Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Odedwa Popanda Chifukwa

Odedwa Popanda Chifukwa

Odedwa Popanda Chifukwa

“Anandida Ine kopanda chifukwa.”​—YOHANE 15:25.

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena amadabwa anthu akamanyoza Akristu, koma kodi n’chifukwa chiyani ife sitiyenera kudabwa nazo? (b) Kodi m’nkhaniyi tiona za “chidani” chamtundu uti? (Onani mawu am’munsi.)

MBONI ZA YEHOVA zimayesetsa kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu. Motero, Mboni zili ndi mbiri yabwino m’mayiko ambiri. Komabe, nthaŵi zina anthu amaziipitsira mbiri yawo. Mwachitsanzo, mkulu wina waboma mu mzinda wa St. Petersburg, ku Russia, anati: “Tinkauzidwa kuti Mboni za Yehova ndi kagulu kachipembedzo ka anthu ochita zinthu mobisa ndipo amapha ana anawo ndiponso amadzipha okha.” Koma mkulu wabomayu atagwira ntchito limodzi ndi Mboni za Yehova pokonzekera msonkhano wawo wa mayiko, anati: “Tsopano ndikuona kuti ndi anthu abwinobwino komanso ansangala . . . Ndi anthu amtendere ndiponso odekha, ndipo amakondana kwambiri.” Ananenanso kuti: “Sindikumvetsa kuti n’chifukwa chiyani anthu amawanamizira choncho.”​—1 Petro 3:16.

2 Atumiki a Mulungu sasangalala anthu akamawaipitsira mbiri, komatu zimenezi siziwadabwitsa. Yesu anachenjezeratu otsatira ake kuti: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. . . . Chitero, kuti mawu olembedwa m’chilamulo chawo akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.” * (Yohane 15:18-20, 25; Salmo 35:19; 69:4) Iye anali atawauza kale ophunzira akewo kuti: “Ngati anamutcha mwinibanja Beelzebule, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?” (Mateyu 10:25) Akristu amadziŵa kuti kupirira kunyozedwa mwamtundu umenewu ndi mbali ya “mtanda” umene anavomera kunyamula pamene anakhala otsatira Kristu.​—Mateyu 16:24.

3. Kodi olambira oona azunzidwa kwambiri motani?

3 Olambira oona anayamba kuzunzidwa kuyambira kalekale, kuchokera pa “Abele wolungamayo.” (Mateyu 23:34, 35) Sikuti izi zakhala zikuchitika maulendo ochepa chabe. Yesu ananena kuti otsatira ake ‘adzadedwa ndi anthu onse’ chifukwa cha dzina lake. (Mateyu 10:22) Komanso, mtumwi Paulo analemba kuti anthu onse otumikira Mulungu, kuphatikizapo tonsefe, ayenera kuyembekezera kuzunzidwa. (2 Timoteo 3:12) Kodi chifukwa chake n’chiyani?

Amene Amachititsa Kuti Tizizunzidwa Popanda Chifukwa

4. Kodi Baibulo limati ndi ndani amene amachititsa kuti tizidedwa popanda chifukwa?

4 Mawu a Mulungu amasonyeza kuti pali munthu wina wosaoneka amene kuyambira pachiyambi wakhala akuchititsa kuti olambira oona azidedwa. Taganizirani za kuphedwa mwankhanza kwa Abele, amene anali munthu woyamba kukhala wokhulupirika. Baibulo limanena kuti mchimwene wake Kaini, amene anamupha, ‘anachokera mwa woipayo,’ amene ndi Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 3:12) Kaini anatengera mtima wa Satana, ndipo Satanayu anam’gwiritsira ntchito kuchita zofuna zake zoipa. Baibulo limatiuzanso zimene Satana anachita povutitsa mwankhanza Yobu ndi Yesu Kristu. (Yobu 1:12; 2:6, 7; Yohane 8:37, 44; 13:27) Buku la Chivumbulutso limatchula mosapita m’mbali munthu amene amachititsa kuti otsatira a Yesu azizunzidwa. Limati: ‘Mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe.’ (Chivumbulutso 2:10) Inde, Satana ndiye amachititsa kuti anthu a Mulungu azidedwa popanda chifukwa.

