Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Gulu la Anabaptist? Linali Lotani?

Kodi Gulu la Anabaptist? Linali Lotani?

Kodi Gulu la Anabaptist? Linali Lotani?

PAFUPIFUPI munthu aliyense amene akukacheza koyamba mu mzinda wa Münster ku Westphalia, m’dziko la Germany, amachita chidwi ndi zitatanga zachitsulo zitatu zimene anazikoloŵeka pansanja ya tchalitchi china kumeneko. Zitatangazi zakhala pamenepa kwa zaka pafupifupi 500, kupatulapo nthaŵi zochepa chabe pamene zakhala zikutsitsidwapo. Poyambirira, m’zitatangamu munali mitembo ya amuna atatu amene anazunzidwa ndi kunyongedwa anthu akuona. Amunaŵa anali a gulu lachipembedzo chotchedwa Anabaptist, ndipo zitatangazi ndi zotsalira za ufumu wawo.

Kodi gulu la Anabaptist linali lotani? Kodi linayamba bwanji? Kodi ziphunzitso zawo zikuluzikulu zinali zotani? N’chifukwa chiyani amunawo ananyongedwa? Ndipo pali kugwirizana kwanji pakati pa zitatanga zitatu zija ndi ufumu winawake?

Zinthu Zinafunika Kusinthidwa M’tchalitchi, Koma Motani?

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1400 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1500, kudzudzula Tchalitchi cha Roma Katolika ndi atsogoleri ake kunakula kwambiri. Zinthu zambiri m’tchalitchichi zinaloŵa pansi komanso munali makhalidwe oipa; motero ambiri anaona kuti zinthu zinafunika kusintha kwambiri. Mu 1517, Martin Luther ananena poyera kuti zinthu ziyenera kusintha, ndipo anthu ena atayamba kuthandizira maganizo amenewo, mosakhalitsa Apulotesitanti anayamba kukonza zinthu m’tchalitchichi.

Koma aliyense wa anthu omwe ankafuna kuti zinthu zisinthewo anali ndi maganizo akeake pankhani ya zoyenera kuchita kapenanso kuti zinthuzo zisinthe mpaka pati. Ambiri ankaona kuti m’pofunika kutsatira kwambiri Baibulo pankhani ya kulambira. Komano, ofuna kuti zinthu zisinthewo ankatanthauzira Baibulo mosiyanasiyana. Ena ankaona kuti ntchito yosintha zinthuyo ikuchedwa kwambiri. Ndipo ndi ena mwa anthu ofuna kusintha zinthuŵa amene anayambitsa gulu lomwe linkati anthu azibatizidwa ali akuluakulu lotchedwa Anabaptist.

“Kwenikweni, sikuti panali gulu limodzi lokha limene linkalimbikitsa zobatiza anthu ali akuluakulu; analipo magulu angapo,” analemba motero Hans-Jürgen Goertz m’buku lake lakuti Die Täufer​—Geschichte und Deutung. Mwachitsanzo, m’chaka cha 1521 azibambo anayi omwe ankatchedwa kuti aneneri a ku Zwickau anagwedeza dziko chifukwa cholalikira ziphunzitso za gulu la Anabaptist ku Wittenberg. Ndipo mu 1525 ku Zurich, m’dziko la Switzerland, kunayambika gulu lina la Anabaptist. Nakonso ku Moravia, lomwe tsopano ndi dziko la Czech, ndi ku Netherlands kunayambika magulu ena a Anabaptist.

Kodi Ubatizo ndi Woyenerera Ana Kapena Akuluakulu?

Magulu ambiri a Anabaptist anali ang’onoang’ono, ndipo anthu ake anali okonda mtendere. Anthu ameneŵa sankabisa zikhulupiriro zawo; ndipotu ankalalikira kwa anthu ena. Zikhulupiriro zikuluzikulu za chipembedzo cha Anabaptist zinafotokozedwa m’chikalata chotchedwa Schleitheim Confession chomwe chinasainidwa mu 1527. Mwa zina, iwo ankakana ntchito zausilikali, sanafune kuloŵa ndale, ndipo ankachotsa mu mpingo anthu olakwa. Koma mfundo yaikulu kwambiri pachipembedzo chawo, imene inasiyanitsa chipembedzo cha Anabaptist ndi zipembedzo zina, inali chikhulupiriro chawo chakuti ubatizo ndi woyenera anthu akuluakulu osati ana. *

Nkhani yobatiza anthu akuluakulu sinali chabe chiphunzitso cha chipembedzo; inkakhudzanso mphamvu za gulu la chipembedzocho. Ngati munthu wachedwa kubatizidwa mpaka kukula, motero n’kukhala ndi mpata wosankha zochita malinga ndi chikhulupiriro chake, mwina sangabatizidwe n’komwe. Tchalitchi sichikhala ndi mphamvu kwenikweni pa anthu osabatizidwa. Kwa matchalitchi ena, kubatiza anthu akuluakulu kukanachititsa kuti achepe mphamvu.

