Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Otopa Koma Osalefuka

Otopa Koma Osalefuka

Otopa Koma Osalefuka

“Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, . . . alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.”​—YESAYA 40:28, 29.

1, 2. (a) Kodi ndi pempho losangalatsa lotani limene likupita kwa onse ofuna kuti azilambira moona? (b) Kodi n’chiyani chingawononge kwambiri moyo wathu wauzimu?

POTI ndife ophunzira a Yesu, tikudziŵa bwino pempho lake losangalatsa lakuti: “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. . . . Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Akristu amapatsidwanso “nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.” (Machitidwe 3:19) N’zosakayikitsa kuti inuyo panokha mwapeza mpumulo pophunzira choonadi cha m’Baibulo, kuyembekezera tsogolo labwino, ndiponso kutsatira mfundo za Yehova pamoyo wanu.

2 Komabe, ena mwa atumiki a Yehova amatopa moti sangathe kuganiza bwinobwino. Nthaŵi zina kutopaku, komwe kumatayitsa mtima, kumakhala kwa nthaŵi yochepa. Koma nthaŵi zina kumatenga nthaŵi yaitali. Pakapita nthaŵi, ena amayamba kuganiza kuti maudindo achikristu omwe ali nawo ayamba kukhala katundu wolemetsa m’malo mopatsa mpumulo mogwirizana ndi lonjezo la Yesu. Maganizo olakwika ameneŵa angathe kuwononga kwambiri unansi wa Mkristu ndi Yehova.

3. N’chifukwa chiyani Yesu anapereka malangizo opezeka pa Yohane 14:1?

3 Yesu atatsala pang’ono kuti amangidwe ndi kuphedwa anauza ophunzira ake kuti: “Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.” (Yohane 14:1) Yesu ananena izi chifukwa chakuti atumwiwo anali atatsala pang’ono kukumana ndi zinthu zoopsa. Pambuyo pa zinthu zimenezi panadzabwera chizunzo. Yesu ankadziŵa kuti atumwi akewo angathe kudzakhumudwa chifukwa chotaya mtima kwambiri. (Yohane 16:1) Popanda kusamala nawo maganizo ameneŵa, atumwiwo akanafooka kwambiri mwauzimu n’kusiya kukhulupirira Yehova. Izi zingachitikirenso Akristu masiku ano. Kukhala wotaya mtima kwa nthaŵi yaitali kumathetsa nzeru, ndipo mitima yathu ingathe kulema. (Yeremiya 8:18) Munthu wa m’kati mwathu angafooke. Pokumana ndi mavuto ameneŵa, tingalefuke mwauzimu ndiponso mwamaganizo, mwinanso mtima wofuna kulambira Yehova ungatithere.

4. Kodi n’chiyani chingatithandize kuteteza mtima wathu wophiphiritsira kuti usalefuke?

4 Ndiyetu malangizo otsatiraŵa a m’Baibulo n’ngoyenerera kwambiri. Malangizo ake ndi akuti: “Tchinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Baibulo limatipatsa malangizo abwino amene amatithandiza kuteteza mtima wathu wophiphiritsira kuti usalefuke kapenanso kutopa mwauzimu. Koma choyamba tikufunika kudziŵa kuti n’zinthu ziti zimene zimatitopetsa.

Kukhala Mkristu Sikolemetsa

5. Kodi pakuoneka ngati pali kutsutsana kotani pankhani ya kukhala wophunzira wa Kristu?

5 N’zoona kuti kukhala Mkristu kumalira khama kwambiri. (Luka 13:24) Yesu ananena kuti: “Amene aliyense sasenza mtanda wake wa mwiniyekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga.” (Luka 14:27) Popanda kuwaganizira bwino mawu ameneŵa, munthu angawaone ngati akutsutsana ndi mawu a Yesu onena kuti katundu wake ndi wopepuka ndiponso wopatsa mpumulo. Koma sikuti akutsutsana ngakhale pang’ono.