5. Kodi n’chifukwa chiyani Satana amadana ndi olambira oona?

5 Kodi n’chifukwa chiyani Satana amadana ndi olambira oona? Pa chiwembu chake chomwe chinasonyeza kuti amafuna ulemu waukulu kwambiri, Satana anayamba kulimbana ndi Yehova Mulungu, amene ndi “Mfumu yosatha.” (1 Timoteo 1:17; 3:6) Iye amanena kuti Mulungu amalamulira zolengedwa zake mopondereza kwambiri ndiponso amanena kuti palibe munthu amene amatumikira Yehova ndi cholinga chabwino, koma kuti anthu amam’tumikira chifukwa chadyera. Satana amanena kuti ngati atapatsidwa mwayi woti ayese anthu, iye angachititse anthu onse kusiya kutumikira Mulungu. (Genesis 3:1-6; Yobu 1:6-12; 2:1-7) Pomunamizira Yehova kuti ndi wopondereza, wabodza, ndiponso wolephera, Satana amafuna kuti nayenso azilamulira nawo chilengedwe chonse ngati Yehova. Motero mtima wofuna kuti azilambiridwa ndiwo ukuchititsa kuti alusire atumiki a Mulungu.​—Mateyu 4:8, 9.

6. (a) Kodi nkhani ya ulamuliro wa Yehova imatikhudza bwanji ifeyo patokha? (b) Kodi kumvetsa nkhani imeneyi kungatithandize motani kuti tikhalebe okhulupirika? (Onani bokosi patsamba 16.)

6 Kodi mukuona mmene nkhaniyi ikukukhudzirani? Mosakayikira, popeza kuti ndinu mtumiki wa Yehova, munaona kale kuti ngakhale kuti pamafunika khama kuti muchite zofuna za Mulungu, phindu lake limakhala lalikulu kwambiri. Komano mungatani ngati zinthu zina pamoyo wanu zikukuchititsani kuti mulephere kutsatirabe malamulo ndi mfundo za Yehova kapena kuti muwamve kuwawa? Ndipo mungatani mukamaona ngati simukupindula chilichonse potumikira Yehova? Kodi munganene kuti kupitiriza kutumikira Yehova n’kopanda phindu? Kapena mungapitirize kuchita zofuna za Yehova chifukwa choti mumam’konda ndiponso mumayamikira makhalidwe ake apamwamba? (Deuteronomo 10:12, 13) Polola Satana kutibweretsera mavuto, Yehova anapatsa aliyense wa ife payekha mwayi wopereka yankho lake pa zimene Satana amanena.​—Miyambo 27:11.

‘Anthu Akamakunyazitsani’

7. Kodi imodzi mwa njira zimene Mdyerekezi amagwiritsa ntchito pofuna kutichotsa kumbali ya Yehova ndi iti?

7 Tiyeni tsopano tione mwatsatanetsatane imodzi mwa njira zimene Satana amagwiritsira ntchito mwaukathyali pofuna kusonyeza kuti zimene iye ananena zokhudza Yehova ndi atumiki ake ndi zoona. Iyi ndi njira ya kunyazitsa, kapena kuti kunyoza pogwiritsa ntchito mabodza. Yesu anatcha Satana kuti ndi “atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Dzina lakuti Mdyerekezi, limene limatanthauza “woipitsa dzina la anzake,” limasonyeza kuti iye ndiye ali patsogolo kuipitsa Mulungu, mawu Ake opindulitsa, ndiponso dzina Lake loyera. Mdyerekezi amagwiritsira ntchito mabodza a mitundu yosiyanasiyana, ena ochita kuonekeratu, polimbana ndi ulamuliro wa Yehova, ndipo amagwiritsiranso ntchito njira yomweyi poipitsa mbiri ya atumiki okhulupirika a Mulungu. Ponena zonyoza zambirimbiri zokhudza Mboni zimenezi, iye angachititse kuti zilephere kupirira chiyeso chachikulu kwambiri.

