Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Kuphunzitsa ana anu?

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Kuphunzitsa ana anu?

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Kuphunzitsa ana anu?

NDIWO za kudimba zimathandiza m’njira zambiri. Koma munthu amafunika kudziŵa bwino malimidwe ake. Pali ndiwo zina zimene zimafunika kuti muyambe mwazifesa kaye pa nazale kenako n’kukaziwokera. Ndiyeno mukaziwokera zimafunika kuziphimbira kaye kuti zisapse ndi dzuŵa. Nthaŵi zina pamafunika kuzisamalira kwambiri. Pangafunike kuzithira mankhwala oziteteza ku matenda komanso tizilombo. Ndipo pali ndiwo zina zimene zimafunika kuthirira kaŵirikaŵiri. Munthu akalima ndiwozi amafunika kuti asamatalikire kudimbako. Motero, anthu ena amene akufuna kuchita ulimi wa ndiwo za kudimbazi nthaŵi zina amaona kuti ndi bwino kufunsira kaye malangizo kwa anthu odziŵa ntchitoyi.

Kulera ana n’kovuta kwambiri kuposa pamenepa ndipo amafunika kuwasamalira kwambiri. Motero makolo ambiri amaona kuti sangathe kulera ana bwino. Ambiri amaona kuti amafunika kuthandizidwa, mofanana ndi mlimi wa ndiwo za kudimba amene amafunika kulandira malangizo kuchokera kwa anthu odziŵa ntchitoyi. N’zodziŵikiratu kuti kholo lililonse limafuna kupeza malangizo abwino kwambiri. Kodi malangizo otero angapezeke kuti?

Ngakhale kuti Baibulo si buku la malamulo olelera ana, Mlengi anauzira anthu omwe analilemba kuti aikemo malangizo abwino kwambiri okhudza nkhaniyi. Baibulo limatsindika kuti m’pofunika kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino, zimene anthu ambiri amaona kuti zimanyalanyazidwa. (Aefeso 4:22-24) Pamfundoyi, malangizo a m’Malemba amafotokoza mbali yofunika kwambiri ya maphunziro okhudza mbali zonse zofunika m’moyo. Anthu ambiri amene agwiritsa ntchito malangizo ameneŵa apindula nawo kale, mosaganizira nthaŵi imene iwo anali ndi moyo ngakhalenso chikhalidwe chawo. Motero, kutsatira malangizo a m’Malemba kungakuthandizeni kuti muphunzitse ana anu bwinobwino.

Chitsanzo cha Makolo Ndicho Maphunziro Abwino Kwambiri

“Ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha?”​—Aroma 2:21, 22.

Wapampando wa bungwe la zamaphunziro la mu mzinda wa Seoul anati: “Chitsanzo chabwino m’mawu ndi m’zochita ndiwo maphunziro abwino kwambiri kwa ana.” Ngati makolo salankhula bwino komanso n’ngopanda mkhalidwe ndipo akupatsa ana awo malangizo pankhanizi, anawo sangachedwe kuganiza kuti makolowo n’ngachinyengo. Zonena za makolowo zingakhale zopanda ntchito. Mwachitsanzo, ngati makolo akufuna kuphunzitsa ana awo kuti azinena zoona, makolowo amayenera kunena zoona. Makolo ena akakhala kuti sakufuna kulandira mlendo, nthaŵi zambiri amauza ana awo kuti alendowo akabwera anene kuti, “Ababa (kapena amayi) kulibe.” Mwana amene wauzidwa zimenezi amavutika kunena kwake ndiponso zimam’sokoneza. M’kupita kwa nthaŵi, mwanayo angathe kuyamba kunama zinthu zikam’vuta ndipo sangachite nazo manyazi n’komwe. Motero, ngati makolo akufunadi kuti ana awo azilankhula zoona, makolowo ayenera kumalankhula zoona komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi zonena zawozo.

Kodi mukufuna kuphunzitsa mwana wanu kuti azilankhula mwaulemu? Ngati ndi choncho muyenera kukhala chitsanzo chabwino. Mwana wanu angathe kukutengereni mosavuta. Sung-sik, bambo wa ana anayi, anati: “Ine ndi mkazi wanga tinaganiza kuti tisamalankhule mawu onyoza. Tinkalemekezana ndipo sitinkakweza mawu ngakhale panthaŵi yoti takhumudwa kapena kukalipa. Chitsanzo chabwinochi chinathandiza kwambiri kusiyana ndi kumangowauza kuti azilankhula bwino. Timasangalala kuti ana athu amalankhula mwaulemu kwambiri.” Pa Agalatiya 6:7, Baibulo limati: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” Makolo amene akufuna kuti ana awo akhale akhalidwe labwino iwowo ndiwo ayenera kuyamba kusonyeza khalidwe lotero.

Muzilankhulana Momasuka Nthaŵi Zonse

[Malamulo a Mulungu] muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”​—Deuteronomo 6:7.

