Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kukondweretsa Mulungu

Mungathe Kukondweretsa Mulungu

Mungathe Kukondweretsa Mulungu

KODI zochita zathu zingathe kukhudza mmene Mulungu amamvera mumtima mwake? Kodi Mulungu amatha kukondwa? Buku lina lotanthauzira mawu limati mawu akuti “Mulungu” amatanthauza “chinthu chachikulu kapena chapamwamba kwambiri kuposa china chilichonse.” Koma bwanji ngati chinthu chachikulu kwambiri chimenecho ndi mphamvu chabe? Kodi tingayembekezere mphamvu chabe kukhala yokondwa? Ayi, n’zosatheka. Komano taonani zimene Baibulo limanena za Mulungu.

“Mulungu ndiye mzimu,” anatero Yesu Kristu. (Yohane 4:24) Mzimu ndi chamoyo chosiyana ndi ife anthu. Ngakhale kuti munthu sangauone, mzimu uli ndi thupi, lomwe ndi “lauzimu.” (1 Akorinto 15:44; Yohane 1:18) Pogwiritsa ntchito mawu oyerekezera zinthu, Baibulo limalankhula za Mulungu ngati kuti ali ndi maso, makutu, manja, ndi zina zotero. * Mulungu alinso ndi dzina, lakuti Yehova. (Salmo 83:18) Motero, Mulungu wa m’Baibulo ndi munthu wauzimu. (Ahebri 9:24) “Ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya.”​—Yeremiya 10:10.

Popeza kuti ndi munthu weniweni wamoyo, Yehova amatha kuganiza ndiponso kuchita zinthu. Iye ali ndi makhalidwe ake ndipo amakhudzidwa mtima, ali n’zimene amakonda ndiponso zimene sakonda. Ndipotu, m’Baibulo muli mawu ambiri osonyeza zinthu zimene iye amasangalala nazo ndi zimene sasangalala nazo. Mosiyana ndi milungu ndi mafano zimene anthu amapanga zomwe zimangosonyeza makhalidwe a anthu owapangawo, Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, ndiye amene anayambitsa makhalidwe amene anthu amatha kusonyeza.​—Genesis 1:27; Yesaya 44:7-11.

Mosakayikira, Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Sikuti amangosangalala ndi zimene analenga koma amasangalalanso akamakwaniritsa zolinga zake. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Ndidzachita zofuna zanga zonse . . . inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.” (Yesaya 46:9-11) Wamasalmo anaimba kuti: “Yehova akondwere mu ntchito zake.” (Salmo 104:31) Koma pali chinanso chimene chimakondweretsa Mulungu. Iye anati: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga.” (Miyambo 27:11) Taganizani tanthauzo la zimenezi. Anthufe tingathe kukondweretsa Mulungu.

Mmene Tingakondweretsere Mtima wa Mulungu

Taonani mmene Nowa, amene anali mutu wa banja, anakondweretsera mtima wa Yehova. Nowa “anapeza ufulu pamaso pa Yehova” chifukwa chakuti anali munthu “wangwiro m’mibadwo yake.” Mosiyana kwambiri ndi anthu oipa a m’nthaŵi imeneyo, chikhulupiriro ndi kumvera kwa Nowa zinakondweretsa kwambiri Mulungu moti amanenedwa kuti ‘Nowa anayenda ndi Mulungu.’ (Genesis 6:6, 8, 9, 22) “Ndi chikhulupiriro Nowa . . . pochita mantha [ndi Mulungu], anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m’nyumba yake.” (Ahebri 11:7) Yehova anakondwera ndi Nowa ndipo anam’dalitsa iye ndi banja lake mwa kuwapulumutsa m’nthaŵi yovuta imeneyo m’mbiri ya anthu.