6, 7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kulambira kwathu sikotopetsa?

6 Kuchita khama kwambiri ndiponso kugwira ntchito zolimba, ngakhale kuti n’kotopetsa, kungakhale kosangalatsa ndiponso kotsitsimula ngati pali cholinga chabwino chochitira zimenezo. (Mlaliki 3:13, 22) Ndipo kodi pali cholinga chinanso chabwino kuposa kuuza ena choonadi chosangalatsa cha m’Baibulo? Komanso, khama lomwe timachita pofuna kukhala motsatira miyezo yapamwamba ya makhalidwe abwino ya Mulungu n’lochepa tikaona phindu lomwe timapeza chifukwa chochita zimenezo. (Miyambo 2:10-20) Ngakhale panthaŵi yoti tikuzunzidwa, timaona kuti ndi ulemu waukulu kuvutikira Ufumu wa Mulungu.​—1 Petro 4:14.

7 Katundu wa Yesu n’ngotsitsimuladi, makamaka tikamuyerekezera ndi mdima wauzimu umene anthu onyamula goli la chipembedzo chonyenga alimo. Mulungu amatikonda kwambiri ndipo satiuza kuti tichite zinthu zoti sitingazikwanitse. “Malamulo [a Yehova] sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Kukhala Mkristu woona, malinga ndi zimene Malemba amanena, sikolemetsa. N’zoonekeratu kuti sititopa kapenanso kulefuka chifukwa cha kulambira kwathu.

‘Tayani Cholemetsa Chilichonse’

8. Kodi nthaŵi zambiri n’chiyani chimene chimapangitsa kuti titope mwauzimu?

8 Nthaŵi zambiri, tikamva kutopa mwauzimu chimakhala chifukwa cha katundu wowonjezera amene dongosolo loipali la zinthu limatisenzetsa. Chifukwa chakuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” tazunguliridwa ndi zinthu zoipa zomwe zingatitopetse ndi kutifooketsa mwauzimu. (1 Yohane 5:19) Kufunafuna zinthu zopanda ntchito kwenikweni kungasokoneze zochita zathu zachikristu. Tingalefuke ndi katundu wowonjezera ameneyu ndipo mwinanso tingathe kuchinyizika naye kumene. N’chifukwa chaketu Baibulo limatilimbikitsa kuti “titaye cholemetsa chilichonse.”​—Ahebri 12:1-3.

9. Kodi kufunafuna chuma kungatifoole motani?

9 Mwachitsanzo, maganizo athu angasokonezedwe ndi mtima wa anthu a m’dzikoli wokonda kutchuka, kukonda ndalama, zosangalatsa, kupanga maulendo ongofuna kusangalala, ndiponso zinthu zina. (1 Yohane 2:15-17) Akristu ena a m’zaka 100 zoyambirira amene anali kufunafuna chuma anadzisokonezera kwambiri miyoyo yawo. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

10. Kodi tingaphunzire chiyani chokhudza chuma m’fanizo la Yesu lonena za wofesa mbewu?

10 Ngati tatopa ndiponso tataya mtima potumikira Mulungu, kodi n’kutheka kuti n’chifukwa chakuti kufunafuna chuma kukupondereza moyo wathu wauzimu? N’zotheka kuti izi zitichitikire, monga momwe fanizo la Yesu lonena za wofesa mbewu limasonyezera. Yesu anayerekezera “malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina” ndi minga zimene ‘zimaloŵa ndi kutsamwitsa’ mbewu za mawu a Mulungu m’mtima mwathu. (Marko 4:18, 19) Motero, Baibulo limatilangiza kuti: “Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.”​—Ahebri 13:5.

