Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakondwera ndi “Chilamulo cha Yehova”?

Kodi Mumakondwera ndi “Chilamulo cha Yehova”?

Kodi Mumakondwera ndi “Chilamulo cha Yehova”?

“Wodala [“wachimwemwe,” NW] munthuyo . . . [amene] m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake.”​—SALMO 1:1, 2.

1. N’chifukwa chiyani tili achimwemwe pokhala atumiki a Yehova?

YEHOVA amatithandiza ndi kutidalitsa popeza ndife atumiki ake okhulupirika. N’zoona kuti timakumana ndi mayesero ambiri. Komabe, timakhalanso ndi chimwemwe chenicheni. Izi n’zosadabwitsa chifukwa chakuti tikutumikira “Mulungu wachimwemwe,” ndipo mzimu wake woyera umatipatsa chimwemwe m’mitima yathu. (1 Timoteo 1:11, NW; Agalatiya 5:22) Chimwemwe ndicho kusangalala chifukwa choyembekezera kapena kupeza chinthu chinachake chabwino. Ndipotu, kunena zoona, Atate wathu wakumwamba amatipatsa mphatso zabwino. (Yakobo 1:17) Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti ndife achimwemwe!

2. Kodi tikambirana masalmo ati?

2 Buku la Masalmo limagogomeza kwambiri za chimwemwe, ndipo chitsanzo chake ndi Salmo 1 ndi 2. Otsatira Yesu Kristu oyambirira ananena kuti salmo lachiŵirili analemba ndi Davide, Mfumu ya Israyeli. (Machitidwe 4:25, 26) Wolemba salmo loyamba, amene sanatchulidwe dzina, akuyamba nyimbo yake youziridwayi ndi mawu akuti: “Wachimwemwe munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa.” (Salmo 1:1) Tiyeni tione m’nkhani ino ndiponso m’nkhani yotsatira, mmene Salmo 1 ndi 2 limatipatsira zifukwa zokhalira osangalala.

Chinsinsi Chopezera Chimwemwe

3. Malinga ndi Salmo 1:1, kodi zina mwa zifukwa zimene munthu womvera malamulo a Mulungu amakhalira wachimwemwe ndi ziti?

3 Salmo 1 limasonyeza chifukwa chimene munthu womvera malamulo a Mulungu amakhalira wachimwemwe. Pofotokoza zina mwa zifukwa zimene munthuyu amakhalira wachimwemwe, wamasalmoyu akuimba kuti: “Wachimwemwe munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m’njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.”​—Salmo 1:1.

4. Kodi Zakariya ndi Elisabeti anapereka chitsanzo chabwino chotani pa moyo wawo?

4 Kuti tikhaledi achimwemwe, tiyenera kutsatira malamulo olungama a Yehova. Zakariya ndi Elisabeti, amene anali ndi mwayi wokhala makolo a Yohane Mbatizi, “anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.” (Luka 1:5, 6) Tingakhale achimwemwe ngati tikukhala moyo woterewu ndi kukanitsitsa ‘kuyenda mu uphungu wa oipa’ kapena kutsatira malangizo awo oipa.

5. Kodi n’chiyani chingatithandize kupeŵa “njira ya ochimwa”?

5 Tikamakana maganizo a anthu oipa, ‘sitingaimirire m’njira ya ochimwa.’ Ndipo sitingapite kumene iwo amapezeka kaŵirikaŵiri, kumalo a zosangalatsa zoipa kapena malo otchuka ndi mbiri zoipa. Koma bwanji ngati takumana ndi mayesero oti tigwirizane ndi anthu ochimwa pa makhalidwe awo otsutsana ndi malemba? Zikatero, tiyenera kupempha thandizo la Mulungu kuti titsatire mawu a mtumwi Paulo akuti: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigaŵana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?” (2 Akorinto 6:14) Tikamadalira Mulungu ndiponso n’kukhala “oyera mtima,” tidzakana maganizo ndi makhalidwe a anthu ochimwa ndipo zolinga ndi zokhumba zathu zidzakhala zabwino, ndiponso tidzakhala ndi “chikhulupiriro chosanyenga.”​—Mateyu 5:8; 1 Timoteo 1:5.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchenjera ndi anthu onyoza?

