Olankhula Zinenero Zamakolo ku Mexico Amva Uthenga Wabwino
Olankhula Zinenero Zamakolo ku Mexico Amva Uthenga Wabwino
PA November 10, 2002, anthu olankhula chinenero chamakolo chotchedwa Mixe ku Mexico anasonkhana ku San Miguel Quetzaltepec. Imeneyi ndi tauni yomwe ili m’boma lokongola lakum’mwera la Oaxaca. Anthuŵa anali kuchita msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Seŵero la m’Baibulo n’limene linali mbali yosangalatsa kwambiri pa pulogalamu ya m’maŵa patsiku limeneli.
Omvera onse anadabwa kwambiri atamva mawu oyamba a seŵero la m’Baibulolo. Iwo anawombera m’manja, ndipo anthu ambiri anagwetsa misozi. Seŵerolo linali m’chinenero chotchedwa Mixe. Seŵerolo litatha, anthu ambiri anayamikira mochokera pansi pa mtima mphatso imene sankaiyembekezerayi. Mayi wina anati: “Aka n’koyamba kwa ine kumvetsa seŵero. Landifika pamtima.” Ndipo mayi winanso anati: “Ngakhale nditafa ndasangalala kuti Yehova wandipatsa mwayi womvera seŵero m’chinenero changa.”
Ntchito yokonza seŵero limene analionetsa m’maŵa umenewu ndi mbali ya ntchito yaikulu imene Mboni za Yehova ku Mexico zachita posachedwapa pofuna kuuza anthu olankhula zinenero zamakolo m’dzikolo uthenga wabwino wa Ufumu.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Yehova Anamva Mapemphero
Ku Mexico kuli anthu oposa 6,000,000 a m’mafuko olankhula zinenero zamakolo za m’dzikoli, moti paokha angathe kukwana dziko, ndipo ndi osiyana zikhalidwe komanso amalankhula zinenero zokwanira 62. Zinenero 15 mwa zinenero 62 zimenezi, chilichonse chimalankhulidwa ndi anthu oposa 100,000. Anthu oposa 1,000,000 mwa anthu ameneŵa salankhula Chisipanya, chomwe ndi chinenero cha boma. Ndipo ambiri mwa anthu amene amalankhula Chisipanyawo angaphunzire mosavuta choonadi cha m’Baibulo m’chinenero chawo. (Machitidwe 2:6; 22:2) Ena aphunzira Baibulo ndipo akhala akupezeka mokhulupirika pamisonkhano yachikristu kwa zaka zambiri, komabe sadziŵa zambiri. Choncho akhala akupemphera kwa nthaŵi yaitali kuti uthenga wa choonadi uzipezeka m’chinenero chawo.
Kuti athetse vuto limeneli, mu 1999 ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mexico inayamba kukonza zoti pazichitika misonkhano ya mpingo m’zinenero za anthu ameneŵa. Ofesiyo inakhazikitsanso magulu omasulira mabuku. Pofika chaka cha 2000, seŵero la msonkhano wachigawo linayamba kuchitika m’chinenero cha Chimaya, kenako m’zinenero zina zingapo.
Ndiyeno anayamba ntchito yomasulira mabuku othandizira kuphunzira Baibulo a Mboni za Yehova. Choyamba, anamasulira kabuku kakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! m’zinenero za Chimaya, Huave, Mazatec, Totonac, Tzeltal, ndi Tzotzil. Kenako anamasulira mabuku ena, komanso anayamba kumasulira nthaŵi zonse Utumiki Wathu wa Ufumu m’Chimaya. Anatulutsanso makaseti a mabuku ena. Kuti aphunzitse anthu ameneŵa kuŵerenga ndi kulemba zinenero zawozi, kabuku kakuti Dziperekeni pa Kuŵerenga ndi Kulemba akukasintha mwina ndi mwina kuti kagwirizane ndi kumeneko. Panopa mabuku ofotokoza za m’Baibulo akufalitsidwa
m’zinenero 15 za anthu ameneŵa, ndipo mabuku ambiri ali m’njira.‘Kuyesetsa’
Ntchito yomasulirayi yakhala yovuta. Chifukwa choyamba n’chakuti, ku Mexico kulibe mabuku ambiri a zinenero zamakolo za anthu a m’dzikolo. Nthaŵi zambiri zimavuta kupeza mabuku otanthauzira mawu. Komanso, zinenero zina anthu amazilankhula mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, chinenero chotchedwa Zapotec chokha chili ndi kalankhulidwe pafupifupi kasanu kosiyanasiyana. Ndipo kalankhulidwe kameneka n’kosiyana kwambiri moti anthu amadera osiyana koma onse olankhula chinenerochi, samvana.
