Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Maganizo A Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu

Khalani ndi Maganizo A Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu

Khalani ndi Maganizo A Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu

‘Aliyense wofuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu.’​—MATEYU 20:26.

1. Kodi anthu m’dzikoli amaona motani nkhani ya kukhala wamkulu?

KUFUPI ndi mzinda wakale wa Thebes (womwe tsopano umatchedwa kuti Karnak) wa ku Egypt, pa mtunda wa makilomita pafupifupi 500 kum’mwera kwa mzinda wa Cairo, kuli chiboliboli chachitali chokwana mamita 18 cha Farao Amenhotep Wachitatu. Munthu akaona chiboliboli chachikuluchi salephera kudziona kuti iye ndi wochepa kwambiri. Chibolibolichi, chimene mosakayikira anachiimika n’cholinga choti anthu aziopa wolamulirayo, ndi chizindikiro cha mmene anthu m’dzikoli amaonera nkhani ya kukhala wamkulu. Iwo amaona kuti kukhala wamkulu ndiye kuti uyenera kukhala ndi mphamvu zambiri ndiponso kuchititsa anthu ena kudziona kuti n’ngopanda ntchito.

2. Kodi Yesu anapatsa ophunzira ake chitsanzo chotani, ndipo kodi tikufunika kudzifunsa mafunso otani?

2 Tasiyanitsani maganizo ameneŵa ndi zimene Yesu Kristu anaphunzitsa. Ngakhale kuti anali “Ambuye ndi Mphunzitsi” wa omutsatira ake, Yesu anawaphunzitsa kuti munthu amakhala wamkulu akamatumikira ena. Patsiku lomaliza la moyo wake wa padziko lapansi, Yesu anasonyeza tanthauzo la zimene anawaphunzitsazo mwa kusambitsa mapazi a ophunzira ake. Iyitu inali ntchito yofunika kudzichepetsa kwambiri! (Yohane 13:4, 5, 14) Kodi n’chiyani chimakusangalatsani kwambiri, kutumikira ena kapena kutumikiridwa? Kodi chitsanzo cha Kristu chikukupatsani maganizo ofuna kukhala wodzichepetsa ngati mmene iye analili? Ndiyetu tiyeni tione maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu powasiyanitsa ndi mmene anthu ambiri m’dzikoli amaonera nkhaniyi.

Peŵani Maganizo a Anthu a M’dzikoli Pankhani ya Kukhala Wamkulu

3. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zimasonyeza zotsatirapo zomvetsa chisoni za maganizo a anthu olakalaka kulandira ulemerero kuchokera kwa anthu?

3 Pali zitsanzo zambiri za m’Baibulo zosonyeza kuti munthu ungaloŵe m’mavuto ngati uli ndi maganizo a anthu a m’dzikoli pankhani ya kukhala wamkulu. Taganizirani za munthu wamphamvu dzina lake Hamani, amene anali ndi udindo waukulu m’bwalo lachifumu ku Perisiya m’masiku a Estere ndi Moredekai. Chotsatirapo cha kulakalaka ulemerero kwa Hamani chinali manyazi ndiponso imfa. (Estere 3:5; 6:10-12; 7:9, 10) Nanga bwanji za Nebukadinezara wodzitukumula uja, amene anachita misala panthaŵi imene ulamuliro wake unafika pachimake? Maganizo ake olakwika pankhani ya kukhala wamkulu anawafotokoza m’mawu aŵa: “Suyu Babulo wamkulu ndinam’manga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wa chifumu changa?” (Danieli 4:30) Ndiyeno pali chitsanzo cha Herode Agripa Woyamba, amene anavomera ulemerero wosamuyenera m’malo mopereka ulemerero kwa Mulungu. Iye “anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.” (Machitidwe 12:21-23) Kusamvetsa mmene Yehova amaonera nkhani ya kukhala wamkulu kunachititsa anthu onseŵa kutha mphamvu mochititsa manyazi kwambiri.

