Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mukani, Phunzitsani”

“Mukani, Phunzitsani”

“Mukani, Phunzitsani”

Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani.”​—MATEYU 28:18, 19.

1, 2. (a) Kodi ndi ntchito yanji imene Yesu anapatsa otsatira ake? (b) Kodi tikambirana mafunso ati okhudzana ndi lamulo la Yesu?

INALI nthaŵi ya masika ku Israyeli m’chaka cha 33 Kristu Atabwera pamene tsiku lina ophunzira a Yesu anasonkhana pa phiri linalake ku Galileya. Ambuye wawo amene anali ataukitsidwa anali pafupi kukwera kumwamba, koma asanatero anali ndi mawu ofunika kwambiri oti awauze. Yesu anali ndi ntchito yoti awapatse. Kodi inali ntchito yotani? Kodi ophunzira ake anachita bwanji pa ntchito imeneyo? Ndipo kodi ntchitoyo ikutikhudza motani ife masiku ano?

2 Zimene Yesu ananena zinalembedwa pa Mateyu 28:18-20. Iye anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Yesu anatchula za “mphamvu zonse,” “mitundu yonse,” “zinthu zonse,” ndi “masiku onse.” Lamulo lake lomwe linaphatikizapo mawu anayi amenewo limadzutsa mafunso ofunika kwambiri, omwe mwachidule tingawafunse m’mawu akuti chifukwa? kuti? chiyani? ndiponso liti? Tiyeni tikambirane mafunsoŵa lililonse palokha. *

“Mphamvu Zonse Zapatsidwa kwa Ine”

3. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera lamulo lakuti tiphunzitse anthu?

3 Choyamba, n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera lamulo lakuti tiphunzitse anthu? Yesu anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani.” Mawu akuti “chifukwa chake” akutionetsa chifukwa chachikulu chomvera lamulo limeneli. N’chifukwa chakuti Yesu, yemwe anapereka lamulo limeneli, ali ndi “mphamvu zonse.” Kodi iye ali ndi mphamvu zochuluka motani?

4. (a) Kodi Yesu ali ndi mphamvu zochuluka motani? (b) Kodi kuzindikira mphamvu zimene Yesu ali nazo kuyenera kukhudza motani mmene timaonera lamulo lakuti tiphunzitse anthu?

4 Yesu ali ndi mphamvu pa mpingo wake, ndipo kuyambira mu 1914 anakhalanso ndi mphamvu pa Ufumu wa Mulungu womwe unangokhazikitsidwa kumene. (Akolose 1:13; Chivumbulutso 11:15) Iye ndi mngelo wamkulu ndipo motero amalamula gulu la kumwamba la angelo mamiliyoni mazanamazana. (1 Atesalonika 4:16; 1 Petro 3:22; Chivumbulutso 19:14-16) Atate wake anamupatsa mphamvu kuti awononge “chiweruzo chonse [“maboma onse,” NW], ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu” zotsutsana ndi mfundo zolungama. (1 Akorinto 15:24-26; Aefeso 1:20-23) Yesu sali ndi mphamvu pa anthu amoyo okha. Iye alinso “woweruza amoyo ndi akufa” ndipo Mulungu anamupatsa mphamvu zoukitsa anthu akufa. (Machitidwe 10:42; Yohane 5:26-28) Ndithudi, lamulo loperekedwa ndi Munthu wopatsidwa mphamvu zochuluka moteromo tiyenera kuliona kuti n’lofunika kwambiri. Choncho, mwaulemu ndiponso mofunitsitsa timamvera lamulo la Kristu lakuti “mukani, phunzitsani.”

5. (a) Kodi Petro anamvera motani mawu a Yesu? (b) Kodi ndi madalitso otani amene Petro anapeza chifukwa chomvera malangizo a Yesu?

