Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Aphunzitseni Kusunga Zinthu Zonse Zimene Ndinakulamulirani’

‘Aphunzitseni Kusunga Zinthu Zonse Zimene Ndinakulamulirani’

‘Aphunzitseni Kusunga Zinthu Zonse Zimene Ndinakulamulirani’

“Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”​—MATEYU 28:19, 20.

1. Kodi wophunzira Filipo anakambirana zotani ndi munthu wa ku Aitiopiya?

MUNTHU wa ku Aitiopiya anayenda ulendo wokafika ku Yerusalemu. Kumeneko analambira Mulungu yemwe anali kumukonda, Yehova. N’zachionekere kuti iye analinso kukonda Mawu ouziridwa a Mulungu. Akubwerera kwawo m’galeta lake, anali kuŵerenga zimene analemba mneneri Yesaya pamene anakumana ndi Filipo, wophunzira wa Kristu. Filipo anafunsa munthu wa ku Aitiopiyayo kuti: “Kodi muzindikira chimene muŵerenga?” Munthuyo anayankha kuti: “Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine?” Filipo anayamba kuthandiza wophunzira Malemba wofunitsitsa ameneyu kuti akhale wophunzira wa Kristu.​—Machitidwe 8:26-39.

2. (a) Kodi yankho la munthu wa ku Aitiopiya linali ndi tanthauzo lalikulu m’njira yotani? (b) Kodi ndi mafunso ati okhudzana ndi lamulo la Kristu la kuphunzitsa anthu amene tikambirane?

2 Yankho la munthu wa ku Aitiopiya limenelo lili ndi tanthauzo lalikulu. Iye anati: ‘Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine.’ Inde, iye anafunika womutsogolera, munthu womuonetsa mmene angatsatirire zimene anali kuŵerengazo. Mawu ameneŵa paokha akusonyeza kufunika kwa malangizo ena achindunji amene Yesu anatchula polamula za kuphunzitsa anthu. Kodi ndi malangizo ati ameneŵa? Kuti tipeze yankho, tiyeni tipitirize kukambirana kwathu mawu a Yesu amene ali pa Mateyu chaputala 28. Nkhani yapitayi yayankha mafunso akuti chifukwa? ndiponso kuti? Tsopano tikambirana mafunso enanso aŵiri okhudzana ndi lamulo la Kristu la kuphunzitsa anthu, mafunso akuti chiyani? ndiponso liti?

“Kuwaphunzitsa, Asunge Zinthu Zonse”

3. (a) Kodi munthu amakhala bwanji wophunzira wa Yesu Kristu? (b) Kupanga ophunzira kumaphatikizapo kuwaphunzitsa chiyani?

3 Kodi tiyenera kuphunzitsa chiyani kuti ena tiwathandize kukhala ophunzira a Kristu? Yesu analamula otsatira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Choncho tiyenera kuphunzitsa zinthu zimene Kristu analamula. * Komabe, kodi n’chiyani chimene chingathandize munthu amene waphunzitsidwa malamulo a Yesu kuti asangophunzira chabe koma kuti apitirize kukhala wophunzira? Tingaone mfundo imodzi yofunika kwambiri kuchokera pa mawu amene Yesu anasankha kugwiritsa ntchito. Onani kuti iye sanangonena kuti: ‘Aphunzitseni zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’ Koma m’malo mwake anati: ‘Aphunzitseni kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’ (Mateyu 19:17) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

4. (a) Kodi kusunga lamulo kumatanthauzanji? (b) Perekani fanizo losonyeza mmene timaphunzitsira munthu kusunga malamulo a Kristu.