Motero, Akatolika limodzi ndi a tchalitchi cha Lutheran ankafuna kuletsa mchitidwe wobatiza anthu akuluakulu. Chaka cha 1529 chitatha, m’madera ena, nthaŵi zambiri anthu amene ankabatiza anthu akuluakulu kapena amene ankabatizidwa atakula anali kulandira chilango cha imfa. Mtolankhani wina dzina lake Thomas Seifert anafotokoza kuti anthu a gulu la Anabaptist “ankazunzidwa koopsa m’madera onse a Ufumu Wopatulika wa Aroma wa dziko la Germany.” Ku Münster n’kumene chizunzo chinanyanya kwambiri.

Anthu a Mumzinda wa Münster Wakale Afuna Kuti Zinthu Zisinthe

Mzinda wa Münster wakale unali ndi anthu pafupifupi 10,000 ndipo unazunguliridwa ndi zinthu zosiyanasiyana zothandiza pachitetezo zomwe zinkaoneka kuti adani sangathe kuzidutsa kuti aloŵe mu mzindawu. Kuti munthu afike m’kati mwa mzindawu kuchokera poyambira zinthu zothandiza pachitetezozi panali mamita pafupifupi 90 ndipo zinazungulira mzindawu kwa makilomita pafupifupi asanu. Koma mu mzinda wotetezedwa moterewu munalibe bata m’pang’ono pomwe. Buku lakuti The Kingdom of the Anabaptists, lofalitsidwa ndi bungwe loyang’anira nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi mu mzinda wa Münster, limafotokoza za “mikangano yandale yochitika mu mzindawo pakati pa bungwe la opanga malamulo ndi mabungwe a zamalonda ndi zaumisiri.” Komanso, anthu a mumzindawu sankakondwa ndi khalidwe la atsogoleri achipembedzo. Zinthu zinasintha mu mzinda wa Münster mu 1533, kuchoka pokhala mzinda wachikatolika n’kufika pokhala mzinda wa a Lutheran.

Mmodzi mwa anthu omwe ankalimbikitsa kwambiri kuti zinthu zisinthe ku Münster anali Bernhard Rothmann, amene ankachita zinthu mopupuluma kwambiri. Wolemba mabuku wina, dzina lake Friedrich Oehninger, anafotokoza kuti “maganizo a [Rothmann] anali oonekeratu kuti ndi wa Anabaptist; iye ndi anzake ena ankakana kubatiza makanda.” Ku Münster anthu ambiri anagwirizana ndi maganizo ake, ngakhale kuti anthu ena ankaona kuti ananyanya nawo maganizo ake ofuna kuti zinthu zisinthe msangamsangawo. “Anthu ambiri amene ankasangalala ndi mmene zinthu zinalili poyamba anachoka mumzindawo chifukwa chokhumudwa ndiponso pochita mantha. Khwimbi la a Anabaptist linakhamukira ku Münster kuchoka kumadera osiyanasiyana, poganiza kuti zolinga zawo zikakwaniritsidwa kumeneko.” Kudzadzana kwa a Anabaptist kotereku mu mzinda wa Münster kunadzetsa vuto lalikulu.

Yerusalemu Watsopano Azingidwa

M’kupita kwa nthaŵi, amuna aŵiri omwe anasamukira ku Münster kuchoka ku Netherlands, mayina awo ndi Jan Mathys wa ku Haarlem, yemwe ntchito yake inali yophika buledi, ndi Jan Beuckelson, yemwe ankadziŵika ndi dzina loti John wa ku Leiden, anachita zinthu zikuluzikulu mumzindawo. Mathys ankadzitcha mneneri ndipo analengeza kuti mwezi wa April chaka cha 1534 ndi nthaŵi ya kubweranso kwachiŵiri kwa Kristu. Mzinda wa Münster anautcha kuti Yerusalemu Watsopano wotchulidwa m’Baibulo, ndipo anthu onse ankachita zinthu ngati kuti nthaŵi yachimaliziro yakwana. Rothmann anakonza zoti munthu aliyense azigwiritsa ntchito katundu wina aliyense wa mu mzindawo ngati kuti ndi wakewake. Nzika zachikulire mu mzindawo zinafunika kusankha pakati pa kubatizidwa kapena kutuluka mu mzindawo. Kunabatizidwa khwimbi la anthu omwe ena mwa iwo ankangofuna kuti asasiye nyumba ndiponso katundu wawo.

Anthu a m’mizinda ina anadabwa kwambiri pamene Münster anakhala mzinda woyamba umene a Anabaptist anakhala ndi mphamvu kwambiri pankhani zachipembedzo ndi zandale. Malinga ndi buku lakuti Die Täufer zu Münster, izi zinachititsa kuti “dziko lonse la Ufumu Wopatulika wa Aroma wa dziko la Germany lidane ndi Münster.” Mkulu wina wotchuka m’deralo, yemwe anali kalonga komanso bishopu, Bwana Franz von Waldeck, anasonkhanitsa asilikali kuti azinge mzinda wa Münster. M’gulu la asilikali limeneli munali a Lutheran ndi Akatolika. Apa zipembedzo ziŵirizi zinagwirizana kuti zimenyane ndi a Anabaptist, ngakhale kuti m’mbuyomo sizinagwirizane pankhani yosintha zinthu m’tchalitchi cha Katolika, ndiponso pasanapite nthaŵi yaitali zinamenyana pa nkhondo ina ya zaka makumi atatu.

