Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kudziŵitsa Anthu Dzina la Yehova”

“Kudziŵitsa Anthu Dzina la Yehova”

“Kudziŵitsa Anthu Dzina la Yehova”

PADZIKO lonse, anthu amayamikira magazini a Nsanja ya Olonda ndiponso Galamukani!, chifukwa chakuti n’ngothandiza mwauzimu ndiponso amaphunzitsa munthu zinthu. Mogwirizana ndi zimenezi, posachedwapa munthu wina woŵerenga magaziniŵa ku France analemba kalata yotsatirayi:

“Ndine mtsikana amene kwathu ndi ku Africa ndipo sukulu sindinapite nayo patali. Posachedwapa ndinayamba kuŵerenga magazini anu. Nkhani zake zinandichititsa chidwi motero ndazindikira kufunika kokonda kuŵerenga. Mwandithandiza kudziŵa mawu ochuluka ndipo panopo ndayamba kutha kulemba kalata popanda kulakwitsalakwitsa.

“Zimandigometsa kuona kuti mumalongosola nkhani zosiyanasiyana zokhudza anthu, dziko lapansili, ndiponso Mlengi. Nkhani zake n’zomveka bwino kwambiri moti zimam’pangitsa munthu kufuna kuyamba kukonda kuŵerenga. Mulibe mnzanu pankhani yophunzitsa anthu osiyanasiyana panthaŵi imodzi.

“Zimandigometsanso kuona kuti zonsezi simuzichita pofuna ndalama ayi koma chifukwa chongofuna kudziŵitsa anthu dzina la Yehova. Ndikudziŵa kuti Yehova amasangalala nanu, ndipo ndikukuthokozani. Musasiye kupempha Mlengi wathuyu kuti azikulimbikitsani kuphunzitsa ena.”

A Mboni za Yehova pakalipano akuchita ntchito yophunzitsa anthu Baibulo m’mayiko 235. Magazini ya Nsanja ya Olonda amaifalitsa m’zinenero 148 ndipo Galamukani! amaifalitsa m’zinenero 87. Magazini ameneŵa sasindikizidwa n’cholinga chotama munthu aliyense. Malangizo ochokera m’Baibulo ndiponso nkhani zatsopanodi zimene zimapezeka m’magaziniŵa cholinga chake chimakhala kulemekeza Mlengi, amene amati: “Ine ndine Yehova, . . . amene ndikuphunzitsa kupindula.” (Yesaya 48:17) Nanunso pindulani ndi kuŵerenga Malemba Opatulika nthaŵi zonse pogwiritsira ntchito magazini othandiza kuphunzira Baibulo ameneŵa.