“Ntchito Yabwino Kwambiri”
“Ntchito Yabwino Kwambiri”
ALEXIS ndi mnyamata wazaka zisanu ndipo amakhala mu mzinda wa Morelia, m’dziko la Mexico. Makolo ake akuphunzira Baibulo komanso amapezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Ali pamsonkhano wadera ndi makolo ake komanso azibale ake, anaona chitsanzo cha ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. Nthaŵi yomweyo iye anayang’ana bambo ake ndi kuwafunsa kuti, “Ababa, ababa, kodi n’chifukwa chiyani simupita kolalikira?” Bambo akewo anayankha kuti, “Sindinamalize kuphunzira.” Alexis ananena mosangalala kuti, “Ababa, imeneyitu ndiye ntchito yabwino kwambiri.”
Kamwana kameneka kanaona kufunika kochita zinthu mogwirizana ndi zimene kanali kudziŵa ponena za Yehova. Popeza kuti kunyumba kwawoko kumakhalanso asuwani ake ena aang’ono, Alexis anayamba kaye wapemphera kwa Yehova n’kuwauza zimene makolo ake anam’phunzitsa m’buku lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Ngakhale kuti Alexis sankadziŵa kuŵerenga, anali kuzidziŵa bwino zedi nkhani za m’bukuli mwa kungoona zithunzi zofotokoza nkhanizo. Iye anatinso ankafuna kuyendera anthu m’nyumba zawo kukawauza zimene anali kuphunzira ponena za zolinga za Mulungu.
N’zoona, ana ndi akulu omwe angachite zimene Yehova, “Woyera,” amafuna kuti azichita motero n’kukhala ndi mwayi wosayerekezereka wolalikira za iye kwa anthu. (Yesaya 43:3; Mateyu 21:16) Ndithudi, imeneyi ndi ntchito imodzi yabwino kwambiri imene munthu angachite.