11. Kodi tingachepetse motani zinthu zomwe zingatifoole?

11 Nthaŵi zina chimene chimasokoneza moyo wathu si kufunafuna chuma ayi, koma ndi zimene timachita ndi zinthu zimene tili nazo kale. Ena angaleme maganizo chifukwa cha matenda aakulu, imfa za anthu amene amawakonda, kapena mavuto ena. Anthu otere aona kufunika kwake kosintha zinthu nthaŵi ndi nthaŵi. Banja lina linaganiza zosiya kuchita zinthu zina zimene linkakonda kuchita panthaŵi yopuma komanso ntchito zina zosafunikira kwenikweni. Ndipo anafufuza pa katundu wawo kuti aone katundu yense wokhudzana ndi ntchito zosafunikirazo n’kumulongedza ndi kumuika pamalo poti asamamuone. Tonsefe tingapindule ngati nthaŵi ndi nthaŵi titamakhala pansi n’kuganizira bwinobwino zinthu zomwe timachita komanso katundu wathu, n’kutaya cholemetsa chilichonse chosafunikira kwenikweni n’cholinga choti tisatope ndi kulefuka m’moyo wathu.

M’pofunika Kuchita Zinthu Mosamala Ndiponso Mosapambanitsa

12. Kodi tiyenera kuzindikira chiyani pankhani ya zolakwa zathu?

12 Zolakwa zathu, ngakhale pazinthu zochepa, zingasokoneze moyo wathu m’kupita kwa nthaŵi. Davide ananena zoona kuti: “Mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga: ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.” (Salmo 38:4) Nthaŵi zambiri kusintha zinthu zina ndi zina zochepa chabe kungatipatse mpumulo pa katundu wolemera.

13. Kodi kuchita zinthu mosamala kungatithandize motani kuti tiziona moyenerera utumiki wathu?

13 Baibulo limatilimbikitsa kuti tikhale ndi “nzeru yeniyeni ndi kulingalira.” (Miyambo 3:21, 22) Baibulo limati ‘nzeru yochokera kumwamba ikhala . . . yaulere,’ kapena kuti yochita zinthu mosamala. (Yakobo 3:17) Ena akhala akupanikizika pofuna kuti mu utumiki wachikristu azichita ntchito yofanana ndi ya ena. Koma Baibulo limatilangiza kuti: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina. Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini.” (Agalatiya 6:4, 5) N’zoona kuti chitsanzo chabwino cha Akristu anzathu chingatilimbikitse kutumikira Yehova ndi mtima wonse, koma kuchita zinthu mwanzeru ndiponso mosamala kungatithandize kukhala ndi zolinga zoyenerera mogwirizana ndi mmene tilili patokha.

14, 15. Kodi tingasonyeze motani nzeru pothana ndi mavuto a m’thupi mwathu ndiponso a maganizo?

14 Kuchita zinthu mosamala ngakhale pa zinthu zimene zingaoneke ngati zosafunika kwenikweni kungatithandize kuti tisatope. Mwachitsanzo, kodi tili ndi chizoloŵezi chochita zinthu zabwino zomwe zimathandiza munthu kukhala ndi moyo wathanzi? Taonani chitsanzo cha mwamuna wina ndi mkazi wake amene akutumikira pa ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova. Banjali linaona kuti kuchita zinthu mwanzeru n’kothandiza kuti munthu asatope. Mkaziyo anati: “Ngakhale tikhale ndi ntchito yochuluka motani, tsiku lililonse sitimasintha nthaŵi yogonera. Nthaŵi ndi nthaŵi, timachitanso maseŵera olimbitsa thupi. Izi zatithandiza kwambiri. Taphunzira kuzindikira zinthu zimene sitingathe kuchita ndipo tasiya zomayesa kuchita zinthu zotere. Timayesetsa kuti tisadziyerekezere ndi anthu amene amaoneka kuti amatha kuchita zinthu zambirimbiri osatopa.” Kodi inuyo mumadya chakudya chabwino ndiponso kupuma mokwanira nthaŵi zonse? Kusamalira thanzi lathu kungathetse kulema mwamaganizo ndiponso mwauzimu.