6 Kuti tikondweretse Yehova, ‘sitiyenera kukhala pansi pa bwalo la onyoza.’ Ena amanyoza kumvera malamulo a Mulungu kwenikweniko, komano ‘m’masiku otsiriza’ ano, nthaŵi zambiri anthu amene kale anali Akristu ndipo tsopano n’ngampatuko ndiwo amachita kunyanya kanyozedwe kake. Mtumwi Petro anachenjeza okhulupirira anzake kuti: ‘Okondedwa, . . . choyamba, muzindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.’ (2 Petro 3:1-4) Ngati ‘sitikhala pansi pa bwalo la onyoza,’ tidzapeŵa mavuto omwe anthu onyozaŵa adzakumane nawo.​—Miyambo 1:22-27.

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera mawu a pa Salmo 1:1?

7 Tikapanda kumvera mawu otsegulira Salmo 1, tingathe kutaya zinthu zauzimu zimene tapeza pophunzira Malemba. Ndipo ngati tingafike potero, moyo wathu ungathe kuipa kwambiri. Kutsatira malangizo a anthu oipa ndicho chingakhale chiyambi cha kubwerera kwathu m’mbuyo mwauzimu. Kenako tingayambe kumacheza nawo pafupipafupi. M’kupita kwa nthaŵi, tingafike mpaka pokhala anthu ampatuko ndiponso onyoza, anthu opanda chikhulupiriro. N’zoonekeratu kuti kugwirizana ndi anthu oipa kungatilimbikitse kukhala ndi mtima wosaopa Mulungu ndipo kungasokoneze unansi wathu ndi Yehova Mulungu. (1 Akorinto 15:33; Yakobo 4:4) Tisalole zimenezi kutichitikira!

8. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziganizira zinthu zauzimu nthaŵi zonse?

8 Pemphero lingatithandize kuti tiziganizira zinthu zauzimu nthaŵi zonse ndi kupeŵa kuyanjana ndi anthu oipa. Paulo analemba kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” Mtumwiyu analimbikitsa kulingalira zinthu zoona, zolemekezeka, zolungama, zoyera, zokongola, zomveka zokoma, za kukoma mtima, ndi zotamandika. (Afilipi 4:6-8) Tiyeni titsatire malangizo a Paulo ameneŵa ndipo tisalole makhalidwe athu kufika pofanana ndi a anthu oipa.

9. Ngakhale kuti timakana makhalidwe oipa, kodi timayesetsa kuwathandiza motani anthu a mitundu yonse?

9 Ngakhale kuti timakana makhalidwe oipa, koma timalalikira mosamala kwa ena, monga momwe mtumwi Paulo analankhulira kwa kazembe wachiroma Felike “za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza.” (Machitidwe 24:24, 25; Akolose 4:6) Timalalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu a mitundu yonse, ndipo timakhala nawo mokoma mtima. Timakhulupirira kuti anthu “ofuna moyo wosatha” adzakhala okhulupirira ndipo adzakondwera ndi chilamulo cha Mulungu.​—Machitidwe 13:48, NW.

Amakondwera ndi Chilamulo cha Yehova

10. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhomereza m’maganizo ndi mumtima mwathu zimene tikuŵerenga paphunziro laumwini?

10 Ponena za munthu wachimwemwe, wamasalmoyu akunenanso kuti: “M’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.” (Salmo 1:2) Popeza ndife atumiki a Mulungu, ‘timakondwera ndi chilamulo cha Yehova.’ Kukakhala kotheka, panthaŵi ya phunziro laumwini ndiponso panthaŵi yosinkhasinkha, timatha kuŵerenga ‘molingalira,’ kapena kuti chapansipansi, motulutsa mawu. Kuchita zimenezi pamene tikuŵerenga chigawo china chilichonse cha m’Malemba kudzatithandiza kukhomereza m’maganizo ndi mumtima mwathu zimene tikuŵerengazo.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuŵerenga Baibulo “usana ndi usiku”?

