Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yense Wochenjera Amachita Mwanzeru”

“Yense Wochenjera Amachita Mwanzeru”

“Yense Wochenjera Amachita Mwanzeru”

ZIMENE limatilangiza Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, ‘n’zofunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa.’ (Salmo 19:7-10) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “malamulo a wanzeru [Yehova] ndiwo kasupe wa moyo, apatutsa ku misampha ya imfa.” (Miyambo 13:14) Tikawagwiritsira ntchito, malangizo a m’Malemba sikuti amangotithandiza kukhala moyo wabwino koma amatithandizanso kupeŵa misampha imene ingawononge moyo wathuwo. Motero, m’pofunika kwambiri kufunafuna nzeru za m’Malemba n’kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene taphunzira.

Malingana ndi zimene lemba la Miyambo 13:15-25 limanena, Mfumu Solomo ya dziko lakale la Israyeli inapereka malangizo amene amatithandiza kuchita zinthu mwanzeru kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso wautali. * Mfumuyi inagwiritsira ntchito miyambi yosapita m’mbali posonyeza kuti Mawu a Mulungu angatithandize kuti tiziyanjana ndi ena, tizikhala okhulupirika mu utumiki wathu, tizimvera malangizo, ndiponso tizisankha anzathu mwanzeru. Inatchulaponso kuti n’kwanzeru kusiyira ana athu choloŵa komanso kuwalanga mwachikondi.

Nzeru Yabwino Imapatsa Chisomo

Solomo anati: “Nzeru yabwino ipatsa chisomo; koma njira ya achiwembu ili makolokoto.” (Miyambo 13:15) Buku lina linati mawu amene anawamasulira kuti “nzeru yabwino,” kapena kuti kumvetsetsa bwino, “amanena za kutha kuganiza m’njira zosiyanasiyana zosonyeza nzeru zozama.” Munthu amene ali ndi nzeru zoterezi savutika kupeza chisomo kapena kuti kuyanjidwa ndi anthu ena.

Taganizirani nzeru zimene Paulo anasonyeza pa zimene anachita ndi Mkristu mnzake Filemoni pomwe ankabweza kapolo wa Filemoniyo wotchedwa Onesimo, yemwe anathaŵa koma pambuyo pake n’kudzakhala Mkristu. Paulo analimbikitsa Filemoni kuti amulandirenso bwino Onesimo, monga mmene angalandirire Pauloyo. Ndipotu, Paulo ananena kuti ngati Onesimo ali ndi ngongole iliyonse ndi Filemoni, Pauloyo anadzipereka kubweza ngongoleyo m’malo mwake. Komatu Paulo akanatha kugwiritsira ntchito mphamvu zake n’kulamula Filemoni kuti am’landire bwino Onesimo. M’malomwake mtumwiyu anaganiza zoyendetsa nkhaniyi mosamala ndiponso mwachikondi. Potero, Paulo sanakayikire kuti Filemoni amvera mochita kufuna yekha, n’kuchita zina kuwonjezera pa zinthu zimene Pauloyu anam’pempha. Kodi nafenso sitiyenera kuchita chimodzimodzi ndi okhulupirira anzathu?​—Filemoni 8-21.

Komano njira ya achiwembu, ili makolokoto kapena kuti “n’njolimba.” Kodi n’njolimba motani? Malingana n’kunena kwa katswiri wina wa maphunziro, mawu amene anatchula pamenepa amatanthauza “chinthu cholimba, ndipo amanena za kukakala mtima kwa anthu oipa. . . . Munthu amene watsimikiza kuchita zinthu zoipa, osamvera ngakhale pang’ono malangizo anzeru a anzake, ndiye kuti akupita kuchiwonongeko.”

