Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchoka M’ndende Zamdima Kupita ku Mapiri a ku Switzerland

Kuchoka M’ndende Zamdima Kupita ku Mapiri a ku Switzerland

Mbiri ya Moyo Wanga

Kuchoka M’ndende Zamdima Kupita ku Mapiri a ku Switzerland

YOSIMBIDWA NDI LOTHAR WALTHER

Nditakhala zaka zitatu m’ndende zamdima za boma lachikomyunizimu ku East Germany, ndinali kulakalaka kwambiri kukhala paufulu ndi kukacheza mosangalala ndi banja langa.

KOMABE sindinaganizire kuti ndikakafika kunyumba mwana wanga wamwamuna wazaka sikisi, Johannes, akandiyang’ana modabwa choncho. Iye anakhala theka la zaka zake asanandione, motero ndinali mlendo weniweni kwa iyeyo.

Mosiyana ndi mwana wanga, makolo anga anali kundikonda komanso anali kucheza nane. Tinali kukhala mwamtendere kunyumba kwathu mu mzinda wa Chemnitz, ku Germany, kumene ndinabadwira mu 1928. Bambo anga anali kuneneratu poyera kuti sanali kusangalala ndi chipembedzo. Anali kunena kuti panthaŵi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, asilikali amene anali “Akristu” a mbali zimene zinali kumenyana anali kufunirana mafuno abwino panyengo ya Khirisimasi pa December 25, koma m’maŵa mwake anali kuphana. Iwo anali kuona kuti chipembedzo ndicho pagona chinyengo.

Ndinakhala ndi Chikhulupiriro M’malo Mokhumudwa

Mwayi wake, ine sindinakhumudwe ngati iwowo. Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inatha ndili ndi zaka 17, ndipo ndinangotsala pang’onong’ono kulembedwa usilikali. Komabe, ndinali kuvutika maganizo kwambiri ndi mafunso monga akuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu akuphana chonchi? Kodi ndi ndani amene ndingam’dalire? N’kuti kumene ndingapeze chitetezo chenicheni?’ Dziko la Soviet Union linayamba kulamulira dziko la East Germany kumene tinali kukhala. Mfundo za Chikomyunizimu zokhudza chilungamo, kukhala mofanana, umodzi, ndiponso kukhalirana mwamtendere zinali zosangalatsa kwa anthu amene anatopa ndi mavuto ankhondo. Posapita nthaŵi anthu ambiri oona mtima ameneŵa anali oti akhumudwitsidwa kwambiri, osati ndi chipembedzo koma ndi ndale.

Ndikufunafuna mayankho okhutiritsa a mafunso anga aja, azakhali anga enaake amene anali a Mboni za Yehova, anandiuza zimene amakhulupirira. Anandipatsa buku lonena za Baibulo limene linandipangitsa kuti ndiŵerenge chaputala chonse cha Mateyu 24 kwa nthaŵi yoyamba. Ndinachita chidwi kwambiri kuti bukuli linafotokoza zinthu momveka ndiponso mogwira mtima, linatchula nthaŵi zathu zino kuti ndi “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” ndiponso linatchula zimene zimachititsa mavuto a anthu.​—Mateyu 24:3; Chivumbulutso 12:9.

Patapita nthaŵi pang’ono, ndinalandira mabuku ambiri a Mboni za Yehova, amene ndinawaŵerenga mwachangu, ndipo ndinazindikira kuti ndapeza choonadi chimene ndinali kuchifunafuna ndi mtima wonse chija. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri nditadziŵa kuti Yesu Kristu anaikidwa pampando wachifumu kumwamba mu 1914 ndiponso kuti posachedwapa adzagonjetsa onse otsutsana ndi Mulungu kuti adalitse anthu omvera. Chinthu chachikulu chimene ndinazindikira chinali kumvetsa bwino nkhani ya dipo. Kunandithandiza kupempha Yehova Mulungu mochokera pansi pa mtima kuti andikhululukire. Pempho lachikondi la pa Yakobo 4:8 linandikhudza mtima kwambiri. Pempholo limati: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”

