Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Boma la Ufumu wa Mulungu Likuchita Zooneka

Boma la Ufumu wa Mulungu Likuchita Zooneka

Boma la Ufumu wa Mulungu Likuchita Zooneka

“Kodi zingatheke bwanji kuti mayiko ambirimbiri chonchi agwirizane pamene mayikoŵa ali ndi zikhalidwe zosiyanasiyana komanso n’ngotukuka mosiyanasiyananso? Anthu ena anenapo kuti chimene chingagwirizanitse mayiko ndicho nkhondo yochokera ku pulaneti ina basi.”​—Inatero nyuzipepala ya ku Australia ya The Age.

KODI nkhondo yochokera ku pulaneti ina ingagwirizanitse mayiko? Kaya nkhondo imeneyo ingagwirizanitsedi mayiko kapena ayi, ulosi wa m’Baibulo umanena kuti posachedwapa kukubwera nkhondo imene idzachititse kuti mayiko onse a padziko lapansi agwirizane. Ndipotu n’zoonadi kuti nkhondoyi idzachokera kwina osati padziko lapansi pano.

Mfumu Davide ya dziko la Israyeli lakale ananena za nkhaniyi mwaulosi. Mouziridwa ndi Mulungu iye analemba kuti: ‘Mafumu a dziko lapansi anachita upo pamodzi ndi akulu, kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti, Tidule zomangira zawo, titaye nsinga zawo.’ (Salmo 2:2, 3; Machitidwe 4:25, 26) Onani kuti olamulira a dziko lapansi adzasonkhana pamodzi kuti alimbane ndi Yehova, Mlengi wa chilengedwe chonse, komanso kuti alimbane ndi wodzozedwa wake, kapena kuti Mfumu yake yoikidwa, Yesu Kristu. Kodi zimenezi zidzachitika bwanji?

Malingana ndi kaŵerengedwe ka nthaŵi ka m’Baibulo, komanso malingana ndi maulosi a m’Baibulo amene akwaniritsidwa kale, Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba m’chaka cha 1914, ndipo Yesu Kristu ndiye Mfumu yake. * Panthaŵi imeneyo mayiko a padziko lapansi lino anagwirizana pa mfundo imodzi. M’malo mogonjera ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu watsopanowu, iwo anagundika kumenyanira ulamuliro pa Nkhondo Yaikulu, kapena kuti nkhondo yoyamba ya padziko lonse.

Kodi Yehova Mulungu amaziona motani zimene anthu olamuliraŵa anachita? “Wokhala m’mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza. Pomwepo adzalankhula nawo mu mkwiyo wake, nadzawaopsa m’ukali wake.” Kenaka Yehova adzauza Mwana wake, yemwe ali Mfumu yodzozedwa ya Ufumu wake kuti: “Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale choloŵa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako. Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.”​—Salmo 2:4, 5, 8, 9.

Kugonjetseratu mayiko otsutsana ndi Mulungu pogwiritsira ntchito ndodo yachitsulo kudzachitika pa Armagedo, kapena kuti Harmagedo. Buku lomalizira la m’Baibulo la Chivumbulutso, limalongosola kuti nkhondo yotsiriza imeneyi ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” imene “mafumu a dziko lonse” akuwasonkhanitsirako. (Chivumbulutso 16:14, 16) Chifukwa cha ziwanda, mayiko a padziko lapansi pano adzafikadi pogwirizana pa mfundo imodzi, mfundo yoti achite nkhondo ndi Mulungu Wamphamvuyonse.

Nthaŵi imene anthu adzasonkhane pamodzi kuti alimbane ndi ulamuliro wa Mulungu ikuyandikira mofulumira kwambiri. Komatu kugwirizana kwawoku sikudzawapindulitsa iwowo paokhapaokha. M’malomwake, zochita zawozi zidzakhala chiyambi cha mtendere umene anthu onse akhala akuudikira kwa nthaŵi yaitali. Kodi zidzatero motani? Pankhondo yotsiriza imeneyi, Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [a padziko lapansi]. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Ufumu wa Mulungu, osati bungwe lina lililonse la anthu, ndiwo boma limene lidzabweretse mtendere wapadziko lonse umene anthu amaulakalaka.

Wolamulira Wamkulu wa Boma la Ufumu

Umenewu ndiwo Ufumu umene anthu ambiri oona mtima akhala akuupempherera ponena kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Ufumu wa Mulungu si chinthu chomwe chimangokhala mumtima mwa anthu ayi, koma ndi boma lenileni limene lachita zinthu zodabwitsa kwambiri chilikhazikitsireni kumwamba mu 1914. Tiyeni tione zinthu zina zikuluzikulu zimene zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni ndipo ukuchita zooneka masiku ano.