Komanso, chinenero china chikakhala kuti chilibe malamulo enieni akalembedwe, omasuliraŵa amakhazikitsa malamulo awo. Izi zimafunika kufufuza kwambiri ndiponso kukambirana ndi anthu. N’chifukwa chake omasulira ambiri poyamba ankamva monga anamvera Élida, yemwe ali m’gulu la anthu omasulira m’chinenero chotchedwa Huave. Iye anati: “Atandiitana ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Mexico kuno kuti ndidzagwire ntchito yomasulira, ndinali wosangalala komanso wamantha.”
Omasulirawo amafunikanso kuphunzira kugwiritsa ntchito kompyuta, kugaŵa ntchito, ndiponso luso lomasulira. Ndithudi, ntchitoyi ndi yovuta kwambiri. Koma kodi amaiona bwanji? Gloria, yemwe ali m’gulu la anthu omasulira m’Chimaya anati: “Tikusoŵa mawu amene tinganene kuti tisonyeze mmene timasangalalira kugwira nawo ntchito yomasulira mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’Chimaya, chomwe n’chinenero chathu.” Ponenapo za omasuliraŵa, woyang’anira Dipatimenti Yomasulira Mabuku ananena kuti: “Iwo amafunitsitsa kwambiri kukhala ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’chinenero chawo moti akuyesetsa kuthetsa vutoli.” Kodi apindula?
“Zikomo Yehova!”
Zikuchita kuoneka kuti Yehova akudalitsa ntchito imene ikuchitika m’gawo la anthu olankhula zinenero zamakolo m’dzikoli. Opezeka pa misonkhano yampingo ndiponso ikuluikulu awonjezeka. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2001 a Mboni 223 olankhula chinenero chotchedwa Mixe anakumana kuti achite Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Komano ataphatikiza anthu onse amene anachita nawo Chikumbutsochi anakwana 1,674, omwe ndi ochuluka moŵirikiza nthaŵi seveni ndi theka kuposa a Mboniwo!
Tsopano anthu ena amene amalandira choonadi akuchimvetsetsa bwinobwino kuyambira pachiyambi. Mirna amakumbukira zimene zinam’chitikira misonkhano isanayambe kuchitika m’Chimaya. Iye anati: “Ndinabatizidwa nditaphunzira Baibulo kwa miyezi itatu. Ndinkadziŵa kuti ndinafunika kubatizidwa, koma sindinali kuchidziŵa bwinobwino choonadi cha m’Baibulo. Ndikuganiza kuti chinali chifukwa chakuti chinenero changa ndi Chimaya, ndipo Chisipanya sindinkachidziŵa bwino. Zinanditengera nthaŵi ndithu kuti ndichimvetsetse bwino choonadi.” Panopa iye ndi mwamuna wake amasangalala kukhala m’gulu la anthu omasulira m’Chimaya.
Anthu onse m’mipingo amasangalala kwambiri kulandira mabuku m’chinenero chawo. Atatulutsa kabuku kamene anakamasulira kumene ka Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! m’chinenero chotchedwa Tzotzil, mayi wina amene anali atayamba kupezeka pamisonkhano yachikristu anakafungata ndipo anati: “Zikomo Yehova!” Malipoti akusonyeza kuti ophunzira
Baibulo ambiri alimbikira kwambiri kufika pobatizidwa, ofalitsa amene anasiya kulalikira akuthandizidwa kuti ayambirenso kulalikira, ndipo abale ambiri achikristu tsopano amaona kuti akuyenerera kulandira maudindo mu mpingo. Eninyumba ena amafunitsitsa kulandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo a m’chinenero chawo ndiponso amafunitsitsa kuwaphunzira mabukuwo.Nthaŵi ina, mayi wina wa Mboni anapita kukachititsa phunziro la Baibulo, koma munthu amene anali kuphunzira naye Baibuloyo sanam’peze. Mwamuna wa wophunzirayo atabwera kudzam’lonjera mayiyo, mayiyo anapempha mwamunayo kuti amuŵerengere za m’kabukuko. Mwamunayo anati: “Sindikufuna.” Mlongoyo anamuuza mwamunayo m’chinenero chotchedwa Totonac kuti kabukuko kanali ka m’chinenero chawo. Mwamunayo atamva zimenezi anakoka mpando n’kukhala pansi. Mayiyo akumuŵerengera, mwamunayo ankangoti, “N’zoona zimenezo. Inde, n’zoona zimenezo.” Tikunena pano amapezeka pamisonkhano yachikristu.