Nayenso Abrahamu, tate wa Aisrayeli, ankadziŵa bwino kwambiri mmene Yehova amamvera mu mtima. Iye anasonyezeratu kuti ankadziŵa bwino maganizo a Mulungu pamene Yehova anamuuza kuti Sodomu ndi Gomora awonongedwa chifukwa cha kuipa kwa makhalidwe awo. Abrahamu ankam’dziŵa bwino Yehova mpaka kufika ponena kuti n’zosatheka kuti Mulungu aphe munthu wolungama limodzi ndi woipa. (Genesis 18:17-33) Patapita zaka zambiri, Abrahamu pomvera malangizo a Mulungu, tinganene kuti “anapereka nsembe Isake,” chifukwa anadziŵa “kuti Mulungu n’ngokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa.” (Ahebri 11:17-19; Genesis 22:1-18) Abrahamu ankazindikira bwino mmene Mulungu amamvera mu mtima ndipo anasonyeza chikhulupiriro cholimba ndiponso kumvera moti “anatchedwa bwenzi la Mulungu.”​—Yakobo 2:23.

Munthu winanso amene anayesetsa kukondweretsa mtima wa Mulungu anali Mfumu Davide ya Israyeli wakale. Ponena za munthu ameneyu, Yehova anati: “Ndapeza Davide, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.” (Machitidwe 13:22) Asanakumane ndi Goliati, amene anali chimphona, Davide anadalira kwambiri Mulungu ndipo anauza Sauli mfumu ya Aisrayeli kuti: “Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m’dzanja la Mfilisti uyu.” Yehova anadalitsa Davide chifukwa chomudalira Iye ndipo anam’thandiza kupha Goliati. (1 Samueli 17:37, 45-54) Davide sanangofuna kukondweretsa Yehova ndi zochita zokha, koma anafunanso kuti ‘mawu a m’kamwa mwake ndi maganizo a mumtima mwake avomerezeke pamaso pa Yehova.’​—Salmo 19:14.

Nanga bwanji ifeyo? Kodi tingam’kondweretse motani Yehova? Tikazindikira bwino mmene Mulungu amamvera mumtima, tidzadziŵanso bwino zimene tifunika kuchita kuti tikondweretse mtima wa Mulungu. Ndiyetu, poŵerenga Baibulo, tifunika kuchita khama kudziŵa mmene Mulungu amamvera mumtima mwake kuti ‘tidzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti tiyende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo.’ (Akolose 1:9, 10) Ndiyeno chidziŵitsocho chidzatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro. Izi n’zofunika kwambiri chifukwa “wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa” Mulungu. (Ahebri 11:6) Inde, tingathe kukondweretsa mtima wa Yehova mwa kuchita khama kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso mwa kukonza moyo wathu kuti ugwirizane ndi zofuna zake. Komanso tifunika kusamala kuti tisavutitse Yehova mumtima.

Musavutitse Mulungu Mumtima

Chitsanzo cha mmene Yehova angavutikire mumtima mwake timachipeza m’nkhani yokhudza masiku a Nowa. Nthaŵi imeneyo, “dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi.” Kodi Mulungu anamva bwanji mumtima mwake ataona kuipa kwa makhalidwe a anthu ndi chiwawa? Baibulo limati: “Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m’mtima mwake.” (Genesis 6:5, 6, 11, 12) Mulungu anamva chisoni chifukwa chakuti makhalidwe a anthu anaipa kwambiri moti anasintha maganizo ake okhudza mbadwo umene unalipo Chigumula chisanachitike. Chifukwa chakuti Mulungu sanakondwe ndi kuipa kwawo, iye anasintha kuchoka pa Mlengi wa anthu, n’kukhala wowawononga.

