Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Yesu anali kutanthauza chiyani pamene anauza ophunzira ake kuti: “Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba”?

Yesu anali atangosankha kumene ophunzira okwana 70, ndipo ‘anawatuma iwo aŵiriaŵiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo alionse kumene ati afikeko mwini.’ Ophunziraŵa atabwera, anali okondwa chifukwa choti ntchito yawoyo inayenda bwino. Iwo anati: “Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.” Pamenepo, Yesu anati: “Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba.”​—Luka 10:1, 17, 18.

Poyamba, zingaoneke ngati kuti Yesu anali kunena za zinthu zimene zinali zitachitika kale. Koma, patatha zaka 60 Yesu atanena mawu ali pamwambaŵa, mtumwi Yohane, yemwe anali wokalamba, anagwiritsa ntchito mawu ofanana ndi ameneŵa pamene analemba kuti: “Chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”​—Chivumbulutso 12:9.

Pamene Yohane analemba mawu ameneŵa, Satana anali akukhalabe kumwamba. Kodi tikudziŵa bwanji zimenezi? Chifukwa chakuti Chivumbulutso ndi buku la maulosi, osati zinthu zimene zinachitika kale. (Chivumbulutso 1:1) Motero, m’masiku a Yohane, Satana anali asanaponyedwe kudziko. Ndipo maumboni amasonyeza kuti izi zinadzachitika patangotha nthaŵi pang’ono Yesu ataikidwa pampando kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 1914. *​—Chivumbulutso 12:1-10.

Ndiye n’chifukwa chiyani Yesu analankhula za kuthamangitsidwa kumwamba kwa Satana ngati kuti kunali kutachitika kale? Akatswiri ena a Baibulo amati Yesu anali kudzudzula ophunzira ake chifukwa chonyada. Akatswiriwo amakhulupirira kuti, polankhula mawu ameneŵa, Yesu anali kunena kuti: ‘Mwagonjetsa ziŵanda inde, koma musadzikuze. Satana anayambanso ndi kunyada, ndipo mosakhalitsa anagwa nazo m’mavuto.’

Palibe umboni wokwanira wotsutsira zimenezi. Komabe, mosakayikira Yesu anali kusangalala nawo pamodzi ophunzira akewo ndipo analankhula za kugwa kwa Satana komwe kunadzachitika m’tsogolo. Mosiyana ndi wophunzira wake wina aliyense, Yesu anali kudziŵa bwino kwambiri nkhanza ndiponso chidani cha Mdyerekezi. Taganizirani mmene Yesu anasangalalira kumva kuti ziŵanda zamphamvu zinali kugonjera ophunzira ake omwe anali anthu opanda ungwiro! Kugonja kwa ziwanda kumeneku kunali chithunzi chabe cha zimene zinadzachitika tsiku lina m’tsogolo pamene Yesu, monga Mikayeli mngelo wamkulu, anadzamenya nkhondo ndi Satana ndi kumuponya pa dziko lapansi kumuchotsa kumwamba.

Yesu ponena kuti anaona Satana “alinkugwa,” mwachionekere anali kutsimikizira zakuti Satana adzagwa ndithu. Izi zikufanana ndi maulosi ena a m’Baibulo amene amanena za zinthu zodzachitika m’tsogolo ngati kuti zinachitika kale. Mwachitsanzo, taonani mmene ulosi wonena za Mesiya pa Yesaya 52:13–53:12 ukufotokozera zinthu mosinthasintha pena ngati kuti zinachitika kale komanso pena ngati kuti sizinachitike. Mosakayikira Yesu anali kufotokoza chikhulupiriro chake chakuti kuthamangitsidwa kumwamba kwa Satana kudzachitika mogwirizana ndi cholinga cha Atate Wake. Yesu analinso wotsimikiza kuti nthaŵi imene Mulungu anakonza ikadzakwana, Satana ndi ziŵanda zake adzaponyedwa m’phompho ndipo kenako adzaphedwa.​—Aroma 16:20; Ahebri 2:14; Chivumbulutso 20:1-3, 7-10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, mutu 10, ndi buku lakuti Revelation​—Its Grand Climax At Hand! mutu 27, ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.