Kuwonongedwa kwa Ufumu wa Anabaptist

Anthu okhala m’kati mwa mzinda wotetezedwa bwinowo sanachite mantha kuti asilikali owazingawo anali amphamvu. Mu April 1534, pamene ankayembekezera kubweranso kwa Kristu, Mathys anayenda pa kavalo woyera kutuluka mumzindawo, ndipo anali ndi chiyembekezo choti Mulungu am’teteza. Taganizirani mmene anadzidzimukira anthu otsatira Mathys pamene anali kusuzumira pamwamba pa makoma a mzindawo ndi kuona asilikali owazinga aja akudula Mathys nthulinthuli n’kupachika mutu wake pamtengo!

John wa ku Leiden analoŵa m’malo mwa Mathys ndipo anapatsidwa dzina lakuti Mfumu Jan ya Anabaptist ku Münster. Popeza kuti mu mzindawo munali akazi ambiri kuposa amuna, iye anayesa kuthetsa vutoli mwa kulimbikitsa amuna kukwatira akazi ochuluka mmene munthu angafunire. Chinthu chosonyeza kuti mu ufumu wa Anabaptist ku Münster ankakhwimitsa kapena kulekerera kwambiri zinthu chinali chakuti, munthu akachita chigololo kapena dama chilango chake chinali imfa, komanso anthu ankaloledwa kuchita mitala, mwinanso ankawalimbikitsa kumene kuti achite mitala. Mfumu Jan mwiniyo anakwatira akazi 16. Mmodzi wa akazi akewo, Elisabeth Wandscherer, atapempha chilolezo chake kuti atuluke mu mzindawo, anadulidwa mutu anthu akuona.

Mzindawu unazingidwa kwa chaka ndi miyezi iŵiri, mpaka mu June 1535 pamene mzindawu unalandidwa. Nthaŵiyi, mzinda wa Münster unawonongedwa kwambiri, ndipo sunawonongedweponso moteromo mpaka pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse. Rothmann anathaŵa, koma Mfumu Jan ndi atsogoleri ena aŵiri a Anabaptist anagwidwa ndi kuzunzidwa ndipo kenako ananyongedwa. Mitembo yawo anaiika m’zitatanga ndi kukazikoloŵeka pa nsanja ya Tchalitchi cha St. Lambert’s. Cholinga chinali choti “likhale chenjezo lamphamvu kwa anthu omwe angafune kuyambitsa chisokonezo,” anatero Seifert. Inde, kuloŵerera m’ndale kunadzetsa mavuto aakulu.

Kodi magulu ena a Anabaptist zinawayendera bwanji? Mu Ulaya, anthu a Anabaptist anapitirizabe kuzunzidwa kwa zaka zingapo zotsatira. Anthu achipembedzo cha Anabaptist anapitirizabe kutsatira mfundo zawo zosagwira nawo ntchito zausilikali, ngakhale kuti panali a Anabaptist ena ochepa omwe ankakonda zankhondo. Patapita nthaŵi, Menno Simons, amene kale anali wansembe, anakhala mtsogoleri wa a Anabaptist, ndipo kenako gululi linayamba kudziŵika ndi dzina loti Amenonite kapena ndi mayina ena.

Zitatanga Zitatu

Kwenikweni a Anabaptist anali anthu achipembedzo amene ankayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. Koma anthu amene ankafuna kusintha zinthu mopitirira muyeso a ku Münster anachititsa kuti a Anabaptist asinthe ndi kuyamba kuloŵerera m’ndale. Atangotero, gululi linasintha n’kuyamba kulimbana ndi zandale. Izi zinadzetsa mavuto aakulu kwambiri kwa a Anabaptist ndiponso ku mzinda wa Münster wakale.

Alendo okacheza mu mzindawu amakumbutsidwa zinthu zoopsa zimenezi, zomwe zinachitika zaka pafupifupi 500 zapitazo. Kodi amakumbutsidwa motani? Amakumbutsidwa ndi zitatanga zitatu zachitsulo zomwe zinakoloŵekedwa pa nsanja ya tchalitchi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Nkhaniyi sikufotokoza mfundo zovomereza kapena zotsutsa ubatizo wa ana. Kuti mumve mfundo zokhudzana ndi ubatizo wa ana, onani nkhani yakuti “Kodi Makanda Ayenera Kubatizidwa?” mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya March 15, 1986.

[Zithunzi patsamba 13]

Mfumu Jan anazunzidwa, kunyongedwa, ndi kupachikidwa pa nsanja ya Tchalitchi cha St. Lambert’s