Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pamoyo Wathu Takhala Tikudalira Mphamvu za Yehova

Pamoyo Wathu Takhala Tikudalira Mphamvu za Yehova

Mbiri ya Moyo Wanga

Pamoyo Wathu Takhala Tikudalira Mphamvu za Yehova

YOSIMBIDWA NDI ERZSÉBET HAFFNER

“Sindilola kuti akuthamangitse m’dziko lino,” anatero Tibor Haffner atamva kuti boma lalamula kuti ndichoke m’dziko la Czechoslovakia. Kenaka anati: “Ngati ungalole, ndikukwatira, ndipo uzikhala m’dziko lomwelino ndi ine mpaka kalekale.”

TINAKWATIRANA pa January 29, 1938, patangotha masabata angapo chabe Tibor atandifunsira mosayembekezeka chonchi. Tibor anali mbale wachikristu yemwe anali munthu woyamba kulalikira banja lathu. Zinandivuta kwambiri kum’vomera. Ndinali nditangokwanitsa zaka 18, ndipo poti ndinali mtumiki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, ndinkafuna kuti nditumikire Mulungu pa zaka zonse za unyamata wanga. Ndinalira ndiponso ndinapemphera. Mtima wanga utakhala pansi m’pamene ndinazindikira kuti si kuti Tibor anangondifunsira pondichitira chifundo ayi, motero ndinayamba kufuna kumanga banja ndi mwamuna ameneyu yemwe ankandikondadi mochokera pansi pamtima.

Koma kodi n’chifukwa chiyani ankafuna kundithamangitsa m’dzikoli lomwenso linkanyadira kwambiri boma lake la demokalase komanso ufulu wopembedza? Mwina ndiyambe kaye ndakuuzani mmene ndinakulira.

Ndinabadwa pa December 26, 1919, m’banja la makolo achikatolika ochokera ku Greece, ndipo umu munali m’katauni kotchedwa Sajószentpéter, kopezeka pamtunda wa makilomita 160 kum’maŵa kwa mzinda wa Budapest, m’dziko la Hungary. N’zomvetsa chisoni kuti bambo anga anamwalira ndisanabadwe. Posakhalitsa, amayi anakwatiwa ndi mwamuna wina wa ana anayi, amene mkazi wake anamwalira, ndipo tinasamukira ku mzinda wokongola wa Lučenec womwe panthaŵiyo unali m’dziko la Czechoslovakia. Nthaŵi imeneyo, kukhala m’banja la bambo kapena mayi okupeza chinali chinthu chovuta. Popeza kuti ineyo ndinali wamng’ono kwambiri m’banja la ana asanuli ndinkangoona ngati ndinali kamunthu kosafunika m’banjamo. Kupeza ndalama kunali kovuta, ndipo ndinkasoŵa zinthu zina zofunika pa moyo wanga komanso chikondi chokwanira cha makolo anga.

Kodi Alipo Amene Angayankhe Mafunsoŵa?

Ndili ndi zaka 16, ndinali ndi mafunso amene ankandithetsa nzeru kwambiri. Ndinkaŵerenga mwachidwi zedi mbiri ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, ndipo ndinadabwa kwambiri kumva za anthu ambirimbiri amene anaphedwa pankhondo ya pakati pa anthu ozindikira a m’mayiko omwe ankati ndi achikristu. Kuphatikiza apo, ndinkaonanso kuti anthu ambiri amalimbikitsa usilikali. Zimene ankachitazi sizinkagwirizana n’komwe ndi zimene ndinaphunzira kutchalitchi zokonda anansi athu.