5 Koyambirira kwa utumiki wake padziko lapansi, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake m’njira yochititsa chidwi kwambiri kuti munthu angadalitsidwe chifukwa chozindikira mphamvu zimene Yesuyo ali nazo ndiponso kumvera malamulo ake. Panthaŵi ina iye anauza Petro, yemwe anali msodzi, kuti: “Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.” Petro anali wotsimikiza kuti m’madzimo munalibe nsomba, motero anauza Yesu kuti: “Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu.” Komano modzichepetsa Petro anawonjezera kuti: “Koma pa mawu anu ndidzaponya makoka.” Petro atamvera lamulo la Kristu, anagwira “unyinji waukulu wa nsomba.” Petro anadabwa nazo, moti “anagwa pansi pa mabondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.” Koma Yesu anayankha kuti: “Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.” (Luka 5:1-10; Mateyu 4:18) Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani?

6. (a) Kodi nkhani ya kusodza nsomba mozizwitsa imasonyeza kuti Yesu amafuna kumvera kotani? (b) Kodi Yesu tingamutsanzire motani?

6 Yesu anapatsa Petro, Andreya, ndi atumwi ena ntchito yokhala “asodzi a anthu” atagwira nsomba modabwitsa chomwechi, osati asanagwire. (Marko 1:16, 17) N’zachionekere kuti Yesu sanafune kuti anthu azimumvera m’chimbulimbuli. Iye anasonyeza amunawo momveka bwino chifukwa chake ayenera kumumvera. Monga mmene kumvera lamulo la Yesu lakuti aponye makoka awo kunawabweretsera zosangalatsa, chomwechonso kumvera lamulo la Yesu la ‘kusodza anthu’ kungabweretse madalitso osaneneka. Atumwiwo pokhala ndi chikhulupiriro chonse anachita zimene Yesu anawauza. Nkhaniyo imamaliza ndi kuti: “Mmene iwo anakocheza ngalaŵa zawo pamtunda, anasiya zonse, namutsata Iye.” (Luka 5:11) Masiku ano tikamalimbikitsa ena kuti azigwira nawo ntchito yophunzitsa anthu, timatsanzira Yesu. Sitifuna kuti anthu azingochita zimene tikuwauza, koma m’malo mwake timawapatsa zifukwa zomveka bwino zowasonyeza chifukwa chake ayenera kumvera lamulo la Kristu.

Zifukwa Zomveka Bwino Ndiponso Zosonkhezera Zoyenera

7, 8. (a) Kodi zifukwa zina za m’Malemba zogwirira ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira ndi ziti? (b) Kodi ndi lemba liti makamaka limene inuyo limakulimbikitsani kupitiriza kugwira ntchito yolalikira? (Onaninso mawu a m’munsi.)

7 Chifukwa chakuti timazindikira mphamvu zimene Kristu ali nazo, timachita nawo ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Kodi pali zifukwa zinanso ziti za m’Malemba zochitira ntchito imeneyi zimene tingafotokozere anthu amene tikufuna kuwalimbikitsa kuchita ntchito zabwino? Talingalirani mawu aŵa omwe zinanena Mboni zokhulupirika zingapo zochokera m’mayiko osiyanasiyana, ndipo onani mmene malemba osonyezedwawo amagwirizirana ndi mawu awowo.

8 Roy, yemwe anabatizidwa mu 1951, anati: “Pamene ndinadzipatulira kwa Yehova, ndinalonjeza kuti ndidzamutumikira nthaŵi zonse. Ndikufuna kusunga lonjezo langa.” (Salmo 50:14; Mateyu 5:37) Heather, yemwe anabatizidwa mu 1962, ananena kuti: “Ndikaganizira zonse zimene Yehova wandichitira, ndimafuna kumusonyeza kuti ndimayamikira pomutumikira mokhulupirika.” (Salmo 9:1, 9-11; Akolose 3:15) Hannelore, yemwe anabatizidwa mu 1954, anati: “Nthaŵi iliyonse imene tili mu utumiki, angelo amatithandiza. Umenewutu ndi ulemu waukulu kwambiri!” (Machitidwe 10:30-33; Chivumbulutso 14:6, 7) Honor, yemwe anabatizidwa mu 1969, anafotokoza kuti: “Nthaŵi ya Yehova yopereka chiweruzo ikadzafika, sindikufuna kuti wina aliyense m’dera lathu adzaimbe Yehova ndi Mboni zake mlandu wakuti anali onyalanyaza ponena kuti, ‘Ine palibe anandichenjezako!’” (Ezekieli 2:5; 3:17-19; Aroma 10:16, 18) Claudio, yemwe anabatizidwa mu 1974, anati: “Pamene tikulalikira, timakhala ‘pamaso pa Mulungu’ ndiponso ‘mu umodzi ndi Kristu.’ Tangoganizirani zimenezo! Tikakhala mu utumiki, timakhala tili limodzi ndi Mabwenzi athu a pamtima kwambiri.”​—2 Akorinto 2:17; NW. *

