Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Anthu ena amati ngalawa imene Paulo anakwera sinaswekere pa chilumba cha Melita, chimene chili kum’mwera kwa mzinda wa Sicily, koma amati inaswekera pa chilumba china. Ndiye kodi ngalawayi inaswekera kuti makamaka?
Funso limeneli labwera chifukwa cha zimene zatchulidwa chaposachedwapa zakuti ngalawa imene mtumwi Paulo anakwera sinaswekere pa chilumba cha Melita, koma ku Cephalonia (kapena, Kefallinía) pafupi ndi Corfu m’nyanja yotchedwa Ionia, kugombe la kumadzulo kwa dziko la Girisi. Mawu ouziridwa amatiuza kuti Paulo ndi anzake anachokera ku Kaisareya ali m’manja mwa kazembe wachiroma wotchedwa Julius pamodzi ndi asilikali ena. Monga mmene mapuŵa akusonyezera, iwoŵa anayenda panyanja n’kukafika ku Sidoni ndi ku Mura. Kenaka anakwera ngalawa yaikulu yonyamula zakudya kuchoka nazo ku Alesandreya, m’dziko la Aigupto, Machitidwe 27:1–28:1.
kuloŵera nazo chakumadzulo n’kukafika ku Knido. Iwo analephera kupitiriza ulendowu potsata njirayi, yodzera m’nyanja yotchedwa Ejani kudutsa kunsonga kwa dziko la Girisi n’kukafika ku Roma. Chifukwa choti panyanja panachita mphepo kwambiri iwo analoŵera kum’mwera cha ku chilumba cha Krete kuti akapeze malo abwino okochezapo ngalawa m’magombe a chilumbachi. Kumeneku anaima pa gombe lotchedwa Pokocheza Pokoma. ‘Atachoka ku Krete,’ chombocho chinawombedwa mwamphamvu ndi “mphepo ya namondwe, yonenedwa Eurokulo.” Ngalawa yonyamula zakudyayi, yomwe inali yolemera kwambiri ‘inatengedwa kwina ndi kwina,’ kapena kuti kukankhidwira uku ndi uku mpaka kufika tsiku la nambala 14 nthaŵi ya usiku. Mapeto ake, ngalawayo yomwe inali ndi anthu 276 inasweka pa chilumba chimene Malemba Opatulika Achigiriki amachitcha kuti Me·liʹte.—M’mbuyo monsemu anthu akhala akunena maganizo osiyanasiyana pankhani yakuti chilumba cha Me·liʹte n’chiti makamaka. Ena akhala akuganiza kuti chinali chilumba chimene chinkatchedwa kuti Melite Illyrica, chomwe panopo chimatchedwa kuti Mljet, ndipo chili m’nyanja yotchedwa Adria chakugombe la dziko la Croatia. Koma zimenezi n’zokayikitsa, chifukwa chakuti chilumba cha Mljet chili kumpoto motero sizingakhale zomveka kuti Paulo atachoka kumeneko analoŵera ku Surakusa, Sicily, ndipo kenaka ku gombe la kumadzulo kwa dziko la Italy.—Machitidwe 28:11-13.
Omasulira Baibulo ambiri amanena kuti chilumba chotchedwa Me·liʹte ndicho chilumba cha Melite Africanus, chimene panopa chimatchedwa kuti Malta kapena kuti Melita, pa Chichewa. Malo otsiriza amene ngalawa imene inatenga Paulo inaimapo anali malo otchedwa Pokocheza Pokoma, a ku Krete. Kenaka chimphepo chinachititsa kuti ngalawayi iloŵere kumadzulo cha ku Kauda. Chimphepo chinakankha ngalawayo kwa masiku ambiri. Motero, n’zochita kuonekeratu kuti poti ngalawayi inali kukankhidwa ndi chimphepo ndiye kuti inkangoloŵera kumadzulo mpaka kukafika ku Melita.
Akatswiri ena odziŵa bwino nkhaniyi, Conybeare ndi Howson, analemba mawu otsatiraŵa m’buku lakuti The Life and Epistles of St. Paul poganizira za mtundu wa mphepo imene inkakankha ngalawayo komanso “kumene mphepoyi inkapititsa ngalawayo.” Iwo anati: “Mtunda wochoka ku Clauda [kapena Kauda] kukafika ku Melita ndi wosakwana makilomita 770. Izi n’zomveka kwabasi, moti n’zodabwitsa kuti anthu ena akukhulupirira kuti nthaka imene anthu a m’ngalawayi anafikapo pa tsiku la nambala 14 nthaŵi yausiku, ndi chilumba china osati cha Melita. Chifukwatu n’zochita kuonekeratu kuti inali nthaka ya chilumba chimenechi.”
Ngakhale kuti pali kusiyana maganizo pankhaniyi, zakuti ngalawayo inawaswekera ku Melita malingana ndi mmene mapu a m’nkhani inoŵa akusonyezera ndizo zikuoneka kuti zikugwirizanadi ndi mmene nkhaniyi inasimbidwira m’Baibulo.
[Mapu/Chithunzi patsamba 31]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Yerusalemu
Kaisareya
Sidoni
Mura
Knido
KRETE
KAUDA
MELITA
SICILY
Surakusa
Roma
MLJET
GIRISI
CEPHALONIA