Choyamba n’chakuti, Ufumuwu uli ndi gawo lamphamvu loyang’anira zamalamulo m’njira yabwino kwambiri ndipo wotsogolera gawo limeneli ndi Mfumu yoikidwa, Yesu Kristu. M’chaka cha 33 Kristu Atabwera, Yehova Mulungu anam’patsa Yesu Kristu udindo wokhala Mutu wa Mpingo wachikristu. (Aefeso 1:22) Kuchokera panthaŵi imeneyi, Yesu wakhala akuchita umutu wake, motero wasonyeza luso lake lotha kulamulira. Mwachitsanzo, ku Yudeya kutagwa njala yaikulu, m’zaka 100 zoyambirira, mpingo wachikristu unachitapo kanthu mwamsanga pothandiza anthu ake. Unakonza ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi vutoli, ndipo Barnaba ndi Saulo anatumidwa kuchokera ku Antiokeya atatenga chithandizo.​—Machitidwe 11:27-30.

Yesu Kristu panopo amatha kuchita zinthu zoposa pamenepa popeza kuti tsopano boma la Ufumu linayamba kugwira ntchito. Kukachitika masoka monga zivomezi, njala, zigumula, mphepo zamkuntho, kapena mapiri akaphulika, mpingo wachikristu wa Mboni za Yehova umachitapo kanthu mwamsanga pothandiza okhulupirira ndiponso anthu ena okhala m’madera okhudzidwa ndi zimenezi. Mwachitsanzo, ku El Salvador kutachitika zivomezi zoopsa mu January ndi February 2001, m’madera onse a dzikolo anakonza ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi vutoli ndipo magulu a Mboni za Yehova ochokera ku Canada, Guatemala, ndi ku United States anapita kukathandiza. Malo atatu mwa malo awo olambirirapo kuphatikizaponso nyumba zoposa 500 zinamangidwanso m’kanthaŵi kochepa chabe.

Anthu Olamulidwa ndi Boma la Ufumu

Chiukhazikitsireni mu 1914, Ufumu wakumwamba wa Mulungu wakhala ukusonkhanitsa ndi kulinganiza anthu ake kuchokera m’mitundu yosiyanasiyana ya anthu padziko lonse. Zimenezi zikukwaniritsa ulosi wochititsa chidwi kwambiri umene Yesaya analemba womwe umati: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova [kulambira koona komwe kuli pamwamba pa kulambira kwina konse] lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, . . . mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.” Ulosiwu umasonyeza kuti “anthu ambiri” adzapita kuphiri limenelo ndi kuvomereza malangizo ndiponso malamulo a Yehova.​—Yesaya 2:2, 3.

Ntchito imeneyi yachititsa kuti pakhale gulu lapadera kwambiri m’nthaŵi ino, gulu la abale apadziko lonse la Akristu oposa 6,000,000 amene ali m’mayiko opitirira 230. Pa misonkhano ya mayiko ya Mboni za Yehova, anthu odzaona zochitika pamsonkhanopo nthaŵi zambiri amadabwa kuona chikondi, mtendere, ndiponso kugwirizana kumene kumakhalapo pakati pa anthu ambirimbiri, ngakhale kuti anthuwo amakhala a m’mayiko osiyana, chikhalidwe chosiyana, ndiponso chinenero chosiyana. (Machitidwe 10:34, 35) Kodi simukuvomereza kuti pokhapokha ngati boma lili lodziŵadi ntchito yake, lokhazikika ndiponso lochita zoonekadi m’pamene lingathe kugwirizanitsa anthu amitundu yambirimbiri kuti azikhala pamodzi mwamtendere?

Ufumu wa Mulungu Pankhani ya Maphunziro

Boma lililonse limakhala ndi malamulo amene limafuna kuti nzika zake zizitsatira, ndipo aliyense amene akufuna kulamulidwa ndi bomalo amayenera kutsatira malamulowo. Nawonso Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo amene aliyense amene ali woyenerera kukhala nzika yake ayenera kumatsatira. Komano kuthandiza anthu ambirimbiri omwe anakulira moyo wosiyanasiyana kuti avomereze ndiponso kuti ayambe kutsatira malamulo ofanana ndi chintchito chovuta kwambiri. Motero, chifukwa china chosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni n’chimenechi, chakuti ukuchita ntchito yothandiza kwambiri ya maphunziro amene amasintha maganizo komanso mitima ya anthu.