9. (a) Kodi nkhani ya zimene zinachitikira Petro ndi atumwi ena posodza imatiuza kuti pomvera Kristu mtima wathu uyenera kusonkhezeredwa ndi chiyani? (b) Kodi masiku ano mtima wathu uyenera kusonkhezeredwa ndi chiyani pomvera Mulungu ndi Kristu, ndipo n’chifukwa chiyani zili choncho?

9 Nkhani ya kusodza nsomba modabwitsa ija ikutisonyezanso kuti pomvera Kristu mtima wathu uzisonkhezeredwa ndi chinthu choyenera, chomwe ndi chikondi. Pamene Petro ananena kuti, “Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa,” Yesu sanachoke, ndiponso sanadzudzule Petro kuti anali wochimwa. (Luka 5:8) Yesu sanadzudzulenso Petro pomuchonderera kuti azipita. Koma mokoma mtima Yesu anayankha kuti: “Usaope.” Ngati akanamvera Kristu chifukwa cha mantha osayenerera, mtima wake ukanasonkhezeredwa ndi chinthu cholakwika. M’malo mwake, Yesu anauza Petro kuti iye limodzi ndi anzake adzakhala othandiza kwambiri posodza anthu. Ifenso masiku ano sitikakamiza ena kuti azimvera Kristu powachititsa kukhala amantha kapena kukhala ndi malingaliro alionse ofooketsa munthu, monga kuwachititsa kudziona kuti ndi olakwa kapena kuwachititsa manyazi. Mtima wa Yehova umasangalala kokha pamene anthu akumvera ndi mtima wawo wonse chifukwa chokonda Mulungu ndi Kristu.​—Mateyu 22:37.

“Phunzitsani Anthu a Mitundu Yonse”

10. (a) Kodi ndi mfundo iti pa lamulo la Yesu la kuphunzitsa anthu imene inapatsa ophunzira ake ntchito yaikulu? (b) Kodi ophunzirawo anachita bwanji ndi lamulo la Yesu?

10 Funso lachiŵiri limene tingafunse lokhudzana ndi lamulo la Kristu ndi lakuti, Kodi ntchito imeneyi yophunzitsa anthu iyenera kuchitikira kuti? Yesu anauza otsatira ake kuti: “Phunzitsani anthu a mitundu yonse.” Isanafike nthaŵi ya utumiki wa Yesu, anthu amitundu anali kulandiridwa ngati anapita ku Israyeli kukatumikira Yehova. (1 Mafumu 8:41-43) Yesu mwini wakeyo analalikira makamaka kwa anthu a mtundu wachiyuda, koma tsopano anauza otsatira ake kuti apite kwa anthu a mitundu yonse. Kwenikweni, malo osodzapo, kapena kuti gawo lolalikiramo, a ophunzira ake anali aang’ono ngati “dziŵe,” popeza anali anthu a mtundu wachiyuda okha, koma posakhalitsa anadzaphatikizapo “nyanja” yonse ya anthu. Ngakhale kuti kusintha kumeneku kunatanthauza kuti ophunzira akhala ndi ntchito yaikulu, iwo mofunitsitsa anamvera malangizo a Yesu. Pasanathe zaka 30 kuchokera nthaŵi imene Yesu anafa, mtumwi Paulo anafika polemba kuti uthenga wabwino unali utalalikidwa osati kwa Ayuda okha, koma ku “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”​—Akolose 1:23.

