Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mudzasankha Chipembedzo Chiti?

Kodi Mudzasankha Chipembedzo Chiti?

Kodi Mudzasankha Chipembedzo Chiti?

‘ZIPEMBEDZO zangokhala njira zosiyanasiyana zopita ku malo amodzi. Ndipotu, pali Mulungu mmodzi yekha, kodi si choncho?’ Ameneŵa ndi maganizo a anthu ambiri amene amalingalira kuti ngakhale kuti kukhala m’chipembedzo chinachake n’kofunika, zilibe kanthu kuti munthu wasankha kukhala m’chipembedzo chiti.

Kungoiona koyamba, mfundo imeneyi ingaoneke ngati yomveka ndithu, popeza n’zoona kuti pali Mulungu mmodzi yekha, Wamphamvuyonse. (Yesaya 44:6; Yohane 17:3; 1 Akorinto 8:5, 6) Komabe, tiyeneranso kuganizira kusiyana koonekeratu, ngakhalenso kutsutsana kumene, komwe kulipo m’zipembedzo zambiri zimene zimati zikutumikira Mulungu woona. Zipembedzo zimasiyana kwambiri zochita zawo, zikhulupiriro, ziphunzitso, ndiponso zimene zimafuna. Kusiyanaku n’kwakukulu kwambiri moti anthu a m’chipembedzo china amaona kuti n’kovuta kumvetsa kapena kuvomereza zimene a zipembedzo zina amaphunzitsa kapena kukhulupirira.

Koma Yesu ananena kuti: “Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Ngati onse akulambira Mulungu m’choonadi, kodi angakhale ndi maganizo otsutsana pankhani yoti Mulungu ndani, zolinga zake n’zotani, ndiponso kuti amafuna kumulambira motani? Kodi n’zomveka kukhulupirira kuti mmene timalambirira Mulungu Wamphamvuyonse si nkhani yaikulu kwa iyeyo?

Akristu Oona Kalelo Ndiponso Masiku Ano

Akristu a m’zaka 100 zoyambirira nthaŵi zina anali kusiyana maganizo pankhani ya mmene anali kuonera zinthu. Mwachitsanzo, polankhula za Akristu a ku Korinto, mtumwi Paulo anati: “Zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Kloe, kuti pali makani pakati pa inu. Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Kristu.”​—1 Akorinto 1:11, 12.

Kodi Paulo anaona kuti zimenezi sizinali nkhani yaikulu kwenikweni? Kodi munthu aliyense anali kungotsatira njira yake yopulumukira? Ayi. Paulo analangiza kuti: “Ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.”​—1 Akorinto 1:10.

Komabe, sikuti anthu angagwirizane pankhani ya chikhulupiriro mwa kuwaumiriza kuti atero. Anthu amagwirizana pa chikhulupiriro ngati munthu aliyense payekha apenda zinthu mosamala ndi kupeza mfundo imodzi n’kugwirizana. Motero, kuphunzira Mawu a Mulungu munthu aliyense payekha ndiponso kufunitsitsa ndi mtima wonse kutsatira zimene munthuyo waphunzira ndi njira zofunika kwambiri kuti pakhale mgwirizano umene Paulo ananena. Kodi n’zotheka kukhala ndi mgwirizano woterewu? Monga mmene taonera, Mulungu wakhala akuchita zinthu ndi anthu ake monga gulu kuyambira kale. Kodi n’zotheka kulidziŵa gulu loterolo masiku ano?

Phindu Lokhala M’gulu Loyenera

Wamasalmo Davide nthaŵi ina anafunsa kuti: “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu? Adzagonera ndani m’phiri lanu lopatulika?” Limenelitu ndi funso lochititsa munthu kuganiza. Davide anayankha kuti: “Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.” (Salmo 15:1, 2) Kulimvetsa molondola Baibulo kungathandize munthu kudziŵa chipembedzo chimene chimachita zimene Mulungu amafunazi. Ndiyeno, mwa kugwirizana ndi gulu limenelo, munthu angakhale pa ubwenzi wabwino ndi anthu amene amalambira Mulungu mogwirizana ndiponso “mumzimu ndi m’choonadi.”

Mboni za Yehova zasonyeza kuti kukhala ndi chikhulupiriro chogwirizana ndiponso kuchita zinthu mogwirizana n’kotheka ngakhale kuti tikukhala m’dziko logaŵanika lamakonoli. Pakati pawo pali anthu amene kale anali a zipembedzo zosiyanasiyana ndiponso a mafuko osiyanasiyana. A Mboni ena kale anali anthu okhulupirira kuti n’zosatheka kumudziŵa Mulungu kapena anali okana Mulungu. Ena anali asanaikirepo mtima kwenikweni pankhani ya chipembedzo. Anthu ochokera m’zipembedzo, chikhalidwe, ndi zikhulupiriro zosiyanasiyana zimenezi tsopano akugwirizana pankhani ya chipembedzo, zomwe n’zosoŵa kwambiri m’dzikoli masiku ano.