15 Enafe tili ndi mavuto ofunika chisamaliro chapadera. Mwachitsanzo, mlongo wina wachikristu wakhala akuchita utumiki wa nthaŵi zonse m’madera ovuta kwambiri. Wadwalapo mobwerezabwera matenda aakulu kwambiri, kuphatikizapo kansa. Kodi n’chiyani chimam’thandiza kupirira nsautso? Iye anati: “Ndimafunika kupeza nthaŵi yokhala ndekha. Ndikatopa kwambiri n’kufika poti sindikuganizanso bwinobwino ndimafuna kungokhala duu pandekha, n’kumaŵerenga ndiponso kupumula.” Nzeru ndiponso kulingalira kumatithandiza kudziŵa ndiponso kuthana ndi mavuto athu ndipo tikatero timapeŵa kutopa mwauzimu.

Yehova Mulungu Amatipatsa Mphamvu

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani kusamalira thanzi lathu lauzimu kuli kofunika kwambiri? (b) Kodi pa zochita zathu za tsiku ndi tsiku payenera kukhala zinthu zotani?

16 Kusamalira thanzi lathu lauzimu n’kofunika kwambiri. Tikakhala paubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu, tingathe kutopa, koma kumulambira sikumatilemetsa. Yehova ndi amene “alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.” (Yesaya 40:28, 29) Mtumwi Paulo amene anadzionera yekha kuti mawu ameneŵa ndi oona, analemba kuti: “Sitifoka koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wam’kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.”​—2 Akorinto 4:16.

17 Ganizirani zimene mawu akuti “tsiku ndi tsiku” akusonyeza. Akusonyeza kuti tsiku ndi tsiku tiyenera kugwiritsira ntchito zinthu zimene Yehova watipatsa. Mmishonale wina amene wakhala akutumikira mokhulupirika kwa zaka 43 wakhala akutopa ndiponso kukhumudwa. Koma sanalefuke. Iye anati: “Chakhala chizoloŵezi changa kudzuka m’maŵa kwambiri n’cholinga choti ndisanayambe ntchito iliyonse, ndipemphere kwa Yehova ndi kuŵerenga Mawu ake. Chizoloŵezi cha tsiku ndi tsiku chimenechi chandithandiza kupirira mpaka pano.” Zoonadi, tingadalire mphamvu zothandiza za Yehova ngati nthaŵi zonse, inde “tsiku ndi tsiku,” timapemphera kwa iye ndi kusinkhasinkha za makhalidwe ake apamwamba ndiponso malonjezo ake.

18. Kodi Baibulo limawalimbikitsa motani anthu okhulupirika amene akalamba kapena amene akudwala?

18 Izi n’zothandiza kwambiri makamaka kwa anthu amene ataya mtima chifukwa cha ukalamba ndiponso chifukwa cha matenda. Anthu ameneŵa angavutike maganizo kwambiri, osati chifukwa chodziyerekezera ndi ena, koma chifukwa chodziyerekezera ndi mmene analili kale. N’zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti Yehova amaona kuti anthu okalamba n’ngofunika. Baibulo limati: “Imvi ndiyo korona waulemu, idzapezedwa m’njira yachilungamo.” (Miyambo 16:31) Yehova amadziŵa zinthu zimene sitingathe kuchita ndipo amayamikira kwambiri tikamamulambira ndi mtima wonse ngakhale kuti ndife ofooka. Ndipo Mulungu sadzaiŵala mpaka kalekale ntchito zabwino zomwe tinachita kale. Malemba amatitsimikizira kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.” (Ahebri 6:10) Tonsefe timasangalala kwambiri kukhala ndi anthu amene akhala okhulupirika kwa Yehova kwa zaka zambiri!

