Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kukhala M’chipembedzo Chinachake?

Kodi Muyenera Kukhala M’chipembedzo Chinachake?

Kodi Muyenera Kukhala M’chipembedzo Chinachake?

‘SINDIFUNIKA kukhala m’chipembedzo chinachake kapena kumapita kutchalitchi nthaŵi zonse kuti ndikhulupirire Mulungu.’ Anthu ambiri amaganiza motero pankhani yokhala m’chipembedzo chinachake. Ndipo ena amati amaona kuti amayandikana ndi Mulungu akamaona chilengedwe kunja kusiyana ndi pamene ali pa mwambo wa mapemphero kutchalitchi. Masiku ano, anthu ambiri amaganiza kuti kukhala m’chipembedzo chinachake kapena mpingo si chinthu chofunika kuti munthu akhulupirire Mulungu.

Komabe, ena ali ndi maganizo osiyana kwambiri ndi ameneŵa. Iwo amati kukhala m’chipembedzo chinachake ndiponso kupita kutchalitchi n’kofunika kwambiri ngati munthu akufuna kuti Mulungu amuyanje. Choncho, nkhani yoti kaya n’kofunikadi kuti munthu akhale m’chipembedzo chinachake sikuti yangogona poti anthu adziŵe chiŵerengero cha anthu amene ali m’zipembedzo ayi. Mulimonse mmene zingakhalire, popeza zimenezi zikukhudza ubwenzi wathu ndi Mulungu, kodi sikungakhale kwanzeru kuona mmene iye amaionera nkhaniyi? Nanga, kodi tingaphunzire chiyani m’Mawu ake, Baibulo, pankhani imeneyi?

Mmene Mulungu Anali Kuchitira Zinthu ndi Anthu Kale

Zaka pafupifupi 4,400 zapitazo, padziko lapansi panachitika chigumula chachikulu. Chigumula chimenechi sichikanaiŵalika msanga, ndipo anthu padziko lonse ali ndi nthano zawo zosimba chigumulachi m’mbiri yawo yakale. Ngakhale kuti nthanozi zimasiyanasiyana, mfundo zambiri n’zofanana, kuphatikizapo mfundo yakuti anthu ochepa okha ndi amene anapulumuka pamodzi ndi nyama zina.

Kodi anthu amene anapulumuka Chigumulacho zinangochitika mwamwayi kuti apulumuke chiwonongekocho? Baibulo limasonyeza kuti sizinali choncho. N’zochititsa chidwi kuti Mulungu sanauze munthu aliyense payekha za Chigumula chimene chinali kubwera. M’malo mwake, anauza Nowa, amene naye anachenjeza anthu a m’nthaŵi yake za Chigumula chimene chinali kubweracho.​—Genesis 6:13-16; 2 Petro 2:5.

Kuti munthu apulumuke zinadalira kuti akhale m’gulu logwirizana limeneli ndiponso kukhala wokonzeka kutsatira malangizo a Mulungu amene iye anapereka kwa Nowa. Ngakhalenso nyama zimene zinali m’chingalaŵa zomwe zinapulumuka Chigumula zinatero chifukwa chakuti zinali pamodzi ndi gulu limeneli. Nowa anapatsidwa malangizo olunjika akuti akonze zoti nyama zina zipulumuke.​—Genesis 6:17–7:8.

Patapita zaka zambiri, mbadwa za Nowa kudzera mwa mwana wake Semu zinakhala akapolo ku Igupto. Komabe cholinga cha Mulungu chinali choti awapulumutse ndi kuwapititsa kudziko limene iye analonjeza kholo lawo Abrahamu. Apanso, sanaulule zimenezo kwa munthu aliyense payekha m’malo mwake anaulula choyamba kwa anthu amene anawasankha kukhala atsogoleri, Mose ndi mbale wake, Aroni. (Eksodo 3:7-10; 4:27-31) Anthu amene anali akapolo kaleŵa atamasulidwa ku Igupto monga gulu, anapatsidwa Chilamulo cha Mulungu pa phiri la Sinai ndipo anakhala mtundu wa Israyeli.​—Eksodo 19:1-6.

Mwiisrayeli aliyense payekha anatha kupulumuka chifukwa chakuti anagwirizana ndi gulu limeneli lomwe Mulungu analikhazikitsa ndipo anatsatira malangizo a atsogoleri oikidwa a gululi. Ngakhalenso Aigupto ena anawalola kugwirizana ndi gulu limeneli lomwe mwachionekere Mulungu anali kuliyanja. Aisrayeli atachoka ku Igupto, anthu ameneŵa anapita nawo limodzi, zimene zinawachititsa kuti adzalandire nawo madalitso a Mulungu.​—Eksodo 12:37, 38.

Ndiyeno, m’zaka 100 zoyambirira, Yesu anayamba ntchito yake yolalikira, kusonkhanitsa anthu pamodzi monga ophunzira ake. Anali kuwachitira zinthu monga gulu, ngakhale kuti analinso kusamalira mwachikondi munthu aliyense payekha malinga ndi zimene munthuyo anafunikira. Yesu anauza atumwi ake okhulupirika 11 kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine.” (Luka 22:28, 29) Kenako, mzimu woyera wa Mulungu unafika pa ophunzirawo pamene anali pamodzi monga gulu.​—Machitidwe 2:1-4.

Zitsanzo zimenezi zikusonyeza bwinobwino kuti kale, Mulungu nthaŵi zonse anali kuchitira zinthu anthu ake monga gulu. Anthu ochepa omwe Mulungu anachita nawo zinthu paokhapaokha, monga Nowa, Mose, Yesu, ndi ena, kwenikweni anawagwiritsa ntchito pofuna kulankhula ndi gulu logwirizana. Palibe chifukwa chokhulupirira kuti Mulungu angachite zosiyana ndi zimenezi kwa atumiki ake masiku ano. Komano, zimenezi zikuchititsa kuti pakhale funso lina lakuti: Kodi kukhala m’chipembedzo china chilichonse ndiye kuti zili bwino? Tikambirana funso lofunika kwambiri limeneli m’nkhani yotsatira.

[Chithunzi patsamba 4]

Kuyambira kale, Mulungu anali kuchitira zinthu anthu ake monga gulu