Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali

Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali

Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali

“Mwazi wa Kristu . . . udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo.”​—AHEBRI 9:14.

1. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti timaona moyo kuti ndi wamtengo wapatali?

MUTAUZIDWA kuti mutchule mtengo wa moyo wanu, kodi mungati ndi wa ndalama zingati? Timaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali, kaya ukhale wathu kapena wa anthu ena. Umboni wa zimenezi ndi wakuti, timapita ku chipatala kuti tikalandire chithandizo tikadwala kapena kuti tikapimidwe pofuna kudziŵa mmene thupi lathu lilili. Timafuna kukhala ndi moyo komanso thanzi labwino. Ngakhalenso ambiri amene tili okalamba kapena olemala sitifuna kufa; timafuna kukhala ndi moyo.

2, 3. (a) Kodi lemba la Miyambo 23:22 limatisonyeza udindo wotani? (b) Kodi udindo wotchulidwa pa Miyambo 23:22 umam’khudza motani Mulungu?

2 Ubwenzi wanu ndi anthu ena umakhudzidwa ndi mmene mumaonera moyo. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako atakalamba.” (Miyambo 23:22) ‘Kumvera’ sikutanthauza kungomva mawu chabe; mwambiwu umatanthauza kumva ndi kutsatira zomwe zanenedwazo. (Eksodo 15:26; Deuteronomo 7:12; 13:18; 15:5; Yoswa 22:2; Salmo 81:13) Kodi Mawu a Mulungu amapereka chifukwa chotani chomvera atate ndi amayi anu? Sikuti ndi chifukwa chokha chakuti iwo ndi aakulu kuposa inu kapenanso chifukwa chakuti aona zambiri m’moyo. Chifukwa chimene Mawu a Mulunguwo akupereka n’chakuti iwo ‘anakubalani.’ Mabaibulo ena, pa vesili amati: “Tamvera atate wako amene anakupatsa moyo.” M’pake kuti ngati mumaona moyo kukhala wamtengo wapatali, mumaona kuti muyenera kumuchitira zinazake amene anakupatsani moyowo.

3 Zoonadi, ngati ndinu Mkristu woona, mumaona kuti Gwero lake lenileni la moyo wanu ndi Yehova. Chifukwa cha iyeyo inu ‘muli ndi moyo;’ mumatha “kuyendayenda,” kuchita zinthu monga wozindikira; ndipo mungathe “kupeza mkhalidwe,” kapena kuti kukhalapo ndi moyo ndi kuganizira kapena kukonza za tsogolo lanu, kuphatikizapo moyo wopanda malire. (Machitidwe 17:28; Salmo 36:9; Mlaliki 3:11) Mogwirizana ndi Miyambo 23:22, m’poyenera ‘kumvera’ Mulungu ndi kutsatira zomwe akunena. Muyenera kukhala wofunitsitsa kudziŵa mmene iye amaonera moyo ndi kutsatira maganizo akewo m’malo motsatira mmene anthu ena amauonera.

Lemekezani Moyo

4. Chakumayambiriro kwa mbiri ya anthu, kodi nkhani ya kulemekeza moyo inakhala yofunika motani ?

4 Kale kwambiri m’mbiri ya anthu, Yehova anasonyeza momveka bwino kuti safuna kuti moyo anthu azingochita nawo chilichonse chomwe akufuna (chabwino kapena choipa). Chifukwa chokwiya ndiponso chifukwa cha nsanje, Kaini anadula moyo wa mbale wake wosalakwa, Abele. Kodi mukuganiza kuti Kaini anali ndi ufulu wochita nawo zimenezo moyo? Mulungu sanaganize choncho. Anauza Kaini kuti afotokoze chifukwa chomwe anachitira zimenezo. Mulungu anati: “Wachita chiyani? Mawu a mwazi wa mphwako andifuulira ine kunthaka.” (Genesis 4:10) Onani kuti mwazi wa Abele womwe unali kunthaka unaimira moyo wake, womwe anaudula mwankhanza, ndipo unali kufuulira Mulungu kuti abwezere.​—Ahebri 12:24.

5. (a) Kodi Mulungu analetsa chiyani m’masiku a Nowa, ndipo lamulo lakelo linakhudza ndani? (b) Kodi lamulo limeneli linali lofunika kwambiri m’njira yotani?