Solomo anapitiriza kunena kuti: “Yense wochenjera amachita mwanzeru; koma wopusa aonetsa utsiru.” (Miyambo 13:16) Munthu wochenjerayu si kamberembere ayi. Kuchenjera kumeneku n’koyenderana ndi kudziŵa bwino zinthu ndipo n’kuchenjera kwa munthu wanzeru, amene amayamba waganiza kaye mosamala asanachite chinthu. Munthu wochenjera chonchi amadziletsa akamanenedwa kapena kunyozedwa ali wosalakwa. Mwapemphero, amayesetsa kuonetsa chipatso cha mzimu woyera n’cholinga choti zimenezi zisam’pweteke mtima kwambiri. (Agalatiya 5:22, 23) Munthu wochenjera m’njira imeneyi salola kuti anthu ena amulakwitse. M’malomwake amaugwira mtima, moti amapeŵa mapokoso amene anthu amtima wapachala amachita kaŵirikaŵiri ena akawalakwira.

Munthu wochenjera amaganiza kaye mofatsa asanachite zinthu. Iye amadziŵa kuti zinthu zanzeru kaŵirikaŵiri sizichitika mongolota, mongotengeka maganizo, kapena mongotsatira zimene anthu ambiri akuchita. Motero, amayamba waiganizira kaye bwinobwino nkhaniyo. Amaona kaye chilichonse chofunikira kudziŵa n’kuganizira njira zina zimene angayendetsere nkhaniyo. Kenaka amafufuza m’Malemba n’kuona malamulo kapena mfundo za m’Baibulo zimene zikugwirizana ndi nkhaniyo. Njira ya munthu wotere imakhala yowongoka nthaŵi zonse.​—Miyambo 3:5, 6.

“Mtumiki Wokhulupirika Alamitsa”

Poti ndife Mboni za Yehova, tinapatsidwa ntchito yolengeza uthenga wochokera kwa Mulungu. Mwambi wotsatirawu ukutithandiza kuti tikhalebe okhulupirika pokwaniritsa ntchito tapatsidwayi. Mwambiwu ukuti: “Mthenga wolakwa umagwa m’zoipa; koma mtumiki wokhulupirika alamitsa.”​Miyambo 13:17.

Pamenepa akugogomezera kwambiri khalidwe la mthengayo. Kodi zingatani ngati mthengayu wakhotetsa kapena kusintha dala uthengawo chifukwa cha mtima woipa? Kodi sangalangidwe nazo? Taganizirani za mtumiki wa mneneri Elisa dzina lake Gehazi, amene chifukwa cha dyera anakanena uthenga wabodza kwa mkulu wankhondo wa ku Aramu wotchedwa Namani. Khate limene Namani anachiritsidwa linapita kwa Gehazi. (2 Mafumu 5:20-27) Nanga kodi zingatani ngati mthengayo wakhala wosakhulupirika n’kungosiyiratu kulengeza uthengawo? “[Ukapanda] kum’chenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m’mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa pa dzanja lako.”​—Ezekieli 33:8.

Komano, mtumiki wokhulupirika amadzilamitsa yekha komanso anthu amene akuwauza uthengawo. Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Taganizirani mmene kulengeza uthenga wabwino waufumu kumalamitsira. Kumalimbikitsa anthu amtima wabwino n’kuwachititsa kuti atsate choonadi chimene chimawamasula. (Yohane 8:32) Ngakhale anthu atakana kumvetsera uthengawo, mthenga wokhulupirika ‘adzalanditsa moyo wake.’ (Ezekieli 33:9) Tiyeni tiyesetse kusanyalanyaza ntchito yolalikira imene tapatsidwayi. (1 Akorinto 9:16) Ndipo nthaŵi zonse tizikhala osamala ‘kulalikira mawu,’ popanda kuwachepetsa mphamvu kapena kuwakometsera pofeŵetsa mfundo zake.​—2 Timoteo 4:2.

“Wolabadira Chidzudzulo Adzalemekezedwa”

Kodi munthu wanzeru ayenera kudana ndi malangizo aliwonse othandiza amene angalandire? Miyambo 13:18 amati: “Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa; koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa.” N’chinthu chanzeru kumvera ngakhale tikamadzudzulidwa pamene sitinachite kupempha. Malangizo abwino amatha kutithandiza kwambiri panthaŵi imene ifeyo sitikuzindikira kuti tikufunikira malangizo otero. Kumvera malangizo otere kungatichepetsere nkhaŵa n’kutithandiza kupeŵa zoopsa. Koma kuwanyalanyaza kungatichotsere ulemu.

