzitamandira’ kapena kuti chosangalalira mu utumiki wawo wopatulika. Zimenezi zimawathandiza kuti asakhumudwe poyerekeza zomwe iwo akuchita ndi zimene Akristu ena akuchita, kapena poyerekeza zochita zawozo ndi zimene ankachita m’mbuyomu.​—Agalatiya 6:4.

13. Kodi akulu angagwiritsire ntchito bwanji luso la okalamba ndiponso zinthu zimene aphunzira m’moyo wawo?

13 Akulu angasonyeze kuyamikira thandizo lalikulu la Akristu okalamba mwa kugwiritsa ntchito zinthu zomwe okalambawo aphunzira m’moyo wawo ndiponso luso lawo. Akristu okalamba achitsanzo chabwino angagwiritsidwe ntchito nthaŵi zina pa zitsanzo kapena powafunsa mafunso. “Anthu amakhala tcheru ndi kumvetsera kwambiri ndikamafunsa mbale kapena mlongo wokalamba amene walera ana ake m’choonadi,” anatero mkulu wina. Akulu mu mpingo wina anati mlongo wina wa zaka 71 amene ndi mpainiya wathandiza ofalitsa Ufumu kuti aziloŵa m’munda mokhazikika. Mlongoyu amawalimbikitsanso kuchita “zinthu zofunika kwambiri,” monga kuŵerenga Baibulo ndi lemba latsiku ndi kumasinkhasinkha zimene aŵerengazo.

14. Kodi bungwe lina la akulu linasonyeza motani kuyamikira woyang’anira mnzawo wokalamba?

14 Akulu amaonanso zochita za oyang’anira anzawo okalamba kukhala zamtengo wapatali. Posachedwapa, a José, amene ali m’zaka za m’ma 70 ndipo akhala mkulu kwa zaka zambiri, anachitidwa opaleshoni yaikulu kwambiri. Poona kuti ziwatengera nthaŵi yaitali kuti achire bwinobwino, iwo anaganiza zosiya kutumikira monga woyang’anira wotsogolera. Iwo anati: “Ndinadabwa ndi zimene akulu anzanga anachita nditawauza zimenezi. M’malo movomera maganizo anga, iwo anandifunsa kuti ndinkafunika thandizo lanji kuti ndipitirize udindo wanga.” Mothandizidwa ndi mkulu wachinyamata, a José anapitiriza kutumikira mosangalala monga woyang’anira wotsogolera, ndipo mpingo wapindula kwambiri ndi zimenezi. Mkulu wina anati: “Abale akuyamikira kwambiri ntchito imene a José akugwira monga mkulu. Amawakonda ndi kuwalemekeza chifukwa cha zimene aphunzira pa moyo wawo ndiponso chitsanzo chawo cha chikhulupiriro. Mpingo wathu ndi wolemera chifukwa chokhala ndi iwo.”

Kusamalirana

15. N’chifukwa chiyani Akristu onse ayenera kudera nkhaŵa umoyo wa okalamba amene ali nawo?

15 Sikuti ndi ana amene ali ndi makolo okalamba okha ndi atumiki oikidwa basi amene ayenera kudera nkhaŵa okalamba. Poyerekeza mpingo wachikristu ndi thupi la munthu, Paulo analemba kuti: “Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosoŵacho; kuti kusakhale chisiyano m’thupi; koma kuti ziŵalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake.” (1 Akorinto 12:24, 25) Kuti mpingo wachikristu ukhale mogwirizana, aliyense mu mpingomo ayenera kudera nkhaŵa umoyo wa okhulupirira anzake, kuphatikizapo okalamba.​—Agalatiya 6:2.

16. Kodi tingasonyeze motani kuti okalamba timawaganizira tikapita ku misonkhano yachikristu?

16 Misonkhano yachikristu imatipatsa mpata wabwino wosonyezera kuti timawadera nkhaŵa okalamba. (Afilipi 2:4; Ahebri 10:24, 25) Kodi timapatula nthaŵi yolankhulana ndi okalamba panthaŵi imeneyi? Ngakhale kuti kungakhale koyenera kuwafunsa za umoyo wawo, kodi tingathe ‘kuwagaŵira mtulo wauzimu,’ mwina mwa kukambirana nawo zinthu zina zolimbikitsa zimene zinakuchitikirani kapena mfundo inayake ya m’Malemba? Popeza kuti okalamba ena sayenda kwambiri, kungakhale kukoma mtima kuti ife tipite pamene pali iwowo m’malo mowayembekezera kuti abwere kwa ife. Ngati amavutika kumva, tingafunike kulankhula pang’onopang’ono komanso momveka bwino. Ndipo kuti ‘titonthozanedi,’ kapena kuti kulimbikitsanadi, tiyenera kumvetsera mwatcheru zonena za okalamba.​—Aroma 1:11, 12.