11 “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatilimbikitsa kuti tiziŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. (Mateyu 24:45) Chifukwa chakuti timafunitsitsa kudziŵa bwino uthenga wa Yehova kwa anthu, ndi bwino kuti tiziŵerenga Baibulo “usana ndi usiku,” kutanthauza kuti tingatero ngakhalenso panthaŵi yomwe tulo sitikubwera chifukwa cha zinthu zinazake. Petro anatilangiza kuti: “Lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nawo kufikira chipulumutso.” (1 Petro 2:1, 2) Kodi mumakondwera ndi kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndiponso kusinkhasinkha Mawu a Mulungu ndi zolinga zake usiku? Wamasalmo ankatero.​—Salmo 63:6.

12. Ngati timakondwera ndi chilamulo cha Yehova kodi tingachite chiyani?

12 Kuti tidzakhale ndi chimwemwe kwamuyaya tiyenera kukondwera ndi chilamulo cha Yehova. N’changwiro ndi cholungama, ndipo kusunga chilamulochi kumadzetsa mphoto yaikulu. (Salmo 19:7-11) Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Iye wakupenyerera m’lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala [“wachimwemwe,” NW] m’kuchita kwake.” (Yakobo 1:25) Ngati timakondweradi ndi chilamulo cha Yehova, sitingathe tsiku osaganizirako zinthu zauzimu. Inde, tingathe kumafuna ‘kusanthula zakuya za Mulungu’ ndi kuika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wathu.​—1 Akorinto 2:10-13; Mateyu 6:33.

Amakhala Ngati Mtengo

13-15. Kodi tingakhale motani monga mtengo wookedwa m’mphepete mwa madzi ambiri?

13 Popitiriza kufotokoza za munthu wolungama, wamasalmoyu akuti: “Akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:3) Mofanana ndi anthu ena onse opanda ungwiro, nafenso amene tikutumikira Yehova timakumana ndi mavuto m’moyo. (Yobu 14:1) Tingathe kuzunzidwa ndiponso kukumana ndi mayesero ena amitundumitundu chifukwa cha chikhulupiriro chathu. (Mateyu 5:10-12) Komabe, ndi thandizo la Mulungu timatha kupirira bwinobwino mayesero ameneŵa, monga mmene mtengo umene ukukula bwino umakhalira wolimba kukamaomba mphepo yamphamvu.

14 Mtengo wookedwa pafupi ndi malo amene saphwa madzi suuma panyengo yadzuŵa kapena panthaŵi ya chilala. Ngati timaopa Mulungu, ndiye kuti mphamvu zathu zimachokera ku Gwero losaphwa, yemwe ndi Yehova Mulungu. Paulo ankadalira Mulungu kuti amuthandiza ndipo anafika ponena kuti: “Ndikhoza zonse mwa Iye [Yehova] wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Mzimu woyera wa Yehova ukamatitsogolera ndi kutithandiza mwauzimu, sitifota, n’kukhala osabala zipatso kapena akufa mwauzimu. Timabala zipatso potumikira Mulungu ndiponso timasonyeza chipatso cha mzimu wake.​—Yeremiya 17:7, 8; Agalatiya 5:22, 23.

15 Pogwiritsira ntchito liwu la Chihebri lomwe linamasuliridwa kuti “akunga,” wamasalmoyu anali kuyerekezera zinthu ziŵiri zosiyana ngakhale kuti n’zofanana penapake. Anthu n’ngosiyana ndi mitengo, komabe n’zoonekeratu kuti kukula bwino kwa mtengo wookedwa pafupi ndi madzi ambiri kunakumbutsa wamasalmoyu za kulemera kwauzimu kwa anthu amene ‘m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chawo.’ Ngati timakondwera ndi chilamulo cha Mulungu, masiku athu angathe kuchuluka ngati a mtengo. Ndipotu, tingathe kudzakhala kwamuyaya.​—Yohane 17:3.