Ngakhale kuti ndinatengeka mtima zedi ndi chikhulupiriro chatsopano chimene ndinapeza, poyamba makolo anga ndi mchemwali wanga sanamvere zimene ndinali kuwauza. Komabe, zimenezi sizinandifooketse kuti ndisamapezeke pamisonkhano yachikristu imene kagulu ka Mboni kanali kuchita pafupi ndi mzinda wa Chemnitz. Ndinadabwa makolo anga ndi mchemwali wanga akutsagana nane paulendo wanga woyamba kupita pamsonkhano. Munali m’chaka cha 1945 m’nyengo yozizira. Kenako, gulu la anthu ophunzira Baibulo litakhazikitsidwa m’tauni ya Harthau kumene tinali kukhala, banja lathu linayamba kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse.

“Ndili Mwana”

Kuphunzira mfundo zofunika za m’Baibulo ndiponso kusonkhana nthaŵi zonse ndi anthu a Yehova kunandipangitsa kupatulira moyo wanga kwa Yehova, ndipo ndinabatizidwa pa May 25, 1946. Ndinasangalala kwambiri kuona makolo anga ndi mchemwali wanga akulimbikira pa moyo wauzimu, ndipo patapita nthaŵi onse anakhala Mboni zokhulupirika. Mchemwali wanga ali mu mpingo wina wa ku Chemnitz ndipo n’ngokangalikabe mpaka pano. Mayi ndi bambo anga anatumikira mokhulupirika mpaka pamene mayi anamwalira mu 1965 ndiponso pamene bambo anamwalira mu 1986.

Patatha miyezi sikisi nditabatizidwa, ndinayamba utumiki waupainiya wapadera. Ichi chinali chiyambi cha moyo wanga wotumikira Mulungu “panthaŵi yabwino ndi panthaŵi yoipa.” (2 Timoteo 4:2, NW) Pasanathe nthaŵi yaitali ndinapeza mwayi wotumikira m’njira zina. Pankafunika alaliki anthaŵi zonse kumadera akutali a kum’maŵa kwa Germany. Ine ndi mbale wina tinafunsira utumiki umenewu, koma ndinali kudziona kuti ndilibe luso komanso sindikukwanira pa udindo waukulu umenewu. Popeza ndinali ndi zaka 18 zokha, ndinali ndi maganizo amene Yeremiya anali nawo. Akuti: “Ha, . . . Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana.” (Yeremiya 1:6) Ngakhale kuti ndinali kukayikira, abale audindo anatilimbikitsa mokoma mtima kuti tikayesere utumikiwo. Choncho, tinatumizidwa ku katauni kakang’ono ka Belzig m’chigawo cha Brandenburg.

Kulalikira m’gawo limeneli kunali kovuta, koma ndinaphunzirapo kanthu. M’kupita kwa nthaŵi, azimayi ena otchuka abizinesi analabadira uthenga wa Ufumu ndipo anakhala Mboni za Yehova. Koma kwa anthu a m’katauni kameneka, zimene anachita azimayi ameneŵa zinali zachilendo kwambiri ndiponso zowapatsa chikayikiro. Atsogoleri achipembedzo achikatolika ndi achipolotesitanti anali kulimbana nafe kwambiri ndipo anali kutinenera zabodza chifukwa cha ntchito yathu yolalikira. Koma chifukwa chokhulupirira Yehova kuti atitsogolere ndi kutiteteza, tinakwanitsa kuthandiza anthu ochita chidwi ndi uthenga wathu kuphunzira choonadi.

Chidani Chiyamba Kukula

Chaka cha 1948 chinali cha madalitso ndi mavuto osayembekezereka. Dalitso loyamba linali kuchita utumiki wa upainiya mu mzinda wa Rudolstadt, ku Thuringia. Kumeneko ndinadziŵana ndi abale ndi alongo ambiri okhulupirika, ndipo ndinali kusangalala kucheza nawo. Mu July chaka chomwecho ndinadalitsidwanso kwambiri. Ndinakwatira Erika Ullmann, mtsikana wachikristu wokhulupirika ndi wokangalika amene ndinadziŵana naye nthaŵi imene ndinayamba kupezeka pamisonkhano mu mpingo wa Chemnitz. Tonse pamodzi tinayamba utumiki wa upainiya ku Harthau, m’mudzi wa kwathu. Koma, patapita nthaŵi, Erika sanapitirize utumiki wa nthaŵi zonse chifukwa cha matenda ndi zifukwa zina.

