Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Odala Ndi Amene Amapatsa Mulungu Ulemerero

Odala Ndi Amene Amapatsa Mulungu Ulemerero

Odala Ndi Amene Amapatsa Mulungu Ulemerero

‘Adzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.’​—SALMO 86:9.

1. Kodi n’chifukwa chiyani ife titha kupatsa Mulungu ulemerero kuposa zolengedwa zopanda moyo?

YEHOVA ayenera kulemekezedwa ndi zolengedwa zake zonse. Ngakhale kuti zolengedwa zake zopanda moyo zimam’patsa ulemerero mosatulutsa mawu, anthufe timatha kuganiza, kumvetsa zinthu, kuyamikira, ndiponso kulambira. Choncho wamasalmo akulankhula ndi ife pamene akuti: “Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. Imbirani ulemerero wa dzina lake; pom’lemekeza mum’chitire ulemerero.”​—Salmo 66:1, 2.

2. Kodi ndani amene amvera lamulo lopatsa dzina la Mulungu ulemerero, nanga n’chifukwa chiyani atero?

2 Anthu ambiri amakana kuti Mulungu aliko kapena safuna kum’patsa ulemerero. Komabe, m’mayiko 235, Mboni za Yehova zoposa 6,000,000 zimasonyeza kuti zimaona makhalidwe ‘osaoneka’ a Mulungu mwa zinthu zimene iye anapanga ndi kuti ‘zamva’ umboni wopanda mawu umene chilengedwe chimapereka. (Aroma 1:20; Salmo 19:2, 3) Chifukwa chophunzira Baibulo, izo zadziŵa Yehova ndi kum’konda. Salmo 86:9, 10 linalosera kuti: “Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu. Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwiza; Inu ndinu Mulungu, nokhanu.”

3. Kodi ndi motani mmene ‘khamu lalikulu limatumikirira usana ndi usiku’?

3 Chivumbulutso 7:9, 15 chimafotokozanso “khamu lalikulu” la olambira amene ‘akutumikira [Mulungu] usana ndi usiku m’Kachisi mwake.’ Sikuti Mulungu amafunadi kuti atumiki ake azim’tamanda osapuma, koma kuti olambira ake ndi gulu limene likupezeka padziko lonse. Ndiye mbali ina ya dziko kukada, atumiki a Mulungu kumbali inayo amakhala kalikiliki kuchitira umboni. Choncho kulikonse kumene kuli anthu amene akupatsa Yehova ulemerero tinganene kuti dzuŵa sililoŵa. Posachedwapa “zonse zakupuma” zidzafuula kutamanda Yehova. (Salmo 150:6) Nangano kodi ife aliyense payekha tingachite chiyani panopa kuti tipatse Mulungu ulemerero? Kodi tingakumane ndi mavuto otani? Ndipo kodi amene amapatsa Mulungu ulemerero adzalandira madalitso otani? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tiyeni tipende nkhani ya m’Baibulo yokhudza fuko la Gadi mu Israyeli.

Vuto Limene Ena Kale Anakumana Nalo

4. Kodi fuko la Gadi linakumana ndi vuto lotani?

4 Asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, a fuko la Gadi mu Israyeli anapempha kuti akhale m’dera labwino kusungiramo ziŵeto kum’maŵa kwa mtsinje wa Yordano. (Numeri 32:1-5) Kukhala m’deralo kunali ndi mavuto ake. Nthaŵi ya nkhondo, mafuko akumadzulo anali kutetezedwa ndi chigwa cha Yordano chimene chinali chotchinga chachilengedwe. (Yoswa 3:13-17) Koma za dera la kum’maŵa kwa Yordano, buku lakuti The Historical Geography of the Holy Land, lolembedwa ndi George Adam Smith limati: “[Deralo] n’lafulati, ndipo lilibe chotchinga chilichonse, lili pa chikweza cha Arabiya. Choncho mafuko anjala amene amangoyendayenda akhala akuliloŵerera kuyambira kale, ndipo ena a iwo amatero mwaunyinji wawo chaka chilichonse kufunafuna msipu.”