4. Kodi ndani amayambitsa mtima wonyada wa anthu a m’dzikoli?

4 Ndi zabwino kufuna kukhala moyo woti anthu azitilemekeza ndi kutipatsa ulemu. Komano, Mdyerekezi amapezera mwayi pa malingaliro ameneŵa mwa kulimbikitsa mtima wonyada, umene umangosonyeza zokhumba zake. (Mateyu 4:8, 9) Tisaiŵale kuti iye ndi “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” ndipo akufunitsitsa kufalitsa maganizo akewo padziko lapansi pano. (2 Akorinto 4:4; Aefeso 2:2; Chivumbulutso 12:9) Pozindikira amene amayambitsa maganizo ameneŵa, Akristu amapeŵa maganizo a anthu a m’dzikoli pankhani ya kukhala wamkulu.

5. Kodi kukwanitsa kuchita zinazake, kutchuka, kapena kulemera zimathandiza munthu kukhala wachimwemwe nthaŵi yaitali? Fotokozani.

5 Ena mwa maganizo amene Mdyerekezi amalimbikitsa ndi akuti kukhala wotchuka m’dzikoli, kulandira ulemu, ndiponso kukhala ndi ndalama zambiri, mosakayikira kumapatsa chimwemwe. Kodi izi n’zoona? Kodi kukwanitsa kuchita zinazake, kutchuka, kapena kulemera kumapangitsa munthu kukhala moyo wosangalala? Baibulo limatichenjeza kuti tisanyengedwe ndi maganizo amenewo. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zom’pindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:4) Anthu ambiri amene aikira mtima kwambiri pa kufuna kutchuka kapena kulemera m’dzikoli angaikire umboni kuti malangizo ouziridwa a m’Baibulo ameneŵa ndi oona. Chitsanzo chimodzi cha zimenezi ndi mwamuna wina amene anathandiza nawo kukonza ndi kuyesera kuulutsa chombo chimene anthu anayendera popita ku mwezi. Iye anati: “Ndinali nditagwira ntchito mwakhama ndipo ndinali katswiri pantchitoyo. Koma sizinandithandize kukhala wachimwemwe ndiponso wamtendere m’maganizo kwa nthaŵi yaitali.” * Maganizo a anthu a m’dzikoli pankhani ya kukhala wamkulu, kaya ndi kumbali ya zamalonda, zamaseŵera, kapena zosangalatsa, sathandiza munthu kukhala wachimwemwe nthaŵi yaitali.

Munthu Amakhala Wamkulu Potumikira Ena Chifukwa Chowakonda

6. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yakobo ndi Yohane anali ndi maganizo olakwika pankhani ya kukhala wamkulu?

6 Zimene zinachitika panthaŵi ina m’moyo wa Yesu zimasonyeza zofunika kuchita kuti munthu akhale wamkuludi. Yesu ndi ophunzira ake anali paulendo wopita kuti Yerusalemu kukachita Paskha wa m’chaka cha 33 Kristu Atabwera. Ali m’njira, Yakobo ndi Yohane, abale ake aŵiri a Yesu omwe mwina anali ana a mchemwali wa amayi ake a Yesuyo, anasonyeza maganizo olakwika pankhani ya kukhala wamkulu. Kudzera mwa amayi awo, iwo anapempha Yesu kuti: ‘Lamulirani kuti tidzakhale kudzanja lanu lamanja, ndi kulamanzere, mu ufumu wanu.’ (Mateyu 20:21) Kwa Ayuda, kukhala kudzanja lamanja kapena lamanzere unali ulemu waukulu kwambiri. (1 Mafumu 2:19) Yakobo ndi Yohane, chifukwa cholakalaka kwambiri malo apamwamba, anafuna kuti awapeze m’njira yosayenera. Iwo anafuna kuti malo audindo ameneŵa akhale awo. Yesu anadziŵa zomwe iwo anali kuganiza ndipo anagwiritsira ntchito mpata umenewu kuwathandiza kukonza maganizo awo olakwika okhudza nkhani ya kukhala wamkulu.