16. N’chifukwa chiyani ‘zonse zimene timachita timapindula nazo’ ndipo zimenezi zimachitika motani?

16 Pamene tikukhala moyo wolungama, Yehova amatithandiza kupirira ziyeso ndi mavuto. Timakhala osangalala ndiponso obala zipatso potumikira Mulungu. (Mateyu 13:23; Luka 8:15) ‘Zonse zimene timachita timapindula nazo’ chifukwa chakuti cholinga chathu chachikulu ndicho kuchita chifuniro cha Yehova. Popeza kuti zofuna zake zimapindula nthaŵi zonse ndipo timakondwera ndi malamulo ake, timakhala olemera mwauzimu. (Genesis 39:23; Yoswa 1:7, 8; Yesaya 55:11) Umu ndi mmene zimakhalira ngakhale panthaŵi yomwe tikukumana ndi mavuto.​—Salmo 112:1-3; 3 Yohane 2.

Oipa Amaoneka Ngati Zinthu Zikuwayendera Bwino

17, 18. (a) Kodi wamasalmo anayerekezera anthu oipa ndi chiyani? (b) Ngakhale kuti zinthu zingamawandere bwino anthu oipa, n’chifukwa chiyani sakhala otetezeka mpaka kalekale?

17 Moyo wa oipa n’ngosiyana kwambiri ndi moyo wa olungama! Anthu oipa angamaoneke ngati zinthu zikuwayendera bwino kwa kanthaŵi, koma sikuti zimawayendera bwino mwauzimu. Tikuona zimenezi m’mawu otsatira a wamasalmoyu, akuti: “Oipa satero ayi; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo. Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama.” (Salmo 1:4, 5) Onani kuti wamasalmoyu akuti, “oipa satero ayi.” Iye akutanthauza kuti iwo sali ngati anthu oopa Mulungu, omwe wangowayerekezera kumene ndi mitengo yosafa msanga, yobala zipatso.

18 Ngakhale anthu oipa zitamawayendera bwino, sakhala otetezeka mpaka kalekale. (Salmo 37:16; 73:3, 12) Iwo n’ngofanana ndi munthu wolemera koma wopusa amene Yesu anam’tchula m’fanizo lina atapemphedwa kuti aweruze nkhani yokhudza chuma chamasiye. Yesu anauza anthu omwe analipo kuti: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” Pamfundoyi, Yesu anapereka fanizo lakuti mbewu za m’munda wa munthu wina wolemera zinabereka bwino kwambiri moti iye anakonza zopasula nkhokwe zake ndi kumanga zina zikuluzikulu zoti zikwane chuma chake chonse. Kenako munthuyo anakonza zakuti azingodya, kumwa, ndi kumakondwera. Koma Mulungu anati: “Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?” Pophera mphongo mfundoyi, Yesu anawonjezera ndi mawu akuti: “Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.”​—Luka 12:13-21.

19, 20. (a) Fotokozani mmene kale ankapunthira ndi kupetera mbewu. (b) N’chifukwa chiyani anthu oipa akuyerekezedwa ndi makoko?