17. Kodi tingasonyeze motani kuti timadera nkhaŵa Akristu okalamba amene sangayende kuchoka panyumba zawo?

17 Bwanji ngati okalamba ena sangathe kufika kumisonkhano yachikristu? Yakobo 1:27 amasonyeza kuti ndi ntchito yathu “kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” Tanthauzo lina la mawu achigiriki amene anawatembenuza kuti “kucheza” ndilo ‘kuzonda.’ (Machitidwe 15:36) Ndipo okalamba amayamikira kwambiri tikamawazonda. Paulo, yemwe anali “nkhalamba,” anali yekhayekha kundende ku Roma pafupifupi m’chaka cha 65 Kristu Atabwera. Ankakhumba ataona wantchito mnzake Timoteo ndipo analemba kuti: “Tayesetsa kudza kwa ine msanga.” (Filemoni 9; 2 Timoteo 1:3, 4; 4:9) Ngakhale kuti okalambawo si andende, ena a iwo sangayende kuchoka panyumba zawo chifukwa cha thanzi lawo. Tinganene kuti, mwina amakhala akunena kuti, ‘Chonde, tayesetsani kudzandizonda msanga.’ Kodi tikuchitapo kanthu pa pempho limenelo?

18. Kodi kuzonda okalamba kungakhale ndi phindu lotani?

18 Musapeputse phindu lochezera mbale kapena mlongo wauzimu wokalamba. Pamene Mkristu wina dzina lake Onesiforo anali ku Roma, anayesetsa kufunafuna Paulo, ndi kum’peza, ndipo kenako ‘anali kum’tsitsimutsa kaŵirikaŵiri.’ (2 Timoteo 1:16, 17) Mlongo wina wokalamba anati: “Ndimakonda kucheza ndi achinyamata. Chimene ndimakonda kwambiri n’chakuti amachita nane zinthu ngati kuti ndimachokera m’banja mwawo. Zimandilimbikitsa kwambiri.” Mkristu wina wokalamba anati: “Ndimayamikira kwambiri wina akandilembera khadi, kundiimbira telefoni kwa mphindi zochepa chabe, kapena kudzandiona kwa nthaŵi yochepa. Zimanditsitsimula kwambiri.”

Yehova Amafupa Amene Amasamalira Okalamba

19. Kodi ndi madalitso otani amene amadza chifukwa chosamalira okalamba?

19 Kusamalira okalamba kumadzetsa madalitso ochuluka kwambiri. Kucheza ndi okalamba komanso kutha kugwiritsa ntchito zinthu zimene iwo akudziŵa ndi zimene aphunzira pa moyo wawo ndi mwayi wina wapadera kwambiri. Anthu amene amawasamalira amapeza chimwemwe chachikulu kwambiri chimene chimadza mwa kupatsa, komanso amakhala ndi mtendere mu mtima mwawo chifukwa chokwaniritsa udindo wawo wa m’Malemba. (Machitidwe 20:35) Kuwonjezera apo, anthu amene amasamalira okalamba sayenera kuda nkhaŵa kuti iwowo akadzakalamba adzakhala okhaokha. Mawu a Mulungu akutitsimikizira kuti: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”​—Miyambo 11:25.

20, 21. Kodi Yehova amaona motani anthu amene akusamalira okalamba, ndipo tipitirize kuchita chiyani?

