Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tizingopeŵa Kuchitira Ena Zoipa?

Kodi Tizingopeŵa Kuchitira Ena Zoipa?

Kodi Tizingopeŵa Kuchitira Ena Zoipa?

“ZIMENE simufuna kuti ena akuchitireni, inunso musawachitire zoterozo.” Mawu olimbikitsa makhalidwe abwino ameneŵa akuti ananena ndi Confucius, yemwe anali mphunzitsi komanso munthu wanzeru wotchuka wa ku China. Masiku ano, patapita zaka 2,500 kuyambira nthaŵi imeneyo, anthu ambiri amakhulupirirabe kuti munthu amasonyeza kuti ndi wabwino mwa kungopeŵa kuchitira ena zoipa.

N’zoona kuti mfundo ya Confucius imeneyi ndi yabwino ndithu. Koma Baibulo limasonyeza mbali inanso yofunika pa khalidwe la munthu ndiponso zimene amachita kwa anzake. Kuwonjezera pa tchimo loti munthu wachita chinachake cholakwika kwa munthu mnzake, Baibulo limanenanso za tchimo loti munthu mwadala sanachite zimene anafunikira kuchita. Wophunzira wachikristu Yakobo analemba kuti: “Iye amene adziŵa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.” (Yakobo 4:17) M’malo mongolangiza Akristu kuti asamachite zoipa kwa ena, Yesu Kristu anapereka langizo ili: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”​—Mateyu 7:12.

Cholinga cha Mulungu poyambirira chinali choti munthu aliyense azichitira ena zinthu zimene iye angafune kuti enawo amuchitire. Mmene analengera anthu, anapereka chitsanzo chabwino posonyeza kuti amaganizira za moyo wa ena: “Mulungu . . . adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adam’lenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.” (Genesis 1:27) Zimenezi zikusonyeza kuti, chifukwa cha chikondi chake, Mulungu anapatsa anthu chikumbumtima chomwe chikaphunzitsidwa bwino, chingawathandize kuti azichitira anthu ena zinthu zimene angafune kuti anthu enawo aziwachitira.

Anthu ambiri masiku ano akuvutika popanda chiyembekezo ndiponso opanda wowathandiza chifukwa cha anthu osaganizira ena ndiponso odzikonda. Mwachionekere, zimene zikufunika sikungopeŵa chabe kuchitira ena zoipa, komanso kuwachitira zabwino anthuwo ndi kuwathandiza. Chifukwa cha zimenezi, Mboni za Yehova modzipereka zimathandiza anthu kuphunzira za chiyembekezo cha mtengo wapatali chimene chili m’Mawu a Mulungu. Zikamafika pa nyumba za anthu anzawo ndi uthenga wabwino wa m’Baibulo, zimatero ndi mtima wachikondi, kuwachitira anthu ena zimene iwo angafune kuti anthu ena awachitire.