5. Kodi Yakobo ananena chiyani kulimbikitsa mbadwa za Gadi kubwezera adani awo akawaukira?

5 Kodi fuko la Gadi likanatha bwanji kupirira vuto losatha limenelo? Kalelo zaka zambiri nthaŵi yawoyo isanafike, kholo lawo Yakobo pomwalira analosera kuti: “Ndi Gadi, achifwamba adzam’psinja iye; koma iye adzapsinja pa chitende chawo.” (Genesis 49:19) Kungowaona koyamba, mawu ameneŵa angamveke ngati osalimbikitsa. Koma kunena zoona, anali lamulo kwa fuko la Gadi kuti iwo azibwezera. Yakobo anawalonjeza kuti iwo akatero, achifwambawo adzathaŵa ndi manyazi, ndipo Agadiwo adzawalondola m’mbuyo kuwapitikitsa.

Mavuto pa Kulambira Kwathu Masiku Ano

6, 7. Kodi zinthu kwa Akristu masiku ano zikufanana bwanji ndi mmene zinalili kwa fuko la Gadi?

6 Mofanana ndi fuko la Gadi, Akristufe masiku ano timakumana ndi mavuto ndi zothetsa nzeru za m’dziko la Satana; tilibe chitetezo chozizwitsa chimene chingatithandize kupeŵa kulimbana nawo mavutowo. (Yobu 1:10-12) Ife ambiri tikulimbana ndi vuto lopita kusukulu, kupeza zofunika pamoyo, ndi kulera ana. Komanso pali mavuto amene munthu payekhapayekha amakumana nawo. Ena akupirira “munga m’thupi” monga kulumala kapena matenda. (2 Akorinto 12:7-10) Ena akuzunzika mtima podziona kuti ndi osafunika. “Masiku oipa” a ukalamba angalepheretse Akristu okalamba kutumikira Yehova ndi mphamvu monga kale.​—Mlaliki 12:1.

7 Ndiponso mtumwi Paulo akutikumbutsa kuti ‘kulimbana kwathu tilimbana . . . ndi a uzimu a choipa m’zakumwamba.’ (Aefeso 6:12) Nthaŵi zonse timayang’anizana ndi “mzimu wa dziko lapansi,” mzimu wachipanduko ndi wa makhalidwe oipa umene Satana ndi ziŵanda zake akulimbikitsa. (1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2, 3) Mofanana ndi Loti amene anali kuopa Mulungu, ife masiku ano tingaleme mtima ndi zinthu zoipa zimene anthu amene timakhala nawo amalankhula ndi kuchita. (2 Petro 2:7) Satananso amatiukira mwachindunji. Iye akuchita nkhondo ndi otsalira a odzozedwa, “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 12:17) Satana amaukiranso “nkhosa zina” za Yesu mwa kuyambitsa ziletso ndi chizunzo.​—Yohane 10:16.

Tigonje Kapena Tilimbane Nazo?

8. Kodi tiyenera kuchita chiyani Satana akamatiukira, nanga chifukwa chake n’chiyani?

8 Kodi tiyenera kuchita chiyani Satana akamatiukira? Mofanana ndi fuko lakale la Gadi, tiyenera kukhala olimba mwauzimu n’kulimbana naye mogwirizana ndi malangizo a Mulungu. Tsoka lake n’loti ena ayamba kugonja chifukwa cha zovuta pamoyo wawo, ndipo anyalanyaza udindo wawo wauzimu. (Mateyu 13:20-22) Wa Mboni wina, pofotokoza chifukwa chake pamisonkhano mu mpingo wawo pamapezeka anthu ochepa, anati: “Abale akutopa. Onse ali opanikizika.” Inde, pali zifukwa zambiri zimene anthu ambiri masiku ano alili otopa. Choncho n’zapafupi munthu kuona kulambira Mulungu monga vuto lalikulu, monga udindo wina wotopetsa. Koma kodi maganizo oterowo ndi abwino?