Kodi boma la Ufumuli limachita bwanji ntchito yovuta imeneyi? Mwa kulalikira ‘kunyumba ndi nyumba’ monga ankachitira atumwi ndiponso mwa kuphunzitsa anthu paokhapaokha za Mawu a Mulungu. (Machitidwe 5:42; 20:20) Kodi maphunziro otereŵa n’ngothandiza motani? Jacques Johnson, yemwe ndi wansembe wa Katolika, analemba nkhani m’nyuzipepala ina ya ku Canada imene imatuluka kamodzi pamlungu ndipo ananena kuti nthaŵi ina iyeyo anayesapo kuletsa mayi winawake kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Iye anati “Ndinadabwa kwambiri ndipo ndinazindikira kuti ndikungodzivutitsa.” Ananenanso kuti: “Ndinayamba kuzindikira kuti pa miyezi ingapo imeneyo azimayi a Mboniwo anali atayamba kugwirizana kwambiri ndi mayiyu amene ankangokhala mobindikira. Iwo anayamba kugwirizana naye pomuthandiza, kum’pangitsa kuti akhale mnzawo, n’kugwirizana nayedi mochoka pansi pamtima. Posakhalitsa iye anayamba kulimbikira kwambiri m’chipembedzo chawochi ndipo ineyo sindikanatha n’komwe kumuletsa.” Uthenga wa m’Baibulo umene Mboni za Yehova zimaphunzitsa ndiponso khalidwe lawo lachikristu zimakhudza mitima ya anthu ambirimbiri padziko lonse monga zinakhudzira mayi amene anali Mkatolikayu.

Maphunziro a Ufumu otereŵa amalongosola makamaka za Baibulo, kulimbikitsa mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino. Amaphunzitsa anthu kuti azikondana ndi kulemekezana ngakhale atakhala kuti anakulira moyo wosiyana. (Yohane 13:34, 35) Amathandizanso anthu kuti amvere mawu akuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Chifukwa chosintha moyo wawo wakale n’kuyamba kutsatira malamulo a boma la Ufumuli mochita kufuna, anthu ambiri apeza mtendere ndi chimwemwe panopo ndiponso ali ndi chiyembekezo chosangalatsa cham’tsogolo.​—Akolose 3:9-11.

Chinthu chothandiza kwambiri kubweretsa mgwirizano wapadziko lonse umenewu ndicho magazini inoyo ya Nsanja ya Olonda. Pogwiritsira ntchito njira zolinganizidwa bwino zomasulira mabuku ndiponso makina osindikizira mabuku m’zinenero zosiyanasiyana, nkhani zikuluzikulu za mu Nsanja ya Olonda amazifalitsa nthaŵi imodzimodzi m’zinenero 135, ndipo oŵerenga opitirira 95 pa 100 aliwonse padziko lonse angaphunzire nkhanizi m’zinenero zawo panthaŵi yofanana.

Wolemba mabuku wina wa chipembedzo chotchedwa Mormon analemba mndandanda wa ntchito za umishonale zomwe zikuyenda bwino kwambiri. Pamndandandawo analembapo ntchito za zipembedzo zina, kupatulapo tchalitchi chake. Iye anatchula kuti magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, omwe amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova, ndiwo magazini abwino kwambiri ophunzitsira anthu uthenga wabwino ndipo anati: “Palibe amene anganene kuti magazini a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! amalimbikitsa anthu kuchita zinthu motayirira, chifukwatu magaziniŵa amachititsa anthu kukhala maso kwambiri, ndipotu izi n’zosoŵa m’mabuku a zipembedzo zina. Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amanena nkhani zosangalatsa zomwe zili zenizeni, zofufuzidwa bwino, ndiponso zochitikadi.”

Pali umboni wochuluka zedi wosonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni ndipo ukugwiradi ntchito yake. Mboni za Yehova zimauza anzawo “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” mosangalala, ndipo zimawalimbikitsa kuti akhale nzika za Ufumuwu. (Mateyu 24:14) Kodi inuyo zimenezi zimakusangalatsani? Inunso mungathe kulandira nawo madalitso amene munthu amapeza chifukwa chokhala ndi anzake amene akuphunzitsidwa ndiponso kuyesetsa kutsatira mfundo za Ufumuwu. Komanso zimenezi zingakuthandizeni kuti mukhale ndi chiyembekezo chodzakhala mu ulamuliro wa Ufumuwu m’dziko lapansi latsopano lolonjezedwa limene ‘mudzakhalitse chilungamo.’​—2 Petro 3:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mudziŵe nkhaniyi mwatsatanetsatane, onani mutu 10 wakuti “Ufumu wa Mulungu Ulamulira,” m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, masamba 90 mpaka 97, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

M’chaka cha 1914 mitundu ya anthu inagundika kuchita nkhondo ya padziko lonse

[Zithunzi patsamba 6]

Ntchito yothandiza ena mongodzipereka pakagwa mavuto ndi umboni wa chikondi cha Akristu

[Chithunzi patsamba 7]

Mboni za Yehova padziko lonse zimaphunzira zinthu zofanana