Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Choloŵa Chamtengo Wapatali Kwambiri pa Zonse

Choloŵa Chamtengo Wapatali Kwambiri pa Zonse

Choloŵa Chamtengo Wapatali Kwambiri pa Zonse

CHAKUMAPETO kwa moyo wake, mtumwi wokalambayo Yohane analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti ali kuyenda m’choonadi.”​—3 Yohane 4.

Mtumwi wokhulupirikayu anali kunena za anthu omwe anali ana ake mwauzimu. Komabe, makolo ambiri angamvenso mofanana ndi mmene mtumwiyu anamvera. Iwo ayesetsa kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye,” ndipo tsopano amasangalala kuona ana awo akuluakulu “ali kuyenda m’choonadi.” (Aefeso 6:4) Ndipotu, choloŵa chamtengo wapatali kwambiri kwa ana ndicho kuwaphunzitsa njira ya kumoyo wosatha. Zili choncho chifukwa chakuti ntchito zokhudzana n’kupembedza Mulungu, zomwe zimaphatikizapo kukhala moyo umene Yehova amafuna kwa Akristu, ‘zikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’​—1 Timoteo 4:8.

Yehova, yemwe ndi Atate wangwiro, amayamikira kwambiri makolo oopa Mulungu amene amayesetsa kuphunzitsa ana awo zinthu zauzimu. Anawo akamatsatira zomwe akuphunzirazo, amapeza chimwemwe chachikulu pogwirizana ndi makolo awo m’kulambira koona. Ana oterowo akamakula, amakhala ndi zinthu zambiri zomwe amadzasangalala nazo m’tsogolo akamazikumbukira. Ena amasangalala akamakumbukira nthaŵi yoyamba yomwe anali ndi mbali m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. * Mwinanso amaganizira za nthaŵi yoyamba imene anatha kuŵerenga lemba la m’Baibulo mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba ali ndi kholo lawo. Kodi angaiŵale bwanji nthaŵi zimene makolo awo ankawaŵerengera Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo kapena buku la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo? * Gabriel anafotokoza motere zimene ankakonda: “Ndili ndi zaka zinayi zokha, amayi ankandiimbira nyimbo tsiku lililonse akamaphika. Ndikukumbukirabe bwinobwino nyimbo ina ya Ufumu imene inkandisangalatsa. Pambuyo pake, nyimbo imeneyo inandithandiza kuona kufunika kotumikira Yehova.” Mwinamwake inunso mukukumbukira nyimbo yabwinoyi yomwe Gabriel anali kunena. Nyimboyi ndi nambala 157 m’buku la nyimbo la Imbirani Yehova Zitamando, ndipo mutu wake ndi wakuti “Lambirani Yehova mu Unyamata.”

Nyimboyi imayamba motere: “Mkamwa mwa ana munatuluka;/​Mawu akutamandadi Yesu.” Zoonadi, panali ana amene anali ndi mwayi wokhala pamodzi ndi Yesu, ndipo mosakayikira iye anasangalala chifukwa cha khalidwe lawo losangalatsa ndiponso kuchita kwawo zinthu moona mtima. Moti Yesu anagwiritsa ntchito kuphunzitsika kwa ana aang’ono monga chitsanzo choti omutsatira ake atsanzire. (Mateyu 18:3, 4) Motero ana nawo ali ndi mbali yofunika pa kulambira Yehova. Ndipo mawu a nyimboyi amapitiriza kuti: “Inde, ana atamanda M’lungu.”

Mwa makhalidwe awo abwino, omwe amasonyeza kunyumba, kusukulu, ndiponso kumalo ena, ana ambiri adzetsa ulemu kwa Mulungu ndiponso ku mabanja awo. Ana otero n’ngodala kwambiri pokhala ndi “makolo okonda choonadi.” (Deuteronomo 6:7) Makolo oopa Mulungu amachita zomwe Mulunguyo amanena, yemwe pokhala Atate wachikondi, amaphunzitsa zolengedwa zake kuyenda m’njira yomwe ziyenera kuyendamo. Ndipotu amadalitsidwa kwambiri! Makolowo nawo akamaphunzitsa ana aang’ono m’banja mwawo, amasangalala kwambiri kukhala ndi ana amene amatsatira mawu akuti, ananu “mverani akondwere”! (Yesaya 48:17, 18) Angélica, yemwe panopa akutumikira pa ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico, anati: “Makolo anga ankayesetsa nthaŵi zonse kutsatira mfundo za m’Baibulo. Zimenezo zinapangitsa kuti ubwana wanga ukhale wabwino kwambiri. Ndinkasangalala.”