Motero, ndinapita kwa wansembe wachikatolika n’kumufunsa kuti: “Kodi ndi lamulo liti limene Akristufe tiyenera kumvera; lopita kunkhondo n’kumakapha anansi athu kapena lokonda anansi athu?” Pokwiya ndi funso langalo, iye anayankha kuti zimene ankaphunzitsa n’zimene akuluakulu anamuuza. Nditapita kwa mbusa wa tchalitchi cha Calvin ndiponso kwa rabi wachiyuda nawonso anachitanso chimodzimodzi. Sanandiyankhe chilichonse chogwira mtima, anangondiuza kuti funso langali likuwadabwitsa. Potsiriza ndinapita kwa mbusa wa tchalitchi cha Lutheran. Iye anapsa mtima koma ndisanachoke, anandiuza kuti: “Ngati ukufunadi kudziŵa zimenezi, kafunse a Mboni za Yehova.”

Ndinawafunafuna a Mboniwo koma sindinawapeze. Patatha masiku angapo ndikuchokera kuntchito ndinaona chitseko cha nyumba yathu chili chotseguka pang’ono. Ndinaona mnyamata wooneka bwino akuŵerengera Baibulo amayi anga. Ndiye ndinaganiza kuti, ‘Basi, wa Mboni za Yehova uja ndi ameneyu!’ Tinamuuza kuti aloŵe, dzina lake linali Tibor Haffner, ndipo ndinamufunsanso mafunso anga aja. M’malo mongondiuza maganizo ake, iye anandisonyeza zimene Baibulo limanena pa za chizindikiro cha Akristu oona, komanso za nthaŵi imene tikukhala ino.​—Yohane 13:34, 35; 2 Timoteo 3:1-5.

Patangotha miyezi yochepa, ndisanakwanitse zaka 17, ndinabatizidwa. Ndinkaona kuti aliyense ayenera kumva choonadi chamtengo wapatali chimene ndinachipeza movutikirachi. Ndinayamba kulalikira nthaŵi zonse, zomwe zinali zovuta kwambiri ku Czechoslovakia m’zaka zakumapeto kwa m’ma 1930. Ngakhale kuti ntchito yathu inali yololedwa mwalamulo, atsogoleri a zipembedzo ankachititsa anthu kulimbana nafe kwambiri.

Kuzunzidwa Koyamba

Tsiku lina chakumapeto kwa chaka cha 1937, ndinkalalikira ndi mlongo wina wachikristu m’mudzi wakufupi ndi ku Lučenec. Pasanathe nthaŵi yaitali anatimanga n’kutipititsa ku ndende. Msilikali wina yemwe anali mlonda pandendepo anatseka chitseko cha chipinda chimene anatiloŵetsamo, mochimenyetsa, ndipo anati: “Mufera muno.”

Pofika madzulo, m’chipindamo tinali titalandira akaidi enanso anayi. Tinayamba kuwalimbitsa mtima ndiponso kuwalalikira. Iwo anakhazika mtima pansi, ndipo usiku wonse tinachezera kuwauza choonadi cha m’Baibulo.

Panthaŵi ya sikisi koloko m’maŵa, mlondayo anandiuza kuti ndituluke m’chipindamo. Ndinauza mnzanga uja kuti: “Tikakumananso mu Ufumu wa Mulungu.” Ndinamuuza kuti akanene zimene zachitikazi kwa achibale anga ngati iye atapulumuka. Ndinapemphera chamumtima ndipo kenaka ndinatsatira mlondayo. Iye anapita nane kunyumba kwake pandende pomwepo. Ndiye anandiuza kuti, “Ndikufuna ndikufunse. Dzulo usiku uja iweyo unanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Tandisonyeza pamene analemba zimenezi m’Baibulo.” Ndinadabwa kwambiri komanso mtima wanga unakhala m’malo! Iye anabweretsa Baibulo lake, ndipo ndinamusonyeza dzina la Yehova, mkazi wake alinso pomwepo. Anandifunsanso mafunso ena ambiri pa zinthu zimene tinakambirana ndi amayi anayi aja usiku. Atakhutira ndi mmene ndinamuyankhira, anauza mkazi wake kuti akonze chakudya cham’maŵa choti ineyo ndi mnzanga uja tidye.

