Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tikufuna Kudzanena Kuti, ‘Inde!’”

“Tikufuna Kudzanena Kuti, ‘Inde!’”

“Tikufuna Kudzanena Kuti, ‘Inde!’”

POSACHEDWAPA ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Nigeria inalandira kalata. Zina zimene zinalembedwamo ndi izi:

“Mwana wathu, Anderson, anamwalira ali ndi zaka 14. Asanamwalire, ankaŵeta nkhuku ziŵiri. Iye ankafuna kudzazigulitsa n’kutumiza ndalama zakezo ku ofesi ya nthambi kuti zikathandizire ntchito yolalikira ya padziko lonse. Komano anamwalira zisanafike pozigulitsa.

“Pofuna kukwaniritsa zimene iyeyu ankalakalaka, ifeyo, makolo ake, tinaŵeta nkhukuzo n’kumugulitsira. Tikukutumizirani ndalamazi, monga zoperekedwa ndi Anderson. Chifukwa cha lonjezo la Yehova, sitikukayika n’komwe kuti posachedwapa tidzamuonanso Anderson. Tikufuna kudzanena kuti, ‘Inde!’ akadzatifunsa ngati tinakwaniritsa zimene mtima wake unkalakalaka. Inde, sikuti tikuyembekezera kudzaona Anderson yekha koma tikuyembekezeranso kudzaona ‘mtambo waukulu wa mboni’ zimene zidzaukitsidwe.”​—Ahebri 12:1; Yohane 5:28, 29.

Monga mmene kalata imeneyi ikuonetsera, kukhulupirira chiukiriro kumalimbikitsa Akristu oona. Mabanja ochuluka kwambiri adzasangalala, monga banja la Anderson, akamadzalandira okondedwa awo amene mdani wotchedwa imfa anawalanda!​—1 Akorinto 15:24-26.

Mawu a Mulungu amatiuza za chiyembekezo cholimbikitsa chimenechi cha chiukiriro chomwe n’chimodzi mwa zinthu zambirimbiri zosangalatsa zimene zidzachitike posachedwapa m’dziko latsopano lolungama lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. (2 Petro 3:13) Ponena zimene Mulungu adzachitire anthu panthaŵi imeneyi, Baibulo limati: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.