Imeneyi inali nthaŵi yovuta kwa anthu a Yehova. Pofuna kuti ndisiye ntchito yolalikira kuti ndiloŵe ntchito yolembedwa, unduna woona za anthu apantchito ku Chemnitz unanena kuti kadi langa logulira chakudya silizigwiranso ntchito. Abale audindo anagwiritsa ntchito nkhani yangayi kukapempha boma kuti tikhale odziŵika mwalamulo. Boma linakana zimenezi, ndipo pa June 23, 1950, anandilamula kupereka faindi kapena kukhala m’ndende masiku 30. Tinachita apilo za nkhaniyi, koma khoti lalikulu linakana apiloyo, ndipo ndinamangidwa.

Ichi chinali chiyambi chabe cha mavuto. Pasanathe mwezi umodzi, mu September 1950, atayamba kampeni yotinyoza kudzera m’nkhani zofalitsidwa, ulamuliro wa Chikomyunizimu unaletsa ntchito yathu. Chifukwa chakuti tinali kuwonjezereka kwambiri ndiponso sitinali kuloŵerera m’ndale, anali kunena kuti tinali kabungwe koopsa ka akazitape ka m’mayiko amene sanali achikomyunizimu, kochita “ntchito yokayikitsa” ponamizira chipembedzo. Tsiku lomwelo limene ntchito yathu inaletsedwa, mkazi wanga kunyumba anabereka mwana wamwamuna, Johannes, ine ndili kundende. Ngakhale kuti azamba anakaniza apolisi oona zachitetezo cha boma kuloŵa m’nyumba yathu, iwo anakakamira kuloŵa m’nyumba yathu ndi kufufuza kuti apeze umboni wa mlandu umene anali kutiimbawo. Koma sanapeze chilichonse. Komabe, patapita nthaŵi anatha kuika kazitape mu mpingo wathu. Zimenezi zinapangitsa kuti abale onse amaudindo ndi ine ndemwe timangidwe, mu October 1953.

M’ndende Zamdima

Atatiweruza n’kutilamula kukhala m’ndende kuyambira zaka zitatu mpaka sikisi, tinakapeza abale athu m’ndende zauve za Osterstein Castle, ku Zwickau. Ngakhale kuti moyo unali woipa kwambiri kumeneko, zinali zosangalatsa kwambiri kucheza ndi abale okhwima mwauzimu. Kusoŵa ufulu sikunatanthauze kusoŵa chakudya chauzimu. Ngakhale kuti tinali kunyozedwa ndiponso kuletsedwa ndi boma, Nsanja ya Olonda inali kufika m’ndende mpaka m’zipinda zathu. Kodi zinali kutheka bwanji?

Abale athu ena anali kukagwira ntchito m’migodi ya malasha, kumene anali kukumana ndi Mboni zimene sizinali m’ndende ndipo zinali kuwapatsa magazini. Ndiyeno abalewo anali kubweretsa mwachinsinsi magaziniwo m’ndendemo ndipo amatifikitsira chakudya chauzimu chimene tinali kuchifuna kwambirichi mwanzeru zapamwamba zedi. Ndinasangalala kwambiri ndiponso ndinalimbikitsidwa kuona Yehova akutisamalira ndiponso kutitsogolera mwa njira imeneyi.

Chakumapeto kwa 1954, anatisamutsira ku ndende yotchuka n’zoipa zedi ya m’tauni ya Torgau. A Mboni amene anali kumeneko anatilandira mosangalala. Iwo anakhalabe olimba mwauzimu pobwereza zimene anali kukumbukira kuchokera m’magazini akale a Nsanja ya Olonda. Si mmene anali kufunira chakudya chauzimu chatsopano! Tsopano unali udindo wathu kuwauza mfundo zimene tinaphunzira ku Zwickau. Koma kodi tikanachita bwanji zimenezi popeza anali kutiletsa kulankhulana panthaŵi yantchito yatsiku ndi tsiku? Abale anali atatiuza mfundo zapadera za mmene tingachitire zimenezi, ndipo dzanja la Yehova lamphamvu ndi loteteza linali nafe. Zimenezi zinatiphunzitsa kufunika kwa phunziro la Baibulo ndi kusinkhasinkha pamene tili paufulu ndiponso tili ndi mpata wochita zimenezo.

