Kodi Muyenera Kukonzera Ana Anu Cholowa Chotani?
Kodi Muyenera Kukonzera Ana Anu Cholowa Chotani?
PAVLOS, bambo wa banja lake wa kum’mwera kwa Ulaya sapezeka pakhomo kuti acheze ndi mkazi wake ndi ana ake. Ana akewo ndi atsikana aŵiri, wa zaka 13 ndi wa zaka 11, ndi mnyamata mmodzi wa zaka 7. Masiku seveni pa mlungu Pavlos amagwira ntchito usana ndi usiku kuti apeze ndalama zokwanira zoti adzakwanitsire kuchita zimene akufuna. Akufuna kuti adzagulire ana ake aakazi aŵiri nyumba, ndipo akufuna adzayambitse bizinesi yaing’ono ya mwana wake wamwamuna. Mkazi wake Sofia amagwira ntchito mwakhama kuti apeze nsalu zosiyanasiyana, ziwiya za kukhitchini, mbale ndi makapu adothi, masipuni, mipeni, mafoloko ndi zina zotero zoti ana awo akadzakula azidzagwiritsa ntchito. Akafunsidwa chifukwa chimene amagwirira ntchito mwakhama choncho, amayankhira limodzi kuti, “Tikuchitira ana athu!”
Mofanana ndi Pavlos ndi Sofia, makolo ambiri padziko lonse lapansi amayesetsa kukonzera ana awo zinthu kuti adzapeze poyambira. Ena amasunga ndalama zoti anawo adzagwiritse ntchito m’tsogolo. Ena amaonetsetsa kuti ana awo aphunzire bwino ndipo aphunzire luso limene lidzawathandize m’tsogolo. Ngakhale kuti makolo ambiri amaona kuti mphatso zimenezi zimasonyeza chikondi chawo, kupeza zinthu zoterozo nthaŵi zambiri kumachititsa makolo kukhala pampanipani kuti achite zimene achibale awo, anzawo, ndi anthu okhala nawo m’deralo amawayembekezera kuchita. Choncho makolo amene amakhudzidwa ndi zimenezi amafunsa moyenerera kuti, ‘Kodi tiyenera kukonzera ana athu zinthu zotani?’
Kukonzekera za M’tsogolo
N’chinthu chachibadwa komanso chogwirizana ndi Malemba kuti makolo achikristu akonzekere tsogolo la ana awo. Mtumwi Paulo anauza Akristu a m’tsiku lake kuti: “Si udindo wa ana kusungira makolo awo chuma, koma ndi udindo wa makolo kusungira ana awo chuma.” (2 Akorinto 12:14, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Paulo ananenanso kuti kusamalira ana si udindo wamaseŵera. Iye analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Nkhani zambirimbiri za m’Baibulo zimasonyeza kuti nkhani ya cholowa inali nkhani yofunika pakati pa atumiki a Mulungu m’nthaŵi za m’Baibulo.—Rute 2:19, 20; 3:9-13; 4:1-22; Yobu 42:15.
Koma nthaŵi zina makolo amakhala ndi nkhaŵa yofuna kupatsa ana awo cholowa chachikulu. Chifukwa chiyani? Manolis, bambo wa banja lake yemwe anasamuka kum’mwera kwa Ulaya kupita ku United States akufotokoza chifukwa chimodzi. Iye akuti: “Makolo
amene anavutika ndi nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, njala, ndi umphaŵi amafunitsitsa kuti ana awo akhale ndi moyo wabwino kuposa umene anali nawo iwowo.” Iye akuwonjezera kuti: “Chifukwa choona molakwika udindo wawo ndi kufunitsitsa kuti ana awo adzapeze poyambira pabwino, makolo ena amadzipweteka okha.” Indedi, makolo ena amadzimana zinthu zofunika pamoyo n’kumakhala moyo wovutika n’cholinga choti asungire ana awo katundu wam’tsogolo. Koma kodi n’chinthu chanzeru kuti makolo akhale ndi moyo woterowo?‘Zachabe ndi Choipa Chachikulu’
Mfumu Solomo ya ku Israyeli wakale inachenjezapo anthu za cholowa. Inalemba kuti: “Ndipo ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzam’siyira izo munthu wina amene adzanditsata. Ndipo ndani adziŵa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe. . . . Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziŵa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirapo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu.”—Mlaliki 2:18-21.
Monga momwe Solomo anafotokozera, anthu amene alandira cholowa akhoza kusachiyamikira kwenikweni chifukwa choti iwowo sanachivutikire. Zotsatirapo zake n’zoti anthu amene alandira cholowa angapeputse zinthu zimene makolo awo anavutika kuti azipeze. Mwina angawononge kumene katundu amene anachita kumuvutikira choteroyo. (Luka 15:11-16) Zimenezo zingakhaledi ‘zachabe ndi choipa chachikulu.’