5 Chigumula chitapita, mtundu wa anthu unayambiranso ndi anthu asanu ndi atatu okha. M’mawu ake okhudza anthu onse, Mulungu anavumbula mfundo zinanso zosonyeza mmene iye amaonera moyo ndi magazi. Iye ananena kuti anthu angathe kudya nyama, koma anaika lamulo ili: “Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama, mmene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.” (Genesis 9:3, 4) Ayuda ena amati mawu ameneŵa amatanthauza kuti anthu sankayenera kudya nyama kapena magazi a nyama yomwe idakali ndi moyo. Koma pambuyo pake zinaoneka kuti Mulungu anali kuletsa kudya magazi ngati chakudya. Kuwonjezera pamenepo, lamulo limene Mulungu anapereka kudzera mwa Nowa linali lofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga Chake chapamwamba chokhudza magazi. Cholinga chimenechi n’chimene chinadzathandiza anthu kupeza moyo wosatha.

6. Kudzera mwa Nowa, kodi Mulungu anagogomezera motani kuti amaona moyo kukhala wamtengo wapatali?

6 Mulungu anapitiriza kuti: “Mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu. Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu Iye anam’panga munthu.” (Genesis 9:5, 6) Mungathe kuona pa lamulo limeneli, lomwe linaperekedwa kwa anthu onse, kuti Mulungu amaona kuti magazi a munthu amaimira moyo wa munthuyo. Mlengi amapatsa munthu moyo, ndipo aliyense sayenera kuchotsa moyo umenewo, womwe umaimiridwa ndi magazi. Ngati wina wapha munthu, monga mmene Kaini anachitira, Mlengi ali ndi ufulu ‘wofunanso’ moyo wa wopha mnzakeyo.

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi ndi lamulo lomwe Mulungu anapereka kwa Nowa pankhani ya magazi?

7 Mwa zimene ananenazi, Mulungu anali kulamula anthu kuti asamagwiritse ntchito magazi molakwa. Kodi munaganizapo kuti n’chifukwa chiyani? Inde, kodi n’chiyani chinachititsa Mulungu kuti aziona magazi motero? Kwenikweni, yankho lake likukhudza mfundo imodzi pa mfundo zofunika kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. Mfundo imeneyi ndiyo maziko a uthenga wachikristu, ngakhale kuti matchalitchi ambiri amasankha kunyalanyaza mfundo imeneyi. Kodi mfundo imeneyo ndi yotani, ndipo kodi moyo, zoganiza, komanso zochita zanu zikukhudzidwa motani ndi mfundoyi?

Kodi Magazi Anayenera Kugwiritsidwa Ntchito Motani?

8. M’Chilamulo, kodi Yehova ananena kuti magazi azigwiritsidwa ntchito motani?

8 Yehova anafotokoza mfundo zinanso pankhani ya moyo ndi magazi pamene anapatsa Aisrayeli mpambo wa Malamulo. Ndi zimenezi, iye anachitanso chinthu chofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga chake. Mwinamwake inu mukudziŵa kuti Chilamulo chinafuna kuti anthu azipereka nsembe kwa Mulungu, monga ufa, mafuta, ndi vinyo. (Levitiko 2:1-4; 23:13; Numeri 15:1-5) Panalinso nsembe za nyama. Ponena za nsembe za nyamazi, Mulungu anati: “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu.” Yehova ananenanso kuti ngati munthu, monga mlenje kapena mlimi, wapha nyama kuti adye, anayenera kukhetsa magazi ake ndi kuwafotsera ndi dothi. Dziko lapansi ndi choikapo mapazi a Mulungu, ndipo mwa kuthira magazi pansi, munthuyo anali kuvomereza kuti moyo uyenera kubwezeredwa kwa Wopatsa Moyo.​—Levitiko 17:11-13; Yesaya 66:1.

9. Kodi Chilamulo chinasonyeza kuti ntchito imodzi yokha ya magazi inali yotani, ndipo cholinga chake chinali chiyani?

9 Lamulo limeneli sikuti linali mwambo wachipembedzo chabe wopanda tanthauzo lililonse kwa ife. Kodi mwaona chifukwa chake Aisrayeli sanayenera kudya magazi? Mulungu anati: “Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu.” Kodi chifukwa chake chinali chiyani? “Ndakupatsani [mwazi] pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu.” Kodi mukuona kuti zimenezi zikutisonyeza chifukwa chake Mulungu anauza Nowa kuti anthu asamadye magazi? Mlengi anasankha kuti magazi aziwaona kuti n’chinthu chofunika kwambiri, anafuna kuti magazi agwire ntchito yapadera yotha kupulumutsa miyoyo yambiri. Magazi anadzagwira ntchito yofunika kwambiri pophimba machimo (chotetezera). Motero, m’Chilamulo, ntchito imodzi yokha ya magazi yomwe Mulungu anaivomereza inali ya pa guwa lansembe potetezera miyoyo ya Aisrayeli, omwe anali kufuna kuti Yehova awakhululukire.