Timalimbikitsidwa kwambiri wina akatiyamikira ngati tikuyenereradi kuyamikiridwa. Koma tiyeneranso kuyembekezera kudzudzulidwa ndipo tizivomereza ena akatidzudzula. Taganizirani makalata aŵiri amene mtumwi Paulo analembera Timoteo. Ngakhale kuti Paulo anamuyamikira Timoteo pa chikhulupiriro chake, m’makalatamo analembamonso malangizo ambirimbiri opita kwa Timoteo. Momasuka, Paulo anamulangiza Timoteo, yemwe anali wachinyamata, pankhani ya kukhalabe wokhulupirika ndiponso kukhala ndi chikumbumtima chabwino, kukhala bwino ndi ena mumpingo, kukhala wodzipereka kwa Mulungu komanso wokhutira ndi zomwe ali nazo, kuphunzitsa ena, kulimbana ndi mpatuko, ndiponso kukwaniritsa utumiki wake. Achinyamata mumpingo ayenera kufuna ndiponso kuvomereza malangizo a achikulire odziŵa zinthu.

‘Yendani ndi Anzeru’

Mfumu yanzeruyi inati: “Chifuniro chikondweretsa moyo chitachitidwa; koma kusiya zoipa kunyansa opusa.” (Miyambo 13:19) Pa za tanthauzo la mwambi umenewu, buku lina linati: “Munthu akakwaniritsa cholinga chake, amakhaladi wokhutira mochoka pansi pamtima . . . Pakuti zimakhala zosangalatsa kwambiri munthu ukakwaniritsa zolinga zako, ndiye kutinso kupeŵa zoipa kuyenera kuti kumawaipira kwambiri anthu opusa. Zolinga zawo angathe kuzikwaniritsa m’njira zoipa basi, ndipo ngati atati asiye zoipa, sangakhalenso osangalala pokwaniritsa zolakalaka zawo.” Tiyeni tiyesetse kumalakalaka zinthu zoyenera!

Anzathu angasinthe kwambiri kaganizidwe kathu, zimene timakonda, ndi zimene sitikonda! Solomo analongosola mfundo yosasintha yakuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Inde, anzathu, ngakhale amene timawaona m’zosangalatsa, pa Intaneti, ndiponso m’zoŵerenga, amasintha khalidwe lathu panopo ndiponso m’tsogolo. Motero, ndi bwino kwambiri kusankha anzathu mwanzeru!

‘Siyirani Ena Choloŵa’

Mfumu ya Israyeliyi inati: “Zoipa zilondola ochimwa; koma olungama adzalandira mphotho yabwino.” (Miyambo 13:21) Kuchita zinthu zabwino kumapindulitsa, chifukwa Yehova amasamalira anthu olungama. (Salmo 37:25) Komabe, tiyenera kuzindikira kuti “nthaŵi ndi zochitika zamwadzidzidzi’ zimatigwera tonse. (Mlaliki 9:11, NW) Kodi pali chilichonse chimene tingachite kuti tikonzekere zinthu zamwadzidzidzi?

Solomo anati: “Wabwino asiyira zidzukulu zake choloŵa.” (Miyambo 13:22a) Makolo amasiya choloŵa chamtengo wapatali kwambiri akathandiza ana awo kuphunzira za Yehova ndi kuyesetsa kumagwirizana naye kwambiri. Koma kodi sichingakhalenso chinthu chanzeru, ngati zili zotheka, kukonzeratu za chisamaliro cha banjalo m’tsogolo ngati wina wa makolo m’banjamo atamwalira mwadzidzidzi? M’madera ambiri, anthu amene ali mitu ya banja angathe kukonza zokhala ndi inshuwalansi, kulemberatu mwalamulo ndondomeko ya kagaŵidwe ka katundu wawo akadzafa, ndiponso kuikiratu padera ndalama zina.

Kodi tinganenepo chiyani pankhani ya choloŵa cha oipa? Solomo anapitiriza kunena kuti: “Wochimwa angosungira wolungama chuma chake.” (Miyambo 13:22b) Kuphatikiza pa madalitso ena aliwonse a panopo, lembali lidzakwaniritsidwa kwambiri Yehova akamadzachita zinthu zimene analonjeza, zopanga “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” ndipo mmenemo ‘mudzakhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Oipa adzakhala atachotsedwa, ndipo “ofatsa adzalandira dziko lapansi.”​—Salmo 37:11.