Kuwonjezera nthaŵi yogwira ntchito kukufala kwambiri. Ana zimawakhudza kwambiri ngati bambo ndi mayi ali pantchito. Nthaŵi yomwe makolo ambiri amacheza ndi ana awo ikucheperachepera. Makolowo akakhala kuti ali panyumba, amakhala akugwira ntchito zapakhomo ndi zinanso, motero amatopa kwambiri. Zinthu zikakhala choncho, kodi mungatani kuti mupitirizebe kulankhulana momasuka ndi ana anu? Mungapeze mpata wolankhulana nawo anawo ngati mumagwirira pamodzi ntchito zapakhomo. Bambo wina anakonza zoti banja lake lisakhalenso ndi TV, makamaka pofuna kukhala ndi nthaŵi yambiri yolankhulana ndi ana ake. Iye anati: “Poyamba anawo sanasangalale nazo, koma ndinkachita nawo maseŵera osiyanasiyana ndi kukambirana nawo nkhani za m’mabuku osangalatsa, kenako anayamba kuzoloŵera.”

Ndi zofunika kwambiri kuti ana azoloŵere kulankhulana ndi makolo awo adakali aang’ono. Kupanda kutero, anawo akasinkhuka ndipo mwina n’kukumana ndi mavuto, iwo sangaone makolo awo ngati mabwenzi awo omwe angawafotokozere mavutowo. Kodi mungawathandize motani kuti azifotokoza zakukhosi kwawo? Miyambo 20:5 imati: “Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.” Makolo angalimbikitse ana awo kufotokoza malingaliro awo, mwa kugwiritsa ntchito mafunso ochititsa munthu kufotokoza maganizo ake, monga lakuti “Ukuganiza bwanji?”

Kodi mungachite chiyani mwana wanu atalakwitsa chinthu chachikulu kwambiri? Iyi ndi nthaŵi yomwe mwana amafunika kum’komera mtima. Musakalipe pamene mukumvetsera zonena za mwanayo. Tate wina ananena izi pofotokoza zomwe amachita zinthu zikatero: “Ana akalakwa, ndimayesetsa kuti ndisakalipe kwambiri. Ndimakhala pansi ndi kumvetsera zomwe akufuna kunena. Ndimayesetsa kuti ndimvetse vutolo. Ndikaona kuti zikundivuta kuchepetsa ukali, ndimadikira kaye ndi kukhazika mtima m’malo.” Ngati simukalipa kwambiri ndipo mumawamvetsera, anawo sanganyinyirike kulandira chilango chomwe mwapereka.

Ana Amafunika Kuwalanga Mwachikondi

“Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”​—Aefeso 6:4.

Kuti ana apindule ndi chilango chanu, zimadalira mmene mumawalangira mwachikondi. Kodi makolo ‘angakwiyitse ana awo’ motani? Ngati chilango sichikuyenerana ndi kukula kwa cholakwa kapena ngati chikuperekedwa mwankhanza, ana sangagwirizane ndi chilango chotero. Nthaŵi zonse, chilango chiyenera kuperekedwa mwachikondi. (Miyambo 13:24) Mukamakambirana nawo anawo kuti aone chifukwa chomwe mukuwalangira, iwo amazindikira kuti mumawalanga chifukwa chakuti mumawakonda.​—Miyambo 22:15; 29:19.

Komanso, ndi bwino kuti ana aziona zotsatirapo zoŵaŵa za makhalidwe oipa. Mwachitsanzo, ngati mwana walakwira mnzake, mungam’limbikitse kuti apepese. Akaswa malamulo omwe banja limayendera, mungam’mane zinthu zina pofuna kumuonetsa kufunika kotsatira malamulo.

Ndi bwino kupereka chilango panthaŵi yoyenera. Mlaliki 8:11 amati: “Popeza sam’bwezera choipa chake posachedwa atam’tsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.” Mofanana ndi zimenezi ana ambiri angaganize zoti aone kuti angapulupudze mpaka pati asanalandire chilango. Motero, mukangom’chenjeza mwana kuti alandira chilango chifukwa cha cholakwa chinachake, onetsetsani kuti mwachitadi zimenezo.

Maseŵera Abwino N’ngofunika

[Pali] . . . mphindi yakuseka . . . ndi mphindi yakuvina.”​—Mlaliki 3:1, 4.

Kuti maganizo ndi thupi la mwana zikule m’pofunika kukhala ndi nthaŵi yopumula ndiponso kuchita maseŵera abwino. Makolo akamaseŵerera limodzi ndi ana awo, banja limakhala logwirizana kwambiri ndipo ana amaona kuti ndi otetezedwa. Kodi ndi maseŵera ati omwe banja lingachitire pamodzi? Mutati mukhale pansi ndi kulingalira mozama, mungapeze zinthu zambiri zosangalatsa zomwe mungachite. Pali maseŵera oseŵerera panja, monga kukwera njinga, ndiponso maseŵera a mpira, monga mpira wamiyendo, wamanja, ndiponso fulaye. Ndipo tangoganizani mmene banja lingasangalalire poimbira nyimbo limodzi! Mungasangalale kwambiri pokaona chilengedwe m’malo akufupi ndi kumene mukukhala, ndipo zimenezi zingakhale zosaiŵalika.