9. Kodi kusenza goli la Kristu kumadzetsa bwanji mpumulo?

9 Taganizani zimene Yesu anauza makamu a m’masiku ake amene anali otopa chifukwa cha mavuto pamoyo wawo. Iye anati: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” Kodi Yesu ananena kuti munthu adzapeza mpumulo mwa kusiya kutumikira Mulungu? Iyayi, m’malo mwake anati: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.” Goli ndi mtengo kapena chitsulo chimene chimathandiza munthu kapena nyama kunyamula katundu wolemera. Nanga munthu angafunirenji kusenza goli limenelo? Kodi sindife ‘olema’ kale? N’zoona, koma mawu achigiriki a palemba limeneli angatanthauzenso kuti: “Loŵani pansi pa goli langa pamodzi ndi ine.” Tangoganizani: Yesu akudzipereka kuti atithandize kukoka katundu wathu wolemera! Choncho sitifunika kuchita zimenezo ndi mphamvu zathu zokha.​—Mateyu 9:36; 11:28, 29; 2 Akorinto 4:7.

10. Kodi chimachitika n’chiyani tikamachita khama kupatsa Mulungu ulemerero?

10 Tikasenza goli lokhala ophunzira a Yesu, ndiye kuti tikulimbana ndi Satana. Yakobo 4:7 amalonjeza kuti: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.” Apa sitikunena kuti n’zapafupi kuchita zimenezi. Kutumikira Mulungu kumafuna khama. (Luka 13:24) Komano Baibulo, pa Salmo 126:5, limatilonjeza kuti: “Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.” Eya, Mulungu amene ife timam’lambira amayamikira. Iye ali “wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye,” ndipo amadalitsa anthu amene amam’patsa ulemerero.​—Ahebri 11:6.

Kupatsa Mulungu Ulemerero mwa Kulalikira Ufumu

11. Kodi utumiki wa kumunda umakhala bwanji ngati chitetezo Satana akamatiukira?

11 Yesu analamula kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” Ntchito yolalikira ndiyo njira yaikulu yoperekera kwa Mulungu “nsembe yakuyamika.” (Mateyu 28:19; Ahebri 13:15) ‘Kudziveka mapazi athu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere’ ndi mbali yofunika kwambiri pa “zida [zathu] zonse,” ndipo ndiyo chitetezo chathu Satana akamatiukira. (Aefeso 6:11-15) Kutamanda Mulungu mu utumiki wa kumunda ndiyo njira yabwino yolimbitsira chikhulupiriro chathu. (2 Akorinto 4:13) Kuchita zimenezo kumatithandiza kusaganizira zinthu zofooketsa. (Afilipi 4:8) Kupita mu utumiki wa kumunda kumatithandiza kukhala ndi mayanjano olimbikitsa ndi olambira anzathu.

12, 13. Kodi banja lingapindule motani ngati limapita mu utumiki wa kumunda nthaŵi zonse? Perekani chitsanzo.

12 Ntchito yolalikira ingakhalenso yabwino kuchitira limodzi pabanja. Kunena zoona, ana amafunikira zosangalatsa zabwino. Koma nthaŵi imene banja limathera mu utumiki wa kumunda siyenera kukhala yotopetsa. Makolo angathandize kuti nthaŵiyo izikhala yosangalatsa mwa kuphunzitsa ana awo kuchita utumiki mogwira mtima. Pajatu ana amakonda kuchita zinthu zimene amazitha bwinobwino. Makolo angathandize ana awo kusangalala ndi utumiki mwa kusawaumiriza anawo kuchita zinthu zimene sangathe.​—Genesis 33:13, 14.