Akristu otereŵa amavomereza kuti kusamalira choloŵa chako chauzimu n’kofunikadi. Mwina ndinu wachinyamata ndipo mukukulira m’mbanja lotsatira mfundo zenizeni zachikristu. Ngati ndi choncho, nyimbo yomweyi ikukulimbikitsani inu monga Mkristu kuti: “Anyamata, khalani oyera.” Idzafika nthaŵi yoti mudzayamba kusankha nokha zochita, ndiye panopa “phunzirani kudalira M’lungu./​Peŵani mayanjano oipa,” musalimbane ndi kufuna kutchuka.

Ngati mutamadzinamiza n’kumaona kuti chinthu chofunika kwambiri m’moyo wanu ndicho kutchuka, zonse zomwe mwaphunzira zingakhale zopanda ntchito ndipo mungathe kuwononga tsogolo lanu. Chilakolako chofuna kutchuka chingakuchititseni kuti musiye kukhala tcheru. Izi zachititsa ena kuyenda ndi anthu amene ngakhale kuti n’ngooneka ngati abwino ndithu mwinanso amaonekedwe ndi makhalidwe ochititsa kaso, safuna kutsatira miyezo yachikristu. Chitsanzo cha zimenezi ndi cha Tara, amene nkhani yonse ya m’seŵero la pa vidiyo yofotokoza za achinyamata ya Young People Ask​—How Can I Make Real Friends? ikukamba za iye. Mofanana ndi Tara, Mkristu aliyense wachinyamata amene amayenda ndi anthu amene kulambira koona alibe nako ntchito m’kupita kwa nthaŵi adzaona kuti mayanjano oipa “aipitsa mkhalidwe wabwino” monga momwe nyimboyi imanenera. Pamatenga nthaŵi yaitali munthu ukuyesetsa kuti ukhale ndi makhalidwe abwino, koma makhalidwewo angathe kusokonezeka m’nthaŵi yochepa.

Ndi zoona kuti kukhala moyo woopa Mulungu sikophweka. Komabe monga momwe nyimboyi imapitirizira, “ngati ukumbuka M’lungu wako,/​kum’tumikira muchoonadi,” udzamanga maziko olimba okuthandiza kuti zinthu zidzakuyendere bwino. Ndipo “utakula udzasangalala.” Mudzayamba kuzindikira kwambiri kuti ndi chisamaliro chomwe Yehova amapereka mwachikondi, palibe chomwe chingakulepheretseni kuchita chinthu chomwe iye amafuna. Iyi ndiyo njira yokhalira munthu wachikulire woopa Mulungu. Kuwonjezera apo, kugwiritsa ntchito mwanzeru mwayi woleredwa m’banja lachikristu kumakupatsani mpata wa “kukondweretsa mtima wa Ya.” Kodi pali mwayi winanso waukulu woposa umenewu umene munthu angakhale nawo?​—Miyambo 27:11.

Chotero, achinyamata, kumbukirani nthaŵi zonse kuti maphunziro ochoka kwa Yehova ndiponso kwa makolo anu achikristu n’ngofunika kwambiri. Chikondi chawo chachikulu pa inu chikulimbikitseni kuchita zinthu zomwe Yehova amasangalala nazo. Mofanana ndi Yesu Kristu ndiponso Timoteo wachinyamata wokhulupirikayo, mudzasangalatsa Atate wanu wakumwamba ndiponso makolo anu. Ndipo ngati nanu mutadzakhala kholo, mosakayikira mudzavomerezana ndi Angélica tam’tchula uja, amene anati: “Ngati ndingadzakhale ndi mwana, ndidzayesetsa kum’phunzitsa kuti mtima wake uzikonda Yehova kungoyambira paukhanda wake, ndi kum’thandiza kuti azitsatira chikondi chimenecho m’moyo wake.” Kunena zoona, njira yowongoka yopita nayo kumoyo wosatha ndiyodi choloŵa chamtengo wapatali kwambiri pa zonse!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Ana ndiponso anthu akuluakulu amachita nawo maphunziro a Baibulo amenewa omwe amachitika m’mipingo ya Mboni za Yehova.

^ ndime 4 Mabuku omwe tatchulaŵa n’ngofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.