Patatha masiku angapo anatimasula, koma woweruza mlandu wathu ananena kuti poti ndinali nzika ya dziko la Hungary, ndinayenera kuchoka ku Czechoslovakia. Izi zitachitika m’pamene Tibor Haffner anandifunsira kuti ndimange naye banja. Tinakwatirana, ndipo ndinasamukira kunyumba kwa makolo ake kumene iyeyo ankakhala.

Chizunzo Chifika Poipa

Ineyo ndi mwamuna wanga tinapitiriza ntchito yolalikira, ngakhale kuti Tibor ankagwiranso ntchito ina yokhudza gululi. Patangotsala masiku ochepa chabe kuti asilikali a ku Hungary aloŵelere mumzinda wathu mu November 1938, mwana wathu yemwe anatenga dzina la bambo ake loti Tibor, anabadwa. Ku Ulaya, nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inali itatsala pang’ono kuyambika. Mbali yaikulu ya dziko la Czechoslovakia inalandidwa ndi dziko la Hungary, zimene zinapangitsa kuti a Mboni za Yehova amene ankakhala m’madera olandidwawo azunzidwe kwambiri.

Pa October 10, 1942, Tibor ananyamuka kupita ku Debrecen kuti akakumane ndi abale ena ndi ena. Koma atapita sanabwerereko. Pambuyo pake anadzandiuza zimene zinachitika. M’malo mokumana ndi abale, apolisi ovala zovala wamba anali pa mlatho pamene abale anakonza zoti achitirepo msonkhanowo. Iwo ankadikirira mwamuna wangayu ndi Pál Nagypál, amene anali omalizira kufika pamalopo. Apolisiwo anapita nawo ku siteshoni ya polisi n’kuyamba kuwamenya ndi zibonga m’mapazi atawavula nsapato mpaka anakomoka ndi ululu.

Kenaka anawauza kuti avale nsapato zawozo n’kuimirira. Ngakhale kuti anali kumva ululu anawakakamiza kuti apite ku siteshoni ya sitima. Apolisiwo anabweretsa munthu wina amene mutu wake anaumanga mabandeji ambirimbiri mwakuti ankachita kulephera kuona bwinobwino. Uyu anali Mbale András Pilling, amenenso anabwera kumsonkhanowo. Mwamuna wanga anapita naye kokam’tsekera m’mudzi wa Alag, kufupi ndi mzinda wa Budapest. Mmodzi mwa alonda amene anaona kuti Tibor wamenyedwa kwambiri m’mapazi anayankhula mwachipongwe amvekere: “Koma ndiye anthu ali ndi nkhanza bwanji! Osadandaula bambo, tikuthandizani kuti mabala anu apole.” Kenaka alonda ena aŵiri anayamba kumumenya Tibor m’mapazi ake muja moti malo onsewo anali magazi okhaokha. Patatha kanthaŵi pang’ono, anakomoka.

Mwezi wotsatira, Tibor komanso abale ndi alongo oposa 60 anatengeredwa kukhoti. Mbale András Bartha, Mbale Dénes Faluvégi, ndi Mbale János Konrád anawapatsa chilango cha imfa yochita kuwamangirira. Mbale András Pilling anapatsidwa chilango chakuti akhale m’ndende kwa moyo wake wonse, ndipo mwamuna wanga anapatsidwa chilango choti akhale m’ndende zaka 12. Kodi analakwa chiyani? Wowaimba mlanduyo ananena kuti iwo anaukira boma, anakana kuloŵa usilikali, anali akazitape, ndiponso ankanena mabodza oipitsa tchalitchi choyera kwambiri. Chilango chakuti akaphedwe chija anadzachisintha kuti angokhala m’ndende kwa moyo wawo wonse.