20 Yehova amafupa ana a anthu okalamba, oyang’anira, limodzinso ndi Akristu ena oopa Mulungu chifukwa chopezera okhulupirira anzawo okalamba zosoŵa zawo mosadzikonda. Mtima umenewu ukugwirizana ndi mwambi uwu wakuti: “Wochitira waumphaŵi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.” (Miyambo 19:17) Ngati chikondi chitilimbikitsa kuchitira chifundo anthu otsika ndiponso aumphaŵi, Mulungu amaona kupatsa koteroko kuti ndi ngongole moti iye amabwezera madalitso. Amatibwezeranso chifukwa chosamalira mwachikondi olambira anzathu okalamba, omwe ambiri mwa iwo ndi ‘osauka a dziko lapansi koma olemera m’chikhulupiriro.’​—Yakobo 2:5.

21 Mulungu amabwezera mowoloŵa manja kwambiri. Pa zimene iye amabwezera palinso moyo wosatha. Kwa atumiki a Yehova ambiri, izi zikutanthauza moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso, momwe simudzakhalanso zotsatira za uchimo womwe timabadwa nawo ndipo okalamba okhulupirika adzakhalanso amphamvu ngati anyamata. (Chivumbulutso 21:3-5) Pamene tikuyembekezera nthaŵi yamadalitso imeneyi, tiyeni tipitirize kukwaniritsa udindo wathu wachikristu wosamalira okalamba.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onani Galamukani! ya February 8, 1994, masamba 3-10, kuti muone mfundo zabwino zokhudza kusamalira makolo okalamba.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ana angalemekeze motani makolo okalamba?

• Kodi akulu amasonyeza motani kuyamikira nkhosa zokalamba?

• Kodi Mkristu aliyense payekha angachite chiyani posonyeza kuwaderadi nkhaŵa okalamba?

• Kodi pamakhala madalitso otani amene amadza chifukwa chosamalira Akristu okalamba?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 17]

Zimene Anachita Pamene Makolo Ake Anafunika Thandizo

Philip anali kutumikira monga wantchito wodzifunira pa ntchito ya zomangamanga ku Liberia mu 1999 pamene anamva kuti atate ake adwala kwambiri. Podziŵa kuti amayi ake sangakwanitse paokha kulimbana ndi vutolo, iye anaganiza zobwerera kumudzi kukakonza zoti atate akewo apeze thandizo la mankhwala.

Philip anati: “Kunali kovuta kuganiza zobwerera kumudzi, koma ndinaona kuti udindo wanga woyamba unali wosamalira makolo anga.” M’zaka zitatu zotsatira, iye anasamutsira makolo akewo kunyumba ina yabwino kwambiri ndipo mothandizidwa ndi Akristu anzake a m’dera lawolo anakonza nyumbayo kuti ikhale ndi zinthu zapadera zogwirizana ndi zofunika za atate akewo.

Amayi a Philip tsopano angathe kulimbana ndi matenda aakulu a atate akewo. Posachedwapa, Philip anavomera kukatumikira monga wantchito wodzifunira ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Macedonia.

[Bokosi patsamba 19]

Sananyalanyaze Zosoŵa Zawo

Mkristu wina wa zaka 85 wa ku Australia, dzina lake Ada, atafika posatuluka m’nyumba chifukwa chodwala, akulu mu mpingo anakonza zomuthandiza. Analinganiza gulu la okhulupirira anzawo oti aziwathandiza. Abale ndi alongo ameneŵa anasangalala kugwira ntchito monga kukonza pakhomo, kuchapa, kuphika, ndi kum’pitira kwina ndi kwina mlongoyu.

Anayamba kuwathandiza pafupifupi zaka khumi zapitazo. Panopa, Mboni za Yehova zoposa 30 zathandiza nawo posamalira a Ada. Mbonizi zikupitiriza kupita kukawaona, kuwaŵerengera mabuku ofotokoza za m’Baibulo, kuwauza mmene anthu mumpingo akupitira patsogolo, ndiponso kupemphera nawo nthaŵi zonse.

Mkulu wachikristu wa mu mpingo mwawo anati: “Anthu amene akusamalira a Ada amaona kuti ndi mwayi wawo kuwathandiza. Ambiri alimbikitsidwa chifukwa choona kuti a Ada atumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri, ndipo n’zowavuta kunyalanyaza zosoŵa za mlongoyu.”

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi timasonyeza chikondi kwa makolo athu okalamba mosachita manyazi?

[Zithunzi patsamba 18]

Onse mu mpingo angasonyeze chikondi chawo kwa okhulupirira anzawo okalamba