Yehova anavutikanso m’maganizo pamene anthu ake, mtundu wakale wa Israyeli, mobwerezabwereza ankachita zinthu mosaganizira mmene iye amamvera mumtima ndiponso mosaganizira malangizo ake amene amapereka chifukwa cha chikondi chake. Wamasalmo anadandaula kuti: “Kaŵirikaŵiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, namumvetsa chisoni m’chipululu. Pakuti anabwerera m’mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israyeli.” Komabe, “iye pokhala n’ngwachifundo, anakhululukira choipa, osawawononga; nabweza mkwiyo wake kaŵirikaŵiri, sanautsa ukali wake wonse.” (Salmo 78:38-41) Ngakhale kuti moyenerana ndi zochita zawo, Aisrayeli opandukawo anavutika ndi zotsatira za kuchimwa kwawo, Baibulo limatiuza kuti “m’mazunzo awo onse [Mulungu] anazunzidwa.”​—Yesaya 63:9.

Ngakhale kuti panali umboni wochuluka wakuti Mulungu anali kuwakonda, Aisrayeli “ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.” (2 Mbiri 36:16) M’kupita kwa nthaŵi, kupanduka ndi kuuma khosi kwawoko ‘kunamvetsa chisoni mzimu wake woyera’ mpaka Yehova anasiya kukondwera nawo. (Yesaya 63:10) Kodi zotsatira zake zinali zotani? Moyenerera, Mulungu anasiya kuwateteza, ndipo mtunduwo unavutika kwambiri pamene Ababulo analanda Yuda ndi kuwononga Yerusalemu. (2 Mbiri 36:17-21) Zimakhala zomvetsa chisoni kwambiri anthu akasankha kuchita zoipa zomwe sizikondweretsa Mlengi wawo ndipo zimam’vutitsa maganizo.

Baibulo limatitsimikizira kuti makhalidwe oipa amachepsa Mulungu, kapena kuti kumupweteka mumtima. (Salmo 78:41) Zina mwa zinthu zimene Mulungu sakondwera nazo, mwinanso kukhumudwa nazo kumene, ndizo kunyada, kunama, kupha, kuchita zamatsenga, kuwombeza maula, kupembedza makolo, khalidwe lotayirira, kugonana amuna okhaokha kapena akazi okhaokha, kusakhulupirika m’banja, kugonana pachibale, ndi kupondereza osauka.​—Levitiko 18:9-29; 19:29; Deuteronomo 18:9-12; Miyambo 6:16-19; Yeremiya 7:5-7; Malaki 2:14-16.

Kodi Yehova amamva bwanji mumtima mwake anthu akamalambira mafano? Eksodo 20:4, 5 amatiuza kuti: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti fano ‘limanyansa Yehova.’ (Deuteronomo 7:25, 26) Mtumwi Yohane anachenjeza kuti: “Tiana, dzisungireni nokha kupeŵa mafano.” (1 Yohane 5:21) Ndipo mtumwi Paulo analemba kuti: “Okondedwa anga, thaŵani kupembedza mafano.”​—1 Akorinto 10:14.

Yesetsani Kuchita Zoti Mukhale Wovomerezeka kwa Mulungu

Chinsinsi kapena kuti chiyanjo cha Mulungu “chili ndi owongoka.” Anthu “angwiro m’njira zawo am’sekeretsa.” (Miyambo 3:32; 11:20) Mosiyana ndi zimenezi, anthu amene akupitiriza kukhumudwitsa Mulungu mwa kunyalanyaziratu kapena kunyoza mmene iye amamvera mumtima mwake posachedwapa adzalandira zotsatira zake za kulephera kum’kondweretsa. (2 Atesalonika 1:6-10) Inde, posachedwapa adzathetsa kuipa konse kumene kwafala masiku ano.​—Salmo 37:9-11; Zefaniya 2:2, 3.

Koma Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti Yehova ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Iye amasangalala kwambiri kusonyeza chikondi chake kwa olungama amene amam’konda kusiyana n’kusonyeza mkwiyo wake kwa anthu osafuna kulapa. Yehova ‘sakondwera nayo imfa ya woipa, koma [amakondwera] kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo.’​—Ezekieli 33:11.