7. Kodi Yesu anafotokoza chiyani pankhani ya mmene Mkristu angakhalire wamkulu?

7 Yesu ankadziŵa kuti m’dziko la anthu onyadali, munthu amene amaonedwa kukhala wamkulu ndi munthu amene amayang’anira ndi kulamulira anzake, ndipo olamulidwawo amachita zinthu nthaŵi yomweyo iye akawatuma china chilichonse. Koma kwa otsatira a Yesu, kugwira ntchito zofunika kudzichepetsa ndicho chizindikiro chodziŵira kuti munthuyo ndi wamkulu. Yesu anati: ‘Aliyense wofuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo aliyense wofuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu.’​—Mateyu 20:26, 27.

8. Kodi kukhala mtumiki kumatanthauza chiyani, ndipo kodi tingadzifunse mafunso otani?

8 Mawu a Chigiriki omwe m’Baibulo anamasuliridwa kuti “mtumiki” amatanthauza munthu amene amayesetsa kutumikira ena mwakhama ndiponso mosalema. Yesu anali kuphunzitsa ophunzira ake phunziro lofunika kwambiri, lakuti: Kulamula anthu kuchita zinthu sikupangitsa munthu kukhala wamkulu; koma munthu amakhala wamkulu mwa kutumikira ena chifukwa cha chikondi. Dzifunseni kuti: ‘Ndikanakhala Yakobo kapena Yohane kodi ndikanatani nditamva zimenezi? Kodi ndikanamvetsa kuti munthu amakhala wamkuludi akamatumikira ena chifukwa cha chikondi?’​—1 Akorinto 13:3.

9. Kodi Yesu anasonyeza chitsanzo chotani pa zochita zake ndi anthu ena?

9 Yesu anasonyeza ophunzira ake kuti maganizo a anthu m’dzikoli pankhani ya munthu amene ali wamkulu ndi osiyana ndi maganizo amene Kristu anaonetsa pa chitsanzo chake. Iye analibe maganizo odziona kuti ndi wapamwamba kuposa anthu amene anali kuwatumikira ndiponso sanachititse anthuwo kumva kuti ndi otsika. Anthu osiyanasiyana, amuna, akazi, ana, olemera, osauka, ndiponso anthu amaudindo awo, komanso anthu odziŵika kuti ndi ochimwa, onse ankakhala momasuka ndi Yesu. (Marko 10:13-16; Luka 7:37-50) Kaŵirikaŵiri anthu amalephera kukhala oleza mtima kwa anthu omwe ali ndi zofooka. Yesu sanali wotero. Ngakhale kuti ophunzira ake nthaŵi zina ankachita zinthu mosaganizirana ndiponso ankakangana, iye moleza mtima anali kuwalangiza, ndi kuwasonyeza kuti iye anali wodzichepetsadi ndiponso wofatsa.​—Zekariya 9:9; Mateyu 11:29; Luka 22:24-27.

10. Kodi moyo wonse wa Yesu unasonyeza motani kutumikira ena mopanda dyera?

10 Chitsanzo chosadzikonda cha Mwana wa Mulungu woposa onse ameneyu chinasonyeza tanthauzo la kukhala wamkuludi. Yesu sanabwere padziko lapansi kudzatumikiridwa koma anabwera kudzatumikira, kuchiritsa “nthenda zamitundumitundu” ndi kumasula anthu ku mphamvu za ziŵanda. Ngakhale kuti ankatopa ndipo ankafunika nthaŵi yoti apumule, iye nthaŵi zonse ankayamba wachita kaye zofuna za ena osati za iyeyo, ndipo ankayesetsa kuti awalimbikitse. (Marko 1:32-34; 6:30-34; Yohane 11:11, 17, 33) Chikondi chake chinamulimbikitsa kuti athandize anthu mwauzimu, anali kuyenda mitunda italiitali m’misewu yafumbi kupita kolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Marko 1:38, 39) Mosakayikira, nkhani yotumikira ena inali yofunika kwambiri kwa Yesu.