11. Kodi ndi kuwonjezeka kotani kwa ‘malo osodzapo’ kumene kwachitika kuyambira m’zaka zoyambirira za m’ma 1900?

11 M’nthaŵi yamakono, pakhalanso kuwonjezeka kofananako kwa gawo lolalikiramo. M’zaka zoyambirira za m’ma 1900, ‘malo osodzapo’ anali m’mayiko ochepa. Komatu otsatira a Kristu nthaŵi imeneyo anatengera chitsanzo cha Akristu oyambirira ndipo mofunitsitsa anawonjezera gawo limene anali kulalikiramo. (Aroma 15:20) Pofika zaka za m’ma 1930, iwo anali kupanga ophunzira m’mayiko pafupifupi 100. Lerolino ‘malo athu osodzapo’ awonjezeka n’kufika m’mayiko 235.​—Marko 13:10.

“A Manenedwe Onse”

12. Kodi ndi vuto lanji limene ulosi wopezeka pa Zekariya 8:23 umasonyeza?

12 Kuphunzitsa anthu m’mitundu yonse ndi ntchito yovuta, osati chabe chifukwa cha kukula kwa malo akewo, komanso chifukwa cha kuchuluka kwa zinenero. Yehova analosera kudzera mwa mneneri Zekariya kuti: ‘Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’ (Zekariya 8:23) Pa kukwaniritsidwa kwake kwakukulu kwa ulosiwu, “munthu ali Myuda” akuimira otsalira a Akristu odzozedwa, ndipo “amuna khumi” akuimira “khamu lalikulu.” * (Chivumbulutso 7:9, 10; Agalatiya 6:16) Khamu lalikulu limeneli la ophunzira a Kristu linali loti lidzapezeka m’mitundu yambiri, ndipo monga ananenera Zekariya, linali loti lizidzalankhula zinenero zambirimbiri. Kodi mbiri yamakono ya anthu a Mulungu imasonyeza kuti ophunzira apezekadi moteromo? Inde, n’zimene imasonyeza.

13. (a) Kodi pakati pa anthu a Mulungu a masiku ano pachitika zotani zokhudza zinenero? (b) Kodi gulu la kapolo lachitapo chiyani pa mfundo yakuti chakudya chauzimu chikufunika kwambiri kuti chizipezeka m’zinenero zosiyanasiyana? (Phatikizanipo bokosi lakuti “Mabuku a Anthu Osaona.”)

13 Mu 1950, anthu pafupifupi atatu mwa anthu asanu alionse a Mboni za Yehova padziko lonse anali oti chinenero chawo ndi Chingelezi. Pofika mu 1980 zimenezo zinasintha kufika pa anthu aŵiri mwa anthu asanu alionse, ndipo masiku ano ndi munthu mmodzi yekha mwa anthu asanu alionse a Mboni yemwe chinenero chake ndi Chingelezi. Kodi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lachitapo chiyani popeza kuti tsopano ambiri amalankhula zinenero zina? Lapereka chakudya chauzimu m’zinenero zinanso zowonjezeka. (Mateyu 24:45) Mwachitsanzo, mu 1950 tinali kufalitsa mabuku athu mu zinenero 90, koma tsopano zawonjezeka kufika pafupifupi zinenero 400. Kodi kuchita chidwi mowonjezereka kumeneku ndi anthu a zinenero zosiyanasiyana kwakhala ndi zotsatirapo zabwino? Inde! Anthu pafupifupi 5,000 ‘ochokera mwa manenedwe alionse’ amakhala ophunzira a Kristu mlungu uliwonse pa chaka. (Chivumbulutso 7:9) Ndipo anthu akuwonjezekabe. M’mayiko ena “makoka” akukhala ndi nsomba zambiri!​—Luka 5:6; Yohane 21:6.