10. N’chifukwa chiyani magazi a nyama sakanathandiza anthu kuti akhululukidwe machimo onse, koma kodi nsembe zomwe zinkaperekedwa m’Chilamulo zinali kuwakumbutsa chiyani anthu?

10 Mfundo imeneyi, yogwiritsa ntchito magazi monga chotetezera, ikugwiranso ntchito m’Chikristu. Pofotokoza mbali ya Chilamulo imeneyi, imene inakonzedwa ndi Mulungu, mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: “Monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang’ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi kulibe kumasuka.” (Ahebri 9:22) Paulo anafotokoza momveka bwino kuti nsembe zomwe zinkafunikazo sizinachititse Aisrayeli kukhala angwiro, anthu opanda uchimo. Analemba kuti: “Mu [nsembezi] muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka. Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.” (Ahebri 10:1-4) Komabe, nsembe zoterozo zinathandiza kwambiri. Zinali kukumbutsa Aisrayeliwo kuti anali ochimwa ndipo anafunikira chinthu chinanso chowonjezera kuti akhululukidwe machimo awo onse. Komano ngati sikukanatheka kuti mwazi umene unali kuimira miyoyo ya nyama uphimbe bwinobwino machimo onse a anthu, kodi mwazi wina uliwonse ukanatha kuchita zimenezo?

Zomwe Wopatsa Moyo Anakonza

11. Kodi timadziŵa bwanji kuti nsembe za mwazi wa nyama zinali kuimira chinthu china?

11 Kwenikweni Chilamulo chinali kulozera anthu chinthu chodzakwaniritsa bwino kwambiri cholinga cha Mulungu. Paulo anafunsa kuti: “Nanga chilamulo tsono?” Anayankha funsoli kuti: “Chinawonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe [Mose].” (Agalatiya 3:19) Mogwirizana ndi mfundoyi, Paulo analemba kuti: “Chilamulo, [chili ndi] mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo.”​—Ahebri 10:1.

12. Ponena za magazi, kodi tikuona motani cholinga cha Mulungu chikuvumbulidwa pang’onopang’ono?

12 Mwachidule, m’nkhaniyi taona kuti m’masiku a Nowa, Mulungu analamula kuti anthu angadye nyama ngati chakudya, koma sanayenera kudya magazi. Panthaŵi ina, Mulungu anati “moyo wa nyama ukhala m’mwazi.” Zoonadi, iye anasankha kuona kuti magazi ndi chinthu choimira moyo ndipo anati: “Ndakupatsani [mwazi] pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu.” Komabe, m’kupita kwa nthaŵi cholinga cha Mulungu chinadzafotokozedwa momveka bwino. Chilamulo chinali mthunzi wa zokoma zomwe zinali m’tsogolo. Kodi zinali zinthu zotani?

13. N’chifukwa chiyani kufa kwa Yesu kunali kofunika?

13 Zinthu zenizeni zimenezi zinagona pa imfa ya Yesu Kristu. Mukudziŵa inu kuti Yesu anazunzidwa ndi kupachikidwa. Anafa ngati chigaŵenga. Paulo analemba kuti: “Pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Kristu anawafera osapembedza. . . . Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.” (Aroma 5:6, 8) Mwa kutifera, Kristu anapereka dipo lophimba machimo athu. Dipo limenelo ndiyo mfundo yaikulu ya uthenga wachikristu. (Mateyu 20:28; Yohane 3:16; 1 Akorinto 15:3; 1 Timoteo 2:6) Kodi zimenezi zikukhudza motani mwazi ndi moyo, ndipo kodi moyo wanu ukukhudzidwa motani?

14, 15. (a) Kodi mabaibulo ena amagogomezera motani imfa ya Yesu pa Aefeso 1:7? (b) Ndi mfundo yotani ya pa Aefeso 1:7 yomwe ingaphonyedwe?