4 Kusunga lamulo kumatanthauza kuti munthu “akugwirizanitsa zochita zake” ndi zimene lamulo limanena, ndiko kuti kumvera, kapena kutsatira lamulolo. Ndiyeno, kodi munthu timamuphunzitsa bwanji kusunga, kapena kuti kumvera, zinthu zimene Kristu analamula? Chabwino, taganizirani mmene munthu wophunzitsa anthu kuyendetsa galimoto amaphunzitsira ophunzira kusunga malamulo a pamsewu. Mphunzitsiyo angalongosolere ophunzirawo malamulo a pamsewu ali m’kalasi. Komabe kuti awaphunzitse kutsatira malamulowo, amayenera kuwalangiza pamene ophunzirawo akuyendetsa galimoto mu msewu mmenenso muli magalimoto ena ndi kumayesetsa kuchita zimene aphunzira. Mofananamo, tikamaphunzira Baibulo ndi anthu, timawaphunzitsa malamulo a Kristu. Komabe, pamene ophunzirawo akuyesetsa kugwiritsa ntchito malangizo a Kristu pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndiponso mu utumiki, timafunikanso kuwatsogolera, ndiko kuti kuwaonetsa mmene angachitire zimenezo. (Yohane 14:15; 1 Yohane 2:3) Motero, kuti tichite zonse zimene timafunika kuchita potsatira lamulo la Kristu lakuti tiphunzitse anthu, timafunika kuwaphunzitsa ndiponso kuwatsogolera. Mwa kutero timatengera chitsanzo cha Yesu ndi Yehova mwiniyo.​—Salmo 48:14; Chivumbulutso 7:17.

5. N’chifukwa chiyani munthu amene tikuphunzira naye Baibulo angamazengereze kutsatira lamulo la Kristu la kuphunzitsa anthu?

5 Kuphunzitsa ena kusunga malamulo a Yesu kumaphatikizapo kuwathandiza kumvera lamulo la kuphunzitsa anthu. Ntchito imeneyi ingakhale yovuta kwa anthu ena amene timaphunzira nawo Baibulo. Ngakhale iwo atakhala kuti kalelo anali okangalika m’tchalitchi chinachake chachikristu, n’zokayikitsa kuti aphunzitsi awo a kumeneko ankawaphunzitsa kuti azipita kukaphunzitsa anthu. Atsogoleri ena a matchalitchi amavomereza mosapita m’mbali kuti pankhani ya kuphunzitsa nkhosa zawo kulalikira, Matchalitchi Achikristu amalephera momvetsa chisoni. Pothirira ndemanga pa lamulo la Yesu la kupita m’dziko kukathandiza anthu ena alionsewo kuti akhale ophunzira, katswiri wa Baibulo John R. W. Stott anati: “Kulephera kwathu kutsatira zimene lamulo limeneli limatanthauza ndiko chofooka chachikulu kwambiri cha alaliki achikristu pa nkhani ya kulalikira masiku ano.” Iye anatinso: “Timakonda kulengezera patali uthenga wathu. Nthaŵi zina timaoneka ngati anthu amene tikuuza zochita anthu omwe akumira m’nyanja pamene ifeyo tili ku gombe pamalo otetezeka. Sitidumphira m’madzimo kuti tikawapulumutse. Timaopa kuti tinyowa.”

6. (a) Pothandiza wophunzira Baibulo, kodi tingatengere motani chitsanzo cha Filipo? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamuganizira wophunzira Baibulo akayamba kuchita nawo ntchito yolalikira?

6 Ngati munthu wina amene tikuphunzira naye Baibulo anali m’chipembedzo chimene anthu ake ‘amaopa kunyowa,’ kungakhale kovuta kuti iye asiye kuopa madzi n’kutsatira lamulo la Kristu la kuphunzitsa anthu. Iye angafunike thandizo. Motero tifunika kukhala oleza mtima pamene tikumulangiza ndi kumutsogolera moyenerera kuti athe kumvetsa bwino zinthu ndi kuchitapo kanthu, mofanana ndi mmene kuphunzitsa kwa Filipo kunatsegulira maso munthu wa ku Aitiopiya n’kusonkhezera mtima wake kuti abatizidwe. (Yohane 16:13; Machitidwe 8:35-38) Ndiponso, chifukwa choti timafunitsitsa kuphunzitsa ophunzira Baibulo kusunga lamulo la kuphunzitsa anthu, timagwira nawo ntchito limodzi kuti tiwatsogolere pamene akuyamba kumene kuchita ntchito yolalikira Ufumu.​—Mlaliki 4:9, 10; Luka 6:40.