Panabuka Nkhani Yaikulu Yofunika Kuti Tisankhe Zochita

Ndi thandizo la Yehova, tinakhalabe olimba. Tinadabwa zedi ambirife atatitulutsa kumapeto kwa 1956. N’zovuta kunena mmene tinasangalalira atatsegula zitseko za ndende kuti tituluke. Panthaŵi imeneyi, mwana wanga uja n’kuti ali ndi zaka sikisi, ndipo ndinasangalala kwambiri kukakhalanso ndi mkazi wanga ndiponso kuthandiza kulera mwana wathuyu. Kwa nthaŵi ndithu Johannes anali kundiona ngati mlendo, koma pasanapite nthaŵi yaitali tinayamba kukondana.

Mboni za Yehova ku East Germany zinali kuvutika kwambiri. Popeza boma linali kudana kwambiri ndi utumiki wathu wachikristu ndiponso kusaloŵerera kwathu m’ndale, nthaŵi zonse tinali kukhala mwamantha, ndipo moyo wathu unali wodzala ndi nkhaŵa ndiponso wosasangalala. Choncho ine ndi Erika titapemphera tinaganizira bwinobwino moyo wathu, ndipo tinaganiza zosamukira kumalo abwino kuti tisamangokhalira kudera nkhaŵa. Tinali kufuna kutumikira Yehova mwaufulu ndiponso kukhala ndi zolinga zauzimu.

M’nyengo yachilimwe mu 1957, unapezeka mpata wosamukira ku Stuttgart, West Germany. Kumeneko ntchito yolalikira sinali yoletsedwa, ndipo timatha kusonkhana momasuka ndi abale athu. Iwo anatithandiza kwambiri ndiponso anali kutikonda. Tinakhala zaka seveni mu mpingo wa ku Hedelfingen. M’zaka zimenezi, mwana wathu anayamba sukulu ndipo analimbikira kwambiri choonadi. Mu September 1962, ndinali ndi mwayi woloŵa nawo Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Wiesbaden. Kumeneko ndinalimbikitsidwa kusamuka ndi banja langa kukatumikira kumene kunali kufunika aphunzitsi a Baibulo achijeremani. Zimenezi zinaphatikizapo madera ena a ku Germany ndi Switzerland.

Kusamukira ku Mapiri a ku Switzerland

Kenako, tinasamukira ku Switzerland mu 1963. Tinauzidwa kuti tikagwire ntchito ndi mpingo waung’ono wa m’tauni ya Brunnen, cha kunyanja yokongola ya Lucerne, m’chigawo chapakati cha m’dera la Swiss Alps. Kwa ife zinali ngati kuti tili m’paradaiso. Tinafunika kuzoloŵera Chijeremani chakumeneko, chikhalidwe cha kumeneko, ndiponso mmene anthu a kumeneko amaganizira. Komabe, tinasangalala kugwira ntchito kumeneku ndiponso kulalikira kwa anthu okonda mtendere. Ku Brunnen tinakhalako zaka 14. N’kumene mwana wathu anakulira.

Mu 1977, ndili ndi zaka pafupifupi 50, tinapemphedwa kukatumikira ku Beteli ya Switzerland ku Thun. Tinaona kuti unali mwayi wosayembekezereka ndipo tinaulandira mosangalala kwambiri. Ine ndi mkazi wanga tinatumikira pa Beteli zaka naini, nthaŵi imeneyi timaiona kuti inali yapadera kwambiri pamoyo wathu wachikristu ndiponso ndi nthaŵi imene tinakula mwauzimu. Tinasangalalanso kulalikira ndi ofalitsa a ku Thun ndi a m’madera oyandikana nawo. Nthaŵi zonse tinali kuona zina mwa ntchito ‘zodabwitsa’ za Yehova, zomwe ndi mapiri aakulu a Bernese Alps amene nsonga zake zili ndi chipale chofeŵa.​—Salmo 9:1.

