Kalata Yopita kwa Nowa
Kalata Yopita kwa Nowa
“WOKONDEDWA a Nowa, Ndaŵerenga m’Baibulo maulendo angapo za inu ndiponso mmene munakhomera chingalawa chomwe inu ndi banja lanu munapulumukiramo Chigumula.”
Umu ndi mmene inayambira kalata imene mtsikana wina wa zaka 15, dzina lake Minnamaria, analemba ndi kuitumiza ku mpikisano wolemba makalata wa ana a sukulu a zaka zoyambira pa 14 mpaka 21. Mpikisanowo anakonza ndi a bungwe loona za mtokoma ku Finland, mogwirizana ndi a Bungwe la Aphunzitsi a Chinenero cha Chifinishi, pamodzi ndi a Bungwe la Zolembalemba la ku Finland. Oloŵa mpikisanowo anafunika kulemba kalata yofotokoza za m’buku lina lililonse. Akanatha kulemba kalatayo ngati kuti ikupita kwa mlembi wa bukulo kapena munthu wina wotchulidwa m’bukumo. Aphunzitsi anasankha makalata oposa 1,400 pa makalata omwe ana awo a sukulu analemba ndipo anawatumiza kwa anthu oti akasankhe makalata abwino. Osankhawo anasankha kalata imodzi imene inali pa nambala wani, makalata teni amene anali pa nambala thu, ndi makalata enanso teni amene anali pa nambala filiyi. Minnamaria anasangalala kwambiri chifukwa chakuti kalata yake inali pa gulu la makalata a pa nambala filiyi.
Kodi n’chifukwa chiyani mtsikana wapasukuluyu, Minnamaria, analembera kalata yake Nowa, munthu amene anakhala ndi moyo zaka pafupifupi 5,000 zapitazo? Iye anati: “Baibulo ndilo ndinaliganizira choyamba. Anthu otchulidwa m’Baibulo ndimawadziŵa bwino kwambiri. Ndaŵerenga nkhani zambiri zokhudza anthu ameneŵa moti kwa ine amangokhala ngati ali moyo. Ndinasankha Nowa chifukwa chakuti moyo wake unali wosangalatsa kwambiri ndiponso wosiyana ndi wanga.”
Kalata imene Minnamaria analembera Nowa inamaliza ndi mawu aŵa: “Mpaka pano ndinu chitsanzo chosonyeza chikhulupiriro ndi kumvera. Moyo wanu umalimbikitsa onse amene amaŵerenga Baibulo kuchita zinthu mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo.”
Kalata ya mtsikana woŵerenga Baibuloyu ikusonyeza bwino kuti Baibulo lilidi ‘lamoyo, ndi lochitachita’ kwa anthu onse, ana ngakhalenso akulu.—Ahebri 4:12.