Nkhani ya Cholowa Ingayambitse Dyera
Palinso mfundo ina imene makolo ayenera kuiganizira. M’madera amene anthu amakhudzidwa kwambiri ndi kulandira cholowa ndiponso malowolo, ana akhoza kuyamba dyera n’kumafuna kuti apatsidwe chuma chambiri, kapena katundu yemwe bambo amapatsa mwana wake wamkazi akamakwatiwa monga mphatso ya mkamwini wake, angafune katundu wambiri kuposa amene makolowo angakwanitse. Loukas, bambo wa banja lake wa ku Greece anati: “Tsoka kwa atate amene ali ndi ana aakazi aŵiri kapena atatu. Ana aakazi angamayerekezere zimene atate awo angathe kupereka ndi zimene makolo ena amaunjikira ana awo ‘moolowa manja.’ Iwo anganene kuti sadzapeza mabanja abwino ngati sakhala ndi katundu wokwanira wodzapereka ku banja la mwamuna.” *
Manolis, amene tamutchula kale uja, anati: “Mnyamata akhoza kumangokhalabe
pachibwenzi ndi mtsikana osamukwatira mpaka pamene bambo a mtsikanayo adzamulonjeze mnyamatayo katundu winawake, nthaŵi zambiri malo, nyumba, kapena ndalama zambiri. Zingafike pokhala ngati kuba kumene.”Baibulo limaletsa dyera lamtundu uliwonse. Solomo analemba kuti: “Cholowa chingalandiridwe msangamsanga (“mwadyera,” NW) poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala.” (Miyambo 20:21) Mtumwi Paulo anatsindika kuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama.”—1 Timoteo 6:10; Aefeso 5:5.
‘Nzeru Pamodzi ndi Cholowa’
N’zoona kuti cholowa chimathandiza, koma nzeru imathandiza kwambiri kuposa katundu. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Nzeru ili yabwino pamodzi ndi cholowa . . . Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:11, 12; Miyambo 2:7; 3:21) Ngakhale kuti ndalama zimamutetezako munthu, kumuthandiza kuti azipeza zimene akufunikira, zingathebe kutayika. Koma nzeru, kapena kuti kudziŵa kugwiritsa ntchito zimene munthu akudziŵa kuti athane ndi mavuto kapena akwaniritse zolinga zinazake, zingamuteteze munthu kuti asachite zinthu zopusa. Ngati nzeruzo zazikidwa pa kuopa Mulungu koyenera, zingamuthandize munthu kupeza moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu limene latsala pang’ono kubwera. Chimenecho ndi cholowadi chamtengo wapatali!—2 Petro 3:13.
Makolo achikristu amasonyeza nzeru zoterozo mwa kuika zinthu pa malo oyenera pa moyo wawo ndi wa ana awo. Katundu amene makolo akusungira ana awo sayenera kutenga malo oyamba kuposa zinthu zauzimu. Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu [wa Mulungu] ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Makolo amene amakhala ndi zolinga zauzimu m’banja lawo lachikristu angayembekezere kudalitsidwa kwambiri. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amako akondwere, amako wakukubala asekere.”—Miyambo 23:24, 25.
Cholowa Chosatha
Kwa Aisrayeli akale, nkhani zokhudza cholowa zinali zofunika kwambiri. (1 Mafumu 21:2-6) Komabe, Yehova anawalimbikitsa kuti: “Mawu awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Makolo achikristu nawonso akuuzidwa kuti: “Muwalere [ana anu] m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.
Makolo amene amaona zinthu mwauzimu amadziŵa kuti kusamalira banja lawo kumaphatikizapo kuwaphunzitsa zinthu zochokera m’Baibulo. Andreas, bambo wa ana atatu, anati: “Ana akaphunzira kugwiritsa ntchito mfundo za Mulungu pa moyo wawo, amakhala okonzeka bwino kudzathana ndi zimene adzakumane nazo m’tsogolo.” Cholowa choterocho chimawathandizanso kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mlengi wawo.—1 Timoteo 6:19.
Kodi mwaganizirapo zokonzekera tsogolo lauzimu la mwana wanu? Mwachitsanzo, kodi makolo angachite chiyani ngati mwana wawo akuchita utumiki wa nthaŵi zonse? Ngakhale kuti mtumiki wa nthaŵi zonse sayenera kukakamiza kapena kuyembekezera anthu kumupatsa ndalama, makolo achikondi angamuthandize pa “zosoŵa” zake kuti apitirize utumiki wa nthaŵi zonse. (Aroma 12:13; 1 Samueli 2:18, 19; Afilipi 4:14-18) Mtima wothandiza woterowo mwachidziŵikire ungasangalatse Yehova.
Choncho kodi makolo ayenera kukonzera ana awo chiyani? Kuwonjezera pa kuwapezera zosoŵa zawo, makolo achikristu amaonetsetsa kuti ana awo alandire cholowa chabwino chauzimu chimene chidzawathandiza mpaka kalekale. Akatero, ndiye kuti mawu a pa Salmo 37:18 adzakwaniritsidwa kwa iwo: “Yehova adziŵa masiku a anthu angwiro: ndipo chosiyira [cholowa] chawo chidzakhala chosatha.”
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Mfundo zomwe zatchulidwa m’ndime ino ndi ndime yotsatira zikusonyeza miyambo ya kumayiko kwina kumene banja la mtsikana limayenera kupereka katundu kapena mphatso ku banja la mwamuna. M’mayiko ambiri ku Africa kuno mwamuna kapena banja lake ndi amene amayenera kupereka malowolo ndi mphatso ku banja la mtsikana. Komabe mfundo zimene zatchulidwazo zikukhudza miyambo iŵiri yonseyi.
[Zithunzi pamasamba 26, 27]
Kodi ana anu mukuwafunira tsogolo lotani?