Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chiyani Chimapangitsa Moyo Kukhala ndi Cholinga Chenicheni?

N’chiyani Chimapangitsa Moyo Kukhala ndi Cholinga Chenicheni?

N’chiyani Chimapangitsa Moyo Kukhala ndi Cholinga Chenicheni?

JESSE, mnyamata wazaka 17 yemwe ali ku sekondale, atafunsidwa za cholinga cha moyo, anayankha kuti, “Malinga munthu uli ndi moyo, uyenera uzingosangalala basi.” Maganizo a Suzie anali osiyana ndi a Jesse. Suzie anati: “Kwa ineyo, cholinga cha moyo ndi zimene iweyo umasankha kuchita ndi moyowo.”

Kodi munaganizapo kuti cholinga cha moyo n’chiyani? Kodi miyoyo ya anthu onse ili ndi cholinga chimodzi? Kapena kodi Suzie analondola, kunena kuti moyo makamaka ndi chimene aliyense waganiza kuchita nawo? Zilibe kanthu kuti ntchito za sayansi zapita patsogolo motani, koma timafunitsitsa titadziŵa cholinga cha moyo. Nthaŵi zina pamoyo wathu, ambirife timadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani tili ndi moyo?’

Asayansi masiku ano akhala akufufuza yankho la funso limeneli. Kodi apeza yankho lotani? “Pa kusanduka kwa zamoyo kuchoka ku zinthu zina, kukhala ndi moyo mwa iko kokha kulibe cholinga,” anatero David P. Barash, pulofesa wa za maganizo a anthu ndiponso wa sayansi ya zinyama. Kwa akatswiri a sayansi yakuti zinthu zinachita kusanduka, pali cholinga chimodzi chokha cha zinthu zamoyo, chakuti zipitirize kukhala ndi moyo ndi kuberekana. Motero Pulofesa Barash anati: “Pokhala mu chilengedwe chonsechi chomwe chilibe cholinga ndipo sichiganizira anthu, ndi udindo wa anthu kuupezera cholinga moyo wawo mwa zinthu zimene amasankha mwaufulu, mozindikira zimene akuchita, ndiponso mochita kufuna.”

Amene Angapangitse Moyo Kukhala ndi Cholinga

Ndiyeno, kodi cholinga cha moyo ndi chokhachi basi, kuti aliyense azichita zomwe iye akufuna? M’malo mongotisiya kuti tizingokhala osoŵa chochita m’dziko lopanda cholinga, Baibulo linafotokoza kalekale kuti pali cholinga chimene tikukhalira padziko pano. Sikuti zinangochitika mwangozi kuti tikhale ndi moyo. Timauzidwa kuti, Mlengi anatenga zaka zambiri akukonza dziko lapansili kuti pakhale anthu. Palibe chimene chinangochitika mwangozi. Iye anaonetsetsa kuti zonse zinali “zabwino ndithu.” (Genesis 1:31; Yesaya 45:18) Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Mulungu anali nawo cholinga anthu.

Koma, chochititsa chidwi n’chakuti Mulungu sanakonzeretu zinthu zoti zidzachitikire munthu aliyense, kaya mwa zochita zake Mulunguyo kapena mwa chibadwa chathu anthufe. Ngakhale kuti timachita zinthu zosiyanasiyana malinga ndi chibadwa chathu, kwakukulukulu timatha kulamulira zochita zathu. Tonsefe tili ndi ufulu wosankha mmene moyo wathu ukhalire.

Ngakhale kuti aliyense payekha angasankhe zomwe akufuna kuchita ndi moyo wake, kungakhale kulakwa kusaganizira Mlengi pa zimene tikufuna kuchita. Ambiri aona kuti kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndiko kumapangitsa munthu kuona cholinga chenicheni cha moyo. Kugwirizana kofunika kumeneku pakati pa Mulungu ndi cholinga cha moyo wathu kumaoneka pa dzina la Mulungu, lakuti Yehova, limene kwenikweni limatanthauza kuti, “Amachititsa Kukhala.” (Eksodo 6:3; Salmo 83:18) Izi zikutanthauza kuti amapitiriza kukwaniritsa chilichonse chomwe walonjeza ndipo nthaŵi zonse amachita zimene akufuna. (Eksodo 3:14; Yesaya 55:10, 11) Tangoganizirani za mfundoyi. Dzina lakuti Yehova limatsimikizira tonsefe kuti iyeyo ndi amene amachititsa moyo wathu kukhala ndi cholinga.