Ku Yucatán, mwamuna wina amene mkazi wake ndi wa Mboni ankatsutsa choonadi ndipo nthaŵi zina ankam’menya mkaziyo akabwera kuchokera ku misonkhano. Misonkhano itayamba kuchitika m’Chimaya, mkaziyo anaganiza zomuitanira mwamuna wakeyo ku misonkhano. Mwamunayo anabwera pamisonkhano ndipo anasangalala nayo. Tsopano amapezeka pamisonkhano nthaŵi zonse, akuphunzira Baibulo, ndipo n’zosachita kufunsa kuti analeka kumenya mkazi wakeyo.
Mwamuna wina wolankhula chinenero chotchedwa Totonac anauza a Mboni aŵiri kuti iye sapemphera chifukwa wansembe wachikatolika anamuuza kuti Mulungu amamva mapemphero 2 Mbiri 6:32, 33; Salmo 65:2.
a Chisipanya okha. Ndipotu, anali kulipira wansembeyo kuti apempherere anthu olankhula chi Totonac. A Mboniwo anafotokoza kuti Mulungu amamva mapemphero a zinenero zonse, ndipo anam’patsa kabuku ka chi Totonac, ndipo analandira mosangalala kwambiri.—“Kualtsin Tajtoua”
Ofalitsa Ufumu ambiri posangalala ndi zonse zimene zikuchitikazi, akuyesetsa kuphunzira chinenero chamakolo cha m’dzikoli kapena kupitiriza kuphunzira bwino chinenero chimene akungochidziŵa pang’ono. Izi n’zimene akuchita woyang’anira dera wina amene amayendera mipingo isanu ya chinenero chotchedwa Nahuatl ya kumpoto kwa Puebla. Iye anati: “Ana amene poyamba anali kugona pamisonkhano tsopano amakhala maso n’kumamvetsera mwatcheru ndikamalankhula chi Nahuatl. Nthaŵi ina titatha misonkhano, mwana wina wazaka zinayi anandiuza kuti: ‘Kualtsin tajtoua’ (mukulankhula bwino). Zimenezi zinandipangitsa kuona kuti khama langa silikupita pachabe.”
Inde, gawo la anthu olankhula zinenero zamakololi ‘layeradi kufikira kumweta,’ ndipo n’zolimbikitsa kwambiri kwa onse amene akuthandiza pantchitoyi. (Yohane 4:35) Roberto, amene anagwira ntchito yolinganiza magulu a anthu omasulira mabuku, mwachidule anati: “Sindidzaiŵala zimene ndinaona, abale ndi alongo akulira chifukwa chosangalala pamene anali kumvetsera choonadi m’chinenero chawo ndi kumvetsa zimene zinali kunenedwazo. Ndikaganiza zimenezi m’maso mwanga mumalengeza misozi.” Mosakayikira, kuthandiza anthu oona mtima ameneŵa kukhala ku mbali ya Ufumu kumakondweretsanso mtima wa Yehova.—Miyambo 27:11.
[Bokosi pamasamba 10, 11]
Dziŵani Ena mwa Omasuliraŵa
● “Makolo anga anandiphunzitsa choonadi ndili mwana. Mwatsoka, bambo anga anachoka mu mpingo wachikristu ndili ndi zaka 11. Patangotha zaka ziŵiri, amayi anatithaŵa. Popeza kuti wamkulu ndinali ineyo m’banja lathu la ana asanu, ndinatenga udindo wa amayi, ngakhale kuti ndinali ndili pasukulu.