8. Kodi Satana anam’nyazitsa motani Yobu, ndipo Yobu anamva bwanji ndi zimenezo?

8 Taganizirani zimene zinamuonekera Yobu, amene dzina lake limatanthauza kuti “Munthu Wodedwa.” Kuwonjezera pa kuwonongetsa chuma cha Yobu, kuphetsa ana ake, ndiponso kumudwalitsa, Satana anapangitsa Yobu kuoneka ngati munthu wochimwa amene anali kulangidwa ndi Mulungu. Ngakhale kuti Yobu poyamba anali munthu wolemekezeka kwambiri, iye anayamba kunyozedwa ndi achibale ake ngakhalenso anzake apamtima. (Yobu 19:13-19; 29:1, 2, 7-11) Kuwonjezera apo, kudzera mwa anthu amene ankanamizira kumulimbikitsa, Satana anafuna ‘kuthyolathyola Yobu ndi mawu.’ Poyamba iwo anali kunena zinthu zosonyeza ngati kuti Yobu anachita tchimo lalikulu ndipo kenako anayamba kum’dzudzula mosapita m’mbali kuti ndi munthu wochita zolakwa. (Yobu 4:6-9; 19:2; 22:5-10) Izi ziyenera kuti zinam’foola kwambiri Yobu!

9. Kodi Yesu anam’chitira zotani pofuna kuti aoneke ngati wochimwa?

9 Monga munthu amene ali patsogolo kuikira kumbuyo mfundo yakuti Yehova ndiyedi ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse, Mwana wa Mulungu anakhala mdani wamkulu wa Satana. Yesu atabwera padziko lapansi, Satana anayesa kumuipitsira mbiri yake, ngati mmene anachitira ndi Yobu, kupangitsa Yesu kuoneka ngati wochimwa. (Yesaya 53:2-4; Yohane 9:24) Anthu anam’tchula kuti ndi woledzera ndi wosusuka ndipo ankamunenanso kuti “ali ndi chiwanda.” (Mateyu 11:18, 19; Yohane 7:20; 8:48; 10:20) Iye anaimbidwa mlandu wabodza wochitira Mulungu mwano. (Mateyu 9:2, 3; 26:63-66; Yohane 10:33-36) Yesu anavutika maganizo kwambiri ndi zimenezi, chifukwa chakuti ankadziŵa kuti izi zinali kunyozetsa Atate wake popanda chifukwa. (Luka 22:41-44) Pomalizira pake, Yesu anapachikidwa ngati chigaŵenga chotembereredwa. (Mateyu 27:38-44) Kuti akhalebe wokhulupirika mpaka mapeto, Yesu anapirira zinthu zotsutsa zimene anthu ochimwa ankam’nenera.​—Ahebri 12:2, 3.

10. Kodi Satana akulimbana motani ndi otsalira a odzozedwa m’masiku athu ano?

10 M’masiku athu ano, nawonso otsalira a odzozedwa a Kristu akhala akudedwa kwambiri ndi Mdyerekezi. Satana amafotokozedwa kuti ndi “wonenera wa abale [a Kristu], wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.” (Chivumbulutso 12:9, 10) Popeza kuti anathamangitsidwa kumwamba n’kuponyedwa kufupi ndi dziko lapansi, Satana wagundika kwambiri pa ntchito yake yofuna kuti abale a Kristu azionedwa ngati anthu ankhanza osayenera kukhala nawo. (1 Akorinto 4:13) M’mayiko ena, abale a Kristu akhala akunamiziridwa kuti ndi kagulu koopsa kachipembedzo, monga momwe zinachitikira kwa Akristu a m’zaka 100 zoyambirira. (Machitidwe 24:5, 14; 28:22) Monga momwe taonera poyamba paja, mbiri yawo yaipitsidwa ndi mabodza amene akhala akufalitsidwa. Komabe, “mwa ulemerero mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino,” abale odzozedwa a Kristu, mothandizidwa ndi anzawo a “nkhosa zina,” ayesetsa modzichepetsa kupitiriza ‘kusunga malamulo a Mulungu, ndi kuchitira umboni za Yesu.’​—2 Akorinto 6:8; Yohane 10:16; Chivumbulutso 12:17.

11, 12. (a) Kodi n’chiyani chimapangitsa mazunzo amene Akristu ena amakumana nawo? (b) Kodi chikhulupiriro cha Mkristu chingam’pangitse bwanji kuzunzidwa popanda chifukwa?

11 Ndi zoona kuti sinthaŵi zonse pamene mtumiki wa Mulungu amanyozedwa “chifukwa cha chilungamo.” (Mateyu 5:10) Mwina mavuto ena angayambe chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu. Palibe madalitso alionse ngati ‘tikupirira pochimwa ndi kubwanyulidwa.’ Koma chimakhala “chisomo [kwa Yehova] ngati [Mkristu], chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.” (1 Petro 2:19, 20) Kodi zinthu zingatero pa zochitika zotani?