19 Oipa alibe “chuma cha kwa Mulungu.” Motero, amakhala osatetezeka ngati mungu kapena kuti makoko a mbewu monga tirigu amene amangouluzika mosavuta. M’nthaŵi zakale, akatha kukolola mbewu monga tirigu, ankapita nazo popunthira. Aŵa anali malo osalazidwa pomwe nthaŵi zambiri pankakhala pokwera. Pamenepo, iwo ankapuntha mbewuzo pofuna kuti maso a mbewuzo achoke m’makoko ake. Ankatero pozipondaponda ndi chinthu changati galeta chokokedwa ndi ziŵeto chimene kunsi kwake kunkakhala miyala kapena zitsulo zakuthwa. Kenako, pankakhala ntchito yosiyanitsa maso a mbewuzo ndi makoko ake potapa mbewuzo ndi chokokolera n’kumaziuluzira m’mwamba. (Yesaya 30:24) Maso a mbewuzo ankagwa pamalo opunthirawo, pamene udzu ndiponso makoko ankauluzikira kutali chifukwa cha mphepo. (Rute 3:2) Akatha kusefa mbewuzo pofuna kuchotsa miyala ndi zinthu zina zotero, ankakazisunga kapena kukazipera. (Luka 22:31) Koma n’kuti makoko ake kapena kuti mungu wake zitauluzika.

20 Mofanana ndi maso a mbewu omwe amagwa pansi ndi kukasungidwa pamene makoko akuuluzika ndi mphepo, nawonso olungama adzatsala ndipo oipa adzachotsedwa. Motero ndife osangalala kuti posachedwapa anthu ochita zoipa oterowo sadzakhalakonso. Iwo kulibe, anthu okondwera ndi chilamulo cha Yehova adzadalitsidwa kwambiri. Zoonadi, pomaliza pake anthu omvera adzalandira mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha.​—Mateyu 25:34-46; Aroma 6:23.

“Mayendedwe a Olungama” N’ngodalitsika

21. Kodi Yehova ‘amadziŵa mayendedwe a olungama’ m’lingaliro lotani?

21 Salmo loyambali likumaliza ndi mawu aŵa: “Yehova adziŵa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.” (Salmo 1:6) Kodi Mulungu ‘amadziŵa mayendedwe a olungama’ m’lingaliro lotani? Ngati moyo wathu n’ngolungama, tisakaike kuti Atate wathu wakumwamba amaona kuti tikutsatira malamulo ake ndipo amationa kuti ndife atumiki ake ovomerezeka. Ndiye tingathe, ndipo tiyenera kutaya nkhaŵa zathu zonse kwa iye tili ndi chikhulupiriro chakuti iye amatisamaliradi.​—Ezekieli 34:11; 1 Petro 5:6, 7.

22, 23. Kodi n’chiyani chidzachitikire oipa ndi olungama?

22 “Mayendedwe a olungama” adzakhalapo kosatha, koma anthu oipa amene safuna kusintha adzafafanizidwa chifukwa choŵeruzidwa ndi Yehova. Ndipo adzathera pamodzi ndi “mayendedwe,” kapena kuti makhalidwe awo. Sitikayikira kuti mawu a Davide otsatiraŵa adzakwaniritsidwa. Mawuwo amati: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:10, 11, 29.

23 Tidzakhalatu ndi chimwemwe chachikulu tikadzapatsidwa mwayi wokhala m’paradaiso padziko lapansi panthaŵi yomwe oipa sadzakhalakonso! Nthaŵi imeneyo ofatsa ndi olungama adzakhala pamtendere weniweni chifukwa chakuti adzakondwera ndi “chilamulo cha Yehova” nthaŵi zonse. Koma nthaŵi imeneyo isanakwane, payenera kuchitika zinthu zimene Yehova watsimikiza. (Salmo 2:7a) Nkhani yotsatirayi itithandiza kuona kuti Yehova watsimikiza zotani ndiponso kuti zikutikhudza motani ifeyo komanso anthu ena onse.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani munthu woopa Mulungu amakhala wachimwemwe?

• Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti timakondwera ndi chilamulo cha Yehova?

• Kodi munthu angakhale bwanji ngati mtengo wolandira madzi ambiri?

• Kodi mayendedwe a olungama n’ngosiyana motani ndi mayendedwe a oipa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

Pemphero lingatithandize kupeŵa kuyanjana ndi anthu oipa

[Chithunzi patsamba 12]

N’chifukwa chiyani munthu wolungama ali ngati mtengo?