Tsanzirani Kudzichepetsa kwa Kristu

11. Kodi abale oikidwa kuti akhale oyang’anira mu mpingo amafunika kukhala ndi makhalidwe otani?

11 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, posankha amuna kuti akhale oimira gulu oyendayenda kuti atumikire anthu a Mulungu, anali kufuna kuti munthu akhale ndi mtima woyenera oyang’anira achikristu. Malinga ndi magazini ya Zion’s Watch Tower ya September 1, 1894, anthu amene ankafunika pantchitoyi anali amuna “ofatsa, n’cholinga choti asadzitukumule . . . , odzichepetsa omwe safuna kudzitchukitsa koma ofuna kulalikira za Kristu, osati ofalitsa zimene iwo amadziŵa, koma ofotokoza Mawu Ake mosavuta kumva ndiponso mosawasukulutsa.” N’zoonekeratu kuti Akristu oona sayenera kufuna udindo n’cholinga chokwaniritsa zokhumba zawo kapena kuti akhale otchuka, amphamvu, ndiponso olamulira ena. Woyang’anira amene ndi wofatsa amakumbukira kuti udindo umene ali nawo ndi “ntchito yabwino,” osati malo apamwamba oti am’bweretsere ulemu. (1 Timoteo 3:1, 2) Akulu onse pamodzi ndi atumiki otumikira ayenera kuyesetsa kutumikira ena modzichepetsa ndi kutsogolera pa utumiki wopatulika, ndi kusonyeza chitsanzo chabwino choti ena atengere.​—1 Akorinto 9:19; Agalatiya 5:13; 2 Timoteo 4:5.

12. Kodi amene akuyesetsa kuti akhale woyenerera kupatsidwa udindo mu mpingo angadzifunse mafunso otani?

12 Mbale aliyense amene akuyesetsa kuti akhale woyenerera kupatsidwa udindo angafunike kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimafufuza mipata yoti nditumikirire ena, kapena ndili ndi chizoloŵezi chofuna kutumikiridwa? Kodi ndimafuna kugwira ntchito zofunika zimene si zoonekera kwa anthu ena?’ Mwachitsanzo, wachinyamata wina angakhale wofunitsitsa kuti azikamba nkhani mu mpingo wachikristu koma mwina angakhale wamphwayi pothandiza achikulire. Angathe kumakonda kucheza ndi abale amaudindo mu mpingo koma angakhale wamphwayi pantchito yolalikira. Ndi bwino kuti wachinyamata wotero adzifunse kuti: ‘Kodi ndimangoika maganizo anga pa mbali za utumiki wa Mulungu zomwe munthu angatamidwe ndi kulemekezedwa nazo? Kodi ndikufuna kutchuka?’ Kunena zoona ngati tikufuna kudzipezera ulemu, ndiye kuti sitikutsatira chitsanzo cha Kristu.​—Yohane 5:41.

13. (a) Kodi anthu ena angakhudzidwe motani ndi chitsanzo cha kudzichepetsa cha woyang’anira? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kwa Mkristu kudzichepetsa sikhalidwe lochita kusankha kukhala nalo?

13 Tikamayesetsa kutsanzira kudzichepetsa kwa Kristu, timasonkhezeredwa kutumikira ena. Taonani chitsanzo cha mbale wina woyang’anira woyendera nthambi amene anali kuyendera ntchito pa maofesi a nthambi ina ya Mboni za Yehova. Ngakhale kuti anali wotanganidwa kwambiri ndiponso anali ndi maudindo ambiri, woyang’anirayu anaima pamalo ena kuti athandize mbale wachinyamata amene anali kuvutika kuchuna makina osokera mabuku. Mbale wachinyamatayo anati: “Ndinadabwa kwambiri! Iye anandiuza kuti anali kugwiritsira ntchito makina amtundu womwewo pamene anali mnyamata akutumikira pa Beteli, ndipo anali kukumbukira mmene makinawo ankavutira kuwachuna bwino. Anandithandiza kwa nthaŵi yaitali ndithu kukonza makinawo ngakhale kuti iye anali ndi zinthu zofunika zambiri zoti achite. Ndinachita nazo chidwi kwambiri zimenezi.” Mbale ameneyu, yemwe tsopano ndi woyang’anira dipatimenti ina pa ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova, amakumbukirabe zimene zinachitikazo zosonyeza kudzichepetsa. Tiyeni tisadzione ngati apamwamba kwambiri moti sitingachite ntchito zofunika kudzichepetsa kapena kudziona kuti ndife ofunika kwambiri moti sitingagwire ntchito zonyozeka. M’malo mwake, tiyenera kuvala “kudzichepetsa mtima.” Izi si zochita ngati munthu utakonda kutero. Ndi mbali ya umunthu “watsopano” umene Mkristu ayenera kukhala nawo.​—Afilipi 2:3; Akolose 3:10, 12; Aroma 12:16.