12 Ena akhala akuzunzidwa chifukwa chokana kuchita nawo miyambo ya maliro yosagwirizana ndi malemba. (Deuteronomo 14:1) Mboni zachinyamata zakhala zikunyozedwa nthaŵi zonse chifukwa chotsatira makhalidwe amene Yehova amafuna. (1 Petro 4:4) Makolo ena achikristu akhala akunamiziridwa kuti ndi “osasamala” kapena “oipa” chifukwa chofunira ana awo chithandizo cha mankhwala chopanda magazi. (Machitidwe 15:29) Akristu akhala akusalidwa ndi achibale awo kapena anthu oyandikana nawo nyumba makamaka chifukwa chosintha n’kukhala atumiki a Yehova. (Mateyu 10:34-37) Anthu onse amene akukumana ndi zimenezi akutsatira chitsanzo cha aneneri ndiponso cha Yesu mwiniwakeyo cha kuzunzidwa popanda chifukwa.​—Mateyu 5:11, 12; Yakobo 5:10; 1 Petro 2:21.

Kupirira Mukamanyozedwa

13. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe olimba mwauzimu pamene tikunyozedwa kwambiri?

13 Tikamanyozedwa kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chathu, tingathe kufooka, ngati mmene anachitira mneneri Yeremiya, n’kuyamba kuganiza kuti sititha kupitiriza kutumikira Mulungu. (Yeremiya 20:7-9) Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe olimba mwauzimu? Yesetsani kuona nkhaniyo ngati mmene Yehova amaionera. Iye amaona kuti anthu amene akupitiriza kukhala okhulupirika poyesedwa n’ngopambana, osati ovutika. (Aroma 8:37) Yesani kuganizira za anthu amene anaikira kumbuyo ulamuliro wa Yehova ngakhale kuti anali kunyozedwa ndi Mdyerekezi. Mungaganizire za amuna ndi akazi monga Abele, Yobu, Mariya amene anali amayi a Yesu, ndi anthu ena akale omwe anakhala okhulupirika, komanso atumiki anzathu a masiku ano. (Ahebri 11:35-37; 12:1) Sinkhasinkhani za mmene anakhalira okhulupirika pamoyo wawo. Mtambo waukulu umenewo wa anthu okhulupirika ukutikodola kuti tidzakhale m’gulu lawo la anthu opambana mwa chikhulupiriro.​—1 Yohane 5:4.

14. Kodi pemphero lochokera pansi pa mtima lingatilimbikitse motani kuti tikhalebe okhulupirika?

14 ‘Zolingalira zikatichulukira m’kati mwathu,’ tingathe kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima ndipo iye angatitonthoze ndi kutilimbikitsa. (Salmo 50:15; 94:19) Iye angatipatse nzeru zotithandiza kupirira chiyeso ndi kupitiriza kuganizira nthaŵi zonse za nkhani yaikulu ya ulamuliro wa Yehova, yomwe ikuchititsa kuti atumiki ake azidedwa popanda chifukwa. (Yakobo 1:5) Yehova angatipatsenso “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.” (Afilipi 4:6, 7) Mtendere wochoka kwa Mulungu umenewu umatithandiza kukhala odekha ndiponso osasunthika tikakhala m’mavuto aakulu, kuti tisakayikire chilichonse kapenanso kuchita mantha. Pogwiritsira ntchito mzimu wake, Yehova angatiteteze pa chilichonse chimene walola kuti chitichitikire.​—1 Akorinto 10:13.

15. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisawawidwe mtima pamene tikuzunzidwa?

