Kodi Anthu Akusoŵeka Malangizo Abwino?
Kodi Anthu Akusoŵeka Malangizo Abwino?
MASIKU ano, anthu ambiri amaganiza kuti amadziŵa kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndipo amaganizanso kuti ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna. Anthu ena amanena kuti munthu akhoza kuchita chilichonse malinga ngati chikum’sangalatsa. Ukwati ndiponso moyo wa banja, zimene anthu akhala akuziona kuti ndi zinthu zofunika, zasokonezeka kwambiri.—Genesis 3:5.
Taganizirani zimene zinam’chitira Verónica, * amene akukhala ku Mexico. Iye anati: “Ine ndi mwamuna wanga titatsala pang’ono kukwanitsa zaka 15 tili m’banja, mwamuna wanga anandiuza kuti anali pachibwenzi ndi mkazi wina. Iye anandiuza kuti sangamusiye mkaziyo chifukwa ndi wachitsikana komanso amam’sangalatsa. Zinkandiwawa kwambiri ndikaganiza kuti mnzanga wa pamtimayo sazikhala nanenso. Ndinkaganiza kuti imfa ya anthu amene timawakonda ndicho chinthu chopweteka kwambiri. Komano kusakhulupirika kwa mwamuna wangaku kunandipweteka koopsa chifukwa ndinataya munthu amene ndinali kumukonda kwambiri komanso chifukwa choti anapitirizabe kuchita zinthu zondipweteka mtima.”
Ndiyeno pali nkhani ya mwamuna wina wazaka 22 amene anasudzulidwa ndipo ali ndi mwana koma safuna kukwanitsa udindo wake monga bambo. Amafuna kuti amayi ake azimusamalira pamodzi ndi mwana wakeyo. Mayi akewo akapanda kuchita zonse zimene iye akufuna, iye amakwiya ndipo amawalalatira, monga mmene amachitira mwana wosimbwa. Amayi akewo amathedwa nzeru kwambiri ndi khalidwe lake loipali.
Izi si zachilendo. Kupatukana ndi kusudzulana kwa maukwati olembetsedwa ku boma n’kofala kulikonse. Ana ambiri amaona makolo awo akusiyana wina n’kukakhala payekha. Ana ena
salemekeza n’komwe anthu ena, ngakhale makolo awo amene, ndipo amachita zinthu zimene m’mbuyomo zinali zovuta kuziganizira. M’mayiko ambiri ana ambiri amagonana ndi anthu osiyanasiyana m’njira zosiyanasiyana pofuna kudziŵa mmene zimakhalira, amagwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, amachita zachiwawa, ndiponso amapha aphunzitsi kapena makolo awo. Ndipo mwina mwaona kuti sikuti n’kulera ana kokha kapenanso ukwati wokha zimene zikuvuta masiku ano.Tikaona zinthu zimenezi, tingafunse kuti kodi anthu atani? Ngati anthu amadziŵadi kusiyanitsa chabwino ndi choipa, n’chifukwa chiyani pali mavuto ambiri chonchi? Kodi anthu akusoŵeka malangizo abwino? Kodi kulipo kumene tingapeze malangizo abwino, amene asonyeza kuti n’ngodalirika? Ngakhale kuti anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira Mulungu ndi Mawu ake olembedwa, zochita zawo sizisonyeza kuti amaterodi. Kodi tingapindule chiyani pofunafuna ndi kupeza malangizo kwa Mulungu? Tiyeni tione zimenezi m’nkhani yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Dzinali talisintha.