Zimene Tingachite Kuti Tikhale ndi Maganizo a Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu

14. Kodi kusinkhasinkha za unansi wathu ndi Mulungu ndiponso ndi anthu anzathu kungatithandize motani kukulitsa maganizo oyenerera pankhani ya kukhala wamkulu?

14 Kodi tingatani kuti tiziona moyenerera nkhani ya kukhala wamkulu? China mwa zinthu zimene tingachite ndicho kusinkhasinkha za unansi wathu ndi Yehova Mulungu. Ukulu wake, mphamvu zake, ndi nzeru zake zimam’pangitsa kukhala wapamwamba kwambiri kuposa nzeru za anthu ofooka. (Yesaya 40:22) Nakonso kusinkhasinkha za unansi wathu ndi anthu anzathu kumatithandiza kuti tikulitse kudzichepetsa. Mwachitsanzo, tingathe kuwaposa anthu ena pankhani zina, koma iwo angamachite bwino kwambiri pambali zina zofunika kwambiri m’moyo, kapena abale athu achikristu angakhale ndi makhalidwe ena amene ifeyo tilibe. Ndipotu, kaŵirikaŵiri anthu ambiri amene Mulungu amawaona kuti ndi ofunika sakhala otchuka popeza amakhala ofatsa ndiponso odzichepetsa.​—Miyambo 3:34; Yakobo 4:6.

15. Kodi kukhulupirika kwa anthu a Mulungu kumasonyeza motani kuti palibe amene ayenera kudziona kuti ndi woposa anzake?

15 Zinthu zimene zachitikira Mboni za Yehova panthaŵi imene zinali kuyesedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo zikuchitira umboni mfundo imeneyi. Nthaŵi ndi nthaŵi, anthu amene dzikoli lingawaone kuti ndi anthu wamba ndiwo amene akhala okhulupirika kwa Mulungu pa ziyeso zoopsa kwambiri. Kusinkhasinkha zitsanzo zimenezi kungatithandize kuti tikhale odzichepetsa ndipo kungatiphunzitse kuti ‘tisadziyese koposa kumene tiyenera kudziyesa.’​—Aroma 12:3. *

16. Kodi onse mu mpingo angayesetse bwanji kukhala ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu?

16 Akristu onse, ana ndi akulu omwe, ayenera kuyesetsa kukhala ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu. Mu mpingo mumakhala ntchito zosiyanasiyana. Tisamadane nazo tikapemphedwa kugwira ntchito zimene zingaoneke ngati ntchito wamba. (1 Samueli 25:41; 2 Mafumu 3:11) Makolo, kodi mumalimbikitsa ana anu, ang’onoang’ono ndiponso achinyamata, kuti azigwira mosangalala ntchito iliyonse yomwe apatsidwa, kaya ndi pa Nyumba ya Ufumu, pamalo a msonkhano wadera, kapena wachigawo? Kodi amakuonani inuyo mukugwira ntchito wamba? Mbale wina amene tsopano akutumikira pa likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova, amakumbukira bwino chitsanzo cha makolo ake. Iye anati: “Mmene ankagwirira ntchito yoyeretsa pa Nyumba ya Ufumu kapena pamalo a msonkhano zinandisonyeza kuti iwo ankaona ntchitoyo kuti ndi yofunika. Nthaŵi zambiri ankadzipereka kugwira ntchito zothandiza pampingo kapena zothandiza abale athu onse, mosaganizira kuti ntchitoyo ikuoneka yonyozeka motani. Mtima umenewu wandithandiza kulandira mosanyinyirika ntchito iliyonse yomwe ndapatsidwa pa Beteli pano.”