“Zinthu Zonse”

7. Kodi kuphunzitsa ena ‘kusunga zinthu zonse’ kumaphatikizapo kuwaphunzitsa malamulo ati?

7 Ophunzira atsopano sitingowaphunzitsa mmene angaphunzitsire anthu ena. Yesu anatilangiza kuti tiphunzitse ena ‘kusunga zinthu zonse’ zimene analamula. Ndithudi zimenezi zikuphatikizapo kuwaphunzitsa malamulo akuluakulu kwambiri aŵiri; kukonda Mulungu ndi kukonda anzathu. (Mateyu 22:37-39) Kodi wophunzira watsopano tingamuphunzitse bwanji kusunga malamulo ameneŵa?

8. Perekani fanizo losonyeza mmene tingaphunzitsire wophunzira watsopano kukhala wachikondi.

8 Taganiziraninso za fanizo lija la munthu amene akuphunzira kuyendetsa galimoto. Wophunzirayo akamayendetsa galimoto ali ndi mphunzitsi wake n’kumadutsana ndi magalimoto ena, iye amaphunzira osati kokha mwa kumvetsera zimene mphunzitsi wake akunena, komanso mwa kuona zimene madalaivala ena akuchita. Mwachitsanzo, mphunzitsiyo angalozere wophunzirayo dalaivala wina amene walola mokoma mtima kuti galimoto ina iloŵe patsogolo pake mu msewuwo; kapena angaloze dalaivala amene mwaulemu wazimitsa pang’ono magetsi a galimoto yake kuti asathobwe m’maso madalaivala a magalimoto amene akubwera kutsogolo kwake; kapena angaloze dalaivala amene mofunitsitsa akuthandiza mnzake yemwe galimoto yake yawonongeka. Zitsanzo zoterozo zimaphunzitsa wophunzirayo zinthu zofunika zimene angagwiritse ntchito pamene akuyendetsa galimoto. N’chimodzimodzinso ndi wophunzira Baibulo watsopano; iye akamayenda pa njira yopita nayo kumoyo amaphunzira kwa mphunzitsi wake komanso kuwonjezera pamenepo, amaphunziranso kuchokera ku zitsanzo zabwino zimene amaona mu mpingo.​—Mateyu 7:13, 14.

9. Kodi wophunzira watsopano amaphunzira bwanji zimene kutsatira lamulo la kusonyeza chikondi kumatanthauza?

9 Mwachitsanzo, wophunzira Baibulo angaone mayi amene alibe mwamuna, yemwe amachita khama kwambiri kufika pa Nyumba ya Ufumu limodzi ndi ana ake ang’onoang’ono. Angaone munthu wovutika maganizo amene amabwera ku misonkhano mokhulupirika ngakhale kuti amavutika ndi matenda ake a maganizowo, angaone mkazi wamasiye wokalamba amene amathandiza okalamba ena kufika pa misonkhano ya mpingo, kapena angaone wachinyamata amene amasamalira nawo pa Nyumba ya Ufumu kuti pakhale paukhondo. Wophunzira Baibuloyo angaonenso mkulu pa mpingowo amene amatsogolera ena mu utumiki wa kumunda mokhulupirika ngakhale kuti ali ndi maudindo ambiri mu mpingo. Angakumane ndi Mboni imene ili yolemala ndipo imangokhala pa nyumba osayenda koma yomwe imalimbikitsa kwambiri mwauzimu onse amene amabwera kudzaichezera. Wophunzira angaone mwamuna ndi mkazi wake amene akusintha zinthu kwambiri pa moyo wawo n’cholinga choti athe kusamalira makolo awo okalamba. Mwa kuona zochita za Akristu okoma mtima, othandiza, ndiponso odalirika oterowo, wophunzira watsopanoyo amaphunzira kuchokera ku chitsanzo cha Akristu amenewo tanthauzo la kutsatira lamulo la Kristu la kukonda Mulungu ndiponso anzako, makamaka okhulupirira anzake. (Miyambo 24:32; Yohane 13:35; Agalatiya 6:10; 1 Timoteo 5:4, 8; 1 Petro 5:2, 3) Mwa njira imeneyi, munthu aliyense wa mu mpingo wachikristu angakhale, ndipo ayenera kukhala, mphunzitsi komanso wotsogolera ena njira.​—Mateyu 5:16.