Kutsatira Mwamuna Wanga

Patatha masiku aŵiri kuchokera panthaŵi imene Tibor ananyamuka kupita kumsonkhano wa ku Debrecen, ndinadzuka m’maŵa nthaŵi isanakwane sikisi koloko, n’kuyamba kusita zovala. Mwadzidzidzi ndinangomva kugogoda mwamphamvu pakhomo. Ndinaganiza kuti ‘Abwera anthu aja.’ Kenaka apolisi sikisi analoŵa m’nyumbamo n’kundiuza kuti alandira chilolezo chakuti afufuze m’nyumbamo. Tonse amene tinali m’nyumbamo, kuphatikizapo mwana wathu wamwamuna wa zaka zitatu, anatimanga n’kutipititsa ku siteshoni ya polisi. Tsiku lomwelo anatisamutsira ku ndende ina ya ku Pétervására m’dziko la Hungary.

Titafika kumeneko, ndinatentha thupi, ndipo anandichotsa pakati pa akaidi anzanga. Nditachira, asilikali aŵiri analoŵa m’chipinda chimene ndinali n’kuyamba kumakangana za ine. Wina anati, “Timuwombere ameneyu! Ndimuwombera ineyo!” Koma winayo amafuna adziŵe kaye kuti ndili bwanji asanachite chilichonse. Ndinawachonderera kuti asandiphe. Mapeto ake iwo anatuluka m’chipindamo ndipo ndinathokoza Yehova pondithandiza.

Asilikaliŵa anali ndi njira yawoyawo yokakamizira munthu kuti aulule zinthu zimene iwowo ankafuna kudziŵa. Anandiuza kuti ndigone chafufumimba, anandiika sokosi mkamwa, anamanga manja ndi mapazi anga, n’kuyamba kundikwapula mpaka kutuluka magazi. Anasiya kundikwapula pamene mmodzi wa asilikaliwo ananena kuti watopa. Anandifunsa kuti mwamuna wanga ankafuna kukakumana ndi ndani tsiku limene anamangidwa lija. Sindinawauze, motero anapitiriza kundimenya kwa masiku atatu. Pa tsiku lachinayi, anandilola kutenga mwana wanga kukamusiya kwa mayi anga. Kunja kukuzizira kwambiri, ndinabereka mwana wanga ngakhale kuti ndinali nditavulazidwa kumsana, n’kuyenda mtunda wokwana makilomita 13 kupita ku siteshoni ya sitima. Kuchoka kumeneku, ndinapitiriza ulendo wanga pasitima, koma ndinayenera kubwerera ku kampu tsiku lomwelo.

Anandilamula kuti ndikhale zaka sikisi m’ndende ya ku Budapest. Nditafika ku ndendeko, ndinamva kuti Tibor anali komwekonso. Tinasangalala kwambiri kuti anatilola kulankhulana, ngakhale kuti tinkalankhulana pa mpanda wa zitsulo kwa kanthaŵi kochepa chabe! Panthaŵi yosaonekaonekayi, ine ndi mwamuna wanga tinaona kuti Yehova amatikonda kwambiri ndipo zimenezi zinatilimbikitsa zedi. Tisanakumanenso, tonsefe tinakumana ndi ziyeso zoopsa kwambiri, mwakuti nthaŵi zambiri tinkachita kupulumuka lokumbakumba.

Kuchoka Kundende Ina Kupita Kundende Inanso

Alongo pafupifupi 80 anatiika m’chipinda chimodzi momwe tinali kupanikizana kwambiri. Tinkalakalaka chakudya chauzimu, koma zinkaoneka kuti zinali zosatheka kuti chakudyacho chifike m’ndendemo. Kodi tikanatha kuchipeza m’ndende momwemo? Taimani ndikuuzeni zimene tinachita. Ndinadzipereka kuti ndizisoka sokosi za makalaliki pa ndendepo. M’sokosi ina, ndinaikamo kakalata kopempha kuti andiuze nambala zimene ndingagwiritse ntchito pobwereka Baibulo ku laibulale ya pa ndendepo. Popeŵa kuti angatikayikire, ndinapemphanso kuti andiuze nambala za mabuku ena aŵiri.