15 Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tisawawidwe mtima kwambiri ndi anthu amene amatida popanda chifukwa? Kumbukirani kuti adani athu akuluakulu ndi Satana ndi ziwanda zake. (Aefeso 6:12) Ngakhale kuti anthu ena amatizunza mwadala, ambiri amene amatsutsa anthu a Mulungu amachita zimenezo mosadziŵa kapena mochita kupangiridwa ndi anthu ena. (Danieli 6:4-16; 1 Timoteo 1:12, 13) Yehova akufuna kuti “anthu onse” apeze mwayi ‘wopulumuka ndi kufika pozindikira choonadi.’ (1 Timoteo 2:4) Ndipo ena omwe kale ankatitsutsa tsopano ndi abale athu achikristu chifukwa choti aona makhalidwe athu abwino. (1 Petro 2:12) Komanso tingaphunzirepo mfundo yabwino pa chitsanzo cha Yosefe mwana wa Yakobo. Ngakhale kuti Yosefe anavutika kwambiri chifukwa cha abale ake, iye sanawasungire chakukhosi. Chifukwa chiyani? Anatero chifukwa choona kuti nkhaniyo inkakhudzanso Yehova, yemwe anali kuyendetsa zinthu pofuna kukwaniritsa cholinga Chake. (Genesis 45:4-8) Panoponso Yehova angachititse kuti kuzunzidwa kwathu popanda chifukwa kuthandize kubweretsa ulemerero pa dzina lake.​—1 Petro 4:16.

16, 17. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuda nkhaŵa ndi zochita za anthu ofuna kulepheretsa ntchito yolalikira?

16 Sitiyenera kuda nkhaŵa ngati panthaŵi ina anthu otitsutsa akuoneka kuti zikuwayendera bwino pantchito yawo yolepheretsa kuti uthenga wabwino ulalikidwe m’madera ambiri. Panopo, Yehova akugwedeza amitundu kudzera m’ntchito yolalikira imene ikuchitika padziko lonse, ndipo zinthu zofunika zikusonkhanitsidwa. (Hagai 2:7) Kristu Yesu, yemwe ndi Mbusa Wabwino, anati: ‘Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine. Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; . . . ndipo palibe munthu adzazikwatula m’dzanja langa.’ (Yohane 10:27-29) Nawonso angelo opatulika akugwira nawo ntchito yaikulu ya kututa kwauzimu imeneyi. (Mateyu 13:39, 41; Chivumbulutso 14:6, 7) Motero, palibe chilichonse chimene otsutsa anganene kapena kuchita chomwe chingalepheretse cholinga cha Mulungu.​—Yesaya 54:17; Machitidwe 5:38, 39.

17 Nthaŵi zambiri, zinthu zimene otsutsawo amayesa kulepheretsa kuti zichitike n’zimene zimachitika. M’mudzi wina ku Africa kuno, anthu anafalitsa mabodza ambiri amkunkhuniza onena za Mboni za Yehova, kuphatikizapo bodza lakuti Mboni zimalambira Mdyerekezi. Chifukwa cha izi, Grace ankakabisala kuseli kwa nyumba yake Mboni zikangofika panyumbapo ndipo ankasokoloka Mbonizo zikapita. Tsiku lina mbusa wa tchalitchi chake anatenga buku lathu n’kulisonyeza kwa anthu onse amene analipo n’kuwauza kuti asaŵerenge buku limeneli chifukwa chakuti lingathe kuwasiyitsa tchalitchi chawo. Izi zinapatsa Grace chidwi chofuna kudziŵa kuti bukulo lili ndi zotani. Ulendo wotsatira womwe Mboni zinafika panyumba pake, m’malo mokabisala iye analankhula nazo ndi kulandira buku lomwe anawaletsa mbusa wawo lija. Anayamba kuphunzira naye Baibulo, ndipo mu 1996 anabatizidwa. Grace tsopano amathera nthaŵi yake pofunafuna anthu ena amene anauzidwa nkhani zabodza zokhudza Mboni za Yehova.

Limbitsani Chikhulupiriro Chanu Panopa

18. N’chifukwa chiyani pakufunika kulimbitsa chikhulupiriro chathu ziyeso zoopsa zisanayambe, ndipo tingachite motani zimenezi?

18 Popeza kuti nthaŵi ina iliyonse Satana angathe kutitembenukira n’kuyamba kutida popanda chifukwa, m’pofunika kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu panopa. Kodi tingachite motani zimenezi? Lipoti lochoka m’dziko lina limene anthu a Yehova akhala akuzunzidwa linati: “Chinthu chimodzi chimene chaonekera kwambiri n’chakuti: Anthu amene ali ndi chizoloŵezi chabwino chochita zinthu zauzimu ndipo amayamikira kwambiri choonadi cha m’Baibulo savutika kupirira pakabuka ziyeso. Koma anthu amene ‘panthaŵi yomwe zinthu zili bwino’ amaphonya misonkhano, sachita mokhazikika utumiki wa kumunda ndiponso amagonja pankhani zing’onozing’ono, nthaŵi zambiri amagonja akakhala pachiyeso ‘choopsa kwambiri.’” (2 Timoteo 4:2, NW) Ngati mukuona zinthu zina zimene mukufunika kukonza, yesetsa kuzikonzadi mosazengereza.​—Salmo 119:60.