“Kufikira Chimaliziro cha Nthaŵi ya Pansi Pano”

10. (a) Kodi tidzapitiriza kuphunzitsa anthu mpaka liti? (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa kagwiridwe ka ntchito yathu?

10 Kodi tiyenera kupitirizabe kuphunzitsa anthu mpaka liti? M’nthaŵi yonse ya chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano. (Mateyu 28:20) Kodi tidzatha kukwaniritsa mbali imeneyi ya lamulo la Yesu? Monga mpingo wa padziko lonse, tili otsimikiza mtima kuchita zimenezi. M’zaka zapitazi, tasangalala kugwiritsa ntchito nthaŵi yathu, nyonga zathu, ndiponso chuma chathu pofuna kupeza anthu amene ali ndi “maganizo oyenerera moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48, NW) Panopa, Mboni za Yehova zimathera maola opitirira mamiliyoni atatu tsiku ndi tsiku kwa chaka chonse zikugwira ntchito yolalikira Ufumu ndi kuphunzitsa anthu padziko lonse. Timachita zimenezi chifukwa chakuti timatengera chitsanzo cha Yesu. Iye anati: ‘Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.’ (Yohane 4:34) Zimenezi ndi zimenenso timakhumba ndi mtima wathu wonse. (Yohane 20:21) Tikufuna kutsiriza ntchito imene tapatsidwa; osati kungoiyamba chabe.​—Mateyu 24:13; Yohane 17:4.

11. Kodi abale ndi alongo athu ena achikristu atani, nanga tiyenera kudzifunsanji?

11 Komabe, timamva chisoni kuona kuti ena mwa okhulupirira anzathu afooka mwauzimu ndipo chotsatira chake n’chakuti sakuchita changu mwinanso asiyiratu kumene kutsatira lamulo la Kristu la kuphunzitsa anthu. Kodi pali njira iliyonse imene tingawathandizire kuti ayambirenso kugwirizana ndi mpingo ndi kumachita nawo ntchito yophunzitsa anthu? (Aroma 15:1; Ahebri 12:12) Tingadziŵe zimene tingachite masiku ano mwa kuona zimene Yesu anachita kuti athandize atumwi ake atafooka kwa kanthaŵi kochepa.

Sonyezani Kuti Mumawadera Nkhaŵa

12. (a) Yesu atatsala pang’ono kufa, kodi atumwi ake anachitanji? (b) Kodi Yesu anatani nawo atumwi ake ngakhale kuti iwo anafooka kwambiri mwauzimu?

12 Kumapeto kwa utumiki wa Yesu pa dziko lapansi, pamene anali pafupi kufa, atumwi “anamusiya Iye, nathaŵa.” Monga Yesu ananeneratu, iwo ‘anabalalika, yense ku zake za yekha.’ (Marko 14:50; Yohane 16:32) Kodi Yesu anatani nawo anzake amene anafooka mwauzimuwo? Atangoukitsidwa, Yesu anauza ena mwa otsatira ake kuti: “Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona ine kumeneko.” (Mateyu 28:10) Ngakhale kuti atumwiwo anali atafooka kwambiri mwauzimu, Yesu anawatchulabe kuti “abale anga.” (Mateyu 12:49) Iye anali kuwadalirabe. Mwa kuchita zimenezi, Yesu anasonyeza chifundo ndiponso kukhululukira, mofanana ndi mmenenso Yehova alili wachifundo ndi wokhululukira. (2 Mafumu 13:23) Kodi Yesu tingamutsanzire motani?