Kungodziŵa kokhako kuti kuli Mlengi kumakhudza kwambiri mmene munthu amaonera moyo. Linet, mtsikana wazaka 19, anati: “Kuona zinthu zabwino zonsezi zimene Yehova analenga ndi kuonanso cholinga cha zinthu zimenezi kumandisonyeza kuti nanenso anandilenga ndi cholinga.” Amber anawonjezera kuti: “Anthu akamalankhula kuti sadziŵa Mulungu, nthaŵi zonse ine zimandipangitsa kuyamikira chifukwa ndikumudziŵa. Zinthu zimene anapangazi ndiwo umboni wakuti kuli Yehova.” (Aroma 1:20) N’zoona kuti kudziŵa kuti kuli Mlengi ndi nkhani yosiyana ndi kukhala naye paubwenzi wabwino.

Ubwenzi ndi Mulungu

Pankhani iyinso Baibulo lingatithandize. Machaputala ake oyambirira amapereka umboni womveka bwino wakuti Yehova Mulungu ndi Atate wachikondi. Mwachitsanzo, sikuti analenga Adamu ndi Hava ndiyeno n’kungowasiya osawauza kuti iye ndi ndani. M’malo mwake, anali kulankhula nawo kaŵirikaŵiri. Sanawasiye mu Edene kuti adzitsogolere okha, iye n’kumakachita zinthu zina. M’malo mwake, anawapatsa malangizo a mmene angakhalire moyo wabwino. Anawapatsa ntchito yosangalatsa kwambiri, ndipo anakonza zoti aziphunzira nthaŵi zonse. (Genesis 1:26-30; 2:7-9) Kodi zimenezi si zimene mumayembekezera kwa kholo lodziŵa ntchito yake ndi lachikondi? Ndiyeno taganizirani tanthauzo la zimenezi. Denielle anati, “Kudziŵa kuti Yehova analenga dziko lapansi ndipo anatilenga ife moti tithe kusangalala ndi zimene iye analenga kumandisonyeza kuti iye amafuna kuti ife tizisangalala.”

Kuwonjezera pamenepo, mofanana ndi tate wina aliyense wabwino, Yehova amafuna kuti ana ake akhale naye paubwenzi. Pankhani imeneyi, lemba la Machitidwe 17:27 limatitsimikizira kuti: “[Iye] sakhala patali ndi yense wa ife.” Kodi mfundo imeneyi ndi yothandiza motani? Amber anati: “Kudziŵa Yehova kumandilimbitsa mtima kuti sindili ndekha. Nthaŵi zonse ndimakhala ndi wina amene angandithandize.” Komanso, pamene mukuphunzira za Yehova, mudzapeza kuti iye ndi wachifundo, wachilungamo, ndiponso wabwino. Mungathe kumudalira. “Pamene Yehova anakhala bwenzi langa lapamtima, ndinazindikira kuti palibenso wina amene ali chire kuti andithandize,” anatero Jeff.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu akhala akunenera Yehova zinthu zoipa zambiri. Anthu amati iye ndiye wachititsa mavuto ambiri amene anthu akukumana nawo ndiponso amati ndiye wachititsa makhalidwe oipa a zipembedzo. Anthu amanena kuti iye wakhala akuchititsa zinthu zina zankhanza kwambiri. Koma lemba la Deuteronomo 32:4, 5 limafotokoza kuti: “Njira zake zonse ndi chiweruzo . . . . Anam’chitira zovunda sindiwo ana ake, chilema n’chawo.” Motero, tili ndi udindo woti tidzifufuzire zoona zake.​—Deuteronomo 30:19, 20.