Tsiku lotsatira, makalaliki anandipatsa mulu wina wa masokosi. M’sokosi ina munali yankho la zimene ndinapempha zija. Ndiyeno ndinam’patsa mlonda nambalazo kuti akanditengere mabukuwo. Tinasangalala kwambiri titalandira mabukuwo, pamodzi ndi Baibulo! Mabuku enawo tinali kubweza mlungu uliwonse ndi kubwereka ena, koma Baibulo sitinkabweza. Mlonda uja akatifunsa za Baibulo lija, tinkamuuza kuti: “Poti ndi buku lalikulu aliyense akufuna kuliŵerenga.” Choncho tinali ndi mwayi woŵerenga Baibulo.

Tsiku lina, ofesala wina anandiitana ku ofesi yake. Ankaoneka waulemu kusiyana ndi masiku ena.

Iye anati: “Mayi Haffner, ndikufuna ndikuuzeni nkhani yabwino. Mukhoza kumapita kwanu m’maŵa, ngakhale lero lomwe ngati pali sitima yopita kwanu.”

Ndinayankha kuti: “Zingakhale bwino kwambiri.”

Iye anati: “Inde, n’zabwinodi. Muli ndi mwana ndipo ndikukhulupirira kuti mukufuna kukamulera.” Ndiye anati, “Mungosaina kalata iyi.”

Ndinamufunsa kuti: “Ndi kalata ya chiyani?”

Iye ananenetsa kuti: “Zimenezo zilibe kanthu, ingosainani, ndipo muzipita.” Ndiye anandiuza kuti: “Mukapita kunyumba mukhoza kukachita chilichonse chimene mukufuna. Koma panopo musaine kuti si inunso wa Mboni za Yehova.”

Ndinabwerera m’mbuyo ndipo ndinakanitsitsa.

“Ndiyetu ufera konkuno, uona!” anatero mokalipa ndipo anandiuza kuti ndizipita.

Mu May 1943, anandipititsa ku ndende ina ya ku Budapest ndipo patapita nthaŵi anandipititsa ku mudzi wa Márianosztra, kumene tinali kukhala m’nyumba ya amonke ndi masisitere pafupifupi 70. Ngakhale kunali njala ndi mavuto ena, tinali okonzeka kuwauza chiyembekezo chathu. Sisitere wina anachita chidwi kwambiri ndi uthenga wathu ndipo anati: “Zimenezi ndi zinthu zabwino kwambiri. Sindinazimveko zimenezi. Pitirizani kundiuza.” Tinamuuza za dziko latsopano ndi moyo wabwino umene udzakhale m’menemo. Tili m’kati mokambirana, panafika sisitere wamkulu. Ndipo nthaŵi yomweyo anamutenga sisitere wachidwi uja kukam’vula zovala, ndi kuyamba kumukwapula kwambiri. Titakumana nayenso, anatichonderera kuti: “Mundipempherere kwa Yehova kuti andipulumutse ndi kundichotsa kuno. Ndikufuna kukhala m’gulu lanu.”

Kenako tinakakhala m’ndende ina yakale ku Komárom, mzinda wa m’mphepete mwa mtsinje wa Danube, umene uli pamtunda wa makilomita 80 kumadzulo kwa mzinda wa Budapest. Moyo kumeneko unali wovuta kwambiri. Monga mmene anachitira alongo ena, ndinadwala kwambiri matenda ofanana ndi tayifodi, ndipo ndinkasanza magazi komanso ndinafooka kwambiri. Tinalibe mankhwala, moti ndinkangoona kuti ndifa basi. Komano maofesala anali kufuna munthu amene angathe kugwira ntchito mu ofesi. Alongo aja anatchula ine. Choncho, anandipatsa mankhwala ndipo ndinachira.