13. Kodi amene afooka mwauzimu tiyenera kuwaona motani?

13 Tiyenera kuwadera nkhaŵa kwambiri anthu amene achepetsa changu chawo kapena kusiya kuchita nawo utumiki. Timakumbukirabe chikondi chimene okhulupirira anzathu amenewo anachisonyeza m’mbuyomo, ena a iwo mwina kwa zaka zochuluka. (Ahebri 6:10) Timalakalakadi titamachita nawonso zinthu limodzi. (Luka 15:4-7; 1 Atesalonika 2:17) Komabe, kodi tingaonetse bwanji kuti timawadera nkhaŵa?

14. Potsanzira Yesu, kodi tingachitenji kuti tithandize munthu wofooka?

14 Yesu anauza atumwi omwe anakhumudwawo kuti apite ku Galileya ndi kuti iyeyo akamuona kumeneko. Tinganene kuti Yesu anawaitanira ku msonkhano wapadera. (Mateyu 28:10) N’chimodzimodzinso masiku ano, timalimbikitsa ofooka mwauzimu kuti azifika pa misonkhano ya mpingo wachikristu, ndipo tingafunike kuwalimbikitsa nthaŵi zingapo kuti achite zimenezi. Kwa atumwi aja, kuwaitanira ku msonkhanowo kunathandizadi chifukwa “ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira.” (Mateyu 28:16) Timasangalala kwambiri pamene ofooka nawonso achitapo kanthu tikawaitana mwachikondi ndi kuyambanso kufika pa misonkhano yachikristu.​—Luka 15:6.

15. Kodi tingatsatire motani chitsanzo cha Yesu polandira ofooka amene amabwera ku misonkhano yathu?

15 Kodi tingachitenji Mkristu wofooka akafika pa Nyumba ya Ufumu? Chabwino, kodi Yesu anachitanji ataona atumwi ake, omwe chikhulupiriro chawo chinafooka kwa kanthaŵi, ali pamalo amene anakonza kuti asonkhane? “Yesu anadza nalankhula nawo.” (Mateyu 28:18) Iye sanawayang’ane ali patali, koma anapita pomwepo. Atumwiwo ayenera kuti mitima yawo inakhala pansi kwambiri ataona kuti Yesu ndiye wayamba kuchitapo kanthu. Tiyeni ifenso tiziyamba ndife kuchitapo kanthu ndipo tiziwalandira ndi manja aŵiri ofooka mwauzimu amene akuyesetsa kubwerera mu mpingo wachikristu.

16. (a) Kodi tikuphunziranji pa zimene Yesu anachita ndi otsatira ake? (b) Kodi tingaonetse motani kuti timaona ofooka mofanana ndi mmene Yesu anali kuwaonera? (Onani mawu a m’munsi.)

16 N’chiyaninso china chimene Yesu anachita? Choyamba, analengeza kuti: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine.” Chachiŵiri, anawapatsa ntchito: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani.” Chachitatu, anawalonjeza kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse.” Koma kodi mwaona chimene Yesu sanachite? Iye sanadzudzule ophunzirawo pa zimene anali kulephera kapenanso zimene anali kukayikira. (Mateyu 28:17) Kodi kachitidwe kotereka kanali kogwira mtima? Inde. Sipanatenge nthaŵi yaitali kuti atumwiwo ayambenso “kuphunzitsa ndi kulalikira” uthenga wabwino. (Machitidwe 5:42) Mwa kutsatira chitsanzo cha Yesu cha mmene tiyenera kuonera ofooka ndiponso zimene tiyenera kuwachitira, tingayembekezere zosangalatsa zangati zimenezi kuchitika mu mpingo wathu. *​—Machitidwe 20:35.

“Ine Ndili Pamodzi ndi Inu Masiku Onse”

17, 18. Kodi ndi mfundo zolimbikitsa zotani zimene zili m’mawu a Yesu akuti, “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse”?