Cholinga cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa

Kaya ife tikhale ndi maganizo otani, koma palibe chidzalepheretse Mulungu kukwaniritsa cholinga chake chonse chokhudza dziko lapansi ndiponso anthu. Ndipo tiyenera kukumbukira kuti iye ndi Mlengi. Ndiyeno kodi cholinga chakecho n’chotani? Yesu Kristu anatchula za cholinga chimenechi pa Ulaliki wake wa pa Phiri pamene anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” Patapita nthaŵi, iye anasonyeza mtumwi wake Yohane kuti Mulungu watsimikiza “kuwononga iwo akuwononga dziko.” (Mateyu 5:5; Chivumbulutso 11:18) Popeza kuti Yesu anali ndi Mulungu panthaŵi yolenga zinthu, iye akudziŵa kuti kuyambira pachiyambi cholinga cha Mulungu n’chakuti anthu olungama akhale ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Genesis 1:26, 27; Yohane 1:1-3) Ndipo Mulungu sasintha. (Malaki 3:6) Mulungu akutilonjeza kuti: “Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala.”​—Yesaya 14:24.

Panopo Yehova wayamba kale kuyala maziko a mtundu wa anthu ogwirizana chifukwa chokonda Mulungu ndi anansi awo, osati chifukwa cha umbombo ndi kudzikonda ngati mmene anthu ambiri alili padziko pano. (Yohane 13:35; Aefeso 4:15, 16; Afilipi 2:1-4) Anthu odzakhala m’dziko limeneli ndi odzipereka ndipo ndi ofunitsitsa kukwaniritsa cholinga chawo chomwe ndi chakuti dongosolo lino la zinthu lisanathe, iwo akhale atalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene ukubwera. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Panopa, m’mayiko oposa 230, Akristu oposa sikisi miliyoni anayamba kale kulambirira pamodzi mu ubale wogwirizana ndi wachikondi wa padziko lonse.

Khalani Nawo Cholinga Moyo Wanu

Ngati mukufunafuna cholinga chenicheni cha moyo wanu, ndiye kuti Yehova Mulungu akukupemphani kuti muyambe panopa kugwirizana ndi anthu ake, omwe ndi “mtundu [wake] wolungama.” (Yesaya 26:2) Mwina mukufunsa kuti, ‘Kodi m’gulu limenelo lachikristu moyo wake ndi wotani? Kodi ndikufunadi kugwirizana ndi anthu ameneŵa?’ Taonani zimene achinyamata ena ananena:

Quentin: “Mpingo umanditeteza ku dzikoli. Kudziŵa kuti zimene ndimachita ndi moyo wanga Yehova zimamukhudza kumandithandiza kuona kuti iye alipo ndipo amafuna kuti ndizisangalala.”

Jeff: “Kumpingo ndiko kumene ndingapite kuti ndikalimbikitsidwe. Kuli abale ndi alongo anga, omwe angandithandize ndi kundilimbikitsa. Iwo ndi achibale anga enieni.”

Linet: “Chimwemwe chomwe chimakhalapo kuona munthu akuvomera choonadi cha Baibulo ndi kusankha zoti atumikire Yehova sitingachiyerekezere ndi china chilichonse. Izi zimapangitsa moyo wanga kukhala wosangalala.”

Cody: “Pakanapanda Yehova bwenzi moyo wanga uli wopanda phindu. Bwenzi ndikungochita zinthu popanda cholinga chenicheni ngati mmene amachitira anthu ena ambiri. Amatero pofunafuna chimwemwe koma sachipezanso. M’malo mwake, Yehova anandipatsa mwayi waukulu wokhala naye paubwenzi, ndipo izi zimapangitsa moyo wanga kukhala ndi cholinga.”

Bwanji osadzifufuzira nokha? Mudzaona kuti mwa kuyandikira kwambiri kwa Mlengi wanu Yehova Mulungu, mudzapeza cholinga chenicheni cha moyo wanu.

[Zithunzi patsamba 31]

Kukhala paubwenzi ndi Mulungu kumapangitsa moyo wathu kukhala ndi cholinga

[Mawu a Chithunzi patsamba 29]

NASA photo