Chimene chachititsa kuti pakhale mgwirizano woterewu ndi Mawu a Mulungu, Baibulo. Komabe, a Mboni za Yehova amazindikira kuti sangaumirize munthu kuti achite zakutizakuti. Koma amayamikira mwayi wolimbikitsa ena kuphunzira Baibulo kuti posankha zochita pankhani ya kulambira atero pa zifukwa zolondola zimene aphunzirazo. Mwa njira imeneyi, anthu ambiri angapeze nawo phindu limene limakhalapo chifukwa cholambira Mulungu “mumzimu ndi m’choonadi.”

Masiku ano n’zosavuta kutengeka ndi zinthu zoipa. Kusankha anthu oyenera oti muzigwirizana nawo n’kofunika kwambiri. Baibulo limanena kuti “ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru” ndiponso kuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Kusonkhana ndi olambira Mulungu enieni kumateteza. Motero, Baibulo limatikumbutsa kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Limakhala dalitso pamene mabwenzi enieni, abale ndi alongo auzimu, akuthandizana mwachikondi kukwaniritsa udindo umene ali nawo kwa Mulungu.

Ottmar akutsimikizira kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Anakulira m’banja la Chikatolika ku Germany, koma anasiya kupita ku tchalitchi. Iye anafotokoza kuti: “Ndinkati ndikapita kutchalitchi, ndinali kutulukamo osadziŵa chilichonse monga momwe ndinalili ndisanaloŵe m’tchalitchimo.” Koma sanataye chikhulupiriro chake mwa Mulungu. Ndiyeno anakumana ndi Mboni za Yehova ndipo anakhutira kuti iwo ndiwo atumiki enieni a Mulungu. Anaona kuti n’kofunika kusonkhana nawo. Panopa iye tsopano akuti: “Popeza ndikugwira ntchito pamodzi ndi gulu lapadziko lonse, ndili ndi mtendere wa maganizo ndi wa mumtima. Ndikuthandizidwa pang’onom’pang’ono kulidziŵa molondola Baibulo. Chimenechi ndi chinthu cha mtengo wapatali kwa ine.”

Pempho kwa Anthu Ofunafuna Choonadi

Anthu ogwirizana akamagwira ntchito limodzi monga gulu angachite zambiri pa ntchitoyo kusiyana ndi anthu amene akugwira ntchitoyo aliyense payekhapayekha. Mwachitsanzo, malangizo a Yesu otsanzikirana ndi otsatira ake anali akuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Kodi zikanatheka bwanji kuigwira bwinobwino ntchito imeneyi pakanapanda malangizo kapena gulu? Kodi munthu angamvere bwanji lamulo la m’Malemba limeneli ngati iye amafuna kutumikira Mulungu mosadalira gulu?

Chaka chatha, Mboni za Yehova padziko lonse zinagaŵira mabuku aakulu ndi aang’ono othandiza kuphunzira Baibulo okwana 91,933,280, pamodzinso ndi magazini okwana 697,603,247, zimene zinathandiza kuti auze anthu miyandamiyanda m’mayiko 235 uthenga wa m’Mawu a Mulungu. Umenewu ndi umboni waukulu wosonyeza kuti ntchito ya gulu logwirizana imakwaniritsa zambiri kuposa zimene munthu woti akungochita zinthu mwayekha angachite.

Kuwonjezera pa kugaŵira mabuku othandiza kuphunzira Baibulo, Mboni za Yehova zimachititsa maphunziro a Baibulo aulere pofuna kuthandiza anthu kumvetsa bwino zimene Mulungu amafuna. Chaka chatha, pafupifupi mlungu uliwonse Mboni zinali kuchititsa maphunziro a Baibulo oterowo okwana 5,726,509 ndi munthu payekha kapena ndi gulu la anthu. Kuphunzira Baibulo kumeneku kwathandiza anthu miyandamiyanda kupeza zifukwa zolondola zimene zawathandiza kusankha chipembedzo. Tikukupemphani kuphunzira zimene Mulungu amafuna zimene zili m’Baibulo. Ndiyeno mungasankhe zochita.​—Aefeso 4:13; Afilipi 1:9; 1 Timoteo 6:20; 2 Petro 3:18.

Ngati mukufuna kusangalatsa Mulungu, n’kofunika kukhala m’chipembedzo, koma osati m’chipembedzo kapena mumpingo uliwonse. Muyenera kusankha chipembedzo mogwirizana ndi kudziŵa kwanu Baibulo molondola, osati potsatira mfundo zosatsimikizika kapena zongomva. (Miyambo 16:25) Phunzirani zimene chipembedzo choona chimafuna. Yerekezerani zimenezo ndi zikhulupiriro zanu. Ndiyeno sankhani mogwirizana ndi zimene mwapeza.​—Deuteronomo 30:19.

[Zithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova n’zogwirizana m’dziko logaŵanikali