Kodi Mungachite Nawo Utumiki Wina Wopindulitsa?

14. Kodi anthu a m’gawo lathu amene amalankhula chinenero china tingawathandize motani? (Phatikizanipo bokosi lakuti “Kuphunzitsa Anthu M’chinenero cha Manja.”)

14 M’mayiko ambiri, anthu obwera kuchokera ku mayiko ena achititsa kuti ntchito yovuta yophunzitsa anthu a ‘manenedwe alionse’ ikhale m’dziko lathu lomwelo. (Chivumbulutso 14:6) Kodi tingawathandize bwanji anthu a m’gawo lathu amene amalankhula chinenero chosiyana ndi chathu? (1 Timoteo 2:4) Tinganene kuti, tiyenera kugwiritsa ntchito zida zosodzera zoyenerera. Anthu oterowo apatseni mabuku a chinenero chawo. Ngati n’kotheka, konzani zoti Mboni ina imene imalankhula chinenero chimenecho ikaonane nawo. (Machitidwe 22:2) Masiku ano n’kosavuta kulinganiza zimenezi chifukwa Mboni zambiri zaphunzira chinenero china pofuna kuthandiza alendo kukhala ophunzira a Kristu. Malipoti akusonyeza kuti kuthandiza ena kotereku n’kopindulitsa kwambiri.

15, 16. (a) Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zikusonyeza kuti ndi kopindulitsa kuthandiza anthu olankhula chinenero china? (b) Kodi ndi mafunso otani okhudza kutumikira m’gawo la chinenero china amene tingawaganizire?

15 Taonani zitsanzo ziŵiri izi kuchokera ku dziko la Netherlands, kumene amalinganiza kugwira ntchito yolalikira Ufumu m’zinenero 34. Mwamuna wina ndi mkazi wake omwe ndi Mboni anadzipereka kuti apite kukaphunzitsa anthu obwera m’dzikolo olankhula chinenero cha Chipolishi. Anthu anasangalala kwambiri ndi ntchito yawo moti mwamunayo anaona kuti ndi bwino kuchepetsako ntchito yake yolembedwa kuti azitha kukhala ndi tsiku linanso limodzi pa mlungu loti aziphunzira Baibulo ndi anthu achidwi. Posakhalitsa banjali linali kuchititsa maphunziro a Baibulo opitirira 20 mlungu uliwonse. Iwo anati: “Utumiki wathu umatichititsa kukhala osangalala kwambiri.” Amene amaphunzitsa anthu m’chinenero china amasangalala kwambiri makamaka anthu amene akumva choonadi cha m’Baibulo m’chinenero chawowo akamanena mawu oyamikira. Mwachitsanzo, pamsonkhano wina wa chinenero cha Chivietenamu, mwamuna wina wokalamba anaimirira ndi kupempha kuti alankhulepo. Misozi italengeza m’maso, anauza Mbonizo kuti: “Ndikuthokoza kuti mukuchita khama kuphunzira chinenero chathu chovutachi. Ndikuyamikira kwambiri kuti, ndili wokalamba chonchi, ndikuphunzira zinthu zosangalatsa zambiri kuchokera m’Baibulo.”

16 Ndiye n’zosadabwitsa kuti amene ali m’mipingo ya zinenero zina amaona kuti zimawapindulitsa kwambiri. Banja lina ku Britain linanena kuti: “Kuchita utumiki m’gawo la chinenero china ndi utumiki wina umene tasangalala nawo kwambiri pa zaka 40 zimene takhala tikuchita utumiki wa Ufumu.” Kodi mukhoza kusintha zinthu zina ndi zina pa moyo wanu kuti muthe kuchita nawo utumiki wokondweretsawu? Ngati mudakali pa sukulu, kodi mukhoza kuphunzira chinenero china pokonzekera kudzachita utumiki woterewu? Mungadzakhale ndi moyo wopindulitsa wokhala ndi madalitso ambirimbiri mutati mwachita zimenezi. (Miyambo 10:22) Bwanji osakambirana nkhaniyi ndi makolo anu?