Kusamukanso

Tinasamukanso kumayambiriro kwa chaka cha 1986. Tinapemphedwa kukakhala apainiya apadera m’gawo lalikulu zedi la mpingo wa Buchs kuchigawo cha kum’maŵa kwa Switzerland. Tinafunika kuzoloŵeranso moyo wina. Komabe, chifukwa chofunitsitsa kutumikira Yehova kumene angatigwiritse ntchito kwambiri, tinachita utumiki watsopanowu ndipo anatidalitsa. Nthaŵi zina, ndimagwirizira malo a woyang’anira woyendayenda, kuyendera ndi kulimbikitsa mipingo. Tsopano papita zaka 18, ndipo takumana ndi zinthu zambiri zosangalatsa polalikira m’dera limeneli. Mpingo wa ku Buchs wakula, ndipo timasangalala kusonkhana mu Nyumba ya Ufumu yokongola imene anaipatulira zaka zisanu zapitazo.

Yehova watisamalira m’njira zambiri zedi. Zaka zambiri za moyo wathu takhala mu utumiki wa nthaŵi zonse, koma sitinasoŵepo kanthu. Timasangalala kuona mwana wathu, mkazi wake ndi ana awo ndiponso mabanja a anawo, akuyenda mu njira ya Yehova mokhulupirika.

Ndikaganizira zam’mbuyo, ndimaona kuti tatumikiradi Yehova “panthaŵi yabwino ndi panthaŵi yoipa.” Kuyesetsa kuchita utumiki wachikristu kunandichotsa m’ndende zamdima za Chikomyunizimu kupita ku mapiri okongola a ku Switzerland. Ine ndi banja langa sitinong’oneza bondo ayi.

[Bokosi patsamba 28]

Anapirira Chizunzo cha Maboma Aŵiri

Mu ulamuliro wa German Democratic Republic (GDR), umene unali kudziŵikanso kuti East Germany, Mboni za Yehova zinazunzidwa mwankhanza zedi. Maumboni amene alipo amasonyeza kuti Mboni zoposa 5,000 zinatumizidwa m’misasa yachibalo kukagwira ukaidi ndiponso m’misasa yandende chifukwa cha utumiki wawo wachikristu ndiponso kusaloŵerera m’ndale.​—Yesaya 2:4.

Ena mwa a Mboni ameneŵa anazunzidwa ndi maboma aŵiri. A Mboni okwana 325 anatsekeredwa m’misasa yachibalo ndiponso m’ndende za boma la chipani cha Nazi. Ndiyeno, m’ma 1950, gulu loona zachitetezo la boma la GDR lomwe anali kulitcha kuti Stasi linawasakanso n’kuwatsekera m’ndende. Ndende zina zinagwiritsidwanso ntchito ndi maboma aŵiri​—koyamba monga ndende za Nazi ndipo kenako monga ndende za Stasi.

M’zaka khumi zoyambirira za chizunzo choopsa, kuyambira mu 1950 mpaka mu 1961, A Mboni amuna ndi akazi okwana 60 anafera m’ndende chifukwa chozunzidwa, kusoŵa chakudya, matenda, ndiponso ukalamba. A Mboni 12 analamulidwa kukhala m’ndende kwa moyo wawo wonse koma anawasinthira kuti akhale zaka 15.

Masiku ano, ku likulu lakale la Stasi ku Berlin, kuli chithunzi chosonyeza nyengo ya zaka 40 zimene Mboni za Yehova ku East Germany zinazunzidwa ndi boma. Zithunzi ndiponso nkhani za anthu ena zimene anakhoma kumeneko zimapereka umboni wakachetechete wakuti Mboni zimenezi zimene zinakhulupirika zikuzunzidwa zinali zopanda mantha ndiponso zolimba mwauzimu.

[Mapu pamasamba 24, 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

EAST GERMANY

Rudolstadt

Belzig

Torgau

Chemnitz

Zwickau

[Chithunzi patsamba 25]

Nyumba ya Osterstein Castle, ku Zwickau

[Mawu a Chithunzi]

Fotosammlung des Stadtarchiv Zwickau, Deutschland

[Chithunzi patsamba 26]

Ndi mkazi wanga, Erika