Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mitsinje Iombe M’manja’

‘Mitsinje Iombe M’manja’

Kukongola kwa Chilengedwe cha Yehova

‘Mitsinje Iombe M’manja’

MUKAONA pa mapu a dziko lapansi, mumaona kuti m’madera ambiri muli mizera yokhotakhota. Mizera imeneyi imadutsa m’zigwa, m’zipululu, ndiponso m’tchire. Imayenda mokhotakhota kudutsa m’zidikha ndi m’nkhalango. (Habakuku 3:9) Imeneyi ndi mitsinje, yomwe ili ngati ngalande zimene zimachititsa dziko lathuli kukhala ndi moyo. Njira za madzi zimenezi zimapereka umboni wa nzeru ndi mphamvu za Mlengi wa dziko lapansi, Yehova. Tikamaona mitsinjeyi, timamva ngati mmene wamasalmo anamvera, amene anaimba kuti: ‘Mitsinje iombe m’manja; mapiri afuule pamodzi mokondwera; pamaso pa Yehova.’​—Salmo 98:8, 9. *

Tikamakamba za mbiri ya anthu sitingalephere kutchula mitsinje. Baibulo limatchula za mitsinje ikuluikulu inayi yomwe inapatuka mumtsinje wochoka mu Edene. (Genesis 2:10-14) Ena mwa anthu oyambirira kukhala moyo wotukuka anali kukhala m’mphepete mwa mitsinje ya Tigris ndi Firate ku Middle East mmene munali mwachonde. Mitsinje ya Hwang ku China, Ganges ndi Indus kum’mwera kwa Asia, ndi Nile ku Egypt inathandiza kuti anthu a m’maderaŵa akhale moyo wotukuka kwambiri.

Ndiye n’zosadabwitsa kuti nthaŵi zonse anthu amachita chidwi ndi mphamvu, kuchuluka, ndiponso kukongola kwa mitsinje. Mtsinje wa Nile wa ku Egypt ndi wautali pafupifupi makilomita 6,670. Mtsinje wa Amazon ku South America ndiwo mtsinje waukulu kwambiri padziko lonse. Ngakhale kuti mitsinje ina ndi ikuluikulu kwambiri, mitsinje ina ndi yokongola kwambiri, monga mtsinje waung’ono koma wothamanga kwambiri wa Tone ku Japan.

Kodi n’chiyani chimachititsa kuti madzi aziyenda mumtsinje? Mwachidule, tingati ndi mphamvu yachilengedwe yokoka zinthu. Ndi mphamvu imeneyi yomwe imakoka madzi kuchoka kumalo okwera kupita kumalo otsika. Nthaŵi zina zimenezi zimachititsa kuti pakhale mathithi amkokomo waukulu. Pofotokoza mmene mitsinje imasonyezera mphamvu ndi ukulu m’njira yotereyi, Baibulo limati: “Mitsinje ikweza, Yehova, mitsinje ikweza mkokomo wawo; mitsinje ikweza mafunde awo.”​—Salmo 93:3.

Yehova anafunsa Yobu, munthu woopa Mulungu, kuti: “Kodi ndani amatumiza chimvula?” (Yobu 38:25, Contemporary English Version) Inde, kodi madzi onseŵa amachokera kuti? Yankho lake lagona pa kuyenda kosalekeza kwa madzi komwe n’kovuta kukumvetsa. Madzi a padzikoli amakhala akuyenda nthaŵi zonse chifukwa cha kutentha kwa dzuŵa ndiponso mphamvu yachilengedwe yokoka zinthu. Madzi akasanduka nthunzi amaulukira kumwamba. M’kupita kwa nthaŵi amazizira n’kuundana kuti apange mitambo. Kenako madontho a madzi ameneŵa amabwerera padziko lapansi ngati chipale chofeŵa kapena mvula. Ambiri mwa madziŵa amasungidwa m’nyanja, m’mitsinje, ena amaundana n’kukhala ngati miyala ikuluikulu kwambiri, ndipo ena amaloŵa pansi pa nthaka.

Polankhula za kayendedwe ka madzi kochititsa chidwi kameneka, Baibulo limati: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” (Mlaliki 1:7) Ndi Yehova yekha, Mulungu wanzeru zosatha ndiponso wosamalira ena mwachikondi, amene akanatha kukonza kuti madzi aziyenda chonchi. Ndipo kodi kulinganiza zinthu kwapamwamba kwambiri kumeneku kumatiuzanji za umunthu wa Mulungu? Iye ndi Mulungu wanzeru kwambiri ndiponso wosamalira ena mwachikondi.​—Salmo 104:13-15, 24, 25; Miyambo 3:19, 20.

M’mitsinje mumayenda madzi ochepa kwambiri opanda mchere a dziko lapansili, ngakhale kuti mitsinjeyi ndi ikuluikulu ndiponso ndi yambiri. Komabe n’njofunika kwambiri pa moyo. “Popanda kukhala ndi madzi komanso popanda kutha kuwawongolera bwino ndi kuwagwiritsa ntchito bwino, kukanakhala kovuta kuti anthu athe kukhala ndi moyo, kaya moyo wake ukhale wosalira zambiri kapena wolira zambiri,” limatero buku lonena za madzi lakuti Water. “Zimene anthu achita mogwirizana ndi mfundoyi zathandiza kwambiri kuti anthu akhale otukuka.”

Kwa zaka zikwi zambiri, mitsinje yapatsa anthu madzi akumwa ndiponso ogwiritsa ntchito m’minda. Nthaka yachonde imene imapezeka m’mphepete mwa mitsinje yambiri n’njothandiza kwambiri paulimi. Taonani mmene mfundo imeneyi yafotokozedwera m’madalitso amene atumiki a Yehova amalandira: “Ha! mahema ako n’ngokoma, Yakobo; zokhalamo zako, Israyeli! Ziyalika monga zigwa, monga minda m’mphepete mwa nyanja [“mitsinje,” NW], monga khonje wowoka Yehova, monga mikungudza m’mphepete mwa madzi.” (Numeri 24:5, 6) Mitsinje imathandizanso zamoyo monga abakha ndi mimbulu zomwe mukuziona panozi. Ndipotu, tikaphunzira kwambiri zokhudza mitsinje, timalimbikitsidwa kuyamika Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani Kalendala ya 2004 ya Mboni za Yehova, miyezi ya May ndi June.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 8]

Mathithi a Iguaçú, omwe ali m’malire mwa mayiko a Argentina ndi Brazil, ndi amodzi mwa mathithi akuluakulu kwambiri. Kuchoka tsidya lina kukafika tsidya lina pali mtunda woposa makilomita atatu. Mathithiŵa ali m’nkhalango yothinana kwambiri yosawonongedwa, ndipo apangidwa ndi mathithi ena ang’onoang’ono pafupifupi 300. Pa sekondi iliyonse m’nthaŵi ya mvula, pa mathithiŵa pamagwa madzi omwe angadzale chithanki chachikulu kuposa mamita 21 kuya kwake, mamita 21 mlitali mwake, ndi mamita 21 mlifupi mwake.

[Chithunzi patsamba 9]

Mtsinje wa Tone, ku Japan