Kusinthasintha Njira Zimene Timagwiritsa Ntchito

17. Kodi anthu ambiri tingathe kuwafikira motani m’gawo la mpingo wathu?

17 Inde, mmene zinthu zilili kwa ambiri a ife sizingatheke kuti tiponye “makoka” athu m’magawo a chinenero china. Komabe tikhoza kufikira anthu ambiri m’gawo la mpingo wathu lomwelo kuposa amene tikufikira panopa. Kodi tingatero motani? Mwa kusinthasintha, osati uthenga wathu, koma njira zimene timagwiritsa ntchito. M’madera ambiri anthu ochulukirachulukira akukhala m’nyumba zokhala ndi chitetezo chokhwima. Anthu ena ambiri sakhala pakhomo nthaŵi imene timapita mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Motero tingafunike kuponya “makoka” athu pa nthaŵi zosiyanasiyana komanso m’malo osiyanasiyana. Mwa kutero timatsanzira Yesu. Iye anapeza njira zolankhulirana ndi anthu m’malo osiyanasiyana.​—Mateyu 9:9; Luka 19:1-10; Yohane 4:6-15.

18. Kodi kuchitira umboni m’malo osiyanasiyana kwakhala kopindulitsa motani? (Phatikizanipo bokosi lakuti “Kuphunzitsa Anthu a Pantchito.”)

18 M’mayiko ena, kuchitira umboni pena paliponse pamene pangakhale anthu ndi njira yofunika kwambiri pophunzitsa anthu. Amene anazoloŵera kuphunzitsa anthu amalimbikira kuchitira umboni m’malo osiyanasiyana. Kuwonjezera pa kuchita nawo utumiki wa kunyumba ndi nyumba, tsopano ofalitsa akuchitiranso umboni m’mabwalo a ndege, m’maofesi, m’masitolo, m’malo oimikapo magalimoto, pokwerera mabasi, m’misewu, ku malo amene anthu ambiri amakachezerako, m’mphepete mwa nyanja, ndi kwina kulikonse. Mboni zambiri ndithu zimene zabatizidwa posachedwapa ku dziko la Hawaii zinakumana koyamba ndi wa Mboni m’malo angati ameneŵa. Kusinthasintha njira zimene timagwiritsa ntchito kumatithandiza kuchita zonse zofunika pomvera lamulo la Yesu lakuti tiphunzitse anthu.​—1 Akorinto 9:22, 23.

19. Kodi ndi mbali ziti za ntchito imene Yesu anatipatsa zomwe tikambirane m’nkhani yotsatira?

19 Zimene Yesu ananena popereka ntchito yophunzitsa anthu zinaphatikizapo osati kokha chifukwa chake tiyenera kugwira ntchitoyo ndi kuti n’kuti kumene iyenera kuchitikira, koma zinaphatikizaponso kuti tikuyenera kulalikira za chiyani ndipo tichite zimenezi mpaka liti. Mbali ziŵiri zimenezi za ntchito imene Yesu anatipatsa tizikambirana m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 M’nkhani ino tikambirana mafunso aŵiri oyambirirawo. Aŵiri omalizirawo tidzakambirana m’nkhani yotsatira.

^ ndime 8 Zifukwa zinanso zogwirira ntchito yolalikira zikupezeka pa Miyambo 10:5; Amosi 3:8; Mateyu 24:42; Marko 12:17; Aroma 1:14, 15.

^ ndime 12 Kuti mumve zambiri pa kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu, onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 2001, tsamba 12, ndiponso buku la Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse, Gawo 2, masamba 407-408, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ntchito yolalikira Ufumu ndi kuphunzitsa anthu timaigwira pa zifukwa ziti komanso mosonkhezeredwa ndi chiyani?

• Kodi masiku ano atumiki a Yehova agwira mpaka pati ntchito imene Yesu anapereka yophunzitsa anthu a mitundu yonse?

• Kodi tingasinthesinthe motani ‘njira zathu zosodzera,’ nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kutero?