Musaleme

19. Kodi timapindula motani chifukwa chochita ntchito zambiri zabwino?

19 Anthu ambiri amakhulupirira kuti kugwira ntchito zolimba nthaŵi ndi nthaŵi kungathandize munthu kuti asamatope. Nakonso kuchita zinthu zauzimu nthaŵi zonse kungatithandize kuti tisamatope mwamaganizo ndiponso mwauzimu. Baibulo limati: “Tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka. Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:9, 10) Ganizirani zimene mawu akuti ‘kuchita zabwino’ ndi ‘kuchitira chokoma’ akusonyeza. Mawu ameneŵa akusonyeza kuti tiyenera kuchita kanthu kenakake. Kuchitira ena zinthu zabwino kungathandizedi kuti tisalefuke pamene tikutumikira Yehova.

20. Kuti tipeŵe kutaya mtima, kodi tiyenera kupeŵa anthu otani?

20 Mosiyana ndi mfundoyi, kucheza ndiponso kuchita zinthu ndi anthu amene amanyalanyaza malamulo a Mulungu kungakhale mtolo wotopetsa. Baibulo limatichenjeza kuti: “Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu; koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake.” (Miyambo 27:3) Kuti tisataye mtima kapenanso kutopa, ndi bwino kupeŵa kucheza ndi anthu amene amakonda kuganizira zinthu zofooketsa ndiponso kukonda kutola ena zifukwa.

21. Kodi anthu ena tingawalimbikitse motani pamisonkhano yachikristu?

21 Misonkhano yachikristu ndi njira yotipatsira mphamvu zauzimu imene Yehova anakonza. Pamisonkhanoyi timapeza mipata yabwino kwambiri yolimbikitsirana kudzera m’malangizo ndiponso macheza abwino. (Ahebri 10:25) Onse mumpingo ayenera kuyesetsa kukhala olimbikitsa akamayankha pamisonkhano kapena akamalankhula ali papulatifomu. Anthu amene amatsogolera pophunzitsa ndiwo ali ndi udindo waukulu makamaka pankhani yolimbikitsa ena. (Yesaya 32:1, 2) Ngakhale patakhala kuti pakufunika kulimbikitsa kapena kudzudzula, kamvekedwe ka mawu olangizawo kayenera kukhala kolimbikitsa. (Agalatiya 6:1, 2) Chikondi chomwe tili nacho pa anthu ena chingatithandize kwambiri kuti titumikire Yehova popanda kutopa.​—Salmo 133:1; Yohane 13:35.

22. Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, kodi n’chifukwa chiyani tingakhale olimbika mtima?

22 Kulambira Yehova m’nthaŵi zamapeto zino kumafunikanso kuchita ntchito. Ndipo Akristu nawonso amatopa ndi kupwetekedwa maganizo, ndiponso kusautsidwa mtima. Popeza kuti ndife anthu opanda ungwiro, ndife ofooka, ngati zipangizo zadothi. Koma Baibulo limati: “Tili nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.” (2 Akorinto 4:7) Inde, timatopa, koma tisamalefuke kapena kulema ngakhale pang’ono. M’malo mwake, tiyeni ‘tinene molimbika mtima [kuti], Mthandizi wanga ndiye Ambuye.’​—Ahebri 13:6.

Kubwereza Mwachidule

• Kodi ndi zinthu zina ziti zolemetsa zomwe tingatule?

• Kodi tingatani kuti tichitire “chabwino” Akristu anzathu?

• Kodi Yehova amatithandiza motani tikataya mtima?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Yesu ankadziŵa kuti atumwi akanavutika maganizo chifukwa chotaya mtima kwa nthaŵi yaitali

[Chithunzi patsamba 24]

Ena achepetsa zinthu zimene amakonda kuchita panthaŵi yopuma ndiponso ntchito zina zosafunikira kwenikweni

[Chithunzi patsamba 26]

Ngakhale kuti pali zinthu zina zimene sitingathe kuchita, Yehova amayamikira kwambiri tikamamulambira ndi mtima wonse