M’nthaŵi ngati zimenezo, makolo angathandize ana awo kuti aziona maseŵera m’njira yoyenerera. Mwamuna wina wachikristu amene ali ndi ana atatu anati: “Zikakhala zotheka ndimaseŵera nawo pamodzi ana anga. Mwachitsanzo, akamaseŵera maseŵera a pakompyuta, ndimawafunsa mmene amaseŵerera. Akamasangalala pondifotokozera, ndimagwiritsa ntchito mpata umenewo kuwauza za kuopsa kwa zosangalatsa zoipa. Ndaona kuti panopa amapeŵa zosangalatsa zoipa.” Inde, ana amene amasangalala ndi maseŵera omwe banja lonse limachitira pamodzi sakonda kwenikweni kuonera zinthu za pa TV, mavidiyo, ndi mafilimu zosonyeza ziwawa, zachiwerewere, ndiponso zogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, komanso sakonda maseŵera otero a pa Intaneti.

Thandizani Ana Anu Kupeza Mabwenzi Abwino

“Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.”​—Miyambo 13:20.

Tate wina wachikristu amene walera bwinobwino ana ake anayi anati: “N’zosachita kunena kuti m’pofunika kuti [ana] azisankha bwino mabwenzi awo. Bwenzi limodzi loipa lingasokoneze ntchito yonse yomwe munachita.” Pofuna kuthandiza ana ake kupeza mabwenzi abwino, tateyu ankafunsa anawo mochenjera mafunso monga: Kodi mnzako wapamtima ndani? N’chifukwa chiyani umam’konda? N’khalidwe lanji limene umakhumbira kwa iye? Kholo lina limakonza zoti ana ake aziitanira anzawo apamtima kunyumba kwawo. Akatero, limaonerera zochita zawo ndi kupatsa ana akewo malangizo oyenerera.

M’pofunikanso kuphunzitsa ana kuti azitha kugwirizana ndi anthu achikulire kuphatikiza pa anzawo ofanana nawo misinkhu. Bum-sun, tate wa ana aamuna atatu, anati: “Ndimathandiza ana anga kuzindikira kuti, monga momwe zinalili pakati pa Davide ndi Yonatani m’Baibulo, anzawo sachita kufunikira kukhala anthu ofanana nawo misinkhu. Ndimaitana Akristu amisinkhu yosiyanasiyana kuti adzacheze ndi ana anga. Izi zachititsa kuti anawo azicheza ndi anthu ambiri omwe si ofanana nawo misinkhu.” Kucheza ndi anthu akuluakulu achitsanzo chabwino kumapatsa anawo mwayi wophunzira zinthu zambiri.

Mungathe Kuphunzitsa Bwinobwino Ana Anu

Malinga ndi kafukufuku wina amene anachitika ku United States, makolo ambiri amene ankayesa kuphunzitsa ana awo makhalidwe monga kudziletsa, kukhala otha kusunga mwambo paokha, ndiponso kukhala onena zoona sizinawayendere bwino kwenikweni. N’chifukwa chiyani kunali kovuta kutero? Mayi wina amene anayankhapo pa kafukufukuyo anati: ‘Chomvetsa chisoni n’chakuti njira yokha yotetezera ana athu ndi yowatsekera m’nyumba, osawalola kutulukira kunja.’ Mayiyu ananena izi poganizira kuti dziko limene ana akukuliramo masiku ano ndi loipa poliyerekezera ndi kale. M’dziko lotereli, kodi n’zothekadi kulera mwana bwinobwino?

Mutakhala kuti mukufuna kulima ndiwo za kudimba koma mukuda nkhaŵa kuti mwina zifa, mungathe kugwa mphwayi. Koma mungasangalale kwambiri ngati mlangizi wa zaulimi atabwera ndi kukupatsani malangizo abwino, ndiyeno n’kunena mokutsimikizirani kuti, “Mukatsatira zimenezi, zinthu zonse ziyenda bwino.” Yehova, Wolamulira Wamkulu wa chibadwa cha anthu, amapereka malangizo abwino olerera ana. Iye amati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” (Miyambo 22:6) Mukaphunzitsa ana anu mogwirizana ndi malangizo a m’Baibulo, mosakayikira mudzasangalala kuwaona akusanduka anthu ochita zinthu mwauchikulire, oganizira ena, ndiponso amakhalidwe abwino. Ndiyeno, anthu adzawakonda koma koposa pamenepo Yehova, Atate wathu wakumwamba, adzawakondanso.