[Mafunso]

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 10]

Mabuku a Anthu Osaona

Albert ndi mkulu mu mpingo wachikristu ndiponso mtumiki wa nthaŵi zonse amene amakhala ku United States. Iye saona. Kugwiritsa ntchito mabuku ofotokoza za m’Baibulo omwe anthu osaona amaŵerenga kumamuthandiza kuchita bwino kwambiri utumiki wake, kuphatikizapo pa ntchito yake monga woyang’anira utumiki. Kodi udindo wake mu mpingo amausamalira bwanji?

James, yemwe ndi woyang’anira wotsogolera mu mpingowo, anati: “Mu mpingo wathu sitinakhalepo ndi woyang’anira utumiki wodziŵa bwino ntchito yake ngati mmene alili Albert.” Albert ndi mmodzi mwa anthu pafupifupi 5,000 osaona a ku United States amene, kwa zaka zonsezi, akhala akulandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo oŵerenga anthu osaona a m’chinenero cha Chingelezi ndi Chisipanya. Ndipotu, kuyambira m’chaka cha 1912 gulu la kapolo wokhulupirika lafalitsa mabuku oposa 100 omwe anthu osaona amaŵerenga. Pogwiritsa ntchito njira zamakono, nyumba zosindikiziramo mabuku za Mboni za Yehova zimasindikiza mabuku otereŵa ambirimbiri chaka chilichonse m’zinenero zoposa teni ndipo amatumizidwa m’mayiko oposa 70. Kodi inu mukudziŵapo munthu wina amene angapindule ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo amene amakonzedwera anthu osaona?

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 11]

Kuphunzitsa Anthu M’chinenero cha Manja

Mboni zikwizikwi padziko lonse, kuphatikizapo achinyamata achangu ambirimbiri, zaphunzira chinenero cha manja pofuna kuthandiza anthu osamva kuti akhale ophunzira a Kristu. Chifukwa cha zimenezi, ku Brazil kokha, posachedwapa anthu osamva okwana 63 anabatizidwa m’chaka chimodzi ndipo Mboni 35 zosamva za kumeneko tsopano ndi alaliki a nthaŵi zonse. Padziko lonse pali mipingo ndiponso magulu a chinenero cha manja oposa 1,200. M’dziko la Russia muli dera limodzi lokha la mipingo ya chinenero cha manja, ndipo tikanena za kukula kwa malo amene derali limatenga, ilo ndilo dera lalikulu kwambiri padziko lonse chifukwa limazungulira Russia yense.

[Bokosi patsamba 12]

Kuphunzitsa Anthu a Pantchito

Ku Hawaii, pamene Mboni ina inali kuyendera anthu a pantchito m’maofesi awo inakumana ndi mkulu wa kampani ina ya zamtengatenga. Ngakhale kuti mkuluyu amakhala wotanganidwa, iye anavomera kuti aziphunzira Baibulo mu ofesi yakeyo kwa mphindi 30 pa mlungu. Lachitatu lililonse m’maŵa amauza antchito ake kuti asamuimbire telefoni ndipo amaika maganizo ake onse pa phunzirolo. Mboni ina ku Hawaii komweko imaphunzira Baibulo kamodzi pa mlungu ndi mwini wake wa malo ena okonzerapo nsapato zong’ambika. Phunzirolo amachitira pagome pokonzera nsapato pomwepo. Amati kukabwera munthu wamalonda, Mboniyo imasunthira pambali. Munthuyo akachoka iwo amapitiriza kuphunzira.

Mkulu wa kampani ija ndiponso mwini wake wa malo okonzera nsapatowo anakumana nawo chifukwa chakuti Mbonizo zinachitapo kanthu kuti ziponye “makoka” awo m’malo ena. Kodi mungaganizire malo ena m’gawo la mpingo wanu kumene mungakumaneko ndi anthu omwe m’povuta kuwapeza pa nyumba?

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi mungathe kutumikira m’gawo la chinenero china?