Kukhaliranso Limodzi ndi Anthu a M’banja Langa

Asilikali a dziko la Soviet atayandikira kum’maŵa kwa dziko lathu tinakakamizika kusamukira kumadzulo kwake. Kuti ndifotokoze mavuto onse amene tinakumana nawo kungatenge nthaŵi yaitali. Ndinatsala pang’onong’ono kufa maulendo angapo, koma ndinapulumuka chifukwa chakuti dzanja la Yehova linanditeteza. Nkhondo itatha, tinali mu mzinda wa Tábor ku Czechoslovakia, umene unali pa mtunda wa makilomita 80 kuchokera ku Prague. Ine ndi mlamu wanga Magdalena panatitengera milungu itatu kuti tikafike kunyumba kwathu ku Lučenec, pa May 30, 1945.

Ndili patali, ndinaona apongozi anga aakazi ndi mwana wanga wokondedwa, Tibor, ali panja. Misozi inalengeza m’maso mwanga, ndipo ndinaitana kuti “Tibike!” Iye anandithamangira ndipo ndinam’nyamula. Mawu ake oyamba anali akuti, “Amayi simuchokanso, eti?” ndipo sindidzaiŵala mawu ameneŵa.

Yehova anachitiranso chifundo mwamuna wanga, Tibor. Kuchoka ku ndende ya ku Budapest, anatumizidwa ku msasa wolangirako anthu ku Bor, pamodzi ndi abale ena pafupifupi 160. Anapulumuka imfa maulendo ambiri, koma onse monga gulu, anapulumutsidwa. Tibor anabwerera kunyumba pa April 8, 1945, patatha pafupifupi mwezi umodzi m’pamene ine ndinafika panyumba.

Nkhondo itatha, tinafunikirabe mphamvu za Yehova kuti tipirire ziyeso zonse m’zaka 40 zotsatira za ulamuliro wachikomyunizimu ku Czechoslovakia. Tibor anamulamulanso kuti akhale m’ndende kwanthaŵi yaitali, ndipo ndinasamalira ndekha mwana wathu. Atatuluka m’ndende, Tibor anakhala woyang’anira woyendayenda. Mu ulamuliro wa zaka 40 wachikomyunizimu, tinagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuuza ena chikhulupiriro chathu. Tinathandiza ambiri kuphunzira choonadi. Ndipo ameneŵa anakhala ana athu auzimu.

Tinasangalala kwambiri kulandira ufulu wopembedza mu 1989. Chaka chotsatira, tinapezeka pamsonkhano wachigawo woyamba m’dziko lathu patatha nthaŵi yaitali zedi. Titaona abale ndi alongo athu ambirimbiri amene anakhala okhulupirika kwa zaka zambiri, tinazindikira kuti Yehova ndiye gwero lalikulu limene linapatsa mphamvu anthu onsewo.

Mwamuna wanga wokondedwa Tibor, anamwalira ali wokhulupirika kwa Mulungu pa October 14, 1993, ndipo tsopano ndikukhala pafupi ndi mwana wanga m’tauni ya Žilina, ku Slovakia. Pano thupi langa lilibe mphamvu kwenikweni, koma maganizo anga ndi olimba chifukwa cha mphamvu za Yehova. Sindikayikira konse kuti mwa mphamvu zake ndingapirire chiyeso chilichonse m’dongosolo lakale lino. Komanso, ndikuyembekezera nthaŵi imene, mwa chisomo cha Yehova, ndidzakhale ndi moyo kosatha.

[Chithunzi patsamba 20]

Mwana wanga, amene anatenga dzina la bambo ake, Tibor, (ali ndi zaka 4) amene ndinamusiya

[Chithunzi patsamba 21]

Mwamuna wanga Tibor, ndi abale ena ku Bor

[Chithunzi patsamba 22]

Ndili ndi Tibor ndi Magdalena, mlamu wanga, mu 1947, ku Brno

[Zithunzi patsamba 23]

Ndinatsala pang’onong’ono kufa maulendo angapo, koma ndinapulumuka chifukwa chakuti dzanja la Yehova linanditeteza