“Abale ndi alongo athu auzimu anali kutithandiza mwachikondi, koma tinali kuvutika ndithu. Nthaŵi zina ndinkafunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani zimenezi zikundichitikira? Ndachepa nazo kwambiri!’ Ndi Yehova yekha amene anandithandiza kuti zindiyendere bwino. Nditamaliza maphunziro pa sukulu ya sekondale, ndinayamba utumiki wanthaŵi zonse, ndipo zimenezi zinandithandiza kwambiri. Atakhazikitsa gulu la anthu omasulira m’chinenero chotchedwa Nahuatl, anandiitana kuti ndidzathandize ntchito imeneyi.
“Panopa bambo anga anabwerera mu mpingo, ndipo azichimwene anga ndi azing’ono anga akutumikira Yehova. Kukhala wokhulupirika kwa Yehova kwatithandiza zedi. Yehova walidalitsa kwambiri banja lathu,” anatero Alicia.
● “Mtsikana wina wa Mboni amene tinali naye m’kalasi imodzi anakamba nkhani ku sukulu ya mmene moyo unayambira. Tsiku limenelo ndinajomba ndipo ndinali kudera nkhaŵa kuti ndidzatani zikadzabwera pamayeso, choncho ndinamuuza kuti andifotokozere nkhaniyo. Nthaŵi zonse ndinkadabwa kuti anthu amaferanji. Atandifunsa ngati ndingakonde kukhala ndi buku la Creation * komanso kuti aziphunzira nane Baibulo, ndinavomera. Cholinga komanso chikondi cha Mlengi chinandikhudza mtima zedi.
“Nditamaliza sukulu, ndinali ndi mwayi wogwira ntchito yophunzitsa zinenero ziŵiri, Chisipanya ndi chi Tzotzil. Koma kuchita zimenezi kukanapangitsa kuti ndisamukire kutali, kuphunziranso pamapeto a mlungu, komanso kusapezeka pamisonkhano yachikristu. Choncho m’malo mwa zimenezi ndinayamba kugwira ntchito ya zomangamanga. Bambo anga amene sanali Mboni sanasangalale nazo zimenezi m’pang’ono pomwe. Kenako, ndikuchita upainiya, kunakhazikitsidwa gulu lomasulira mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’chinenero chotchedwa Tzotzil. Ndinalimbikitsidwa kuti ndikagwire nawo ntchitoyi.
“Ndimatha kuona kuti abale ndi alongo athu amadzimva kukhala ofunika komanso olemekezeka ngati ali ndi mabuku a m’zinenero zawo. Izi n’zosangalatsa kwambiri. Ndimaona kuti ndi mwayi kwambiri kupatsidwa ntchito imeneyi,” anatero Humberto.
● “Ndili ndi zaka sikisi, amayi anatithaŵa. Ndidakali mtsikana, bambo anga anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Tsiku lina mlongo wina anandipempha kuti aziphunzira nane buku lofotokoza za m’Baibulo limene linali ndi malangizo a achinyamata. Monga wachinyamata wopanda mayi, ndinaona kuti zimenezi n’zimene ndinali kufunika. Ndinabatizidwa ndili ndi zaka 15.
“Mu 1999 bambo anga anaphedwa ndi anthu ena oipa amene ankafuna kuwalanda malo. Ndinathedwa nzeru. Ndinali kuvutika maganizo kwambiri ndipo ndinkaona kuti ndifa. Koma ndinali kupemphera kwa Yehova kuti andipatse mphamvu. Woyang’anira woyendayenda ndi mkazi wake anandilimbikitsa kwambiri. Posapita nthaŵi ndinayamba upainiya wokhazikika.
“Nthaŵi ina ndinaona anthu amene anayenda maola sikisi kuti akangomvera nkhani ya mphindi 20 ya m’chinenero chotchedwa Totonac, ngakhale kuti msonkhano wonse unali m’Chisipanya chimene sankamva. Choncho ndinasangalala atandiitana kuti ndidzathandize nawo kumasulira mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’chinenero cha Totonac.
“Ndinkakonda kuwauza bambo anga kuti ndimalakalaka kukatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Iwo ankandiuza kuti n’zovuta kwa mtsikana wosakwatiwa ngati ine. Akadzaukitsidwa si mmene adzasangalalire kumva kuti ndinatumikiradi pa ofesi ya nthambi, kumasulira mabuku ofotokoza za m’Baibulo m’chinenero chathu,” anatero Edith.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 28 Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova mu 1985.
[Chithunzi patsamba 9]
Amene amagwira ntchito yomasulira m’chinenero cha chi Tzotzil akukambirana mawu ovuta kumasulira