17. Kodi akazi odzichepetsa angakhale motani dalitso pampingo?

17 Pankhani yoika patsogolo zofuna za ena m’malo mwa zofuna zathu, tili ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha Estere, yemwe anakhala mfumukazi ya Ufumu wa Perisiya m’zaka za m’ma 400 Kristu Asanabwere. Ngakhale kuti ankakhala kunyumba yachifumu, iye anali wokonzeka kuika moyo wake weniweniwo pangozi m’malo mwa anthu a Mulungu, pochita zinthu zogwirizana ndi cholinga cha Mulungu. (Estere 1:5, 6; 4:14-16) Mosaganizira kuti kaya ndi olemera kapena ayi, akazi achikristu masiku ano angasonyeze mtima ngati wa Estere mwa kulimbikitsa ofooka, kuzonda odwala, kuchita nawo ntchito yolalikira, ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi akulu. Alongo odzichepetsa oterowo amakhala dalitso lalikulu pampingo!

Madalitso Okhala ndi Maganizo a Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu

18. Kodi kukhala ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu kuli ndi madalitso otani?

18 Mumapeza madalitso ambiri pokhalabe ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu. Kutumikira ena mopanda dyera kumabweretsa chimwemwe kwa anthu amene mukuwatumikirawo ndiponso kwa inuyo. (Machitidwe 20:35) Pamene mukudzipereka ndi mtima wonse kutumikira abale anu, iwo amakukondani kwambiri. (Machitidwe 20:37) Chofunika kwambiri n’chakuti, Yehova amaona kuti zinthu zimene mukuchita pothandiza Akristu anzanu ndi nsembe yosangalatsa yomuyamika nayo.​—Afilipi 2:17.

19. Kodi titsimikize mtima kuchita chiyani ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu?

19 Aliyense wa ife ayenera kuona zimene zili mumtima wake n’kufunsa kuti: ‘Kodi ndizingolankhula za kukhala ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu, kapena ndiziyesetsa kuti ndikhaledi ndi maganizo ameneŵa?’ Tikudziŵiratu mmene Yehova amaonera anthu odzikuza. (Miyambo 16:5; 1 Petro 5:5) Tiyeni tizichita zinthu zosonyeza kuti tikusangalala kusonyeza maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu, kaya ndi mumpingo wachikristu, m’banja mwathu, kapena pa zimene timachita tsiku ndi tsiku ndi anthu ena. Tiyeni tizichita zonse kuti Mulungu alemekezedwe ndi kutamandidwa.​—1 Akorinto 10:31.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani nkhani yakuti “Kufunafuna Kukhala Moyo Wopambana,” mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya May 1, 1982, masamba 3 mpaka 6.

^ ndime 15 Onani buku la 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 181 mpaka 182, ndi Nsanja ya Olonda ya September 1, 1993, masamba 27 mpaka 31, kuti mupeze zitsanzo za nkhaniyi.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupeŵa maganizo a anthu a m’dzikoli pankhani ya kukhala wamkulu?

• Kodi Yesu anati wamkulu ndi munthu wotani?

• Kodi oyang’anira angatsanzire motani kudzichepetsa kwa Kristu?

• N’chiyani chingatithandize kukhala ndi maganizo a Kristu pankhani ya kukhala wamkulu

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 17]

Ndani Ali ndi Maganizo a Kristu Pankhani ya Kukhala Wamkulu?

Munthu amene amafuna kutumikiridwa kapena amene amafuna kutumikira ena?

Munthu wokonda kutchuka kapena munthu wovomera ntchito yofunika kudzichepetsa?

Munthu wodzikweza kapena munthu amene amakweza ena?

[Chithunzi patsamba 14]

Chiboliboli chachikulu cha Farao Amenhotep Wachitatu

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi mukudziŵa zimene zinagwetsa Hamani pa ulemerero wake?

[Zithunzi patsamba 16]

Kodi mumafufuza mipata yoti mutumikire anthu ena?