13 Ndiponso, banja limene limatamanda Mulungu ubwenzi wawo umalimba. Taonani chitsanzo cha mlongo amene mwamuna wake wosakhulupirira anam’siya ali ndi ana asanu. Mlongoyu anakumana ndi vuto logwira ntchito yolembedwa ndi kupezera ana ake zofunika pamoyo. Kodi zimenezi zinam’topetsa kwambiri moti n’kunyalanyaza moyo wauzimu wa ana ake? Iye anati: “Ndinaphunzira Baibulo mwakhama ndi mabuku ofotokoza Baibulo ndipo ndinayesetsa kutsatira zimene ndinaŵerenga. Ndinali kupita ndi ana anga ku misonkhano ndi mu ulaliki wa khomo ndi khomo. Mukudziŵa zotsatira zake? Ana asanu onsewo ndi obatizidwa.” Ngati mukuchita utumiki mokwanira, ungakuthandizeni inunso pamene mukuyesetsa kulera ana anu “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”​—Aefeso 6:4.

14. (a) Kodi ndi motani mmene achinyamata angapatsire Mulungu ulemerero kusukulu? (b) Kodi n’chiyani chingathandize achinyamata ‘kusachita manyazi ndi uthenga wabwino’?

14 Achinyamatanu, ngati mukukhala m’dziko limene malamulo amalola anthu kukambirana za chipembedzo, kodi mumapatsa Mulungu ulemerero mwa kuchitira umboni kusukulu, kapena mumalephera chifukwa choopa anthu? (Miyambo 29:25) Wa Mboni wina wa zaka 13 ku Puerto Rico analemba kuti: “Sindinachitepo manyazi kulalikira kusukulu chifukwa ndikudziŵa kuti chimenechi n’choonadi. M’kalasi ndimatukula dzanja ndi kuwauza zimene ndaphunzira m’Baibulo. Ngati sitikuphunzira, ndimapita ku laibulale kukaŵerenga buku la Achichepere Akufunsa.” * Kodi Yehova wam’dalitsa iye chifukwa cha khama lake? Iye akuti: “Nthaŵi zina anzanga m’kalasi amandifunsa mafunso mpaka amandipempha bukulo.” Ngati inu mwakhala mukuzengereza pankhani imeneyi, mwina mufunikira kutsimikiza chimene chili “chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Mukakhutira kuti zimene mwaphunzirazo ndi choonadi, simudzachita ‘manyazi ndi uthenga wabwino’ m’pang’ono pomwe.​—Aroma 1:16.

‘Khomo Lotseguka’ la Utumiki

15, 16. Kodi ndi “khomo lalikulu ndi lochititsa” liti limene Akristu ena aloŵapo, ndipo apeza madalitso otani?

15 Mtumwi Paulo analemba kuti “khomo lalikulu ndi lochititsa” linam’tsegukira. (1 Akorinto 16:9) Kodi moyo wanu ungakuloleni kuloŵa pakhomo lochititsa kapena kuti la ntchito? Mwachitsanzo, kuchita upainiya wokhazikika kapena wothandiza kumafuna kuti munthu azithera maola 70 kapena 50 mwezi uliwonse pa ntchito yolalikira. Mosakayika, apainiya amayamikiridwa kwambiri ndi Akristu anzawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo pa utumiki. Apainiya saganiza kuti amaposa abale ndi alongo awo chifukwa chakuti iwo amathera nthaŵi yambiri mu utumiki ayi. M’malo mwake, iwo ali ndi maganizo amene Yesu analimbikitsa, akuti: “Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.”​—Luka 17:10.

