Kuchita Chokoma Panthaŵi ya Mavuto
Kuchita Chokoma Panthaŵi ya Mavuto
“TICHITIRE onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro,” analimbikitsa motero mtumwi Paulo. (Agalatiya 6:10) Mboni za Yehova padziko lonse zimayesetsa mwakhama kutsatira mfundo imeneyi pa moyo wawo, kuchitira chokoma aliyense, makamaka okhulupirira anzawo. Zimenezi zimaoneka mobwerezabwereza panthaŵi ya mavuto. Tiyeni tione zitsanzo zaposachedwapa za m’mayiko atatu.
Mu December 2002, mkuntho wamphamvu unagwa ku Guam, ndipo mphepo yake imathamanga pa liŵiro loposa makilomita 300 pa ola limodzi. Nyumba zambiri zinagumuka mbali zina ndipo zina zinawonongekeratu. Mipingo ya kumeneko inalinganiza mwamsanga za anthu oyeretsa kuti athandize mabanja a Mboni amene zimenezi zinawakhudza kwambiri. Nthambi ya ku Guam inapereka zipangizo ndiponso anthu oti akonze nyumba zimene zinawonongeka, ndipo nthambi ya ku Hawaii inathandizanso. M’milungu yochepa chabe, gulu la akalipentala linafika kuchokera ku Hawaii kudzathandiza pantchito yokonza nyumbazo, ndipo pofuna kuwathandiza abaleŵa, abale ena a ku Guam komweko anatenga tchuti kuntchito kwawo. Mtima wogwirizana umene anasonyeza unakhala umboni kwa anthu onse m’deralo.
M’dera lina la mumzinda wa Mandalay, ku Myanmar, moto unabuka mwadzidzidzi pafupi ndi Nyumba ya Ufumu ina. Pafupi ndi pamene panabuka motowo panali nyumba ya mlongo wina amene anasiya kulalikira ndipo anali kukhalamo ndi banja lake. Mphepo imaloŵera ku nyumba yawoyo, motero mlongoyo anathamanga kupita ku Nyumba ya Ufumu kukapempha kuti abale amuthandize. Panthaŵiyi n’kuti Nyumba ya Ufumuyo ikukonzedwa mwina ndi mwina, motero panali abale ambiri. Anadabwa kwambiri kumuona mlongoyo chifukwa sanali kudziŵa kuti ankakhala m’deralo. Abalewo anathandiza mwamsanga kusamutsa katundu wa banjalo kukaika pamalo otetezeka. Mwamuna wa mlongoyo, yemwe sanali Mboni, atamva za motowo, anathamangira kunyumbako ndipo anapeza abalewo akusamalira banja lakelo. Anachita chidwi ndipo anayamikira, komanso mtima wake unakhala pansi chifukwa anthu akuba nthaŵi zambiri amagwiritsa ntchito mipata ngati imeneyi kuti abe. Kukoma mtima kumene abaleŵa anasonyeza kunalimbikitsa mlongoyu ndi mwana wake wamwamuna kuyambanso kusonkhana ndi mpingo wachikristu, ndipo tsopano amapezeka pa misonkhano yonse.
M’chaka chautumiki chapitachi, anthu ambiri ku Mozambique anakumana ndi njala chifukwa cha chilala ndiponso chifukwa chakuti mmera unavuta m’munda. Ofesi ya nthambi ya
Mboni za Yehova ya kumeneko inachitapo kanthu mwamsanga mwa kupereka chakudya kwa anthu amene analibe. Anali kugawa chakudyachi pa Nyumba za Ufumu, nthaŵi zina amachita zimenezi misonkhano ya mpingo ikatha. Mlongo wina yemwe amalera yekha ana anati: “Ndinafika ku misonkhano ndikuvutika maganizo, ndisakudziŵa kuti ndikawapatsa chiyani ana anga choti adye tikabwerera kunyumba.” Thandizo limene abale anapereka chifukwa cha chikondi linatsitsimula moyo wake nthaŵi yomweyo. Iye anati: “Kwa ine, zinali ngati kuuka kwa akufa.”Mboni ‘zimachitanso chokoma’ mwauzimu pouza ena uthenga wa m’Baibulo wotonthoza ndiponso wopatsa chiyembekezo. Izo zimakhulupirira zimenenso munthu wina wanzeru wakale ankakhulupirira zakuti: ‘Womvera [nzeru za Mulungu] adzakhala osatekeseka, nadzakhala phee osaopa zoipa.’—Miyambo 1:33.
[Zithunzi patsamba 31]
1, 2. Kugaŵa chakudya kwa anthu amene analibe chakudya ku Mozambique
3, 4. Mkuntho ku Guam unawononga nyumba zambiri
[Mawu a Chithunzi]
Child, left: Andrea Booher/FEMA News Photo; woman, above: AP Photo/Pacific Daily News, Masako Watanabe