14 Matchalitchi ena amagogomezera kwambiri imfa ya Yesu, ndipo anthu a m’matchalitchi amenewo amanena mawu akuti “Yesu anandifera.” Taganizirani zimene mabaibulo ena amanena pa Aefeso 1:7: “Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulugu anatipulumutsa, ndipo anakhululukira zolakwa zathu.” (Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) “Ndi imfa ya Kristu tinamasulidwa, ndipo machimo athu anakhululukidwa.” (Today’s English Version, 1966) “Tinamasulidwa kudzera mwa Kristu ndi nsembe ya moyo wake, kumasulidwa kumene kumatanthauza kukhululukidwa machimo.” (The New Testament, la William Barclay, 1969) “Kuli kudzera mu imfa ya Kristu kuti machimo athu amakhululukidwa ndipo timamasulidwa.” (The Translator’s New Testament, 1973) Mungathe kuona kuti mabaibulo ameneŵa amagogomezera kwambiri imfa ya Yesu. Ena anganene kuti, ‘Komatu imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Motero n’chiyani chikusoŵeka m’mabaibulo ameneŵa?’

15 Kunena zoona, mutati muzingodalira mabaibulo otero, mukhoza kuphonya mfundo ina yofunika kwambiri, ndipo zimenezo zingakulepheretseni kumvetsa bwino uthenga wa m’Baibulo. Mabaibulo ameneŵa amabisa mfundo yakuti m’malemba oyambirira, lemba la Aefeso 1:7 lili ndi mawu achigiriki omwe amatanthauza kuti “mwazi.” Motero, zimene mabaibulo ambiri, monga Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu, amanena pa vesili zimagwirizana ndi zimene zili m’malemba oyambirirawo, zakuti: ‘Tili ndi mawomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake.’

16. Kodi mawu akuti “mwa mwazi wake” ayenera kutikumbutsa zotani?

16 Mawu akuti “mwa mwazi wake” ali ndi tanthauzo lapadera ndipo ayenera kutikumbutsa zinthu zambiri. Imfa payokha, ngakhale imfa ya Yesu, yemwe anali munthu wangwiro, sinali yokwanira. Iye anakwaniritsa zimene Chilamulo chinali kuchitira mthunzi, makamaka pa Tsiku la Chitetezero. Patsiku lapadera limeneli, pankaperekedwa nsembe za nyama zimene Chilamulo chinkafuna. Kenako wansembe ankatenga magazi ena a nyamazo n’kupita nawo m’Malo Opatulikitsa m’chihema kapena m’kachisi. M’Malo Opatulikitsawo iye ankapereka magaziwo kwa Mulungu, ngati kuti waima pamaso pa Mulunguyo.​—Eksodo 25:22; Levitiko 16:2-19.

17. Kodi Yesu anakwaniritsa motani zinthu zomwe zinkaimiridwa ndi Tsiku la Chitetezero?

17 Malinga ndi mmene Paulo anafotokozera,Yesu anakwaniritsa zinthu zomwe zinkaimiridwa ndi zochitika za pa Tsiku la Chitetezero. Poyamba iye anatchula kuti mkulu wa ansembe ku Israyeli ankaloŵa kamodzi pachaka m’Malo Opatulikitsa atatenga mwazi umene ankapereka “chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu.” (Ahebri 9:6, 7) Mofanana ndi zochitika patsikuli, Yesu ataukitsidwa monga mzimu, anapita kumwamba. Poti anali mzimu motero sanali ndi thupi la nyama ndi mwazi, iye anatha kukaonekera “pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.” Kodi anapereka chiyani kwa Mulungu? Sanapereke chinthu chooneka ndi maso koma anapereka chinthu chofunika kwambiri. Paulo anapitiriza kufotokoza motere: “Atafika Kristu, Mkulu wa Ansembe . . . [osati ndi] mwazi wa mbuzi ndi ana a ng’ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analoŵa kamodzi ku malo opatulika, atalandirapo chiwombolo chosatha. Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo . . . upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi; koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda chirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?” Inde, Yesu anapereka kwa Mulungu mtengo wa mwazi wake.​—Ahebri 9:11-14, 24, 28; 10:11-14; 1 Petro 3:18.