16 Upainiya umafuna munthu wodziletsa, wadongosolo, ndi wokonzeka kudzimana. Koma m’pake kutero, chifukwa madalitso ake ndi ambiri. Mpainiya wina wachinyamata dzina lake Tamika anati: “Kuti munthu uzitha kulunjika nawo bwino Mawu a Mulungu ndi dalitso lalikulu. Ukamachita upainiya, umagwiritsa ntchito Baibulo kwambiri. Panopa ndikamapita khomo ndi khomo, ndimatha kukumbukira malemba oyenerera kwa mwininyumba aliyense.” (2 Timoteo 2:15) Mpainiya wina dzina lake Mica anati: “Dalitso lina lalikulu ndi kuona mmene choonadi chimakhudzira moyo wa anthu.” Mnyamata wina dzina lake Matthew nayenso anafotokoza chisangalalo chimene amakhala nacho “kuona munthu ataloŵa m’choonadi. Palibe zimene zimasangalatsa kuposa zimenezi.”

17. Kodi zinatheka bwanji kuti Mkristu wina asiye kuganiza kuti sangauthe upainiya?

17 Bwanji inuyo osaganiza zoloŵa pakhomolo n’kuyamba upainiya? Mwina mumafuna kutero koma mukuganiza kuti simungathe. Mlongo wina wachitsikana dzina lake Kenyatte anati: “Sindinafune kuchita upainiya. Ndinaganiza kuti sindingathe. Sindinali kudziŵa kukonzekera moyambira makambirano kapena kugwiritsa ntchito Malemba pothandiza munthu kuganiza.” Ndiyeno akulu anasankha mlongo wina mpainiya wokhwima maganizo kuti azigwira naye ntchito. Kenyatte anati: “Zinali zosangalatsa kugwira naye ntchito mlongo ameneyo. Zimenezi zinandilimbikitsa kuchita upainiya.” Mwina inunso mungafune kuchita upainiya wina atakulimbikitsani ndi kukuphunzitsani.

18. Kodi amene amayamba utumiki waumishonale angalandire madalitso otani?

18 Upainiya umatsegulira munthu khomo lolandirira mwayi wina wa utumiki. Mwachitsanzo, mwamuna ndi mkazi wake angayenerere kuphunzitsidwa kukhala amishonale oti n’kutumizidwa kukalalikira kudziko lina. Amishonale ayenera kuzoloŵera dziko latsopanolo, mwinanso kuphunzira chinenero china, chikhalidwe china, ndi kuzoloŵera zakudya zina. Koma chifukwa cha kuchuluka kwa madalitso amene amapeza, zovuta ngati zimenezo samaziyesa kanthu. Mildred, mmishonale amene watumikira zaka zambiri ku Mexico, anati: “Palibe tsiku limene ndimaganiza kuti ndinalakwitsa kukhala mmishonale. Kuyambira ndili mtsikana wamg’ono, ndakhala ndikulakalaka ntchito imeneyi.” Kodi iye wapeza madalitso otani? “Kwathu, zinali zovuta kupeza phunziro la Baibulo. Koma kuno, zimatheka kuti ophunzira anayi mwa ophunzira anga onse amayamba kuloŵa mu utumiki panthawi imodzi!”

19, 20. Kodi amene amachita utumiki wa pa Beteli, utumiki wa m’mayiko, ndi oloŵa Sukulu Yophunzitsa Utumiki apeza madalitso otani?

19 Amenenso amachita utumiki wa pa Beteli pa maofesi a nthambi a Mboni za Yehova amapeza madalitso ochuluka. Sven, mbale wachinyamata amene akutumikira pa Beteli ku Germany, anafotokoza za ntchito yake kuti: “Ineyo ndimaganiza kuti zimene ndikuchitazi n’zaphindu pa moyo wanga wonse. Ndikanafuna ndikanagwiritsa ntchito luso langali kudziko. Koma kuteroko kukanakhala ngati kuika ndalama kubanki imene ili pafupi kugwa.” Kunena zoona, kudzipereka kugwira ntchito yopanda malipiro kumafuna mtima wodzimana. Koma Sven akuti: “Ukaŵeruka, umadziŵa kuti zonse zimene wachita tsikulo wachitira Yehova. Ndipo chifukwa cha zimenezi umamva bwino kwambiri.”

