Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Anatiphunzitsa Kulemekeza Chipembedzo Chake’

‘Anatiphunzitsa Kulemekeza Chipembedzo Chake’

Anatiphunzitsa Kulemekeza Chipembedzo Chake’

MAYI wina wa Mboni za Yehova wa ku Rovigo, m’dziko la Italy, anauzidwa kuti ali ndi chotupa ndi kuti moyo wake unali pangozi. Atagonekedwa maulendo angapo m’chipatala, komwe anali kupempha kuti athandizidwe popanda kumuika magazi, anayamba kuthandizidwira kunyumba ndi gulu la manesi osamalira odwala matenda a kansa m’dera lakwawoko.

Madokotala ndi manesi omwe ankam’thandizawo anachita chidwi kwambiri poona chikhulupiriro cholimba cha mayi wazaka 36 ameneyu komanso poona kuti anali wofunitsitsa kugwirizana nawo. Patatsala nthaŵi yochepa kuti mayiyu amwalire ndi matenda a kansawo, mmodzi mwa manesi omuthandizawo analemba m’magazini ina ya zaunesi nkhani yofotokoza zomwe anaona posamalira wodwalayu yemwe anamutcha kuti Angela.

“Angela ndi wansangala komanso akufunitsitsa kukhala ndi moyo. Akudziŵa za moyo wake ndiponso matenda ake aakuluwo, ndipo mofanana ndi zimene wina aliyense wa ife angachite, iye akufunafuna njira kapena mankhwala othetsera vuto lake. . . . Pang’ono ndi pang’ono manesife tinali kuzoloŵerana naye. Sanakane thandizo lathu. M’malo mwake, chifukwa choti Angela ankalankhula mosabisa kanthu, zinthu zonse zinakhala zopepuka. Tinkasangalala kupita kukam’samalira, popeza tinkadziŵa kuti inali nthaŵi yokakumana ndi munthu wamtima wabwino komanso nthaŵi yoti tonse, ifeyo ndi iyeyo, tikapindula. . . . Sitinachedwe kuzindikira kuti tilephera kumuthandiza bwino chifukwa cha chipembedzo chake.” Izi ndi zimene nesiyu ankaganiza chifukwa chakuti ankaganiza kuti Angela ayenera kuikidwa magazi, zomwe mwiniwake anakana.​—Machitidwe 15:28, 29.

“Poti ndife ogwira ntchito ya zachipatala, tinauza Angela kuti sitikugwirizana ndi maganizo akewo, koma iye anatithandiza kumvetsa mmene amaonera moyo. Tinamvetsanso kuti iye ndi banja lake amaona kuti chipembedzo chawo n’chofunika kwambiri. Angela sanataye mtima. Iye sanagonje nawo matendaŵa. Ali ndi mphamvu. Akufuna kukhala ndi moyo, kulimbana ndi matendaŵa, ndi kupitiriza kukhalabe ndi moyo. Ananena zomwe mtima wake unatsimikiza kuchita, zimene iye amakhulupirira. Iye ali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri; chikhulupiriro chathu sicholimba ngati chakecho. . . . Angela anatiphunzitsa kufunika kolemekeza chipembedzo chake, zomwe n’zosemphana kwambiri ndi mfundo zimene timatsatira pantchito yathu. . . . Tikukhulupirira kuti zinthu zimene taphunzira kwa Angela n’zofunika kwambiri, chifukwa chakuti timakumana ndi anthu a mitundu yosiyanasiyana, mavuto osiyanasiyana, anthu a zipembedzo zosiyanasiyana, ndipo tingaphunzire kenakake kwa munthu aliyense amene takumana naye komanso ifeyo tingam’phunzitse kanthu kena.”

Kenako, nkhaniyo inafotokoza za malamulo amene manesi a ku Italy amatsatira pantchito yawo, omwe anavomerezedwa mu 1999, amene amati: “Nesi amagwira ntchito zake, moganizira chipembedzo, mfundo, ndi chikhalidwe cha munthu wodwala, komanso poganizira fuko ndiponso kuti munthuyo ndi mwamuna kapena mkazi.” Nthaŵi zina, zimavuta kuti madokotala ndi manesi atsatire zimene wodwala akufuna mogwirizana ndi chipembedzo chake, moti timayamikira kwambiri madokotala amene ndi ofunitsitsa kutsatira zimenezi.

Mboni za Yehova sizingosankha mwachisawawa zinthu zoti zichite pankhani ya thanzi lawo ndiponso chithandizo chamankhwala; zimakhala zitalingalira mofatsa. Zimaona kuti zimene Malemba amanena ndi zofunika kwambiri, ndipo monga momwe taonera pa zomwe zinachitikira Angela, sikuti ndi anthu aliuma. (Afilipi 4:5) Padziko lonse, anthu ochulukirachulukira ogwira ntchito ya zachipatala amafuna kutsatira chikumbumtima cha odwala awo a Mboni.