18. Kodi n’chifukwa chiyani mfundo za m’Baibulo zokhudza magazi ziyenera kukhala zofunika kwa Akristu masiku ano?

18 Choonadi chochoka kwa Mulungu chimenechi chikutithandiza kumvetsa mfundo zochititsa chidwi zimene Baibulo limanena zokhudza magazi; mfundo monga chifukwa chimene Mulungu amaonera magazi motero, mmene ifeyo tiyenera kuwaonera, ndi chifukwa chake timafunika kumvera malamulo a Mulungu okhudza ntchito ya magazi. Mukamaŵerenga mabuku a Malemba Achigiriki Achikristu, mumaona malo ambiri otchula za mwazi wa Kristu. (Onani bokosi.) Malembaŵa amasonyezeratu kuti Mkristu aliyense ayenera kukhulupirira ‘mwazi [wa Yesu].’ (Aroma 3:25) N’zotheka kukhululukidwa machimo ndi kukhala pamtendere ndi Mulungu kokha ‘mwa mwazi’ umene Yesu anakhetsa. (Akolose 1:20) Umu ndi mmene zimakhaliradi kwa anthu amene Yesu anapangana nawo pangano lapadera lokalamulira naye kumwamba. (Luka 22:20, 28-30; 1 Akorinto 11:25; Ahebri 13:20) Zimakhalanso choncho kwa a “khamu lalikulu” masiku ano amene adzapulumuke ‘chisautso chachikulu’ ndi kukhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi pano. Mophiphiritsa, anthu ameneŵa ‘amatsuka zovala zawo m’mwazi wa Mwanawankhosa.’​—Chivumbulutso 7:9, 14.

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu anasankha kuti anthu asagwiritse ntchito magazi mwachisawawa, ndipo tiyenera kumva motani ndi zimenezi? (b) Kodi tiyenera kukhala ofunitsitsa kudziŵa chiyani?

19 N’zoonekeratu kuti magazi ali ndi tanthauzo lapadera kwa Mulungu. Amafunikanso kukhala otero kwa ife. Mlengi amene amaona kuti moyo ndi wofunika ali ndi ufulu woika malire a mmene anthu angagwiritsire ntchito magazi. Chifukwa choganizira kwambiri ngakhale moyo wathuwu, iye anakonza zopatula magazi kuti azigwiritsidwa ntchito m’njira imodzi yokha yofunika kwambiri, yomwe ikuchititsa kuti anthu adzathe kupeza moyo wosatha. Njira imeneyo inali yogwiritsira ntchito mwazi wamtengo wapatali wa Yesu. Tiyeneratu kukhala oyamikira kwambiri kuti Yehova Mulungu anachita zinthu zotipindulitsa mwa kugwiritsa ntchito mwazi, mwazi wa Yesu, m’njira yopulumutsa moyo! Ndipo tiyenera kumuyamikira kwambiri Yesu chifukwa chopereka mwazi wake monga nsembe yathu! Zoonadi, tingamvetse zimene mtumwi Yohane anafotokoza, kuti: “Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula ku machimo athu ndi mwazi wake; natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthaŵi za nthaŵi. Amen.”​—Chivumbulutso 1:5, 6.

20 Mulungu wathu wanzeru kwambiri ndiponso Wopatsa Moyo anayamba kale kwambiri kuganizira za ntchito yopulumutsa moyo imeneyi. Ndiye, tingafunse kuti, ‘Kodi zimenezi ziyenera kukhudza motani zimene timasankha ndiponso zimene timachita?’ Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi kuchokera pa nkhani ya Abele ndi ya Nowa tingaphunzire zinthu zotani zokhudza mmene Mulungu amaonera magazi?

• M’Chilamulo, kodi Mulungu anati magazi azigwiritsidwa ntchito m’njira yotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

• Kodi Yesu anakwaniritsa motani zinthu zimene zinkaimiridwa ndi Tsiku la Chitetezero?

• Kodi mwazi wa Yesu ungapulumutse moyo wathu motani?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 18]

KODI NDI MAGAZI A NDANI AMENE AMAPULUMUTSA MOYO?

“Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira, kuti muŵete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi [wa Mwana] wa iye yekha.”​—Machitidwe 20:28.

“Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa iyeyo.”​—Aroma 5:9.

“Munali . . . opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m’dziko lapansi. Koma tsopano mwa Yesu Kristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m’mwazi wa Kristu.”​—Aefeso 2:12, 13.

“Kunam’komera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire, mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake.”​—Akolose 1:19, 20.

‘Ndipo tikhala nacho, abale, chilimbikitso chakuloŵa m’malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu.’​—Ahebri 10:19.

“Simunawomboledwa ndi zovunda, . . . kusiyana nawo makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwana wa nkhosa wopanda chirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu.”​—1 Petro 1:18, 19.

“Ngati tiyenda m’kuunika, monga Iye ali m’kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.”​—1 Yohane 1:7.

“Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse.”​—Chivumbulutso 5:9.

“Wagwetsedwa wonenera wa abale athu . . . Ndipo iwo anam’laka iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mawu a umboni wawo.”​—Chivumbulutso 12:10, 11.

[Chithunzi patsamba 16]

Kudzera m’Chilamulo, Mulungu anamveketsa bwino kuti magazi adzagwiritsidwa ntchito pa kukhululukira machimo

[Chithunzi patsamba 17]

Kudzera m’mwazi wa Yesu, miyoyo yambiri ingapulumutsidwe