Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Boma Labwino

Kufunafuna Boma Labwino

Kufunafuna Boma Labwino

“Kudalirana kwa mayiko padziko lonse kwachititsa kuti padziko pano pabuke mavuto osiyanasiyana amene mayiko paokhapaokha afika poti sangakwanitsenso kuwathetsa. Njira yokhayo imene tingathetsere zinthu zimene zikutiopsa ndiponso kutivutitsazi ndi yakuti tigwirizane padziko lonse.”​—Anatero Ghulam Umar, katswiri wodziŵa bwino zandale wa ku Pakistan.

MASIKU ano padziko pano pali zinthu zambiri zovuta kuzimvetsa. Dzikoli ndi lolemera kwadzaoneni koma pali anthu ambiri amene akuvutika kuti apeze zinthu zofunikira kuti angokhala ndi moyo. N’kutheka kuti mbadwo wa makompyuta uno ndiwo mbadwo wophunzira kwambiri kusiyana n’kale lonse, komano pali anthu ambiri amene akuvutika kuti apeze ntchito yodalirika. Ngakhale zikuoneka kuti anthu ali ndi ufulu wambiri kuposa kale lonse, pali anthu ambirimbiri amene akukhalabe mwamantha. Mwina pangakhale zinthu zosiyanasiyana zopindulitsa zimene tingathe kuchita, koma ambiri tataya mtima chifukwa cha chinyengo ndiponso kusamvera malamulo kwa anthu osiyanasiyana, osauka ndi olemera omwe.

Mavuto amene anthu ali nawo n’ngaakulu kwambiri moti palibe dziko kapena gulu la mayiko lililonse limene lingathane nawo palokha. Motero, anthu ambiri amene akutsata bwino nkhani zimenezi anafika pongonena kuti, kuti dzikoli likhaledi ndi mtendere ndiponso kuti likhaledi lotetezeka, mayiko onse ayenera kugwirizana n’kukhala ndi boma limodzi. Mwachitsanzo, Albert Einstein analimbikitsa kwanthaŵi yaitali mfundo imeneyi. M’chaka cha 1946, iye ananena kuti: “Sindikayika ngakhale pang’ono kuti ambiri mwa anthu padziko pano angakonde atamakhala mwamtendere ndiponso motetezeka . . . Kuti anthu apezedi mtendere umene akuulakalakawu payenera kukhala boma la padziko lonse.”

Patha zaka zoposa 50 tsopano, koma mfundo yofunika kwambiriyi sinakwaniritsidwebe. Potchulapo mavuto a zaka 100 zimene tinaziyamba m’chaka cha 2000, nkhani ina ya m’nyuzipepala yotchedwa Le Monde ya mumzinda wa Paris ku France inati: “M’pofunika kukhazikitsa njira zoŵeruzira anthu, zokhazikitsira malamulo ndiponso zoyendetsera boma la padziko lonse limene lingachitepo kanthu mwamsanga ngati anthu a fuko linalake atayamba kuphedwa kwina kulikonse padziko pano. Tiyenera kuvomereza kuti panopo dziko lapansi lonseli lili ngati dziko limodzi.” Kodi ndani kapena n’chiyani chimene chili ndi mphamvu zothetsa vutoli kuti anthu akhale ndi tsogolo lamtendere?

Kodi Bungwe la United Nations Lingathetse Vutoli?

Anthu ambiri akukhulupirira kuti bungwe la United Nations ndilo lidzabweretse mtendere padziko lonse. Kodi bungwe la United Nations ndilo lingathe kubweretsa mtendere ndiponso chitetezo padziko lonse? Mosakayikira, pali zinthu zambiri zandale zimene zanenedwa pokopa anthu kuti azikhulupirira kuti bungweli lingakwanitsedi kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, m’chikalata chotchedwa “Millennium Declaration” cha m’chaka cha 2000, Gulu Loyendetsa Ntchito za Bungwe la United Nations linanena motere zimene latsimikiza kuchita: “Tiyesetsa kupereka mtendere kwa anthu athu amene akuvutika ndi nkhondo, kaya n’zapachiweniweni kapena zomenyana ndi mayiko ena, zimene zaphetsa anthu oposa 5 miliyoni m’zaka 10 zapitazi.” Mawu otereŵa achititsa anthu osiyanasiyana, kuphatikizapo munthu amene anapambana mphoto yapamwamba ya zamtendere ya Nobel Peace Prize m’chaka cha 2001, kutamanda bungwe la United Nations ndi kulitayira kamtengo. Potamanda bungweli, komiti yoona za mphoto ya Nobel ku Norway inati, “njira imodzi yokha yobweretsera mtendere padziko lonse ndiyo yodzera m’bungwe la United Nations.”

Zonsezi zili apo, kodi bungwe la United Nations, lomwe analikhazikitsa mu 1945, lasonyezadi kuti ndi boma limene lingabweretse mtendere weniweni komanso wokhalitsa padziko lonse? Ayi, popeza kuti ntchito zambiri za bungweli siziphula kanthu chifukwa mayiko a m’bungweli amafuna kuchita zinthu zongowakomera iwowo. Malingana ndi mkonzi wa nyuzipepala inayake, anthu ena onse bungweli amangoliona kuti ndi “njira yodziŵira maganizo a anthu padziko lonse” ndiponso kuti “limangokambirana za mavuto amene anthu akhala akukambirana kwa zaka zambirimbiri popanda kuchitapo kanthu kalikonse kooneka.” Ndiye funso limene lidakalipobe n’lakuti: Kodi mayiko padziko lonse angathedi kudzagwirizana tsiku lina?

Baibulo limalongosola kuti kugwirizana kotereku kuchitika posachedwapa. Kodi kudzachitika motani? Ndipo kodi ndi boma lanji limene lidzatheketse zimenezi? Kuti mudziŵe mayankho a mafunsoŵa ŵerengani nkhani yotsatirayi.

[Chithunzi patsamba 3]

Einstein analimbikitsa kuti m’pofunika kukhala ndi boma limodzi padziko lonse

[Mawu a Chithunzi]

Einstein: U.S. National Archives photo