Motero aliyense angathe kupeŵa mkwiyo wa Yehova. “Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Pokhala ndi chidaliro chonse pa mmene Mulungu amamvera mumtima mwake, mungathe “kutaya pa Iye nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.” (1 Petro 5:7) Khalani otsimikiza kuti anthu amene amakondweretsa mtima wa Mulungu angathe kukhala ovomerezeka kwa iye ndiponso kukhala mabwenzi ake. Motero, tsopano kusiyana ndi kale lonse m’pofunika kwambiri kutsimikizira “chokondweretsa Ambuye n’chiyani.”​—Aefeso 5:10.

N’zosangalatsa kwambiri kuti chifukwa cha kukoma mtima kwake, Mulungu watidziŵitsa makhalidwe ake apamwamba ndiponso mmene iye amamvera mumtima mwake. Ndipo inu mungathe kukondweretsa mtima wake. Ngati mukufuna kutero, tikukulimbikitsani kuti mulankhule ndi Mboni za Yehova kwanuko. Zidzasangalala kukusonyezani zomwe izo zaona kuti n’zothandiza ndiponso zotheka pamene zikuyesetsa kukondweretsa Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani bokosi lakuti “N’chifukwa Chiyani M’Baibulo Mulungu Amamufotokoza Ngati Kuti Ndi Munthu?”

[Bokosi patsamba 7]

N’chifukwa Chiyani M’Baibulo Mulungu Amamufotokoza Ngati Kuti Ndi Munthu?

Popeza kuti “Mulungu ndiye mzimu,” anthufe sitingathe kumuona. (Yohane 4:24) Motero Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oyerekezera zinthu, monga kufananitsa zinthu ndi kutchula chinthu chimene si munthu ngati kuti ndi munthu pofuna kutithandiza kumvetsa mphamvu, ukulu, ndi zochita za Mulungu. Motero, ngakhale kuti sitidziŵa mmene thupi lauzimu la Mulungu limaonekera, Baibulo limalankhula za Mulungu ngati kuti ali ndi maso, makutu, manja, mikono, zala, miyendo, ndiponso mtima.​—Genesis 8:21; Eksodo 3:20; 31:18; Yobu 40:9; Salmo 18:9; 34:15.

Mawu ofotokoza zinthu ameneŵa satanthauza kuti thupi lauzimu la Mulungu lili ndi ziwalo zofanana ndi za matupi a anthu. Kutchula kuti Mulungu ali ndi ziwalo za munthu sizikutanthauza kuti alidi ndi ziwalo zimenezo. Izi zimangothandiza anthufe kuti timvetse bwinopo mmene Mulungu alili. Akanapanda kugwiritsa ntchito mawu oyerekezera zinthu, kukanakhala kovuta, ndipo mwinanso kosatheka, kuti anthu timvetse mawu ena alionse ofotokoza za Mulungu. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti anthu anangopeka makhalidwe a Yehova Mulungu. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti munthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, osati Mulungu m’chifanizo cha munthu. (Genesis 1:27) Popeza kuti olemba Baibulo ‘anauziridwa ndi Mulungu,’ mmene iwo anafotokozera makhalidwe a Mulungu ndi mmene Mulunguyo anafotokozera makhalidwe akewo, omwe anapatsa anthu ndipo anthuwo amawasonyeza mosiyanasiyana. (2 Timoteo 3:16, 17) M’malo monena kuti Mulungu anatengera makhalidweŵa kwa anthu, kwenikweni Mulungu ndi amene anapatsa anthu makhalidweŵa.

[Chithunzi patsamba 4]

Nowa anakondweretsa Mulungu

[Chithunzi patsamba 5]

Abrahamu ankazindikira bwino mmene Mulungu amamvera mumtima

[Chithunzi patsamba 6]

Davide anadalira kwambiri Yehova

[Chithunzi patsamba 7]

Pamene mukuŵerenga Baibulo, mungadziŵe mmene mungakondweretsere Mulungu

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Courtesy of Anglo-Australian Observatory, photograph by David Malin