19. Kodi n’chiyani chimene chimachitika chifukwa cha kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu panthaŵi yomwe akudedwa popanda chifukwa?

19 Kukhulupirika kwa olambira oona panthaŵi yomwe akudedwa kwambiri ndi Satana ndi umboni wakuti Yehova ndi woyenereradi, ndipo ndi chilungamo kuti iye akhale wolamulira chilengedwe chonse. Mulungu amasangalala ndi kukhulupirika kwa anthu ameneŵa. Ngakhale kuti anthu angathe kunena zambirimbiri zowanyoza, Yehova amene ali ndi ulemu waukulu kwambiri padziko ndi kumwamba konse “sachita manyazi nawo poitanidwa Mulungu wawo.” Zoonadi, sikulakwa kunena kuti “dziko lapansi silinayenera [anthu okhulupirika ameneŵa].”​—Ahebri 11:16, 38.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 M’Malemba, mawu akuti “chidani” ali ndi matanthauzo angapo. Nthaŵi zina, amangotanthauza kusakonda kwambiri chinthu chinachake. (Deuteronomo 21:15, 16) Mawu akuti “chidani” nthaŵi zina amatanthauzanso kuipidwa kwambiri ndi chinthu chinachake popanda maganizo alionse ochiwononga, koma n’kumachipeŵa chifukwa chonyansidwa nacho. Koma mawu akuti “chidani” angatanthauzenso kuipidwa kwambiri ndiponso kwa nthaŵi yaitali ndi chinthu chinachake ndipo nthaŵi zambiri kophatikiza ndi dumbo. Ndi chidani chamtundu umenewu chimene tifotokoze m’nkhaniyi.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi n’chiyani chimachititsa kuti olambira oona azidedwa popanda chifukwa?

• Kodi Satana ananyoza Yobu ndi Yesu m’njira yotani pofuna kuwalepheretsa kukhala okhulupirika?

• Kodi Yehova amatilimbikitsa motani kuti tikhale olimba pamene tikudedwa ndi Satana?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 16]

Anazindikira Pamene Panagona Nkhani

Mwamuna wina yemwe ndi wa Mboni za Yehova m’dziko la Ukraine, komwe ntchito yolalikira za Ufumu inali yoletsedwa kwa zaka zoposa 50, anati: “Tikamaona mmene Mboni za Yehova zinali kukhalira, si bwino kumangoona zinthu zokhazo zimene anthu ena anali kutichitira. . . . Chifukwatu ambiri mwa akuluakulu a boma anali kungochita ntchito yawo. Boma litasintha, akuluakulu abomawo anasinthanso n’kuyamba kumvera anthu ena, koma ife sitinasinthe. Tinazindikira kuti Baibulo linatchula kale amene makamaka amachititsa mavuto athu.

“Sikuti tinkangodziona kuti ndife anthu osalakwa amene akuvutika chifukwa cha anthu opondereza. Kumvetsa nkhani yomwe inayambika m’munda wa Edene, nkhani yakuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira, n’kumene kunatithandiza kuti tipirire. . . . Sitinabwerere m’mbuyo pa nkhani imeneyi yomwe imakhudza zofuna za anthu komanso za Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Tinkazindikira bwino kwambiri pamene panagona nkhani imene tinkazunzidwira. Izi zinatithandiza kukhala olimba ndiponso kupitirizabe kukhala okhulupirika ngakhale panthaŵi imene zinthu zinafika poipa kwambiri.”

[Chithunzi]

Victor Popovych, amene anamangidwa mu 1970

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi ndi ndani anachititsa kuti Yesu anyozedwe?

[Zithunzi patsamba 15]

Yobu, Mariya, ndi atumiki a Mulungu a masiku ano, monga Stanley Jones, anaikira kumbuyo ulamuliro wa Yehova