20 Abale ena alandira dalitso pochita utumiki wa m’mayiko, wogwira ntchito yomanga nthambi m’mayiko akunja. Mwamuna wina ndi mkazi wake, amene atumikira m’mayiko asanu ndi atatu, analemba kuti: “Abale kuno ndi abwino kwambiri. Zidzatipweteka tikamachoka​—ulendo uno zitipweteka kachisanu ndi chitatu. Koma ndiye takhala ndi moyo wosangalatsa kwambiri!” Palinso Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Imeneyi imapereka maphunziro auzimu kwa abale osakwatira amene ali oyenerera. Wina amene anamaliza maphunzirowa analemba kuti: “Zikundivuta kuti ndingakuthokozeni bwanji chifukwa cha sukulu yabwino kwambiri imeneyi. Kodi ndi gulu liti limene limachita khama ngati limeneli kuphunzitsa anthu ake?”

21. Kodi ndi nkhondo yotani imene Akristu onse ali nayo potumikira Mulungu?

21 Inde, pali makomo ambiri otseguka a ntchito. Komabe ambiri a ife sititha kutumikira pa Beteli kapena kudziko lina. Yesu mwiniwakeyo anavomereza kuti Akristu adzabala “zipatso” mosiyanasiyana chifukwa cha kusiyana kwa moyo wawo. (Mateyu 13:23) Ndiye nkhondo imene tili nayo monga Akristu n’njoti tigwiritse ntchito moyo wathu bwino lomwe​—kutumikira Yehova mokwanira mpaka pamene moyo wathu umatilola. Tikamatero, timapatsa Yehova ulemerero, ndipo tidziŵe kuti iye amasangalala kwambiri. Taganizani za Ethel, mlongo wokalamba amene amakhala m’nyumba yosungirako okalamba ndi odwala. Iye nthaŵi zonse amalalikira anzake m’nyumbayo ndipo amachita ulaliki wa patelefoni. Ngakhale kuti satha kuchita zambiri, amachita utumiki wake ndi moyo wonse.​—Mateyu 22:37.

22. (a) Kodi ndi njira zina ziti zimene tingapatsire Mulungu ulemerero? (b) Kodi ndi nthaŵi iti yosangalatsa imene tikuidikira?

22 Koma kumbukirani kuti kulalikira kwangokhala imodzi mwa njira zimene timapatsira Yehova ulemerero. Ngati timakhala ndi khalidwe labwino ndi kaonekedwe kabwino kuntchito, kusukulu, ndi panyumba pathu, timakondweretsa mtima wa Yehova. (Miyambo 27:11) Miyambo 28:20 imalonjeza kuti: “Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri.” Choncho tiyenera ‘kufesa moolowa manja, kuti tidzatute moolowa manjanso.’ (2 Akorinto 9:6) Tikatero, tidzachita mwayi ndipo tidzakhalapo panthaŵi yosangalatsa pamene “zonse zakupuma” zidzapatsa Yehova ulemerero umene umam’yenerera kwambiri!​—Salmo 150:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Buku la Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi anthu a Yehova amam’tumikira motani “usana ndi usiku”?

• Kodi fuko la Gadi linakumana ndi vuto lotani, ndipo zimenezi zikuwaphunzitsa chiyani Akristu masiku ano?

• Kodi utumiki wa kumunda umakhala bwanji ngati chitetezo Satana akamatiukira?

• Kodi ndi ‘khomo lotseguka’ liti limene ena aloŵapo, ndipo apeza madalitso otani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Mofanana ndi Agadi amene analimbana ndi achifwamba, Akristu ayenera kulimbana ndi Satana

[Chithunzi patsamba 17]

Timakhala ndi mayanjano olimbikitsa mu utumiki wa kumunda

[Zithunzi patsamba 18]

Upainiya ungatsegule khomo lolandirira mwayi wina wa utumiki, monga:

1. Utumiki wa m’mayiko

2. Utumiki wa pa Beteli

3. Utumiki waumishonale