Kodi Mukukumbukira?
Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwapindula poŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:
• Kodi Baibulo lotchedwa Complutensian Polyglot linali lotani, ndipo kodi linali lofunika motani?
Linali Baibulo losindikizidwa lokhala ndi Malemba abwino kwambiri amene analipo panthaŵiyo a zilankhulo za Chihebri, Chigiriki ndi Chilatini, komanso ndi mbali zina za Chialamu ndipo Malembaŵa anawaika m’madanga ogundizana patsamba lililonse la Baibuloli. Baibulo la zinenero zingapo limeneli linathandiza kwambiri pantchito yokonza Malemba olondola a zilankhulo zoyambirira za m’Baibulo.—4/15, tsamba 28 mpaka 31.
• Kodi zingatheke bwanji kuti anthu asangalatse Mulungu?
Chifukwa chakuti Yehova ndi munthu weniweni wamoyo, amatha kuganiza, kuchita zinthu, ndiponso kusangalala kapena kupwetekedwa mtima. Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe” ndipo amasangalala akakwaniritsa cholinga chake. (1 Timoteo 1:11, NW; Salmo 104:31) Tikamachita zinthu moganizira kwambiri mmene Mulungu angamvere mumtima mwake, ndiye kuti tizichita zinthu moganiziranso kwambiri mmene tingam’sangalatsire.—5/15, tsamba 4 mpaka 7.
• N’chifukwa chiyani Davide analola mkazi wake Mikala kukhala ndi terafi, kapena kuti chifanizo?
Mfumu Sauli atakonza chiwembu chopha Davide, Mikala anathandiza Davide kuthaŵa poika pakama chifanizo chimene mwina chinali chosemedwa ngati munthu. N’kutheka kuti Mikala anali ndi chifanizochi chifukwa chakuti sankalambira Mulungu ndi mtima wonse. Mwina Davide sankadziŵa zimenezi, apo ayi anachita kuzilekerera dala chifukwa chakuti Mikala anali mwana wa Mfumu Sauli. (1 Mbiri 16:25, 26)—6/1, tsamba 29.
• Kodi mfundo yaikulu imene malamulo a Mulungu okhudza magazi ankagogomezera inali yotani?
Mulungu anapereka malamulo pambuyo pa Chigumula, m’Chilamulo cha Mose, komanso pa Machitidwe 15:28, 29, posonyeza nsembe imene Yesu anapereka ndi mwazi wake umene unakhetsedwa. Ndi mwazi wokhawu umene umatheketsa kuti tikhululukidwe ndiponso kukhala pamtendere ndi Mulungu. (Akolose 1:20)—6/15, tsamba 14 mpaka 19.
• Kodi ndi zozizwitsa zochuluka motani zimene Yesu anachita zimene zinatchulidwa m’Baibulo?
Nkhani za m’Mauthenga Abwino zimatchula zozizwitsa 35 zimene Yesu anachita. Koma chiŵerengero cha zozizwitsa zonse zimene Yesu anachita, kuphatikizapo zimene sizinalembedwe, sichikudziŵika. (Mateyu 14:14)—7/15, tsamba 5.