Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chifukwa chiyani Davide, mtumiki wokhulupirika wa Yehova, analola mkazi wake Mikala kukhala ndi terafi kapena kuti chifanizo, monga mmene pa 1 Samueli 19:12, 13 pakufotokozera?

Choyamba tiyeni tione nkhani yonse mwachidule. Mkazi wa Davide atamva kuti Mfumu Sauli ikukonza zoti iphe Davide, iye anachitapo kanthu mwamsanga. Baibulo limati: “Mikala anam’tsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathaŵa, napulumuka. Ndipo Mikala anatenga chifanizo [chomwe mwachionekere chinali cha usinkhu wofanana ndi munthu ndiponso chooneka ngati munthu] nachiika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda.” Amithenga a Sauli atafika kuti adzamugwire, Mikala anawauza kuti: “Iye alikudwala.” Machenjera ameneŵa anachedwetsa anthu amene ankafunafuna Davidewo, ndipo iye anatha kupulumuka.​—1 Samueli 19:11-16.

Zimene ofukula za m’mabwinja apeza zikusonyeza kuti kale, anthu ankasunga zifanizo za aterafi kuti azigwiritsa ntchito pa kupembedza komanso kuzigwiritsa ntchito pa zamalamulo. Monga mmene masiku ano zikalata zosonyeza mwini malo ndi zikalata za wilo zimasonyeza amene ayenera kutenga chuma chamasiye, kale zifanizo za terafi zinkagwiritsidwanso ntchito chimodzimodzi. Zikuoneka kuti, m’zochitika zina, mkamwini akakhala ndi terafi anali ndi ufulu wotenga chuma cha apongozi ake amene anamwalira. Zimenezi zingathandize kumvetsa chifukwa chake nthaŵi ina zimenezi zisanachitike, Rakele anatenga aterafi a atate ake, ndiponso chifukwa chake atate akewo mtima sunali m’malo kufuna kuti mpaka apeze aterafiwo. Pankhani imeneyi, mwamuna wa Rakele, Yakobo, sanadziŵe zimene mkazi wake anachita.​—Genesis 31:14-34.

Aisrayeli atakhala mtundu, analandira Malamulo Khumi, ndipo lamulo lachiŵiri linaletsa mosapita m’mbali kupanga mafano. (Eksodo 20:4, 5) Patapita nthaŵi, mneneri Samueli anakhudza lamulo limeneli polankhula kwa Mfumu Sauli. Iye anati: “Kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula [“aterafi,” NW].” (1 Samueli 15:23) Pachifukwa chimenechi, zikuoneka kuti aterafi sanali kugwiritsidwa ntchito pankhani ya amene angatenge chuma chamasiye mu Israyeli. Komabe, zikuoneka kuti zikhulupiriro zakale zimenezi za Ayuda zinapitirira m’mabanja ena. (Oweruza 17:5, 6; 2 Mafumu 23:24) Mfundo yoti Mikala anali ndi chifanizo cha terafi ikusonyeza kuti sanali ndi mtima woongoka pamaso pa Yehova. Mwina Davide sanali kudziŵa za chifanizo cha teraficho kapena analola kuti akhale nacho chifukwa chakuti Mikala anali mwana wa Mfumu Sauli.

Maganizo a Davide pankhani yolambira Yehova yekha basi anawafotokoza m’mawu aŵa akuti: “Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse. Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano; koma Yehova analenga zakumwamba.”​—1 Mbiri 16:25, 26.

[Chithunzi patsamba 29]

Lamulo lachiŵiri pa Malamulo Khumi linaletsa kupanga mafano, monga chifanizo cha terafi chimene chili pano

[Mawu a Chithunzi]

From the book The Holy Land, Vol. II, 1859