17 Mawu omalizira a lamulo la Yesu akuti, ‘Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse,’ ali ndi mfundo yolimbikitsa kwa onse amene amachita khama kukwaniritsa lamulo la Kristu la kuphunzitsa anthu. Palibe chifukwa choopera china chilichonse chimene adani athu angachite potsutsa ntchito yathu yolalikira Ufumu, ngakhalenso bodza lina lililonse limene angatinenere. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa? N’chifukwa chakuti Mtsogoleri wathu, Yesu, amene ali ndi ‘mphamvu zonse Kumwamba ndi padziko lapansi,’ ali nafe kuti atithandize.

18 Lonjezo la Yesu lakuti ‘Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse’ ndi lokhazikanso mtima pansi kwambiri. Pamene tikuyesetsa kutsatira lamulo la Kristu lakuti tiphunzitse anthu, pali masiku ena amene timakhala okondwa komanso pali masiku ena amene timakhala achisoni. (2 Mbiri 6:29) Ena a ife timakumana ndi nthaŵi zachisoni polira maliro a munthu amene tinali kumukonda. (Genesis 23:2; Yohane 11:33-36) Ena akuvutika ndi ukalamba, pamene thupi limakhala ndi thanzi lofooka ndiponso mphamvu zochepa. (Mlaliki 12:1-6) Palinso ena amene amakhala masiku ambiri ali ndi mtima wachisoni, kapena kuti akuvutika maganizo. (1 Atesalonika 5:14) Ndipo anthu okuvutika kwambiri ndi mavuto a zachuma tikuchulukirachulukira. Komabe ngakhale kuti pali zovuta zonsezi, utumiki wathu umayenda bwino chifukwa chakuti Yesu ali pamodzi nafe ‘masiku onse,’ kuphatikizapo masiku amene timakhala achisoni kwambiri.​—Mateyu 11:28-30.

19. (a) Kodi lamulo la Yesu la kuphunzitsa anthu lili ndi malangizo ati? (b) Kodi n’chiyani chimene chimatithandiza kukwaniritsa ntchito imene Kristu anatipatsa?

19 Monga taonera m’nkhani ino ndiponso m’nkhani ina ija, lamulo la Yesu la kuphunzitsa anthu limakhudza mbali iliyonse. Yesu anatiuza chifukwa chake tiyenera kumvera lamuloli ndiponso kuti zimenezo tizichitire kuti. Anatiuzanso zimene tiyenera kuphunzitsa ndiponso kuti tiyenera kuchita zimenezi mpaka liti. N’zoona kuti kugwira ntchito yaikulu imeneyi n’kovuta. Komatu chifukwa tikuthandizidwa ndi mphamvu za Kristu ndiponso popeza kuti iye mwini ali nafe, tikhoza kuikwanitsa. Kodi simukuvomereza?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Buku lina limanena kuti lamulo la kubatiza ndi kuphunzitsa “sikuti kwenikweni limanena za . . . ntchito ziŵiri zimene zimachitika motsatizana.” Koma, “kuphunzitsa ndi ntchito imene imayamba munthu asanabatizidwe . . . ndipo imapitirirabe munthu akabatizidwa.”

^ ndime 16 Mfundo zina zonena za mmene tiyenera kuonera ofooka ndiponso mmene tingawathandizire zikupezeka mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2003, masamba 15-18.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ena timawaphunzitsa bwanji kusunga zimene Yesu analamula?

• Kodi wophunzira watsopano angaphunzire zotani kwa anthu ena mu mpingo?

• Kodi tingachite chiyani kuti tithandize amene afooka mwauzimu?

• Kodi lonjezo la Yesu lakuti “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse” limatilimbikitsa ndiponso kutikhazika mtima pansi motani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 15]

Anthu timafunika kuwaphunzitsa ndiponso kuwatsogolera

[Zithunzi patsamba 17]

Wophunzira watsopano amaphunzira zinthu zofunika kuchokera ku zitsanzo za anthu ena