Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Muwolokere Kuno Mudzatithangate Ife’

‘Muwolokere Kuno Mudzatithangate Ife’

Olengeza Ufumu Akusimba

‘Muwolokere Kuno Mudzatithangate Ife’

MU JULY 2000, Mboni zolankhula Chijeremani za ku Austria, Germany, ndi Switzerland zinapemphedwa kuti zipite ku Bolivia. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti midzi ya alimi yakutali yomwe ili m’dera lozungulira makilomita 300 kuchokera ku Santa Cruz, ku Bolivia, anthu a mpingo wa Amenonite olankhula Chijeremani anasonyeza chidwi ndi Baibulo.

Mboni pafupifupi 140 zinavomera kuti zipita. Ena anakakhalako kwa mlungu umodzi pamene ena anakhalako kwa chaka kapena kuposa pamenepo. Mwa kuchita zimenezi, Mbonizo zinasonyeza mtima wofanana ndi umene amishonale a m’zaka 100 zoyambirira anasonyeza pamene anavomera pempho lakuti: “Muwolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.”​—Machitidwe 16:9, 10.

Kodi ntchito yolalikira m’gawo limeneli imayenda bwanji? Mkulu wa mpingo wakomweko anafotokoza kuti: “Kuyenda pa galimoto yamphamvu m’misewu yokumbikakumbika kukafika m’mudzi umodzi mwa midzi 43 ya Amenonite kungatenge maola asanu ndi atatu. Kukafika kumalo akutali nthaŵi zambiri kumatenga masiku anayi ndiponso kugona m’matenti masiku ena usiku. Koma m’poyenera kuchita zimenezi, chifukwa anthu onse kumeneko sanamvepo uthenga wabwino.”

Poyamba, Amenonite ambiri sanasangalale ndi kuyenderedwako. Koma kuwayendera mobwerezabwereza kwawathandiza kuzindikira zimene Mboni za Yehova zawatengera. Mwachitsanzo, mlimi wina anati anakhala akuŵerenga magazini ya Galamukani! kwa chaka chimodzi. Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ndikudziŵa kuti anthu ambiri kuno sagwirizana ndi zimene inu mumanena, koma ndimakhulupirira kuti ndi choonadi.” M’mudzi wina, mwamuna wina anati: “Anthu ena amene ndayandikana nawo amanena kuti ndinu aneneri onyenga, ena amati muli ndi choonadi. Ndikufuna ndidzionere ndekha.”

Panopa kuli mpingo wa Chijeremani ku Bolivia, womwe uli ndi ofalitsa 35, pamodzi ndi alaliki a nthaŵi zonse okwana 14. Tsopano, anthu okwana 14 omwe kale anali a mpingo wa Amenonite ndi olengeza Ufumu, ndipo ena 9 amapezeka pa misonkhano nthaŵi zonse. Munthu wina wachikulire amene anabatizidwa posachedwapa anati: “Tikuona bwinobwino kuti Yehova akutitsogolera. Watumiza abale ndi alongo olankhula Chijeremani amene akudziŵa bwino ntchito imeneyi kuti atithandize. Tikuyamikira kwambiri.” Mwana wamkazi wa mkulu ameneyu wa zaka 17 yemwenso ndi wobatizidwa, anawonjezera kuti: “Changu cha abale ndi alongo achinyamata amene anabwera kuno ambiri akuchitengera. Ambiri mwa iwo ndi apainiya, amene amagwiritsa ntchito nthaŵi yawo ndi ndalama zawo kuthandiza ena. Inenso ndikufuna kuchita chimodzimodzi.”

Kunena zoona, amene anayetsetsa ‘kuwoloka’ kuti akathangate anzawo akupeza chimwemwe chochuluka ndipo akusangalala.