Munthu wanzeru amachita zinthu mozindikira ngakhale atakhala kuti alibe chuma. Miyambo 13:23 amati: “M’kulima kwa osauka muli zakudya zambiri; koma zinazo zimawonongeka posoŵa chiweruzo.” Ngakhale akhale ndi zinthu zochepa iye amatha kuzitupitsa pogwira ntchito molimbika ndiponso podalitsidwa ndi Mulungu. Koma pakasoŵeka chilungamo chuma chosaneneka chingathe kuwonongeka chonse.

‘Musazengereze Kumulanga’

Anthu opanda ungwiro amafunika kuwalanga, kungoyambira akadali ana mpaka akamakula. Mfumu ya Israyeliyi inati: “Amene aleka kukwapula mwana wake adana naye; koma wom’konda sazengereza kum’langa.”​Miyambo 13:24, Malembo Oyera.

Kukwapula mwana kumene kwatchulidwa pa Miyambo 13:24 ndi kukwapula kogwiritsa ntchito ndodo imene imasonyeza ulamuliro ndipo pa lembali ndodoyi imaimira ulamuliro wa makolo. Palembali kukwapula mwana sikuti kumatanthauza kukwapula kwenikweni. Koma, kumatanthauza kumuphunzitsa m’njira ina iliyonse kuti akhale ndi khalidwe labwino. Nthaŵi zina, kungomudzudzula mwana bwinobwino n’kokwanira kumuphunzitsa mwanayo kuti asiye khalidwe linalake loipa. Mwana wina angafunike kumudzudzula mwamphamvu ndithu. Miyambo 17:10 amati: “Chidzudzulo chiloŵa m’kati mwa wozindikira, kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri.”

Makolo akamalanga ana, nthaŵi zonse azitero mwachikondi ndiponso mwanzeru kuti anawo athandizidwe. Makolo achikondi salekerera mphulupulu za ana awo. M’malomwake iwo, amakhala tcheru kuti aletse mphulupuluzo zisanam’loŵerere kwambiri mwanayo. Inde, makolo okonda ana awo amamvera malangizo a Paulo akuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”​—Aefeso 6:4.

Nanga bwanji ngati makolo ali olekerera ndipo samuphunzitsa mwana m’njira yoyenerera? Kodi makolo otere angadzayamikiridwe m’tsogolo chifukwa choti anali olekerera? Ayi ndithu! (Miyambo 29:21) Baibulo limati: “Mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) Mukapanda kuonetsa ulamuliro wanu monga makolo zimasonyeza kuti sizikukhudzani kapena kuti anawo simuwakonda. Komabe, kuonetsa ulamuliro wanu moganizira koma mosalekerera, kumasonyeza chikondi.

Munthu wanzeru ndiponso woongoka mtima amene amachita zinthu mozindikiradi amadalitsidwa. Solomo anatitsimikizira kuti: “Wolungama adya nakhutitsa moyo wake; koma mimba ya oipa idzasoŵa.” (Miyambo 13:25) Yehova amadziŵa zimene zingatipindulitse m’njira zosiyanasiyana pa moyo wathu, kaya n’zokhudza moyo wathu wa m’banja, ubwenzi wathu ndi ena, utumiki wathu, kapenanso kupatsidwa malangizo. Ndipo tikachita mwanzeru potsatira malangizo a m’Mawu ake, ndithu tidzakhala ndi moyo wosangalala kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

[Chithunzi patsamba 28]

Munthu wochenjera amadziletsa kuti asalankhule molakwika akamadzudzulidwa ali wosalakwa

[Chithunzi patsamba 29]

Wolengeza Ufumu wokhulupirika amachita zinthu zambiri zabwino

[Chithunzi patsamba 30]

Ngakhale kuti timalimbikitsidwa ena akamatiyamikira, tiyenera kumvera ena akamatilangiza

[Chithunzi patsamba 31]

Kholo lachikondi sililekerera mphulupulu za mwana wake